Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Muyezo Wapamwamba Kaamba ka Otsatira Ake
ATSOGOLERI achipembedzo akulingalira Yesu kukhala wakuswa Chilamulo cha Mulungu ndipo osatikale kwambiri iwo anachitadi chiwembu cha kumupha. Chotero pamene Yesu akupitirizabe Ulaliki wake wa pa Phiri, iye akufotokoza kuti: “Musaganize kuti ndinadza ine kudzapasula chilamulo kapena aneneri: sindinadza kupasula, koma kukwaniritsa.”
Yesu ali ndi ulemu waukulu koposa ponena za Chilamulo cha Mulungu ndipo akulimbikitsa ena kukhalanso nawo. Kwenikweni, iye akuti: “Yense wa kumasula limodzi la malangizo amenewa ang’onong’ono, nadzaphunzitsa anthu chomwecho, adzatchulidwa wamng’onong’ono mu ufumu wakumwamba,” kutanthauza kuti munthu wotero sakalowa konsemu Ufumuwo.
Mmalo mwa kukhala wonyalanyaza Chilamulo cha Mulungu, Yesu akutsutsa ngakhale maganizo amene amathandizira kuchiswa. Pambuyo pa kunena kuti Chilamulo chimati “Usaphe,” Yesu akuwonjezera kuti: ‘Koma ine ndinena kwa inu, kuti yense wa kupitirizabe kukwiyira mbale wake adzakhala wopalamula mlandu.’
Popeza kuli kwakuti kukwiyira tsamwali nkowopsa motero, mwinamwake kutsogoleradi ku kuchita mbanda, Yesu akufotokoza mwafanizo mlingo ku umene munthu ayenera kupita kuti apeze mtendere. lye akulangiza kuti: “Chifukwa chake ngati uli kupereka mtulo wako [wansembe] paguwa lansembe ndipo pomwepo ukakumbukira kuti mbale wako ali ndi kanthu pa iwe, usiye pomwepo mtulo wako kuguwako, nuchoke, nuyambe kuyanjana ndi mbale wako, ndipo pamenepo idza nupereke mtulo wako.”
Potembenuzira chisamaliro ku lachisanu ndi chiwiri la Malamulo Khumi, Yesu akupitirizabe kuti: ‘Munamva kuti kunanenedwa, Usachite chigololo. Koma ndinena kwa inu kuti mwamuna aliyense amene apitirizabe kuyang’ana mkazi kuti akhale ndi chilakolako naye wachita naye kale chigololo mu mtima mwake.’
Yesu panopa sakulankhula za ganizo lachisembwere lopita mofulumira koma za ’kupitirizabe kuyang’ana.’ Kupitirizabe kuyang’ana kotero kumadzutsa nyere, imene, ngati mpata upezeka, ingatsirizire m’chigololo. Kodi munthu angatetezere motani kuti ichi chisachitike? Yesu akulongosola mwafanizo mmene mchitidwe wonkitsa ungakhalire wofunika, mwakumati: “Koma ngati diso lako lamanja likulakwitsa iwe, ulikolowole, nulitaye. . . . Ndipo ngati dzanja lako lamanja likulakwitsa iwe, ulidule, nulitaye.”
Kawirikawiri anthu ali ofunitsitsa kutayikiridwa ndi chiwalo chenicheni chimene chagwidwa ndi nthenda kuti apulumutse miyoyo yawo. Koma mogwirizana ndi kunena kwa Yesu, kulidi kofunika kwambiri ‘kutaya’ chirichonse, ngakhale kanthu kamtengo wapatali kwambiri monga diso kapena dzanja, kupewa ganizo ndi kuchita chisembwere. Yesu akufotokoza kuti, apo phuluzi, anthu otero adzaponyedwa m’Gehena (mulu wa zinyalala zoyaka moto pafupi ndi Yerusalemu), amene amaphiphiritsira chiwonongeko chamuyaya.
Yesu akulongosolanso njira ya kuchita nayo ndi anthu amene amavulaza ndi kukhumudwitsa. “Musakanize munthu woipa,” ndiwo uphungu wake. “Koma amene adzakupanda iwe patsaya lako lamanja umtembenuzire linanso.” Yesu sakutanthauza kuti munthu sayenera kudzitetezera kapena banja lake ngati waukiridwa. Pama silimamenyedwera kuvulaza mwakuthupi koma, mmalo mwake, kuputa. Chotero, zimene Yesu akunena nzakuti ngati munthu aliyense ayesa kuyambitsa ndewu kapena mkangano, kaya mwa kuwomba pama lenileni ndi chikhatho kapena mwa kutulutsa mawu achipongwe otukwana, kukakhala kulakwa kubwezera.
Pambuyo pa kusonya ku lamulo la Mulungu la kukonda mnansi wa munthuwe, Yesu akulongosola kuti: “Koma ine ndinena kwa inu, Kondanani nawo adani anu, ndi kupempherera iwo akuzunza inu.” Akumapereka chifukwa champhamvu cha kuchitira chomwecho, iye akuwonjezera kuti: “Kotero kuti mungakhale ana a Atate wanu wakumwamba; chifukwa iye amakwezera dzuwa lake pa oipa ndi pa abwino.”
Yesu akumaliza mbali yaulaliki imeneyi mwakulangiza kuti: “Chifukwa chake inu mukhale angwiro, monga Atate wanu wakumwamba ali wangwiro.” Yesu sakutanthauza kuti anthu angathe kukhala angwiro m’lingaliro lokwanira. Mmalo mwake, iwo angathe, mwa kutsanzira Mulungu, kukulitsa chikondi chawo ku phatikizapo ngakhale adani awo. Cholembedwa chofananacho cha Luka chikusimba mawu a Yesu motere: “Khalani inu achifundo monga Atate wanu ali wachifundo.” Mateyu 5:17-48; Luka 6:36.
◆ Kodi Yesu anasonyeza motani ulemu waukulu ponena za Chilamulo cha Mulungu?
◆ Kodi ndimalangizo otani amene Yesu anapereka ochotsa magwero a kuchita mbanda ndi chigololo?
◆ Kodi Yesu anatanthauzanji pamene analankhula za kutembenuzira tsaya lina?
◆Kodi tingakhale angwiro motani mofanana ndi Mulungu ali wangwiro?