MUTU 9
“Khristu Ndi Mphamvu ya Mulungu”
1-3. (a) Kodi ophunzira a Yesu anakumana ndi zoopsa zotani panyanja ya Galileya, nanga Yesu anatani? (b) N’chifukwa chiyani n’zomveka kuti mtumwi Paulo ananena kuti “Khristu ndi mphamvu ya Mulungu”?
PA NTHAWI ina ophunzira a Yesu anachita mantha kwambiri. Iwo ankawoloka nyanja ya Galileya ndipo mwadzidzidzi panyanjapo panayambika chimphepo. N’zosakayikitsa kuti anali atakumanapo kale ndi mphepo panyanja chifukwa ena mwa iwo anali asodzi odziwa bwino ntchito yawo.a (Mateyu 4:18, 19) Koma imeneyi inali “mphepo yamphamvu,” ndipo inachititsa kuti panyanjapo payambike mafunde akuluakulu. Ophunzirawo anachita mantha ndipo anapalasa ngalawa ndi mphamvu zawo zonse koma mphepoyo inkawaposa mphamvu. Mafunde “ankawomba ngalawayo” ndipo inayamba kudzaza madzi. Ngakhale kuti zinthu zinali chonchi, Yesu anali m’tulo tofa nato kumbuyo kwa ngalawayo chifukwa anali atatopa ndi kuphunzitsa gulu la anthu pa tsikulo. Poopa kufa, ophunzirawo anamudzutsa n’kumupempha kuti: “Ambuye, tipulumutseni tikufa!”—Maliko 4:35-38; Mateyu 8:23-25.
2 Yesu sanachite mantha chifukwa ankadziwa kuti ali ndi mphamvu zoletsa mphepoyo. Choncho anadzudzula mphepo komanso nyanjayo kuti: “Leka! Khala bata!” Nthawi yomweyo, mphepo ndi nyanjayo zinamvera moti mafunde aja anasiya ndipo “panachita bata lalikulu.” Koma ophunzirawo ataona zimenezi anachita mantha kwambiri. Anayamba kufunsana kuti: “Kodi munthu ameneyu ndi ndani kwenikweni?” Zimenezi n’zomveka, nanga ndi munthu uti amene angadzudzule mphepo ndi nyanja ngati kuti akudzudzula mwana wosamvera?—Maliko 4:39-41; Mateyu 8:26, 27.
3 Komatu Yesu sanali munthu wamba. Yehova ankagwiritsa ntchito mphamvu zake pothandiza Yesu m’njira zapadera komanso kumulola kuti azithandiza ena. Mouziridwa ndi Mulungu, mtumwi Paulo ananena moyenerera kuti: “Khristu ndi mphamvu ya Mulungu.” (1 Akorinto 1:24) Kodi Yesu amasonyeza mphamvu za Mulungu m’njira ziti? Nanga timapindula bwanji ndi mmene amagwiritsira ntchito mphamvu zimenezi?
Mphamvu za Mwana Wobadwa Yekha wa Mulungu
4, 5. (a) Kodi Yehova anapatsa Mwana wake wobadwa yekha mphamvu komanso udindo wochita chiyani? (b) Kodi n’chiyani chinkathandiza Mwanayu kuti akwanitse kugwira ntchito yolenga zinthu imene Atate wake anamupatsa?
4 Taganizirani mphamvu zimene Yesu anali nazo asanakhale munthu. Yehova anasonyeza “mphamvu zake zosatha” pamene analenga Mwana wake wobadwa yekha, yemwe kenako ankadziwika kuti Yesu Khristu. (Aroma 1:20; Akolose 1:15) Kenako Yehova anapatsa Mwanayu mphamvu zambiri komanso udindo waukulu ndipo anamugwiritsa ntchito polenga zinthu zina zonse. Ponena za Mwana ameneyu, Baibulo limati: “Zinthu zonse zinakhalako kudzera mwa iye ndipo palibe chinthu ngakhale chimodzi chimene chinakhalapo popanda iyeyo.”—Yohane 1:3.
5 Tikhoza kungomvetsa zochepa chabe zokhudza kukula kwa ntchito imeneyi. Taganizirani mphamvu zomwe zinafunika kuti alenge angelo amphamvu mamiliyoni ambiri, nyenyezi zosawerengeka komanso zinthu zamoyo zambirimbiri zapadzikoli. Kuti akwanitse kugwira ntchito imeneyi, Yehova anapatsa Mwana wobadwa yekhayu mzimu woyera womwe ndi wamphamvu kwambiri m’chilengedwe chonse. Mwanayu anasangalala kwambiri kukhala Mmisiri Waluso amene Yehova anagwiritsa ntchito polenga zinthu zina zonse.—Miyambo 8:22-31.
6. Kodi chinachitika n’chiyani Yesu atafa n’kuukitsidwa?
6 Kodi Yehova akanapatsanso Mwana wake mphamvu komanso udindo wina wowonjezera? Yesu atafa padzikoli n’kuukitsidwa, anati: “Ulamuliro wonse waperekedwa kwa ine kumwamba ndi padziko lapansi.” (Mateyu 28:18) Zimenezi zikusonyeza kuti Yesu anapatsidwa mphamvu zoti angathe kulamulira chilichonse m’chilengedwechi. Popeza iye ndi ‘Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye,’ wapatsidwa mphamvu zoti adzathetse “maboma onse, ulamuliro wonse ndi mphamvu zonse” zimene zimatsutsana ndi Atate wake. (Chivumbulutso 19:16; 1 Akorinto 15:24-26) Mulungu “anaika zinthu zonse pansi pa” Yesu, kungopatulapo iyeyo.—Aheberi 2:8; 1 Akorinto 15:27.
7. N’chifukwa chiyani tingakhale otsimikiza kuti Yesu sangagwiritse ntchito molakwika mphamvu zimene Yehova anamupatsa?
7 Kodi tiyenera kumada nkhawa kuti mwina Yesu akhoza kugwiritsa ntchito mphamvu zake molakwika? Ayi ndithu. Yesu amakonda kwambiri Atate ake ndipo sangachite chilichonse chimene chingawakhumudwitse. (Yohane 8:29; 14:31) Iye amadziwa kuti ngakhale kuti Yehova ali ndi mphamvu zonse, sagwiritsa ntchito molakwika mphamvu zakezo. Yesu anaona yekha kuti Yehova amafunafuna mipata “kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu odzipereka ndi mtima wonse kwa iye.” (2 Mbiri 16:9) Mofanana ndi Atate ake, Yesu nayenso amakonda anthu. Choncho tisamakayikire ngakhale pang’ono kuti nthawi zonse azigwiritsa ntchito bwino mphamvu zake. (Yohane 13:1) Ndipotu Yesu wakhala akugwiritsa ntchito mphamvu zake moyenera. Tiyeni tione mmene ankazigwiritsira ntchito pamene anali padzikoli komanso chifukwa chake ankachita zimenezo.
“Wamphamvu . . . M’mawu”
8. Kodi Yesu atadzozedwa anapatsidwa mphamvu zochita chiyani, nanga anazigwiritsa ntchito bwanji?
8 N’zodziwikiratu kuti Yesu sanachitepo zodabwitsa pamene anali mnyamata ku Nazarete. Koma zinthu zinasintha atabatizidwa mu 29 C.E., ndipo pa nthawiyi n’kuti ali ndi zaka pafupifupi 30. (Luka 3:21-23) Baibulo limati: “Mulungu anamudzoza ndi mzimu woyera ndi mphamvu. Popeza Mulungu anali naye, anayenda m’dziko lonse n’kumachita zabwino ndiponso kuchiritsa anthu onse amene Mdyerekezi ankawazunza.” (Machitidwe 10:38) Mawu akuti “n’kumachita zabwino,” akusonyeza kuti Yesu ankagwiritsa ntchito mphamvu zake pothandiza anthu. Atadzozedwa, anakhala “mneneri wamphamvu m’zochita komanso m’mawu.”—Luka 24:19.
9-11. (a) Kodi nthawi zambiri Yesu ankaphunzitsira kuti, nanga panali mavuto otani? (b) N’chifukwa chiyani gulu la anthu linadabwa ndi mmene Yesu ankaphunzitsira?
9 Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti anali wamphamvu m’mawu? Nthawi zambiri ankaphunzitsira panja. Mwachitsanzo, ankaphunzitsira m’mbali mwa nyanja, m’munsi mwa mapiri, m’misewu ndiponso m’misika. (Maliko 6:53-56; Luka 5:1-3; 13:26) Omvera ake akanatha kuchoka mosavuta zikanakhala kuti zolankhula zake sizikuwafika pamtima. Popeza pa nthawiyi kunalibe mabuku osindikiza, anthu amene ankasangalala ndi zomwe Yesu ankaphunzitsa ankafunika kuzisunga m’maganizo mwawo n’kumazikumbukirabe. Choncho zimene Yesu ankaphunzitsa zinkafunika kukhala zokopa, zomveka bwino ndiponso zosavuta kukumbukira. Koma limeneli silinali vuto kwa Yesu. Mwachitsanzo, taganizirani ulaliki wake wa paphiri.
10 Tsiku lina m’mawa chakumayambiriro kwa chaka cha 31 C.E., gulu la anthu linasonkhana m’mbali mwa phiri pafupi ndi nyanja ya Galileya. Ena anachokera ku Yudeya enanso ku Yerusalemu, mtunda wa makilomita pafupifupi 100 kapena 110. Ena anachokera kumpoto m’madera a m’mbali mwa nyanja, a ku Turo ndi Sidoni. Anthu ambiri odwala ankayandikira Yesu kuti amugwire, ndipo iye ankawachiritsa. Atachiritsa odwala onse pagululo, anayamba kuwaphunzitsa. (Luka 6:17-19) Atamaliza kulankhula, iwo anadabwa ndi zimene anamva. Chifukwa chiyani?
11 Patatha zaka zingapo, munthu wina amene anamva ulaliki umenewo analemba kuti: “Gulu la anthulo linakhudzidwa moti linadabwa ndi kaphunzitsidwe kake, chifukwa ankawaphunzitsa monga munthu waulamuliro.” (Mateyu 7:28, 29) Zonena za Yesu zinali zogwira mtima. Ankalankhula m’malo mwa Mulungu ndipo chilichonse chimene ankaphunzitsa chinkachokera m’Mawu a Mulungu. (Yohane 7:16) Mfundo za Yesu zinali zomveka bwino, zosatsutsika komanso zogwira mtima moti anthu ankazitsatira. Ankathandiza omvera ake kudziwa pamene pali vuto ndiponso kudzifufuza moona mtima. Anawaphunzitsa zimene angachite kuti azisangalala, aziika Ufumu wa Mulungu pamalo oyamba, akhale ndi tsogolo labwino komanso mmene angapempherere. (Mateyu 5:3 mpaka 7:1-27) Mawu ake anathandiza kuti anthu amene ankafunafuna choonadi ndi chilungamo achitepo kanthu. Anthuwa anali okonzeka ‘kudzikana’ n’kusiya chilichonse kuti ayambe kumutsatira. (Mateyu 16:24; Luka 5:10, 11) Umenewu ndi umboni wakuti mawu a Yesu analidi ndi mphamvu.
“Wamphamvu M’zochita”
12, 13. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yesu anali “wamphamvu m’zochita”? (b) Kodi ndi zodabwitsa zosiyanasiyana ziti zimene iye anachita?
12 Yesu analinso “wamphamvu m’zochita.” (Luka 24:19) Mabuku a Uthenga Wabwino amatchula zodabwitsa zoposa 30 zimene iye anachita mothandizidwa ndi “mphamvu ya Yehova.”b (Luka 5:17) Zodabwitsa zimene anachitazi zinathandiza anthu ambiri. Mwachitsanzo, pa nthawi ina anadyetsa amuna 5,000 ndipo kenako amuna 4,000. Ngati titaphatikizapo akazi ndi ana, ndiye kuti anadyetsa anthu masauzande ambiri.—Mateyu 14:13-21; 15:32-38.
13 Zodabwitsa zimene Yesu ankachita zinali zosiyanasiyana. Anali ndi mphamvu kuposa ziwanda ndipo sankavutika kuzitulutsa. (Luka 9:37-43) Ankathanso kusandutsa madzi kukhala vinyo. (Yohane 2:1-11) Komanso taganizirani mmene ophunzira ake anadabwira pamene “anaona Yesu akuyenda panyanja.” (Yohane 6:18, 19) Analinso ndi mphamvu zogonjetsa matenda moti ankachiritsa olumala, odwala matenda okhalitsa ndiponso amene anali atatsala pang’ono kufa. (Maliko 3:1-5; Yohane 4:46-54) Anthuwa ankawachiritsa m’njira zosiyanasiyana. Anthu ena anawachiritsa ali kutali, pamene ena, ankachita kuwagwira. (Mateyu 8:2, 3, 5-13) Ena ankachira nthawi yomweyo pamene ena ankachira pang’onopang’ono.—Maliko 8:22-25; Luka 8:43, 44.
“Anaona Yesu akuyenda panyanja”
14. Kodi ndi nkhani ziti zomwe zikusonyeza kuti Yesu anali ndi mphamvu zoukitsa akufa?
14 Koma chochititsa chidwi kwambiri n’choti Yesu analinso ndi mphamvu zoukitsa akufa. Pali nkhani zitatu zomwe zinalembedwa. Anaukitsa mtsikana wazaka 12 n’kumupereka kwa makolo ake, mnyamata yemwe anali mwana yekhayo wa mayi wamasiye ndiponso munthu wina amene azichemwali ake ankamukonda kwambiri. (Luka 7:11-15; 8:49-56; Yohane 11:38-44) Panalibe chimene chinalepheretsa Yesu kuti aukitse anthuwa. Mtsikana wazaka 12 anamuukitsira pamalo omwe anamugoneka atangomwalira kumene. Mwana wa mayi wamasiyeyo ayenera kuti anamuukitsa pa tsiku lomwe anamwalira ndipo anamuukitsira pachithatha chimene anamunyamulirapo. Koma Lazaro anamuukitsa kumanda patatha masiku 4 kuchokera pamene anamwalira.
Ankagwiritsa Ntchito Mphamvu pa Zifukwa Zoyenera Komanso M’njira Yoyenera
15, 16. Kodi pali umboni wotani wosonyeza kuti Yesu sankagwiritsa ntchito mphamvu zake modzikonda?
15 Kodi mukuganiza kuti mphamvu za Yesu zikanaperekedwa kwa wolamulira yemwe si wangwiro akanazigwiritsa ntchito bwanji? Nthawi zambiri olamulira a m’dzikoli amakhala odzikonda, onyada ndiponso adyera, choncho amagwiritsa ntchito mphamvu zawo molakwika. Koma Yesu sanachimwepo ndipo sankachita zimenezi.—1 Petulo 2:22.
16 Yesu sankagwiritsa ntchito mphamvu zake modzikonda koma ankazigwiritsa ntchito kuti athandize ena. Mwachitsanzo, pamene anali ndi njala, anakana kusandutsa miyala kuti ikhale mkate woti iyeyo adye. (Mateyu 4:1-4) Umboni woti sanagwiritse ntchito mphamvu zake kuti adzilemeretse ndi woti analibe katundu wambiri. (Mateyu 8:20) Komanso sankachita zodabwitsa n’cholinga choti apindulepo kenakake. Ndipotu Yesu akamachita zodabwitsa, ankaluzapo zinthu zina. Mwachitsanzo, akachiritsa odwala mphamvu zina zinkatuluka m’thupi mwake ndipo iye ankadziwa zimenezi ngakhale akangochiritsa munthu mmodzi. (Maliko 5:25-34) Komabe ankalola kuti anthu ambirimbiri amukhudze n’kuchiritsidwa. (Luka 6:19) Izitu zikusonyeza kuti Yesu sanali wodzikonda.
17. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti sankagwiritsa ntchito mphamvu zake mwachisawawa?
17 Yesu sankagwiritsa ntchito mphamvu zake mwachisawawa. Sanachitepo zodabwitsa pofuna kungodzionetsera kapena kutchuka. (Mateyu 4:5-7) Mwachitsanzo, anakana kuchita zodabwitsa atazindikira kuti Herode akungofuna kumuona akuchita zimenezo. (Luka 23:8, 9) M’malo molengeza zokhudza mphamvu zake, nthawi zambiri akachiritsa munthu ankamuuza kuti asauze aliyense. (Maliko 5:43; 7:36) Sankafuna kuti anthu adziwe zoti iye ndi Mesiya chifukwa chongomva nkhani zosangalatsa zokhudza zodabwitsa zimene ankachita.—Mateyu 12:15-19.
18-20. (a) Kodi n’chiyani chinkachititsa kuti Yesu azigwiritsa ntchito mphamvu zake kuthandiza ena? (b) Kodi mukumva bwanji mukaganizira mmene Yesu anachiritsira munthu wina yemwe anali ndi vuto losamva?
18 Ngakhale kuti Yesu anali ndi mphamvu zambiri chonchi, anali wosiyana kwambiri ndi olamulira amene amagwiritsa ntchito mphamvu zawo mosaganizira zimene anthu akufunikira komanso mavuto amene akukumana nawo. Iye ankachita zinthu moganizira ena. Akaona anthu akuvutika, zinkamukhudza kwambiri moti ankawathandiza. (Mateyu 14:14) Ankaganizira mmene ena akumvera komanso zomwe akufunikira, choncho ankagwiritsa ntchito mphamvu zake kuti awathandize. Chitsanzo chochititsa chidwi cha zimenezi chili pa Maliko 7:31-37.
19 Pa nthawiyi gulu la anthu litapeza Yesu, linamubweretsera odwala ambiri ndipo iye anachiritsa onsewo. (Mateyu 15:29, 30) Koma kenako anasankhapo munthu wina kuti amuthandize mwapadera. Bambo ameneyu anali ndi vuto losamva komanso ankavutika kulankhula. Mwina Yesu anazindikira kuti munthuyu anali ndi mantha kapena ankachita manyazi. Choncho posonyeza kumuganizira, Yesu anamutengera pambali. Kenako anachita zinthu zingapo pofuna kuthandiza munthuyo kudziwa zomwe ankafuna kuchita. “Anapisa zala zake m’makutu a munthuyo, ndipo atalavulira pazala zake anakhudza lilime la munthuyo.”c (Maliko 7:33) Kenako Yesu anayang’ana kumwamba n’kupumira m’mwamba. Zimenezi zinathandiza munthuyo kudziwa kuti zomwe amuchitire zitheka chifukwa chothandizidwa ndi Mulungu. Kenako Yesu anati: “Tseguka.” (Maliko 7:34) Nthawi yomweyo munthuyo anayamba kumva ndiponso kulankhula bwinobwino.
20 N’zochititsa chidwi kwambiri kudziwa kuti Yesu akamachiritsa anthu pogwiritsa ntchito mphamvu zimene Mulungu anamupatsa, ankachita zimenezi mwachifundo komanso mowaganizira. Kodi si zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova wasankha Yesu, yemwe ali ndi makhalidwe amenewa, kuti akhale Mfumu ya Ufumu wake?
Anasonyeza Zimene Adzachite M’tsogolo
21, 22. (a) Kodi zodabwitsa zimene Yesu anachita zinasonyeza chiyani? (b) Popeza Yesu amatha kulamulira zinthu zam’chilengedwe, kodi tingayembekezere zotani mu ulamuliro wake?
21 Zodabwitsa zimene Yesu anachita ali padzikoli zinkangosonyeza madalitso ambiri amene tidzasangalale nawo mu ulamuliro wake. M’dziko latsopano, Yesu adzachitanso zodabwitsa, koma adzazichita padziko lonse. Taonani zina mwa zinthu zomwe tikuyembekezera.
22 Yesu adzabwezeretsa zinthu zonse zachilengedwe zimene zinawonongeka padzikoli. Kumbukirani kuti anasonyeza kuti akhoza kulamulira zinthu zam’chilengedwe poletsa mphepo panyanja. Choncho mu ulamuliro wa Khristu, anthu sazidzaopa kuti akhoza kuvulazidwa ndi mphepo zamkuntho, zivomerezi, kuphulika kwa mapiri kapena ngozi zina zam’chilengedwe. Popeza Yesu ndi Mmisiri Waluso, yemwe Yehova anamugwiritsa ntchito polenga dziko lapansi ndi zamoyo zonse, amadziwa mmene dzikoli linapangidwira. Amadziwanso mmene tingagwiritsire ntchito bwino zinthu zapadzikoli. Mu ulamuliro wake, dziko lonseli lidzakhala Paradaiso.—Luka 23:43.
23. Monga Mfumu, kodi Yesu adzathandiza bwanji anthu?
23 Nanga kodi Yesu adzathandiza bwanji anthu? Iye ankatha kudyetsa mokwanira anthu masauzande ambiri pogwiritsa ntchito chakudya chochepa. Zimenezi zikutitsimikizira kuti sikudzakhala njala akamadzalamulira. Aliyense adzakhala ndi chakudya chambiri. (Salimo 72:16) Yesu anali ndi mphamvu zochiritsa matenda ndipo zimenezi zimasonyeza kuti anthu odwala, ovulala, olumala komanso amene ali ndi vuto losaona ndiponso losamva adzachiritsidwa ndipo sadzadwalanso. (Yesaya 33:24; 35:5, 6) Popeza Yesu, yemwe ndi Mfumu yamphamvu ya Ufumu wa Mulungu, ankatha kuukitsa akufa, ndiye kuti adzaukitsa anthu mamiliyoni osawerengeka amene Atate ake asankha kuwakumbukira.—Yohane 5:28, 29.
24. Tikamaganizira zokhudza mphamvu za Yesu, kodi tiyenera kukumbukira chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?
24 Tikamaganizira zokhudza mphamvu za Yesu, tizikumbukira kuti iye amatsanzira kwambiri Bambo ake. (Yohane 14:9) Choncho mmene Yesu amagwiritsira ntchito mphamvu zimasonyeza bwino mmene Yehova amagwiritsira ntchito mphamvu zake. Mwachitsanzo, taganizirani mmene Yesu anachitira zinthu mokoma mtima pamene ankachiritsa munthu wina wakhate. Atagwidwa chifundo, Yesu anakhudza munthuyo n’kunena kuti: “Ndikufuna.” (Maliko 1:40-42) Tikamawerenga nkhani ngati zimenezi, zimakhala ngati Yehova akutiuza kuti, ‘Mphamvu zanga ndimazigwiritsa ntchito chonchi.’ Kunena zoona, tiyenera kutamanda komanso kuthokoza Mulungu wathu wamphamvuyonse chifukwa choti amagwiritsa ntchito mphamvu zake mwachikondi.
a Nthawi zambiri panyanja ya Galileya pamatha kuyamba mphepo mwadzidzidzi. Chifukwa chakuti nyanjayi ili pamalo otsika kwambiri, mpweya wapanyanjayi umakhala wotentha kwambiri kusiyana ndi madera ozungulira. Chifukwa cha zimenezi, nyengo imakhala yosakhazikika. M’chigwa cha Yorodano mumawomba mphepo yamphamvu yochokera m’phiri la Herimoni lomwe lili kumpoto kwa nyanjayi. Nyengo yabata imatha kusintha mwadzidzidzi kenako mphepo ya mkuntho n’kuyamba.
b Kuwonjezera pamenepa, nthawi zina mabuku a Uthenga Wabwino amaphatikiza zodabwitsa zambiri n’kuzifotokozera pamodzi. Mwachitsanzo, pa nthawi ina “anthu onse amumzinda” anabwera kudzaona Yesu, ndipo iye anachiritsa “anthu ambiri.”—Maliko 1:32-34.
c Ayuda komanso anthu amitundu ina ankakhulupirira kuti kulavula malovu ndi njira kapena chizindikiro cha kuchiritsa, ndipo mabuku a Arabi amafotokozanso za kuchiritsa pogwiritsa ntchito njirayi. Mwina Yesu analavula malovu pongofuna kuuza munthuyu kuti anali atatsala pang’ono kumuchiritsa. Koma sikuti anagwiritsa ntchito malovu ake ngati mankhwala.