MUTU 128
Pilato Komanso Herode Sanamupeze Yesu ndi Mlandu
MATEYU 27:12-14, 18, 19 MALIKO 15:2-5 LUKA 23:4-16 YOHANE 18:36-38
PILATO KOMANSO HERODE ANAFUNSA YESU MAFUNSO
Yesu sanabise kwa Pilato kuti iye ndi mfumu. Ngakhale kuti anayankha zimenezi, ufumu wake sunali woti ulowe m’malo mwa ulamuliro wa Aroma. Yesu ananena kuti: “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino. Ufumu wanga ukanakhala mbali ya dziko lino, atumiki anga akanamenya nkhondo kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda. Koma ufumu wanga si wochokera pansi pano ayi.” (Yohane 18:36) Ndi zoona kuti Yesu ndi Mfumu koma Ufumu wake si wochokera padzikoli.
Koma Pilato sanasiyire nkhaniyo pomwepo. Iye anafunsanso kuti: “Chabwino, koma kodi ndiwe mfumu?” Yesu anathandiza Pilato kudziwa kuti akuganiza molondola chifukwa anamuyankha kuti: “Mukunena nokha kuti ndine mfumu. Chimene ndinabadwira, ndiponso chimene ndinabwerera m’dziko, ndicho kudzachitira umboni choonadi. Aliyense amene ali kumbali ya choonadi amamvera mawu anga.”—Yohane 18:37.
Nthawi ina Yesu anauza Tomasi kuti: “Ine ndine njira, choonadi ndi moyo.” Ndiyeno pa nthawiyi Pilato anamva Yesu akunena kuti anatumizidwa padziko lapansi kuti adzachitire umboni “choonadi” ndipo choonadi chimenechi ndi chonena za Ufumu wake. Yesu anali wokonzeka kukhala wokhulupirika poikira kumbuyo choonadichi ngakhale kuti zimenezi zinachititsa kuti aphedwe. Pilato anamufunsa kuti: “Choonadi n’chiyani?” koma sanadikire kuti Yesu amufotokozere. Iye ankaona kuti wamva mfundo zokwanira moti atha kumuweruza Yesu.—Yohane 14:6; 18:38.
Pilato anabwereranso panja pomwe panali gulu la anthu. Iye anauza ansembe aakulu komanso anthu ena omwe anali nawo kuti: “Sindikupeza mlandu uliwonse mwa munthu uyu.” Pamene ankanena mawu amenewa Yesu anali ataima pambali pake. Gulu la anthulo linakwiya kwambiri ndi zimene Pilato ananenazi ndipo linkakuwa kuti: “Iyeyu akusokoneza anthu mwa kuphunzitsa mu Yudeya monse, ngakhalenso kuyambira ku Galileya mpaka kudzafika kuno.”—Luka 23:4, 5.
Pilato ayenera kuti anadabwa kwambiri ataona kuti Ayudawo ankakakamira kuti Yesu ali ndi mlandu. Pamene ansembe aakulu komanso akulu ankakuwa, Pilato anafunsa Yesu kuti: “Kodi sukumva zonse zimene akukunenezazi?” (Mateyu 27:13) Yesu sanayankhe kalikonse. Ngakhale kuti anthu ankamunamizira zinthu zambiri zoipa, Pilato anadabwa kuti pa nthawi yonseyi Yesu anali wodekha.
Ayuda ananena kuti Yesu anasokoneza anthu ‘kuyambira ku Galileya.’ Atamva zimenezi Pilato anadziwa kuti Yesu anali wa ku Galileya. Choncho Pilato anapezerapo mwayi wofuna kuthawa udindo woweruza Yesu. Herode Antipa (yemwe anali mwana wa Herode Wamkulu) ndi amene ankalamulira ku Galileya ndipo pa nthawiyi n’kuti ali ku Yerusalemu ku mwambo wa Pasika. Ndiyeno Pilato anatumiza Yesu kwa Herode. Herode Antipa ndi amene analamula kuti Yohane M’batizi adulidwe mutu. Yohane M’batizi ataphedwa, Herode anamva kuti Yesu akuchita zinthu zodabwitsa moti iye anayamba kuganiza kuti Yesu ndi Yohane ndipo wauka kwa akufa.—Luka 9:7-9.
Herode anasangalala atadziwa kuti akumana ndi Yesu. Sikuti ankasangalala chifukwa chakuti ankafuna kuthandiza Yesu kapenanso kuti ankafuna kumva ngati panalidi zifukwa zomveka zoimbira Yesu mlandu. Iye ankangofuna kuona Yesu ndipo ‘ankayembekezera kuona chizindikiro chimene iye angachite.’ (Luka 23:8) Koma Yesu sanachite zimene Herode ankayembekezera ndipo pamene ankamufunsa mafunso, Yesu sanayankhe chilichonse. Chifukwa chokhumudwa, Herode ndi asilikali ake ‘anapeputsa’ Yesu kapena kuti kumuchititsa manyazi. (Luka 23:11) Anamuveka chovala chonyezimira ndipo anamuchitira zachipongwe. Kenako Herode analamula kuti Yesu abwererenso kwa Pilato. M’mbuyomu, Herode ndi Pilato sankagwirizana koma kungoyambira nthawi imeneyi anayamba kugwirizana.
Yesu atafikanso kwa Pilato, Pilato anasonkhanitsa ansembe aakulu, olamulira a Ayuda komanso gulu la anthu n’kuwauza kuti: “Inetu ndamufunsa pamaso panu, ndipo sindinamupeze ndi chifukwa chomuimbira milandu imene mukumunenezayi. Ndipotu ngakhale Herode sanam’peze ndi mlandu, n’chifukwa chake wam’bweza kwa ife. Ndithudi ameneyu sanachite chilichonse choyenera chilango cha imfa. Choncho ndingomukwapula ndi kumumasula.”—Luka 23:14-16.
Pilato ankafunitsitsa kumasula Yesu atadziwa kuti ansembe anapereka Yesu chifukwa chakuti ankadana naye. Koma panalinso chifukwa china chimene Pilato ankafunira kumasula Yesu. Atakhala pampando wake woweruzira, mkazi wake anamutumizira uthenga wonena kuti: “Nkhani ya munthu wolungamayu isakukhudzeni. Inetu ndavutika kwambiri lero m’maloto [amene Mulungu anamulotetsa] chifukwa cha iyeyu.”—Mateyu 27:19.
Popeza Pilato anali ndi mphamvu zomasula Yesu, kodi anakwanitsadi kuchita zimenezi?