A Magi Atatu Chenicheni Kapena Nthano?
“C + M + B”
Kodi malemba amenewa amatanthauza chirichonse kwa inu? Ngati mumakhala mkati mwa gawo la Chiroma Katolika la Federal Republic of Germany, iwo angatero. Kumeneko inu kaŵirikaŵiri mudzawona zirembozo limodzi ndi chaka zitalembedwa pa mphuthu. Nchifukwa ninji ziri tero?
Mwambo wotchuka umanena kuti malemba amenewa ali malemba oyambirira a chiGerman a chomwe chikutchedwa a Magi atatu, kapena “amuna anzeru,” Gaspar (chiGerman, Caspar), Melchior, ndi Balthasar.a Molingaliridwa, mafupa a Magi anasamutsidwira ku Cologne m’chaka cha 1164 ndipo pambuyo pake kuikidwa mu cathedral ya mzindawo, mwakutero kupangitsa Cologne kukhala maziko a kudzipereka kwawo. Chaka ndi chaka, pa January—chodziŵika monga Phwando la Mafumu Atatu Oyera—magulu a achichepere ovala monga mafumu akale amapita ku khomo ndi khomo akumalemba malembawo pa mphuthu. Mogwirizana ndi mwamba, ichi chimapereka kwa eninyumba chitetezero kuchokera ku tsoka.
Luso la chipembedzo ndi mwambo limasonyeza kuti a Magi atatu, kapena “mafumu,” anatsogozedwa ndi “nyenyezi” kupita kumene Yesu anabadwira. M’chiyang’aniro cha ulemu, ngakhale kudzipereka, koperekedwa kwa “mafumu” amenewa, funso limadzuka ponena za kuti kaya chikhulupiriro chimenechi chiri chozikidwa pa Malemba.
Mateyu uli Uthenga Wabwino wokha womwe umalozera kwa alendo amenewa. (2:1-12) Koma kodi Mateyu amatchula kuti iwo anali atatu ndipo kuti iwo anali mafumu, ndipo kodi iye analemba maina awo? Nyuzipepala ya Chikatolika Kirchenzeitung für das Bistum Aachen ikuvomereza kuti: “Mafumu Atatu Oyerawo sakulozeredwako monga otero m’Baibulo. Kuyambira m’zana la chisanu ndi chimodzi, amuna anzeru anamvetsetsedwa kukhala . . . mafumu atatu. . . . Ponena za chiŵerengero cha openda nyenyezi, . . . Mateyu sakupereka tsatanetsatane. . . . M’zana la chisanu ndi chinayi iwo anawonekera choyamba pansi pa maina a Gaspar, Melchior, ndi Balthasar.” M’kuwonjezerapo, ntchito ya chilozero ya Chikatolika Lexikon für Theologie und Kirche imadziŵitsa kuti liwu la Chigriki maʹgoi silimatanthauza mafumu koma, m’malomwake, “okhala ndi chidziŵitso cha chinsinsi cha kupenda nyenyezi.” Justin Martyr, Origen, ndi Tertullian aliyense wa iwo anamvetsetsa liwulo kutanthauza “wopenda nyenyezi.” Matembenuzidwe amakono a Baibulo amagwiritsiranso ntchito “openda nyenyezi” pa Mateyu 2:1, 7.—The Living Bible; An American Translation.
Ngakhale kuti zochitika za Kumudzi za Yesu monga khanda mosapeweka zimaphatikiza “mafumu atatu,” kodi iwo analiko pa kubadwa kwake? Bukhu lopereka matanthauzo a mawulo likuwonjezera kuti: “Mateyu 2:16 imasonyeza kuti ulendowo unachitika mwinamwake chaka chimodzi kapena zowonjezereka atabadwa Yesu.” Ndithudi, versi 11 likulankhula za “nyumba,” osati modyera ng’ombe, kumene iwo “anawona mwana wamng’onoyo.”—King James Version.b
Bwanji ponena za mawu akuti “Mafumu Oyera”? Kodi alendowo moyenerera angatchedwa oyera? Lemba silimalongosola iwo nkomwe monga otero. Io anali, m’chienicheni, onyalanyaza a prinsipulo la umulungu. Pa Yesaya 47:13, 14 (NW) Mulungu amatsutsa “olambira [“openda nyenyezi,” mogwirizana ndi Septuagint] kumwamba, oyang’ana nyenyezi.” (Yerekezani ndi Deuteronomo 18:10.) Openda nyenyezi amenewa anabwera “kuchokera ku mbali za kum’mawa,” motsimikizirika kwenikweni amene pa nthaŵiyo anali malo apakati a kulambira matsenga, Babulo wodetsedwa, kumene anali kulambira milungu yonyenga. Chotero, iwo anatsogozedwa ndi chimene analingalira kuti chinali “nyenyezi” yoyenda, imene palibe wina aliyense akusimbidwa kukhala anaiwona. Ndiponso, Mateyu akusonyeza kuti “nyenyeziyo” inawatsogoza iwo choyamba kwa Mfumu Herode, yemwe kenaka anayesera kupha Yesu.—Mateyu 2:1, 2.
Ayi, Mulungu sanatumize “nyenyezi” kuwatsogoza iwo kwa Yesu. Kodi icho sichiri motsimikizirika kuti “nyenyezi” imeneyi inatumizidwa ndi winawake wofunafuna kupha Yesu asanakhale wokhoza kukwaniritsa ntchito yake yopatsidwa ndi Mulungu?—Yerekezani ndi Genesis 3:15.
Yesu anachenjeza kuti Mawu a Mulungu angapangidwe kukhala “achabe” mwa kusakaniza iwo ndi “mwambo.” (Mateyu 15:6) Miyambo yozungulira anthu amenewa iri mwachiwonekere yosakhala ya m’malemba. Chotero, kodi simukuvomereza kuti chikakhala cholakwika kulemekeza openda nyenyezi kapena kuwalingalira iwo monga oyera?
[Mawu a M’munsi]
a Atsogoleri achipembedzo amalozanso ku mawu a chiLatin akuti Christus mansionem benedicat, “Lolani Kristu adalitse nyumba iyi,” monga kalongosoledwe kake.
b Kaamba ka chidziŵitso chowonjezereka ponena za kufika kwa openda nyenyeziwo, onani kope la Nsanja ya Olonda la December 15, 1979, tsamba 30, m’Chingelezi.