NKHANI YOPHUNZIRA 29
‘Pitani Mukaphunzitse Anthu Kuti Akhale Ophunzira Anga’
“Pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga.”—MAT. 28:19.
NYIMBO NA. 60 Akamvera Adzapeza Moyo
ZIMENE TIPHUNZIREa
1-2. (a) Malinga ndi lamulo la Yesu pa Mateyu 28:18-20, kodi ntchito yaikulu ya mpingo wachikhristu ndi yotani? (b) Kodi tikambirana mafunso ati munkhaniyi?
YESU ataukitsidwa anakonza zoti akakumane ndi ophunzira ake m’mbali mwa phiri linalake. (Mat. 28:16) Ophunzira akewo ayenera kuti ankayembekezera mwachidwi kuti amve zimene angawauze. N’kutheka kuti pa nthawiyi m’pamene Yesu ‘anaonekera kwa abale oposa 500 pa nthawi imodzi.’ (1 Akor. 15:6) N’chifukwa chiyani Yesu anakonza zoti akumane ndi ophunzira akewo? Iye ankafuna kuwapatsa ntchito yofunika kwambiri, chifukwa anawauza kuti: “Pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga.”—Werengani Mateyu 28:18-20.
2 Ophunzira amene anamva mawu a Yesuwa anadzakhala mumpingo wachikhristu woyambirira. Ntchito yaikulu ya mpingowo inali yothandiza anthu kuti akhale ophunzira a Khristu.b Masiku ano, padzikoli pali mipingo masauzande ambiri ndipo ntchito yake yaikulu ndi yomweyi. Munkhaniyi tikambirana mafunso 4 awa: N’chifukwa chiyani kuthandiza anthu kuti akhale ophunzira n’kofunika? Kodi tingachite zotani pothandiza anthu kuti akhale ophunzira? Kodi Mkhristu aliyense angathandize bwanji pa ntchitoyi? Nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kukhala oleza mtima?
N’CHIFUKWA CHIYANI KUTHANDIZA ANTHU KUTI AKHALE OPHUNZIRA N’KOFUNIKA?
3. Malinga ndi Yohane 14:6 ndi 17:3, n’chifukwa chiyani ntchito yothandiza anthu kukhala ophunzira ndi yofunika kwambiri?
3 N’chifukwa chiyani ntchito yothandiza anthu kukhala ophunzira ndi yofunika kwambiri? Zili choncho chifukwa ophunzira a Khristu okha ndi amene angakhale anzake a Mulungu. Komanso anthu amene amatsatira Khristu amakhala ndi moyo wabwino panopa ndipo amayembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha m’tsogolo. (Werengani Yohane 14:6; 17:3.) Kunena zoona, Yesu watipatsa udindo waukulu kwambiri. Koma sitigwira ntchitoyi patokha. Ponena za iyeyo komanso anzake ena, mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndife antchito anzake a Mulungu.” (1 Akor. 3:9) Anthufe si angwiro koma Yehova ndi Khristu anatipatsa mwayi waukulu kwambiri.
4. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira Ivan ndi Matilde?
4 Ntchito yothandiza anthu kukhala ophunzira ndi yosangalatsa kwambiri. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zimene zinachitikira Ivan ndi mkazi wake Matilde, omwe amakhala ku Columbia. Iwo analalikira mnyamata wina dzina lake Davier, yemwe anawauza kuti: “Ndikufuna kusintha moyo wanga koma zikundivuta.” Davier anali katswiri pa nkhonya, ankagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, ankaledzera komanso ankakhala ndi chibwenzi chake dzina lake Erika. Ivan ananena kuti: “Tinayamba kupita kukaphunzira naye m’mudzi wakutali umene ankakhala. Tinkayenda pa njinga maola ambiri m’misewu yamatope kuti tikafikeko. Ataona kuti Davier akusintha, Erika anayamba kukhala nawo pa phunziroli.” Patapita nthawi, Davier anasiya mankhwala osokoneza bongo, kumwa mowa komanso nkhonya. Iye ndi Erika anakwatirana mwalamulo. Matilde anati: “Pamene Davier ndi Erika anabatizidwa mu 2016, tinakumbukira zimene Davier ankanena zija kuti, ‘Ndikufuna kusintha moyo wanga koma zikundivuta.’ Tinasangalala kwambiri mpaka kufika pogwetsa misozi.” N’zosachita kufunsa kuti tonsefe timasangalala kwambiri tikamathandiza anthu kuti akhale ophunzira a Khristu.
KODI TINGACHITE ZOTANI POTHANDIZA ANTHU KUTI AKHALE OPHUNZIRA?
5. Kodi chinthu choyamba chimene tiyenera kuchita pa ntchito yathu n’chiyani?
5 Chinthu choyamba pa ntchito yathuyi ndi ‘kufufuza’ anthu amene ali ndi mtima wabwino. (Mat. 10:11) Tikamayesetsa kuchitira umboni kwa anthu onse amene timakumana nawo, timasonyeza kuti ndifedi Mboni za Yehova. Ndipo tikamatsatira lamulo la Khristu lakuti tizilalikira, timasonyeza kuti ndife Akhristu enieni.
6. N’chiyani chingatithandize kuti zinthu zizitiyendera bwino mu utumiki?
6 Anthu ena amafuna kuphunzira mfundo za m’Baibulo. Koma ambiri sasonyeza chidwi pa nthawi yoyamba moti timafunika kuwalimbikitsa kuti akhale ndi mtima wofuna kuphunzira. Choncho kuti zinthu zitiyendere mu utumiki, timafunika kukonzekera bwino. Tiyenera kusankha nkhani zimene anthu akhoza kuchita nazo chidwi. Kenako tingasankhe mawu omwe tingagwiritse ntchito poyamba kukambirana nawo.
7. (a) Kodi mungayambe bwanji kukambirana ndi munthu? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kumvetsera komanso kulemekeza maganizo a anthu?
7 Mwachitsanzo, tingauze munthu kuti: “Ndimafuna kumva maganizo anu pa nkhani inayake. Mavuto amene timakumana nawo amapezeka padziko lonse. Kodi mukuganiza kuti pangafunike boma lolamulira dziko lonse kuti lithetse mavutowa?” Kenako mungayambe kukambirana naye lemba la Danieli 2:44. Apo ayi, mukhoza kufunsa munthu kuti: “Kodi mukuganiza kuti n’chiyani chingathandize makolo kuti alere bwino ana awo?” Kenako mungakambirane naye lemba la Deuteronomo 6:6, 7. Kaya musankha nkhani yotani, chofunika ndi kuganizira za anthu amene mungakumane nawo. Muziganizira mmene mfundo za m’Baibulo zingawathandizire. Mukamakambirana nawo, muzimvetsera zimene akunena komanso kulemekeza maganizo awo. Mukamatero mukhoza kuwamvetsa bwino ndipo iwonso angamvetsere uthenga umene mwawatengera.
8. N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita khama popanga maulendo obwereza?
8 Munthu asanayambe kuphunzira Baibulo, timafunika kuchita maulendo obwereza angapo. Tikutero chifukwa chakuti nthawi zambiri, anthu sapezeka tikapita kukachita ulendo wobwereza. Nthawi zina pangafunikenso kuchita maulendo obwereza angapo kuti munthu afike pomasuka nafe n’kuyamba kuphunzira. Tiyenera kukumbukira kuti maluwa amakula akamathiriridwa pafupipafupi. N’chimodzimodzinso ndi munthu amene timakambirana naye Baibulo. Iye akhoza kuyamba kukonda kwambiri Yehova komanso Yesu tikamakambirana naye Mawu a Mulungu pafupipafupi.
KODI MKHRISTU ALIYENSE ANGATHANDIZE BWANJI PA NTCHITOYI?
9-10. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Mkhristu aliyense amathandiza kupeza anthu amtima wabwino?
9 Mkhristu aliyense amathandiza pofufuza anthu amtima wabwino. Tingayerekezere ntchitoyi ndi kufufuza mwana amene wasowa. Pa nthawi ina, mnyamata wazaka zitatu anasowa ndipo anthu 500 anathandiza pomufufuza. Patapita maola 20, munthu wina anamupeza m’munda wachimanga. Koma munthuyo anakana kuti ayamikiridwe ndipo anati: “Pali anthu mahandiredi angapo amene anagwira ntchito yofufuza mwanayu.”
10 Anthu ambiri ali ngati mwana amene anasowayu chifukwa chakuti amamva ngati asochera. Iwo alibe chiyembekezo chilichonse koma amafuna kuthandizidwa. (Aef. 2:12) Anthu oposa 8 miliyoni akuyesetsa kupeza anthu amtima wabwino. Mwina inuyo simunapeze munthu woti muphunzire naye Baibulo. Koma ofalitsa ena omwe amayendanso m’gawo lanu akhoza kupeza munthu amene akufuna kuphunzira. M’bale kapena mlongo akapeza munthu n’kufika pokhala wophunzira wa Khristu, aliyense amene anathandiza pofufuza anthu amasangalala.
11. Kodi mungathandize bwanji anthu kuti akhale ophunzira ngakhale pamene simukuphunzira Baibulo ndi munthu?
11 Mwina panopa simukuphunzira Baibulo ndi munthu. Koma mukhoza kuthandiza anthu m’njira zina kuti akhale ophunzira. Mwachitsanzo, mungalandire anthu atsopano akabwera ku Nyumba ya Ufumu n’kumacheza nawo. Mukatero mudzawathandiza kuzindikira kuti ndife Akhristu enieni chifukwa choti timasonyeza chikondi. (Yoh. 13:34, 35) Ndemanga zimene mumapereka pamisonkhano, ngakhale zachidule, zingathandize anthu atsopano kuti adziwe mmene angayankhire mochokera mumtima komanso mwaulemu. Mukhozanso kupita ndi wofalitsa watsopano mu utumiki n’kumuthandiza kudziwa mmene angagwiritsire ntchito Malemba pokambirana ndi anthu. Mukamachita zimenezi, mumakhala kuti mukumuphunzitsa kuti azitsanzira Khristu.—Luka 10:25-28.
12. Kodi timafunika kukhala ndi luso lapadera kuti tizithandiza anthu kukhala ophunzira? Fotokozani.
12 Sitiyenera kuganiza kuti timafunika kukhala ndi luso lapadera kuti tizithandiza anthu kuti akhale ophunzira a Yesu. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Faustina amene amakhala ku Bolivia. Pa nthawi imene anayamba kuphunzira ndi Mboni za Yehova sankadziwa kuwerenga. Koma kenako anaphunzira kuwerenga pang’ono. Panopa anabatizidwa ndipo amakonda kwambiri kuphunzitsa anthu Baibulo. Nthawi zambiri amachititsa maphunziro a Baibulo 5 pa mlungu. Iye sawerenga bwino ngati mmene amawerengera anthu ambiri amene amaphunzira nawo koma wathandiza anthu 6 mpaka kufika pobatizidwa.—Luka 10:21.
13. Ngakhale kuti timatanganidwa kwambiri, kodi chingachitike n’chiyani mu utumiki?
13 Akhristu ambiri amatanganidwa chifukwa chokhala ndi maudindo ambiri. Komabe amapeza nthawi yophunzira Baibulo ndi anthu ndipo amasangalala kwambiri ndi ntchitoyi. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina dzina lake Melanie. Iye ankakhala ku Alaska ndipo ankalera yekha mwana wake wazaka 8. Mlongoyu anali pa ntchito yolembedwa ndipo ankathandizanso kusamalira bambo ake omwe ankadwala khansa. Iye anali wa Mboni mmodzi yekha m’tauni imene ankakhala. Koma ankapempha Mulungu kuti azimupatsa mphamvu yopirira nyengo yozizira ndipo ankapita kukalalikira chifukwa ankafunitsitsa kuti apeze munthu woti azimuphunzitsa Baibulo. Kenako anakumana ndi Sara yemwe anasangalala kwambiri ataphunzira kuti Mulungu ali ndi dzina lakelake. Patapita nthawi, Sara anavomera kuphunzira Baibulo. Melanie anati: “Lachisanu madzulo ine ndi mwana wanga tinkapita kukaphunzira naye ngakhale kuti ndinkakhala nditatopa kwambiri. Tinkakonda kufufuza mayankho a mafunso a Sara ndipo tinasangalala kwambiri pamene anayamba kukhala mnzake wa Yehova.” Sara analimba mtima n’kusiya chipembedzo chake ngakhale kuti ankatsutsidwa. Kenako anabatizidwa.
N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUKHALA OLEZA MTIMA?
14. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti ntchito yolalikira ili ngati ntchito yopha nsomba? (b) Kodi mungatsatire bwanji mawu a Paulo pa 2 Timoteyo 4:1, 2?
14 Musataye mtima ngati mukuvutika kupeza munthu woti muziphunzira naye Baibulo. Musaiwale kuti Yesu anayerekezera ntchito yothandiza anthu kukhala ophunzira ndi ntchito yopha nsomba. Asodzi amatha kugwira ntchito kwa nthawi yaitali asanapeze nsomba. Nthawi zambiri amagwira ntchito usiku kapena mbandakucha ndipo nthawi zina amayenda mtunda wautali kuti akapeze nsomba. (Luka 5:5) Nawonso Akhristu amakhala oleza mtima ndipo amagwira ntchito yolalikira kwa maola ambiri. Iwo amatha kusinthasintha nthawi komanso malo pofufuza anthu. Amatero n’cholinga choti akumane ndi anthu ambiri. Akhristu amene amachita khama, nthawi zambiri amapeza anthu amene amachita chidwi ndi uthenga wathu. Mwina inunso mungasinthe nthawi yolalikira kapena malo kuti muzipeza anthu ambiri.—Werengani 2 Timoteyo 4:1, 2.
15. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala oleza mtima tikamaphunzira Baibulo ndi anthu?
15 N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala oleza mtima tikamaphunzira Baibulo ndi munthu? Chifukwa chimodzi n’chakuti timafunika kuchita zambiri, osati kungothandiza munthuyo kuti adziwe ndiponso kukonda mfundo za m’Baibulo. Timafunikanso kuthandiza munthuyo kuti adziwe ndiponso kukonda Yehova, yemwe analemba Baibulo. Tiyeneranso kumuphunzitsa zinthu zimene Yesu amafuna kuti ophunzira ake azichita, komanso mmene angachitire zinthuzo. Tiyenera kumuthandiza moleza mtima kuti ayambe kutsatira mfundo za m’Baibulo. Anthu ena amatha kusintha maganizo ndi makhalidwe awo patangopita miyezi yochepa koma ena zimawatengera nthawi yaitali.
16 Kodi mwaphunzira chiyani pa nkhani ya Raúl?
16 Zimene mmishonale wina ku Peru anakumana nazo zimasonyeza kufunika koleza mtima. Iye anati: “Ndinaphunzira mabuku awiri ndi munthu wina dzina lake Raúl. Koma anali adakali ndi mavuto aakulu. Banja lake silinkayenda bwino, ankakonda kutukwana ndipo ana ake sankamulemekeza. Koma ndinapitiriza kumuthandiza limodzi ndi banja lake chifukwa chakuti ankabwera kumisonkhano mlungu uliwonse. Kuchokera pamene ndinakumana naye, panatenga zaka zoposa zitatu kuti ayenerere kubatizidwa.”
17. Kodi tidzakambirana chiyani munkhani yotsatira?
17 Yesu anatiuza kuti ‘tipite kukaphunzitsa anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira ake.’ Kuti tigwire ntchitoyi, nthawi zambiri timafunika kulankhula ndi anthu omwe amaganiza mosiyana ndi ifeyo. Mwachitsanzo, timalankhula ndi anthu amene sali m’chipembedzo chilichonse kapena amene sakhulupirira zoti kuli Mulungu. Munkhani yotsatira tidzakambirana zimene tingachite kuti tiziuza anthu oterewa uthenga wabwino.
NYIMBO NA. 68 Tizifesa Mbewu za Ufumu
a Ntchito yaikulu ya Akhristufe ndi yothandiza anthu kuti akhale ophunzira a Khristu. Munkhaniyi muli mfundo zimene zingatithandize kuti tizigwira bwino ntchitoyi.
b TANTHAUZO LA MAWU ENA: Ophunzira a Khristu samangophunzira zimene Yesu ankaphunzitsa koma amatsatiranso mfundozo pa moyo wawo. Amayesetsa kutsatira mapazi a Yesu mosamala kwambiri, kapena kuti kutengera chitsanzo chake.—1 Pet. 2:21.
c MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Munthu amene akupita kutchuthi watenga kapepala kwa a Mboni kubwalo la ndege. Tsiku lina akukaona malo, waona a Mboni ena akulalikira m’malo opezeka anthu ambiri. Atabwera kutchuthi, a Mboni afika kunyumba kwawo.
d MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Munthu uja wavomera kuphunzira Baibulo. Patapita nthawi, akubatizidwa.