-
Pitirizani Kuchita Zinthu Mogwirizana MumpingoMungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
3. Kodi muyenera kuchita chiyani mukasemphana maganizo ndi Mkhristu mnzanu?
Ngakhale kuti ndife anthu ogwirizana, timasemphana maganizo kapena kukhumudwitsana chifukwa chakuti ndife anthu ochimwa. Choncho, Mawu a Mulungu amatiuza kuti: “Pitirizani . . . kukhululukirana ndi mtima wonse . . . monga Yehova anakukhululukirani ndi mtima wonse, inunso teroni.” (Werengani Akolose 3:13.) Anthufe timakhumudwitsa Yehova kambirimbiri komabe iye amatikhululukira. Choncho iye amafuna kuti nafenso tizikhululukira abale ndi alongo athu. Mukazindikira kuti mwakhumudwitsa winawake, inuyo muziyesetsa kukambirana ndi mnzanuyo n’cholinga choti muthetse kusamvana.—Werengani Mateyu 5:23, 24b
-
-
Pitirizani Kuchita Zinthu Mogwirizana MumpingoMungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
Nthawi zina nafenso timakhumudwitsa ena. Ndiye tizitani zimenezi zikachitika? Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso lotsatirali.
Kodi mlongo wamuvidiyoyi anachita zotani kuti akhazikitse mtendere?
-