Kodi Tizikhala Bwanji ndi Anzathu?
“Zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muwachitire zimenezo.”—LUKA 6:31.
1, 2. (a) Kodi ulaliki wapaphiri unali wotani? (b) Kodi tikambirana chiyani m’nkhani ino ndi yotsatira?
YESU KHRISTU analidi Mphunzitsi Waluso. Nthawi ina adani ake achipembedzo atatumiza anthu kukamugwira, anabwerera chimanjamanja ndipo anati: “Palibe munthu analankhulapo ngati iyeyu n’kale lonse.” (Yoh. 7:32, 45, 46) Nthawi inanso pamene Yesu anakamba nkhani yochititsa chidwi ndi pa ulaliki wapaphiri. Ulalikiwu unalembedwa mu Uthenga Wabwino wa Mateyo, kuyambira chaputala 5 mpaka 7. Umapezekanso pa Luka 6:20-49.a
2 Mwina mfundo yodziwika kwambiri muulaliki umenewu ndi yokhudza mmene tiyenera kukhalira ndi anzathu. Yesu anati: “Zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muwachitire zimenezo.” (Luka 6:31) Iye anachitiradi anthu zinthu zabwino zambiri. Mwachitsanzo, anachiritsa odwala ndi kuukitsa akufa. Koma anthu anadalitsidwa kwambiri pamene analandira uthenga wake wabwino. (Werengani Luka 7:20-22.) Mofanana ndi Yesu, ifenso Mboni za Yehova timasangalala tikamalalikira za Ufumu. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Munkhani ino ndi yotsatira, tikambirana mawu a Yesu okhudza ntchito yolalikira ndi mfundo zinanso za muulaliki wapaphiri za mmene tiyenera kukhalira ndi ena.
Khalani Ofatsa
3. Kodi munthu wofatsa tingamudziwe bwanji?
3 Yesu anati: “Osangalala ali iwo amene ali ofatsa, popeza adzalandira dziko lapansi.” (Mat. 5:5) M’Malemba, kukhala wofatsa sikutanthauza kupanda mphamvu. Munthu wofatsa amachita zimene Mulungu amafuna ndipo amadziwika ndi mmene amakhalira ndi anthu ena. Mwachitsanzo, iye ‘sabwezera choipa pa choipa.’—Aroma 12:17-19.
4. Kodi ofatsa amakhala osangalala chifukwa chiyani?
4 Ofatsa amakhala osangalala chifukwa “adzalandira dziko lapansi.” Yesu, yemwe anali “wofatsa ndi wodzichepetsa,” ndiye “wolandira zinthu zonse monga cholowa” ndipo ndiye woyamba kulandira dziko lapansi. (Mat. 11:29; Aheb. 1:2; Sal. 2:8) Baibulo linalosera kuti “mwana wa munthu,” yemwe ndi Mesiya, adzalamulira pamodzi ndi anzake mu Ufumu wakumwamba. (Dan. 7:13, 14, 21, 22, 27) Akhristu ofatsa odzozedwa okwana 144,000, omwe ndi “olowa ufumu anzake a Khristu,” adzalandiranso dziko lapansi. (Aroma 8:16, 17; Chiv. 14:1) Anthu enanso ofatsa adzapatsidwa moyo wosatha ndipo adzakhala pa dziko lapansi pano Ufumuwo ukadzayamba kulamulira.—Sal. 37:11.
5. Kodi kukhala ofatsa ngati Khristu kumatithandiza bwanji?
5 Tikakhala munthu wovuta, timasowetsa mtendere anzathu ndipo iwo amatithawa. Koma tikakhala ofatsa ngati Khristu, timakhala bwino ndi ena ndipo timalimbikitsa anzathu mumpingo. Kufatsa ndi chimodzi cha zipatso zimene mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu imabala mwa ife ‘tikamakhala ndi kuyenda mwa mzimu.’ (Werengani Agalatiya 5:22-25.) Ndithudi, ifenso timafuna kukhala m’gulu la anthu ofatsa amene amatsogoleredwa ndi mzimu woyera wa Yehova.
Achifundo Amakhala Osangalala
6. Kodi anthu “achifundo” amatani?
6 Muulaliki wake wapaphiri, Yesu ananenanso kuti: “Osangalala ali iwo amene ali achifundo, popeza adzachitiridwa chifundo.” (Mat. 5:7) Anthu “achifundo” amaganizira ena ndiponso amamvera chisoni anthu ovutika. Yesu mozizwitsa anathandiza anthu ovutika chifukwa ‘chowamvera chifundo’ kapena chifukwa ‘chogwidwa ndi chifundo.’ (Mat. 14:14; 20:34) Choncho, kuganizira ena kuyenera kutipangitsa kuwachitira chifundo.—Yak. 2:13.
7. Kodi Yesu anachita zotani chifukwa cha chifundo?
7 Pamene khamu la anthu linakumana ndi Yesu akupita kokapuma, iye “anawamvera chifundo, chifukwa anali ngati nkhosa zopanda m’busa.” Choncho, “anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.” (Maliko 6:34) Nafenso timakhala osangalala tikamauza ena uthenga wa Ufumu ndi za chifundo chachikulu cha Mulungu.
8. N’chifukwa chiyani anthu achifundo amakhala osangalala?
8 Achifundo amakhala osangalala chifukwa chakuti ‘amachitiridwa chifundo.’ Tikamachitira anthu chifundo, iwonso amatichitira chifundo. (Luka 6:38) Ndiponso Yesu anati: “Ngati mukhululukira anthu zolakwa zawo, Atate wanu wa kumwamba adzakhululukiranso inu.” (Mat. 6:14) Mulungu amakhululuka machimo a anthu achifundo okha, n’chifukwa chake iwo amakhala osangalala.
N’chifukwa Chiyani Anthu ‘Odzetsa Mtendere’ Amakhala Osangalala?
9. Ngati ndife anthu odzetsa mtendere, kodi tiyenera kumachita zotani?
9 Yesu anatchulanso chinthu china chimene chimapangitsa anthu kukhala osangalala. Anati: “Osangalala ali iwo amene adzetsa mtendere, popeza adzatchedwa ‘ana a Mulungu.’” (Mat. 5:9) Ngati ndife anthu odzetsa mtendere, sitingachite kapena kulekerera chilichonse chimene ‘chimagawanitsa mabwenzi,’ monga miseche. (Miy. 16:28, NW) Timayesetsa kudzetsa mtendere mwa zonena ndi zochita zathu, mumpingo kapena kunja kwa mpingo. (Aheb. 12:14) Ndipo timayesetsa kwambiri kukhala pamtendere ndi Yehova Mulungu.—Werengani 1 Petulo 3:10-12.
10. N’chifukwa chiyani anthu ‘odzetsa mtendere’ amakhala osangalala?
10 Yesu anati ‘odzetsa mtendere’ amakhala osangalala “popeza adzatchedwa ‘ana a Mulungu.’” Chifukwa chokhulupirira Yesu monga Mesiya, Akhristu odzozedwa amapatsidwa “mphamvu zokhala ana a Mulungu.” (Yoh. 1:12; 1 Pet. 2:24) Nanga bwanji za “nkhosa zina” za Yesu zomwenso ndi zodzetsa mtendere? Kwa iwowa, Yesu adzakhala “Atate Wosatha” mu ulamuliro wake wa zaka 1,000. Nthawi imeneyi Yesu adzalamulira limodzi ndi anzake kumwamba. (Yoh. 10:14, 16; Yes. 9:6; Chiv. 20:6) Kumapeto kwa ulamuliro wakewo, anthu odzetsa mtendere adzakhala ana a Mulungu enieni a padziko lapansi.—1 Akor. 15:27, 28.
11. Tikamatsogoleredwa ndi “nzeru yochokera kumwamba,” kodi timakhala bwanji ndi anzathu?
11 Kuti tikhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova, “Mulungu wa mtendere,” tiyenera kutsanzira makhalidwe ake, kuphatikizaponso kukonda kwake mtendere. (Afil. 4:9) Tikamatsogoleredwa ndi “nzeru yochokera kumwamba,” timakhala mwamtendere ndi anzathu. (Yak. 3:17) Mapeto ake, timakhala odzetsa mtendere osangalala.
“Onetsani Kuwala Kwanu”
12. (a) Kodi Yesu ananena chiyani za kuwala kwauzimu? (b) Kodi tingaonetse bwanji kuwala kwathu?
12 Njira yabwino kwambiri yochitira ena zabwino ndi kuwaphunzitsa za kuwala kwauzimu kochokera kwa Mulungu. (Sal. 43:3) Yesu anauza ophunzira ake kuti iwo ndi “kuwala kwa dziko” ndipo anawalangiza kuti ayenera kuonetsa kuwala kwawo kuti anthu aone ‘ntchito zawo zabwino’ zimene amachitira ena. Zimenezi zinachititsa kuti kuwala kwauzimu kuonekere “pamaso pa anthu,” kapena kuti anthuwo apindule nako. (Werengani Mateyo 5:14-16.) Masiku ano timaonetsa kuwala kwathu mwa kukhala bwino ndi anzathu ndiponso mwa kulalikira uthenga wabwino “m’dziko lonse” kapena kuti “m’mitundu yonse.” (Mat. 26:13; Maliko 13:10) Ndi mwayi waukulu kugwira nawo ntchito imeneyi.
13. Kodi anthu amatizindikira chifukwa chiyani?
13 Yesu anati: “Mzinda ukakhala paphiri subisika.” Mzinda uliwonse umene uli pa phiri suvuta kuuona. Mofanana ndi zimenezi, anthu amatizindikira chifukwa cha ntchito zathu zabwino monga alaliki a Ufumu ndiponso chifukwa cha khalidwe lathu loyera ndi lodziletsa.—Tito 2:1-14.
14. (a) Kodi nyale zakale zinali zotani? (b) Kodi tingatani kuti tisabise kuwala kwauzimu pansi pa “mtanga wopimira”?
14 Yesu ananena za kuyatsa nyale ndi kuiika poonekera kuti iunikire m’nyumba, m’malo moivindikira ndi mtanga. Nthawi imeneyo nyale inali youmbidwa ndi dongo ndipo inali kukhala ndi kachingwe kokoka mafuta (amaolivi). Nthawi zambiri anali kuika nyaleyo pathabwa kapena pakachitsulo ndipo “imaunikira onse m’nyumbamo.” Anthu sakanayatsa nyale ndi kuivindikira ndi “mtanga wopimira” womwe unali kukhala wa malita pafupifupi 9. Yesu sanafune kuti ophunzira ake azibisa kuwala kwawo kwauzimu ndi mtanga wophiphiritsira. Choncho, tiyenera kuonetsa kuwala kwathu ndipo tisalole chitsutso kapena chizunzo kutichititsa kubisa choonadi chathu.
15. Kodi ‘ntchito zathu zabwino’ zimakhudza bwanji anthu ena?
15 Atanena za nyale, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Mofananamo onetsani kuwala kwanu pamaso pa anthu, kuti aone ntchito zanu zabwino ndi kuti alemekeze Atate wanu wa kumwamba.” Poona ‘ntchito zathu zabwino,’ ena ‘amalemekeza’ Mulungu mwa kukhala atumiki ake. Zimenezi zimatilimbikitsa kupitirizabe ‘kuwala monga zounikira m’dzikoli.’—Afil. 2:15.
16. Kodi timafunika kuchita chiyani kuti tikhale “kuwala kwa dziko”?
16 Kuti tikhale “kuwala kwa dziko,” timafunika kugwira nawo ntchito yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira. Koma pali chinthu chinanso chimene tiyenera kuchita. Mtumwi Paulo anati: “Yendanibe ngati ana a kuwala. Pakuti zipatso za kuwala ndizo chilichonse chabwino ndi chilichonse cholungama ndi choona.” (Aef. 5:8, 9) Tiyenera kukhala zitsanzo pakhalidwe labwino. Indedi, tifunika kumvera malangizo a Petulo akuti: “Sungani khalidwe labwino pakati pa anthu amitundu, kuti pamene akukunenerani monga ochita zoipa, pa mapeto pake iwo pokhala mboni zimene zikuona ndi maso zochita zanu zabwino, adzatamande Mulungu m’tsiku lake la kuyendera.” (1 Pet. 2:12) Ndiyeno munthu ayenera kuchita chiyani ngati wayambana ndi wokhulupirira mnzake?
“Pita Ukayanjane ndi M’bale Wako”
17-19. (a) Kodi “mphatso” yotchulidwa pa Mateyo 5:23, 24, inali chiyani? (b) Kodi kuyanjana ndi m’bale wathu n’kofunika motani, ndipo Yesu anasonyeza bwanji zimenezi?
17 Muulaliki wake wapaphiri, Yesu anachenjeza ophunzira ake kuti asamapsere mtima m’bale wawo kapena kumunenera mawu oipa achipongwe. M’malo mwake anawalangiza kuti asamachedwe kukhazikitsa mtendere ndi m’bale amene wakhumudwa. (Werengani Mateyo 5:21-25.) Tingachite bwino kuganizira mwakuya malangizo a Yesu. Mukanakhala kuti ndinuyo amene mukukapereka nsembe kuguwa ndipo mwakumbukira kuti mwalakwirana ndi m’bale wina, kodi mukanatani? Munayenera kusiya mphatso yanu kuguwa komweko ndi kupita kaye kukayanjana ndi m’bale wanuyo. Pambuyo pake, mukanabwerera ndi kukapereka mphatso yanu.
18 Kawirikawiri, “mphatso” imene Yesu ananena inali nsembe imene munthu anali kupereka ku kachisi wa Yehova. Nsembe zanyama zinali zofunika kwambiri, chifukwa m’Chilamulo cha Mose, Aisiraeli analamulidwa ndi Mulungu kupereka nsembe pa kulambira kwawo. Koma ngati munthu wakumbukira kuti walakwirana ndi m’bale wake, anafunika kaye kuyanjana ndi m’bale wakeyo asanapereke nsembe. Yesu anati: “Siya mphatso yako patsogolo pa guwa la nsembe pomwepo. Pita ukayanjane ndi m’bale wako choyamba, ndipo ukabwerako, pereka mphatso yako.” Kuyanjananso ndi m’bale wako kunayenera kukhala koyambirira kuposa zimene zinalembedwa m’Chilamulo.
19 Sikuti Yesu anangonena nsembe zamtundu winawake kapena zolakwa zinazake zokha ayi. Choncho, ngati munthu wakumbukira kuti walakwirana kenakake ndi m’bale wake, anayenera kuimika kaye nsembe iliyonse. Ngati nsembeyo inali nyama yamoyo, inali kusiyidwa “patsogolo pa guwa la nsembe” pabwalo la ansembe kukachisi. Anthuwo akayanjana, munthu wolakwira mnzakeyo akanatha kubwerera ndi kukapereka nsembe.
20. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kuyanjana mwamsanga ndi m’bale amene watikwiyitsa?
20 Malinga ndi mmene Mulungu amaonera, kuyanjana ndi m’bale wathu n’kofunika kwambiri pa kulambira koona. Nsembe zanyama zinali zopanda phindu kwa Yehova ngati operekawo sanali kuchitira zabwino abale awo. (Mika 6:6-8) N’chifukwa chake Yesu analimbikitsa ophunzira ake kuti ‘azithetsa nkhani mofulumira.’ (Mat. 5:25) Pankhani yomweyi, Paulo anati: “Kwiyani, koma musachimwe. Dzuwa lisalowe muli chikwiyire, ndipo musam’patse malo Mdyerekezi.” (Aef. 4:26, 27) Tikakwiya pa zifukwa zomveka, tiyenera kuyesetsa kuthetsa nkhaniyo mwachangu kuti tisakhale tili chikwiyire ndi kum’patsa malo Mdyerekezi.—Luka 17:3, 4.
Muzilemekeza Ena
21, 22. (a) Kodi tingagwiritse ntchito bwanji malangizo a Yesu amene takambiranawa? (b) Kodi m’nkhani yotsatira tidzakambirana chiyani?
21 Takambirana mfundo zina ndi zina za muulaliki wa Yesu wapaphiri ndipo zimenezi ziyenera kutithandiza kukomerana mtima ndiponso kulemekeza anthu ena. Ngakhale kuti tonsefe ndi opanda ungwiro, tingatsatirebe malangizo a Yesu amenewa chifukwa iye pamodzi ndi Atate wake wakumwamba, sayembekezera kuti tizichita zimene sitingathe. Pemphero, khama, ndiponso thandizo la Yehova Mulungu, zingatithandize kukhala ofatsa, achifundo ndi odzetsa mtendere. Zingatithandizenso kuonetsa kuwala kwauzimu kumene kumalemekeza Yehova. Komanso zingatithandize kukhala mwamtendere ndi abale athu ngakhale zinthu zitavuta.
22 Kuti Yehova avomereze kulambira kwathu, timafunika kuchitira anzathu zabwino. (Maliko 12:31) M’nkhani yotsatira, tidzakambirana mfundo zinanso za muulaliki wapaphiri zimene zingatithandize kuchitira ena zabwino. Pambuyo posinkhasinkha mfundo zochititsa chidwi za muulaliki wa Yesu wapaphiri, tingadzifunse kuti, ‘Kodi ineyo ndimakhala bwanji ndi anthu ena?’
[Mawu a M’munsi]
a Mungachite bwino kuwerenga malembawa paphunziro lanu laumwini, musanawerenge nkhani ino ndi yotsatira.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi kukhala wofatsa kumatanthauza chiyani?
• Kodi “achifundo” amakhala osangalala chifukwa chiyani?
• Kodi tingaonetse bwanji kuwala kwathu?
• N’chifukwa chiyani tiyenera kufulumira ‘kuyanjananso ndi m’bale wathu’?
[Chithunzi patsamba 4]
Kulengeza uthenga wa Ufumu ndi njira yabwino yoonetsera kuwala kwathu
[Chithunzi patsamba 5]
Akhristu ayenera kukhala zitsanzo pakhalidwe labwino
[Chithunzi patsamba 6]
Muyenera kuyesetsa kuyanjana ndi m’bale wanu