Makolo, Kodi Mukuthandiza Ana Anu Kuti Ayenerere Kubatizidwa?
“Nanga ukuchedweranji? Nyamuka, ubatizidwe.”—MAC. 22:16.
1. Kodi makolo amafuna kutsimikizira za chiyani ana awo asanabatizidwe?
MLONGO wina dzina lake Blossom Brandt anafotokoza zimene zinamuchitikira asanabatizidwe. Iye ananena kuti: “Kwa mwezi wathunthu, ndinakhala ndikuuza mayi ndi bambo anga kuti ndikufuna kubatizidwa, ndipo nthawi zambiri ankakambirana nane za nkhaniyi. Iwo ankafuna kutsimikizira ngati ndikumvetsadi zimene munthu amayenera kuchita akabatizidwa. Kenako tsiku lofunika kwambiri pamoyo wangali linafika ndipo ndinabatizidwa pa 31 December 1934.” Masiku anonso makolo amafunitsitsa kuthandiza ana awo kuti azisankha zinthu mwanzeru. Mwana akazengereza kubatizidwa zingasokoneze ubwenzi wake ndi Yehova. (Yak. 4:17) Komabe mwana asanabatizidwe makolo amafunika kutsimikizira ngati mwanayo angakwaniritsedi udindo wake wokhala Mkhristu.
2. (a) Kodi oyang’anira madera ena anadandaulapo za chiyani? (b) Kodi munkhaniyi tikambirana chiyani?
2 Oyang’anira madera ena adandaulapo kuti amakumana ndi achinyamata ena omwe makolo awo ndi a Mboni koma sanabatizidwe ngakhale kuti atsala pang’ono kukwanitsa zaka 20 kapena kupitirira. Nthawi zambiri achinyamatawa amasonkhana komanso kulowa mu utumiki ndipo amangoona kuti ndi a Mboni za Yehova. Koma pa zifukwa zina amazengereza kudzipereka kwa Yehova ndiponso kubatizidwa. Kodi n’chifukwa chiyani amachita zimenezi? Nthawi zina makolo ndi amene amalimbikitsa achinyamata kuti asabatizidwe msanga. Munkhaniyi tikambirana zifukwa 4 zimene zimachititsa makolo ena kuti asamathandize ana awo kuti ayenerere kubatizidwa.
KODI MWANA WANGA WAFIKA MSINKHU WOTI N’KUBATIZIDWA?
3. Kodi makolo ake a Blossom ankadera nkhawa za chiyani?
3 Makolo a Blossom, omwe tawatchula mundime yoyamba ija, ankadera nkhawa ngati mwana wawoyu anafika msinkhu woti n’kubatizidwa komanso kumvetsa kuti kubatizidwa ndi nkhani yaikulu. Kodi makolo angadziwe bwanji ngati mwana wawo ali woyenerera kudzipereka kwa Yehova?
4. Kodi lamulo limene Yesu anapereka pa Mateyu 28:19, 20 lingathandize bwanji makolo akamaphunzitsa ana awo?
4 Werengani Mateyu 28:19, 20. Munkhani yapita ija tinakambirana kuti Baibulo silinena kuti munthu amafunika kubatizidwa akafika zaka zinazake. Koma makolo angachite bwino kuganizira tanthauzo la kuthandiza munthu kuti akhale wophunzira. Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti ‘kuphunzitsa munthu kuti akhale wophunzira wa Yesu’ pa Mateyu 28:19 amatanthauza kuphunzitsa munthu n’cholinga choti akhale wophunzira. Ndipo wophunzira ndi munthu amene amaphunzira komanso kumvetsa zimene Yesu ankaphunzitsa ndipo amafunitsitsa kuti azitsatira zimene ankaphunzitsazo. Choncho cholinga cha makolo chiyenera kukhala kuphunzitsa ana awo kuyambira ali aang’ono kwambiri mpaka anawo atakhala ophunzira obatizidwa a Khristu. N’zoona kuti khanda siliyenera kubatizidwa. Koma Baibulo limasonyeza kuti ngakhale ana aang’ono akhoza kumvetsa ndiponso kuyamikira mfundo zoona za m’Baibulo.
5, 6. (a) Malinga ndi zimene Baibulo limanena, kodi Timoteyo ayenera kuti anabatizidwa pa msinkhu uti? (b) Kodi makolo anzeru angathandize bwanji ana awo?
5 Timoteyo anali Mkhristu amene anayamba kukonda choonadi ali wamng’ono. Mtumwi Paulo ananena kuti Timoteyo anaphunzira choonadi cha m’Malemba kuyambira ali wakhanda. Ngakhale kuti bambo a Timoteyo sankalambira Yehova, mayi ake ndiponso agogo ake ankamuphunzitsa zimene Ayuda ankakhulupirira kuchokera m’Malemba. Zimenezi zinathandiza Timoteyo kuzindikira kufunika kwa Malemba komanso kukhala ndi chikhulupiriro cholimba kwambiri. (2 Tim. 1:5; 3:14, 15) Timoteyo asanakwanitse zaka za m’ma 20 kapena atapitirira pang’ono, anali atakhala Mkhristu woyenerera kulandira maudindo apadera mumpingo.—Mac. 16:1-3.
6 Koma ana amakhala osiyana ndipo aliyense amaphunzira zinthu mosiyana ndi mnzake. Ana ena amayamba kuchita zinthu ngati munthu wamkulu ali aang’ono ndipo amafuna kubatizidwa. Koma ena sachita zimenezi mpaka atakulirapo. Choncho makolo anzeru sakakamiza ana awo kuti abatizidwe. M’malomwake amathandiza mwana aliyense kuti aphunzire zinthu mogwirizana ndi msinkhu wake komanso luso lake lomvetsa zinthu. Makolo angasangalale mwana wawo akamakumbukira mfundo ya pa Miyambo 27:11. (Werengani.) Komabe sayenera kuiwala cholinga chawo chothandiza ana awo kuti akhale Akhristu obatizidwa. Choncho makolo angachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi mwana wathu akudziwa zinthu zokwanira moti angayenerere kudzipereka kwa Mulungu ndiponso kubatizidwa?’
KODI MWANA WANGA AKUDZIWA ZINTHU ZOKWANIRA?
7. Kodi munthu amafunika kudziwa zinthu zambirimbiri kuti abatizidwe? Fotokozani.
7 N’zomveka kuti makolo amafunika kuphunzitsa bwino ana awo n’cholinga choti ana adziwe choonadi molondola kenako n’kudzipereka kwa Mulungu. Koma sikuti munthu amafunika kudziwa zinthu zambirimbiri kuti ayenerere kudzipereka komanso kubatizidwa. Paja Mkhristu aliyense akabatizidwa amafunika kupitiriza kuphunzira kuti adziwe Malemba molondola. (Werengani Akolose 1:9, 10.) Ndiye kodi munthu amafunika kudziwa zinthu zochuluka bwanji kuti abatizidwe?
8, 9. Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani ya Paulo ndi woyang’anira ndende?
8 Zimene zinachitikira banja lina m’mbuyomu zingatithandize kuyankha funso limeneli. (Mac. 16:25-33) Paulo ali pa ulendo wachiwiri waumishonale cha mu 50 C.E., anafika ku Filipi. Iye anali ndi Sila ndipo ali kumeneko ananamiziridwa mlandu n’kumangidwa. Ndiyeno usiku kunachitika chivomezi chomwe chinagwedeza ndendeyo n’kutsegula zitseko zake. Woyang’anira ndendeyo ankafuna kudzipha poganiza kuti akaidi onse athawa, koma Paulo anamuletsa. Kenako Paulo ndi Sila analalikira woyang’anira ndendeyo ndi banja lake. Kodi banjalo linatani litakhulupirira mfundo zokhudza Yesu zimene linaphunzira pa nthawiyo? Iwo anabatizidwa nthawi yomweyo. Ndiye kodi tikuphunzirapo chiyani?
9 Kalelo, oyang’anira ndende ankakonda kukhala anthu amene anapuma pa ntchito yausilikali. Choncho ayenera kuti sankadziwa Malemba. Iye ankafunika kuphunzira mfundo zoyambirira za m’Baibulo, kuzindikira zimene atumiki a Mulungu ayenera kuchita komanso kukhala ndi mtima wofuna kutsatira zimene Yesu anaphunzitsa. Pa kanthawi kochepa chabe, mfundo zimene anaphunzira zinamufika pa mtima ndipo ankafuna kubatizidwa. N’zosachita kufunsa kuti atabatizidwa anapitiriza kuphunzira mfundo zina za m’Malemba. Ndiye poganizira zimene zinachitikira banjali, kodi muyenera kuchita chiyani ngati mwana wanu akusonyeza kuti amakonda mfundo zoyambirira za m’Baibulo komanso akumvetsa bwino tanthauzo la kudzipereka komanso kubatizidwa? Mwina mungamulimbikitse kuti akaonane ndi akulu kuti akambirane naye n’kuona ngati akuyenerera ubatizo.a Mofanana ndi Akhristu ena onse obatizidwa, iye adzapitiriza kuphunzira za Yehova ndiponso za cholinga chake mpaka muyaya.—Aroma 11:33, 34.
KODI NDIKUTHANDIZA MWANA WANGA KUTI ZINTHU ZIMUYENDERE BWINO?
10, 11. (a) Kodi makolo ena amaganiza zotani? (b) Kodi makolo ayenera kuona kuti chofunika kwambiri n’chiyani?
10 Makolo ena amaona kuti mwana wawo ayenera kudikira kaye asanabatizidwe kuti achite maphunziro amene angamuthandize kupeza ntchito yapamwamba. Makolo otere mwina amaona kuti akachita zimenezo ndiye kuti akufunira mwana wawo zabwino. Koma kodi maganizo amenewa angathandizedi kuti zinthu zizimuyendera bwino? Funso lofunika kwambiri kudzifunsa ndi lakuti, Kodi maganizowa akugwirizana ndi Malemba? Kodi Mawu a Yehova amalimbikitsa achinyamata kuchita chiyani?—Werengani Mlaliki 12:1.
11 Tiyenera kukumbukira kuti maganizo a anthu a m’dzikoli ndi osemphana ndi maganizo a Yehova. (Yak. 4:7, 8; 1 Yoh. 2:15-17; 5:19) Ndipotu ubwenzi wolimba ndi Yehova ndi umene ungathandize mwana kuti asamasokonezedwe ndi Satana, dzikoli komanso maganizo oipa a m’dzikoli. Makolo akamalimbikitsa mwana kuti aziika maphunziro kapena ntchito pamalo oyamba akhoza kusokoneza mwanayo komanso kumubweretsera mavuto. Kodi makolo achikondi angafune kuti mwana wawo atengere maganizo a m’dzikoli pa nkhani ya moyo wabwino? Zoona zake n’zakuti munthu amakhala wosangalala pokhapokha ngati amaika Yehova pamalo oyamba.—Werengani Salimo 1:2, 3.
NANGA BWANJI NGATI MWANA WANGA ATACHITA TCHIMO?
12. N’chifukwa chiyani makolo ena safuna kuti ana awo abatizidwe msanga?
12 Mlongo wina analetsa mwana wake kubatizidwa ndipo pofotokoza chifukwa chake ananena kuti: “Chimene chimandidetsa nkhawa ndi chakuti mwanayu akhoza kudzachotsedwa mumpingo akalakwitsa chinachake.” Mofanana ndi mlongoyu, makolo ambiri amaganiza kuti ndi bwino kuti mwana wawo asabatizidwe mpaka maganizo achibwana atamuthera. (Gen. 8:21; Miy. 22:15) Maganizo awo amakhala akuti, ‘Ngati mwana wangayu sabatizidwa ndiye kuti sangachotsedwe.’ N’chifukwa chiyani tinganene kuti makolo oterewa amadzipusitsa?—Yak. 1:22.
13. Kodi munthu amene sanabatizidwe ndiye kuti sangaimbidwe mlandu ndi Yehova? Fotokozani.
13 N’zoona kuti makolo achikhristu sangakonde kuti mwana wawo abatizidwe ali wamng’ono kwambiri moti sangamvetse zimene akuchita podzipereka kwa Mulungu. Koma si nzeru kuganiza kuti mwana amene sanabatizidwe ndiye kuti sangaimbidwe mlandu ndi Yehova. N’chifukwa chiyani tikutero? Ubatizo si umene umachititsa kuti munthu aimbidwe mlandu ndi Yehova kapena ayi. Yehova amaona kuti mwana akhoza kuweruzidwa ngati wafika potha kusiyanitsa zoyenera ndi zolakwika. (Werengani Yakobo 4:17.) Choncho m’malo moletsa mwana kuti abatizidwe, makolo anzeru amayesetsa kupereka chitsanzo chabwino kwa ana awo. Amayesetsa kuthandiza mwana wawo kuti azikonda mfundo zapamwamba za Yehova kuchokera mumtima. (Luka 6:40) Akatero mwanayo amafunitsitsa kuti azitsatira mfundo zachilungamo za Yehova.—Yes. 35:8.
ANTHU ENA ANGATHANDIZE
14. Kodi akulu angathandize bwanji makolo amene akulimbikitsa ana awo kuti ayenerere kubatizidwa?
14 Akulu mumpingo omwe ndi abusa, angathandize makolo akamalimbikitsa ana kuti akhale ndi zolinga zauzimu. Mlongo wina amene anachita upainiya kwa zaka zoposa 70 ananena mmene M’bale Charles T. Russell anamulimbikitsira iye ali ndi zaka 6 zokha. Mlongoyo anati: “M’baleyu anakambirana nane kwa maminitsi 15 zokhudza zolinga zanga zauzimu.” Apa n’zoonekeratu kuti mawu abwino komanso olimbikitsa angathandize anthu kwa nthawi yaitali. (Miy. 25:11) Akulu angapemphenso makolo ndi ana awo kuti azithandiza pa ntchito za pa Nyumba ya Ufumu. Angapereke ntchito kwa ana mogwirizana ndi msinkhu komanso luso lawo.
15. Kodi anthu ena amumpingo angalimbikitse bwanji ana?
15 Abale ndi alongo ena mumpingo angathandizenso makolo akamalimbikitsa ana awo. Kuti achite zimenezi, ayenera kukhala tcheru kuti aone zimene ana akuchita mumpingo. Mwachitsanzo, mwina mwana angapereke ndemanga yochokera pansi pa mtima, kukamba nkhani kapena kuchita chitsanzo pamisonkhano yampingo. Kapena mwina wakhalabe wokhulupirika atakumana ndi mayesero kapenanso walalikira kwa anzake kusukulu. Mukaona zimenezi musamachedwe kuwayamikira ndi mtima wonse. Mungachitenso bwino kukhala ndi cholinga choti muzicheza ndi mwana mmodzi misonkhano isanayambe kapena itatha. Mukamachita zinthu ngati zimenezi, mungathandize ana kuzindikira kuti ndi ofunika kwambiri mu “mpingo waukulu.”—Sal. 35:18.
MUZITHANDIZA MWANA WANU KUTI AYENERERE KUBATIZIDWA
16, 17. (a) Kodi kubatizidwa kungathandize bwanji munthu kukhala ndi tsogolo labwino? (b) Kodi makolo amafunitsitsa kuti ana awo achite chiyani? (Onani chithunzi choyambirira.)
16 Kunena zoona, ndi mwayi waukulu kwambiri kulera ana “m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.” (Aef. 6:4; Sal. 127:3) Mosiyana ndi ana a Aisiraeli akale, masiku ano ana a Mboni za Yehova sabadwa ali odzipereka kwa Mulungu. Komanso mwana sakonda Mulungu kapena choonadi chifukwa chongotengera makolo. Kuyambira nthawi imene mwana wabadwa, makolo ayenera kukhala ndi cholinga choti azithandiza mwanayo kuti adzipereke kwa Yehova komanso kubatizidwa. Kuchita zimenezi n’kofunika kwambiri. Tikutero chifukwa chakuti munthu amafunika kudzipereka kwa Yehova, kubatizidwa komanso kutumikira Yehovayo mokhulupirika kuti aikidwe chizindikiro choti adzapulumuke.—Mat. 24:13.
17 Pamene Blossom Brandt anasankha kuti abatizidwe, makolo ake ankafuna kutsimikizira kuti anali wokonzekadi kuchita zimenezi. Atatsimikizira, anamulola kubatizidwa. Usiku woti abatizidwa mawa lake, bambo ake anachita chinthu chosaiwalika. Blossom anafotokoza kuti: “Bambo anauza tonse kuti tigwade ndipo anapemphera. Iwo anauza Yehova kuti anali osangalala kwambiri kuti mwana wawo wasankha kudzipereka kwa iye.” Patapita zaka zoposa 60, Blossom ananena kuti: “Zimene bambo anachita tsiku limenelo sindidzaiwala mpaka kalekale.” Ngati ndinu makolo, nanunso mukhoza kusangalala kwambiri ana anu akadzipereka kwa Yehova ndiponso kubatizidwa.
a Mfundo zothandiza makolo pokambirana ndi ana zili m’buku lakuti Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri tsamba 304-310. Onaninso “Bokosi la Mafunso” mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa April 2011, tsamba 2.