Kodi Ndimotani Mmene Munthu Angakhalire m’Chifanizo cha Mulungu?
“MULUNGU ndipo adalenga munthu m’chifanizo chake, m’chifanizo cha Mulungu adamlenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi.” Chimatero cholembedwa chouziridwa, koma kodi chimatanthauzanji? Ndimotani mmene mwamuna ndi mkazi oyamba analengedwera m’chifanizo cha Mulungu?—Genesis 1:27.
Kodi iwo anali ofanana ndi Mulungu mwakuthupi? Iyayi, zimenezo nzosatheka. Munthu ali waumunthu, wanyama, wopangidwira kukhala padziko lapansi. Mulungu ali mzimu, wokhala muulemerero wosalingalirika wakumwamba umene palibe munthu aliyense angaufikire. (Eksodo 33:18-20; 1 Akorinto 15:50) Nangano ndimotani mmene munthu anapangidwira m’chifanizo cha Mulungu? Ndimlingaliro lakuti munthu anapatsidwa mphamvu yakusonyeza mikhalidwe yapadera ya Mulungu—chikondi, chilungamo, nzeru, ndi mphamvu—limodzinso ndi mikhalidwe ina.
Mikhalidwe ya Yehova
Mikhalidwe ya Yehova Mulungu imaonekera mwa zolengedwa zake zonse, koma inasonyezedwa mokulira kwambiri m’zochita zake ndi anthu aŵiri oyambirira, Adamu ndi Hava. (Aroma 1:20) Chikondi chake chinaonedwa mwakuti iye analenga dziko lapansi mumkhalidwe woyenerera munthu kukhalapo. Yehova analengera mwamuna mkazi wangwiro kuti akhale womthangata ndi amayi wa ana ake. Iye anaika aŵiriwo m’munda wokongola nawapatsa zinthu zonse zochuluka zofunikira kuti apitirize kukhala ndi moyo wachimwemwe. Chabwino koposa zonse, Mulungu anawapatsa mwaŵi wa kukhala ndi moyo kosatha.—Genesis 2:7-9, 15-24.
Nzeru ya Mulungu inaonedwa mwa kuyesa kwake anthu aŵiri oyambirira. Ngati anati akhalebe ziŵalo za banja la Yehova la chilengedwe chonse ndipo ngati anati akhale ndi moyo kosatha monga makolo a fuko la anthu, akafunikira kukhala zitsanzo za kukhulupirika ndi kulambira kowona. Chifukwa chake, Yehova anawapatsa mwaŵi wa kusonyeza mkhalidwe wa mtima wawo pansi pa chiyeso choyenerera—iwo sanafunikire kudya zipatso za mtengo wodziŵitsa chabwino ndi choipa. Kunali kwanzeru chotani nanga kwa Yehova kuti analola anthu kudzitsimikizirira kumvera kwawo ndi chikondi kwa iye asanawapatse mitundu ya mwaŵi yodabwitsa imene anawalinganizira!
Chilungamo cha Mulungu chinaonedwa m’kuumirira kwake pamiyezo yapamwamba kwa zolengedwa zake ndi m’kusalolera kwake molakwa miyezo imeneyo. Chinaonedwa m’kupatsa kwake Adamu ndi Hava mwaŵi uliwonse wa kuchita choyenera. Ndipo pamene analephera kuchita motero, chilungamo chake chinaonedwa m’kuwaweruza kwake kuti adzakumane ndi chilango cha kupanduka chonenedwacho.
Mphamvu ya Yehova inaonedwa m’kuchita kwake mogwirizana ndi chiweruzo chake. Satana, mpandu wamkulu, anali atatanthauza kuti Yehova anali wonama, ndipo Satana analonjeza zinthu zazikulu kwa Hava ngati akachita mosamvera Mulungu. (Genesis 3:1-7) Koma Satana sanathe kukwaniritsa lonjezo lake. Iye sanakhoze kuletsa Yehova kuti asathamangitse Adamu ndi Hava kuchoka m’munda wa Edene, ndipo analephera kuletsa kukwaniritsidwa kwa mawu a Mulungu kwa Adamu akuti: “Chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.” (Genesis 3:19) Komabe, Yehova sanapereke pomwepo chilango cha imfa, ndipo mwa kusatero anasonyezanso chikondi chake. Anapatsa Adamu ndi Hava nthaŵi yakuti abale ana mwa amene chifuno chake choyambirira kwa mtundu wa anthu chikakwaniritsidwa m’kupita kwanthaŵi.—Genesis 1:28.
Chomalizira, chilungamo cha Yehova Mulungu, chikondi chake, mphamvu, ndi nzeru zinaonekera m’lonjezo lake la kupereka mbewu imene ikawononga ntchito za Satana ndi kuchotsa zotulukapo zoipa za chipanduko choyambirira pa uchifumu waumulungu. (Genesis 3:15) Ha, ali Mlengi wodabwitsa chotani nanga amene tili naye!
Zoyesayesa za Kutsanzira Mulungu
Chinkana kuti salinso angwiro, anthu akhozabe kusonyeza mikhalidwe ya Mulungu. Chifukwa chake, Paulo analimbikitsa Akristu a m’tsiku lake kuti: “Khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa.” (Aefeso 5:1) Komabe, m’mbiri yonse anthu ambiri asonyeza kunyalanyaza kwakukulu mikhalidwe ya Mulungu. Pofika m’nthaŵi ya Nowa, anthu anali ataipa chiipire kwakuti Yehova anatsimikiza mtima za kuwononga mtundu wonse wa anthu kusiyapo Nowa yekha ndi banja lake. Nowa anali “munthu wolungama ndi wangwiro m’mibadwo yake,” ndipo anasonyeza chikondi chake kwa Mulungu mwa kutsatira malamulo a Mulungu. “Anachita Nowa, monga mwa zonse anamlamulira iye Mulungu, momwemo anachita.” (Genesis 6:9, 22) Nowa anasonyeza chikondi kwa anthu anzake ndi kumamatira kwake pa chilungamo mwa kukhala “mlaliki wa chilungamo.” (2 Petro 2:5) Iye anasonyeza nzeru ndipo anagwiritsira ntchito mwanjira yabwino mphamvu yake yakuthupi mwa kutsatira chitsogozo cha Mulungu cha kumanga chingalawa chachikulu, kusunga chakudya mkati mwakemo, kusonkhanitsa zinyama, ndi kuloŵa m’chingalawamo atalamulidwa ndi Yehova. Anasonyezanso kukonda kwake chilungamo mwa kusalola anansi ake oipa kumnyenga.
Baibulo limasimba za anthu ena ambiri amene mofananamo anasonyeza mikhalidwe yaumulungu. Woposa onse anali Yesu Kristu, yemwe anali wangwiro m’chifanizo cha Mulungu ndipo chotero anakhoza kunena kuti: “Iye amene wandiona ine waona Atate.” (Yohane 14:9) Pakati pa mikhalidwe imene Yesu anasonyeza, wopambana unali chikondi chake. Chikondi chake kwa Atate wake ndi mtundu wa anthu chinamsonkhezera kusiya mudzi wake wakumwamba ndi kudzakhala monga munthu padziko lapansi. Chinamsonkhezera kulemekeza Atate wake mwa kudzisungira kolungama ndi mwa kulalikira kwa mtundu wa anthu mbiri yabwino yachipulumutso. (Mateyu 4:23; Yohane 13:31) Ndiyeno, chikondi chinasonkhezera Yesu kupereka nsembe moyo wake wangwiro kaamba ka chipulumutso cha mtundu wa anthu, ndipo chofunika koposa, kaamba ka kuyeretsedwa kwa dzina la Mulungu. (Yohane 13:1) Poyesetsa kutsanzira Mulungu, kodi pali chitsanzo china chilichonse choyenera kutsatiridwa kuposa Yesu Kristu?—1 Petro 2:21.
Kodi Ndimotani Mmene Tingafananire Kwambiri ndi Mulungu Lerolino?
Kodi ndimotani mmene ifeyo, lerolino, tingasonyezere mikhalidwe ya Mulungu, ndipo motero kuchita zinthu m’chifanizo cha Mulungu? Eya, choyamba talingalirani za mkhalidwe wa chikondi. Yesu anati: “Uzikonda [Yehova, NW] Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse.” Kodi timasonyeza motani chikondi kwa Mulungu? Mtumwi Yohane akuyankha kuti: “Pakuti ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa.”—Mateyu 22:37; 1 Yohane 5:3.
Ndithudi, kuti timvere malamulo a Yehova, tiyenera kuwadziŵa. Zimenezo zimaphatikizapo kuŵerenga, kuphunzira, ndi kusinkhasinkha pa Mawu a Mulungu, Baibulo, ndi pa mabuku ofotokoza Baibulo. Mofanana ndi wamasalmo, tiyenera kukhala okhoza kunena kuti: “Ha! Ndikondadi chilamulo chanu; Ndilingiriramo ine tsiku lonse.” (Salmo 119:97) Pamene tipeza chidziŵitso chozamirapo kwambiri cha Mawu a Mulungu, timayambukiridwa ndi njira ya Mulungu ya kulingalira. Timafikira pakukonda chilungamo ndi kuda kusaweruzika. (Salmo 45:7) Mpamene Adamu analakwa pamenepa. Iye anadziŵa lamulo la Yehova, koma sanalikonde kwenikweni moti nkulimamatira. Poŵerenga Mawu a Mulungu, tiyenera kumadzifunsa nthaŵi zonse kuti, ‘Kodi zimenezi zimandikhudza motani? Kodi ndingachitenji kuti ndichititse khalidwe langa kugwirizana ndi mikhalidwe ya Mulungu?’
Yesu ananenanso kuti: “Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.” (Mateyu 22:39) Munthu aliyense wamaganizo abwino amadzikonda yekha ndipo amadzifunira zabwino koposa. Kumeneko sikulakwa. Koma kodi timasonyeza chikondi chofananacho kwa mnansi wathu? Kodi timatsatira chilangizo cha m’Baibulo chakuti: “Oyenera kulandira zabwino usawamane; pokhoza dzanja lako kuwachitira zabwino”?—Miyambo 3:27; Agalatiya 6:10.
Bwanji ponena za mkhalidwe wa nzeru? Kuyesayesa kwathu kusonyeza mkhalidwe umenewu kumatichititsa kuphunzira Baibulo chifukwa chakuti ndilo nkhokwe ya nzeru yaumulungu. Salmo 119:98-100 limati: “Malamulo anu andipatsa nzeru yakuposa adani anga; pakuti akhala nane chikhalire. Ndili nayo nzeru yakuposa aphunzitsi anga onse; pakuti ndilingalira mboni zanu. Ndizindikira koposa okalamba popeza ndinasunga malangizo anu.” Pa Miyambo 3:18, nzeru ikunenedwa kukhala “mtengo wa moyo.” Ngati tipeza nzeru ndi kuigwiritsira ntchito, tidzalandira chiyanjo cha Mulungu ndi mphotho ya moyo wosatha.—Mlaliki 7:12.
Bwanji ponena za chilungamo? M’dziko loipali, chilungamo ndimkhalidwe wofunika kwambiri kwa awo ofuna kukondweretsa Mulungu. Yesu anakonda chilungamo ndi kuda kusaweruzika. (Ahebri 1:9) Akristu lerolino amachita zofananazo. Chilungamo chimawasonkhezera kuyamikira mikhalidwe yoyenera. Amapeŵa njira zosalungama za dziko lino ndi kuchititsa kuchita chifuniro cha Mulungu kukhala chinthu chofunika koposa m’miyoyo yawo.—1 Yohane 2:15-17.
Ponena za mphamvu, tonsefe tili nayo pamlingo winawake. Mwachibadwa tili ndi mphamvu yakuthupi ndi yamaganizo, ndipo pamene tikukula monga Akristu, timakulitsa mphamvu yauzimu. Yehova amalimbitsa mphamvu yathu ndi mzimu woyera kumlingo umene ifeyo, ngakhale kuti ndife ofooka, tikhoza kuchita chifuniro cha Yehova. Paulo anati: “Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.” (Afilipi 4:13) Timapeza nyonga imodzimodziyo ngati tipempherera mzimu wa Yehova.
Kulalikira Mbiri Yabwino
Kusonyeza kwathu mikhalidwe yaikulu inayiyo ya Mulungu kumaonekera bwino m’kulabadira kwathu lamulo lakuti: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu; ndipo onani, Ine ndiri pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano.” (Mateyu 28:19, 20) Ntchito yophunzitsa yoteroyo imapatsa moyo kwa awo olabadira. Ha, ndichisonyezero chotani nanga cha chikondi kwa awo, amene kwakukulukulu, amayamba monga alendo kwenikweni kwa ife!
Ndiponso, kuphunzitsa koteroko ndiko njira ya nzeru. Kumadzetsa zipatso zimene zimakhalitsa. Kodi ndintchito ina iti imene inganenedwe kuti: “Pochita ichi udzadzipulumutsa iwe wekha ndi iwo akumva iwe”? (1 Timoteo 4:16) Palibe amene amatayikiridwa kanthu m’ntchito yakupanga ophunzira. Ponse paŵiri awo amene amamvetsera ndi awo amene amaphunzitsa amapeza madalitso osatha.
Ponena za chilungamo, Akristu amaphunzitsa makhalidwe olungama kwa ophunzira Baibulo awo. Tikuwathandiza kuti atumikire Yehova, “Mulungu wa [chilungamo, NW].” (Malaki 2:17) Lerolino awo amene amapatulira miyoyo yawo pakutumikira Yehova ndi kuchita mogwirizana ndi zimenezo mokhulupirika amalengezedwa kukhala olungama, oyenda m’njira imene idzawapulumutsa pa Armagedo.—Aroma 3:24; Yakobo 2:24-26.
Ndichisonyezero chotani nanga cha mphamvu choonekera m’kulalikira ndi kuphunzitsa mbiri yabwino padziko lonse! (Mateyu 24:14) Pamafunikira chipiriro kuti munthu alalikire mopitirizabe m’magawo kumene anthu ochuluka safuna kumvetsera. Koma Yehova, kupyolera mwa mzimu wake, amapereka nyonga yofunikira kupirira kufikira mapeto.—Yesaya 40:30, 31; Mateyu 24:13; Luka 11:13.
Ndithudi, monga ana opanda ungwiro a Adamu, sitingathe kusonyeza mikhalidwe yabwino imeneyi mwangwiro. Komabe, kumbukirani, munthu anapangidwa m’chifanizo cha Mulungu, ndipo ngati tiyesayesa kuti tifanane kwambiri ndi Mulungu, pamenepo tidzakhala tikukwaniritsa mbali imodzi ya chifukwa chathu chokhalirapo ndi moyo. (Mlaliki 12:13) Ngati tilimbikira mwaphamvu kuchita zimene tingakhoze ndi kupempha chikhululukiro pamene tilakwa, pamenepo tingayembekezere kupulumuka ndi kuloŵa m’dziko latsopano lolungama la Mulungu, mmene potsirizira pake tingadzapeze ungwiro. Ndiyeno, tidzakhala m’dziko lapansi laparadaiso lokhalidwa ndi anthu olungama, onse akumasonyeza bwino lomwe mikhalidwe ya Yehova Mulungu mwangwiro. Nzosangalatsa chotani nanga! Potsirizira pake, m’lingaliro lenileni la mawuwo, anthu adzakhala m’chifanizo cha Mulungu.
[Chithunzi patsamba 25]
Yesu anatisonyeza mmene tingakulitsire mikhalidwe yaumulungu ya Yehova
[Chithunzi patsamba 26]
Potsirizira pake, anthu m’lingaliro lenileni adzakhala m’chifanizo cha Mulungu