Kodi Muyenera Kusunga Sabata?
KUMAPETO kwa zaka za m’ma 1980, magulu a anthu a tchalitchi cha Methodist anavuta mumzinda wa Suva, womwe ndi likulu la zilumba za Fiji. Amuna, akazi, ndiponso ana, amene anavala mayunifolomu a kutchalitchi, anaima m’malodibuloko 70. Ankaimitsa magalimoto onse a anthu amalonda kapena mabasi. Anaimitsanso maulendo a pa ndege za m’dzikolo kapena zopita m’mayiko ena. Kodi n’chifukwa chiyani ankachita zimenezi? Iwo ankafuna kuti dzikolo likhwimitsenso lamulo loti aliyense azisunga Sabata.
M’dziko la Israel anakhazikitsa lamulo lakuti, kuyambira mu 2001 nyumba iliyonse yosanja imene ingamangidwe izikhala ndi chikepi choti chiziima chokha pakhomo lililonse lolowera m’zipinda za m’mwamba. Anachita zimenezi n’cholinga choti Ayuda otsatira kwambiri miyambo ya chipembedzo chawo, amene amasunga Sabata kuyambira Lachisanu madzulo mpaka Loweruka madzulo, asamagwire ntchito yotobwanya mabatani oimitsira chikepicho.
Kuzilumba za Tonga, zomwe zili m’nyanja yamchere ya South Pacific, anthu saloledwa kugwira ntchito iliyonse Lamlungu. Patsikuli, ndege siziloledwa kutera ndiponso sitima za m’madzi siziloledwa kukocheza m’madoko a pazilumbazi. Pangano lililonse limene anthu angagwirizane pa tsiku limeneli, limaonedwa kuti ndi losavomerezeka. Malamulo a boma la Tonga amanena kuti munthu wa chipembedzo chilichonse ayenera kuona kuti tsiku Lamlungu ndi lopatulika. Kodi n’chifukwa chiyani anaika lamulo limeneli? Anachita zimenezi pofuna kuti aliyense m’dzikolo azisunga Sabata.
Zitsanzo zimenezi zikusonyeza kuti anthu ambiri amaganiza kuti Mulungu amafuna kuti iwowo azisunga Sabata mlungu uliwonse. Ndipo ena amanena kuti kusunga Sabata n’kofunika kwambiri chifukwa amakhulupirira kuti n’kumene kudzathandize kuti tidzapulumuke. Enanso amakhulupirira kuti lamulo lalikulu kwambiri lochokera kwa Mulungu ndi lakuti tizisunga Sabata. Koma kodi Sabata n’chiyani? Ndipo kodi Baibulo limalamula Akhristu kuti azisunga Sabata mlungu uliwonse?
Kodi Sabata N’chiyani?
Mawu akuti “Sabata” anachokera ku mawu achiheberi amene amatanthauza “kupuma” kapena “kusiya kugwira ntchito.” Buku la Genesis limafotokoza kuti pa tsiku la 7 Yehova Mulungu anapuma pa ntchito yake yolenga. Komabe, Mulungu sanapereke lamulo loti anthu azikhala ndi tsiku lathunthu lopuma kapena kusunga Sabata. Lamulo limeneli analipereka m’nthawi ya Mose. (Genesis 2:2) Aisiraeli atachoka ku Igupto, mu 1513 B.C.E., Yehova anawapatsa mana mozizwitsa ali m’chipululu. Ndipo Mulungu anawapatsa malangizo oyenera kutsatira potola mana. Anawauza kuti: “Muziwola uwu masiku asanu ndi limodzi; koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo la Sabata, pamenepo padzakhala palibe.” (Eksodo 16:26) Kenako Baibulo limanena kuti “anthu anapumula tsiku lachisanu ndi chiwiri,” kuyambira Lachisanu dzuwa litalowa mpaka Loweruka madzulo dzuwa litalowa.—Eksodo 16:30.
Patangopita nthawi yochepa atapereka malangizo amenewa, Yehova anaperekanso lamulo lakuti anthu azisunga Sabata ndipo analiphatikiza pa Malamulo Khumi amene anapereka kwa Mose. (Eksodo 19:1) Lamulo lachinayi la malamulo amenewa lili ndi mawu akuti: “Uzikumbukira tsiku la Sabata, likhale lopatulika. Masiku asanu ndi limodzi uzigwira, ndi kumaliza ntchito zako zonse; koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata la kwa Yehova Mulungu wako.” (Eksodo 20:8-10) Choncho, kusunga Sabata kunali kofunika kwambiri pamoyo wa Aisiraeli onse.—Deuteronomo 5:12.
Kodi Yesu Ankasunga Sabata Mlungu Uliwonse?
Inde, Yesu ankasunga Sabata. Ponena za iye, Baibulo limati: “Nthawi itakwana yonse, Mulungu anatumiza Mwana wake, amene anadzabadwa kwa mkazi ndipo anadzakhala pansi pa chilamulo.” (Agalatiya 4:4) Yesu anabadwa m’banja lachiisiraeli ndipo pachifukwa chimenechi ankafunika kutsatira Chilamulo chimene chinali ndi lamulo losunga Sabata. Pangano la Chilamulo linapitirizabe kugwira ntchito mpaka pamene linachotsedwa Yesu atafa. (Akolose 2:13, 14) Kudziwa nthawi imene zinthu zimenezi zinachitika, kumatithandiza kumvetsa mmene Mulungu amaonera nkhani imeneyi.—Onani tchati chimene chili patsamba 15.
N’zoona kuti Yesu anati: “Musaganize kuti ndinabwera kudzawononga Chilamulo kapena Zolemba za aneneri. Sindinabwere kudzawononga, koma kudzakwaniritsa.” (Mateyo 5:17) Koma kodi mawu akuti ‘kukwaniritsa’ amatanthauza chiyani? Tiyerekezere chonchi: Tikanena kuti mmisiri womanga nyumba wakwaniritsa pangano sizitanthauza kuti wang’amba pepala limene panalembedwa panganolo koma amakhala kuti wamaliza kumanga zimene munagwirizana. Akamaliza kumanga bwinobwino zimene munapangana, amakhala kuti wakwaniritsa pangano lanu ndipo mmisiriyo sangafunikire kutsatirabe panganolo. Mofanana ndi zimenezi, sikuti Yesu anaswa kapena kung’amba Chilamulo, koma anachikwaniritsa potsatira zonse za m’Chilamulocho popanda kulakwitsa. Yesu atakwaniritsa “pangano” la Chilamulo limeneli, anthu a Mulungu sankafunikiranso kulitsatira.
Kodi Akhristu Ayenera Kusunga Sabata?
Popeza kuti Khristu anakwaniritsa Chilamulo, kodi Akhristu ayenera kusunga Sabata mlungu uliwonse? Mouziridwa ndi Mulungu, mtumwi Paulo anayankha kuti: “Choncho munthu asakuweruzeni ponena za kudya ndi kumwa kapena chikondwerero chinachake, kapena kusunga tsiku la mwezi watsopano, kapena sabata; pakuti zinthu zimenezo ndi mthunzi wa zimene zinali kubwera, koma zenizeni zake zili mwa Khristu.”—Akolose 2:16, 17.
Mawu ouziridwa amenewa akusonyeza kuti pali kusintha kwakukulu pa nkhani ya zimene Mulungu amafuna kuti atumiki ake azitsatira zokhudza lamulo la kusunga Sabata. Koma kodi n’chifukwa chiyani anasintha choncho? N’chifukwa chakuti Akhristu ayenera kutsatira chilamulo chatsopano, chomwe ndi “chilamulo cha Khristu.” (Agalatiya 6:2) Pangano la Chilamulo limene linaperekedwa kwa Aisiraeli kudzera mwa Mose, linasiya kugwira ntchito pamene linakwaniritsidwa ndi imfa ya Yesu. (Aroma 10:4; Aefeso 2:15) Kodi ndiye kuti lamulo losunga Sabata nalonso linatha? Inde. Paulo atanena kuti “tsopano tamasulidwa ku Chilamulo,” anatchula limodzi la Malamulo Khumi aja. (Aroma 7:6, 7) Choncho, Malamulo Khumi, kuphatikizapo lamulo losunga Sabata, ndi mbali ya Chilamulo chimene chinatha. Chotero, Atumiki a Mulungu safunikiranso kusunga Sabata mlungu uliwonse.
Zinthu zinasintha pamene kulambira kwa Aisiraeli kunalowedwa m’malo ndi kulambira kwa Chikhristu. Zimenezi tingaziyerekezere ndi kusintha kwa malamulo a m’dziko. Malamulo atsopano akangovomerezedwa, anthu samafunikiranso kuyendera malamulo akale aja. Ngakhale kuti ena mwa malamulo atsopanowo angafanane ndi akale aja, ena angakhale osiyana ndi akalewo. Choncho, munthu angafunike kuwerenga bwinobwino malamulo atsopanowo kuti adziwe malamulo amene ayenera kumayendera. Komanso nzika yokhulupirika ku dziko lake iyenera kudziwa tsiku limene malamulo atsopanowo anayamba kugwira ntchito.
Mofanana ndi zimenezi, Yehova Mulungu anapereka kumtundu wa Isiraeli malamulo oposa 600, kuphatikizapo malamulo akuluakulu okwana 10. Ena mwa malamulo amenewa anali okhudza makhalidwe abwino, nsembe, nkhani zaumoyo, ndiponso kusunga Sabata. Komabe, Yesu ananena kuti otsatira ake odzozedwa adzapanga “mtundu” watsopano. (Mateyo 21:43) Kuyambira mu 33 C.E. kupita mtsogolo, mtundu umenewu wakhala ukutsatira “malamulo” atsopano. Malamulo amenewa akuchokera pa malamulo awiri aakulu, omwe ndi kukonda Mulungu ndi kukonda mnansi wako. (Mateyo 22:36-40) Ngakhale kuti “chilamulo cha Khristu” chili ndi malamulo ena ofanana ndi amene ali m’Chilamulo chimene chinaperekedwa kwa Aisiraeli, sitiyenera kudabwa tikaona kuti malamulo ena ndi osiyana kwambiri ndi akalewo ndiponso kuti malamulo ena akale safunikanso kutsatiridwa. Lamulo loti anthu azisunga Sabata mlungu uliwonse ndi limodzi mwa malamulo amene safunikiranso kutsatiridwa masiku ano.
Kodi Ndiye Kuti Mulungu Wasintha Mfundo Zake?
Kodi kusintha kumeneku, kuchoka ku Chilamulo cha Mose kufika ku chilamulo cha Khristu, kukutanthauza kuti Mulungu wasintha mfundo zake? Ayi. Zili ngati mmene makolo amachitira. Iwo amatha kusintha malamulo oti ana awo aziyendera poganizira msinkhu wa anawo komanso zochitika zina. Nayenso Yehova wasintha malamulo amene anthu ake akufunikira kutsatira. Mtumwi Paulo anafotokoza nkhaniyi motere: “Chikhulupirirocho chisanafike, tinali kuyang’aniridwa ndi chilamulo, tonse titaperekedwa m’manja mwake kuti chitisunge. Tinali choncho tikuyembekezera chikhulupiriro chimene chinali kudzavumbulutsidwa. Ndiye chifukwa chake Chilamulo chakhala namkungwi wotitsogolera kwa Khristu, kuti tikayesedwe olungama chifukwa cha chikhulupiriro. Koma popeza chikhulupirirocho tsopano chafika, sitilinso pansi pa namkungwi.”—Agalatiya 3:23-25.
Kodi zimene Paulo ananenazi zikukhudza bwanji nkhani ya Sabata? Taganizirani chitsanzo ichi: Wophunzira akakhala kusukulu, angafunikire kuphunzira phunziro linalake, mwachitsanzo kupala matabwa, tsiku limodzi mlungu uliwonse. Koma akadzayamba ntchito, angafunikire kugwiritsa ntchito luso limene anaphunziralo tsiku lililonse pa mlungu, osati tsiku limodzi lokha limene ankaphunzira ntchito kusukulu. Mofanana ndi zimenezi, pamene Aisiraeli ankayendera Chilamulo, ankafunika kupatula tsiku limodzi mlungu uliwonse kuti azipuma ndi kulambira Mulungu. Mosiyana ndi Aisiraeliwa, Akhristu amafunika kulambira Mulungu tsiku lililonse, osati tsiku limodzi lokha pa mlungu.
Ndiyeno, kodi n’kulakwa kupatula tsiku limodzi mlungu uliwonse kuti tizipuma ndi kulambira Mulungu? Ayi. Mawu a Mulungu amati munthu aliyense angathe kusankha zimene akufuna. Mawuwa amati: “Wina amaona tsiku lina ngati loposa linzake, koma wina amaona tsiku lina mofanana ndi ena onse; munthu aliyense payekha akhale wotsimikiza kwenikweni m’maganizo mwake.” (Aroma 14:5) Ngakhale kuti ena angasankhe kuona tsiku lina kukhala lopatulika kuposa ena, Baibulo limasonyeza kuti Mulungu samayembekezera kuti Akhristu azisunga Sabata mlungu uliwonse.
[Mawu Otsindika patsamba 12]
“Muziwola uwu masiku asanu ndi limodzi; koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo la Sabata, pamenepo padzakhala palibe.”—EKSODO 16:26
[Mawu Otsindika patsamba 14]
“Chilamulo chakhala namkungwi wotitsogolera kwa Khristu, kuti tikayesedwe olungama chifukwa cha chikhulupiriro. Koma popeza chikhulupirirocho tsopano chafika, sitilinso pansi pa namkungwi.”—AGALATIYA 3:24, 25
[Bokosi/Chithunzi patsamba 13]
Kawerengedwe ka Masiku Kamasokoneza Osunga Sabata
Pali mzere wongoyerekezera umene anthu padziko lonse amagwiritsira ntchito powerengera masiku. Mzerewu unayambira kumpoto kwa dziko lapansi ndipo umadutsa m’nyanja yamchere ya Pacific mpaka kukafika kum’mwera kwenikweni kwa dziko lapansili. Mayiko amene ali kumadzulo kwa mzere umenewu amatsogola ndi tsiku limodzi kuposa amene ali kummawa kwa mzerewu. Kuwerengera masiku mwanjira imeneyi kumasokoneza anthu amene amakhulupirira kuti anthu padziko lonse ayenera kusunga Sabata pa tsiku lofanana.
Mwachitsanzo, ngati ku Fiji ndi ku Tonga tsiku lili Lamlungu, ku Samoa ndi ku Niue limakhala lili Loweruka. Choncho, ngati munthu wa ku Fiji akusunga Sabata tsiku Loweruka, anthu a m’chipembedzo chake a ku zilumba za Samoa, chomwe chili pa mtunda wa makilomita 1,145 okha kuchokera ku Fijiko, amakhala akugwira ntchito patsikuli chifukwa kumeneko limakhala lili Lachisanu.
Anthu a mpingo wa Seventh-Day Adventist a ku Tonga amasunga Sabata pa tsiku Lamlungu. Iwo amaganiza kuti kuchita zimenezi kumawathandiza kuti azisunga Sabata tsiku lofanana ndi limene anthu a m’chipembedzochi a ku zilumba za Samoa amasunga. Chonsechotu zilumbazi zili pa mtunda wa makilomita oposa 850 okha kuchokera ku Tonga. Komabe, pa nthawi yofananayi, anthu a Seventh-Day Adventist a ku zilumba za Fiji amakhala akugwira ntchito chifukwa kwawoko limakhala lili Lamlungu pamene iwo amasunga Sabata Loweruka. Komatu zilumba za Fiji zili pa mtunda wa makilomita osakwana 800 kuchokera ku Tonga.
[Chithunzi]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
\
\
\
\ SAMOA
\
— ― ― ― ― ― ― ―
FIJI \
Lamlungu \ Lamlungu
\
\
TONGA \
\
\
\
[Tchati patsamba 15]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Mfundo Zofunika Kuziganizira Zokhudza Sabata:
Tikawerenga lemba lina m’Baibulo lonena kuti tifunika kusunga Sabata mlungu uliwonse, tiyenera kufufuza kuti mawuwo ananenedwa liti.
4026 B.C.E. ISANAFIKE NTHAWI YA MOSE
KULENGEDWA KWA ADAMU Lamulo lonena za Sabata silinaperekedwe kwa anthu
amene anakhalapo isanafike
nthawi ya Mose ndi Aisiraeli.—Deuteronomo 5:1-3,
1513 B.C.E. MULUNGU ANAPEREKA LAMULOLI KWA AISIRAELI
AISIRAELI ANAPATSIDWA CHILAMULO Lamulo lonena
za Sabata silinaperekedwe ku mitundu ina.
(Salmo 147:19, 20) Lamulo lilinaperekedwa kuti likhale “chizindikiro”
pakati pa Yehova ndi ana a Isiraeli.—Eksodo
Sabata la mlungu uliwonse linali limodzi mwa
masabata ambiri amene Aisiraeli analamulidwa kuti
azisunga. —Levitiko 16:29-
33 C.E. CHILAMULO CHA KHRISTU
33 C.E. KUTHA KWA Mu 49 C.E., Atumwi ndi akulu ku Yerusalemu
CHILAMULO CHOPEREKEDWA anafotokoza zimene Mulungu amafuna kuti Akhristu
KWA AISIRAELI azitsatira. Koma iwo sanatchulepo kuti Akhristu
afunika kusunga Sabata mlungu uliwonse.
Mtumwi Paulo anadandaula za Akhristu amene
ankakondakwambiri kusunga masiku amene amawaona
kuti ndi apadera.—Agalatiya
2010 C.E.
[Chithunzi patsamba 11]
Manyuzipepala analemba za malodibuloko amene magulu a tchalitchi cha Methodist anakhazikitsa pofuna kuti dziko la Fiji likhwimitsenso lamulo loti aliyense azisunga Sabata
[Mawu a Chithunzi]
Courtesy of the Fiji Times