MUTU 35
Ulaliki Wotchuka wa Paphiri
MATEYU 5:1-48; 6:1-34; 7:1-29 LUKA 6:17-49
ULALIKI UMENE UNACHITIKA PAPHIRI
Yesu ayenera kuti anali atatopa kwambiri chifukwa anali atapemphera usiku wonse. Kenako anasankha ophunzira 12 kuti akhale atumwi ake. Pofika chakumasana anali akadali ndi mphamvu komanso anali wofunitsitsa kuti athandize anthu. Choncho anayamba kuwaphunzitsa atakhala m’mbali mwa phiri ku Galileya chakufupi ndi ku Kaperenao kumene ankakhala nthawi zambiri.
Anthu ambiri ochokera m’madera akutali anabwera kumene kunali Yesu. Ena anali ochokera chakumwera ku Yerusalemu komanso m’madera ena a ku Yudeya. Enanso anali ochokera kumpoto chakumadzulo m’mizinda ya Turo ndi Sidoni yomwe inali m’mbali mwa nyanja. N’chifukwa chiyani anthuwa anabwera kwa Yesu? Anthuwa “anabwera kudzamumvetsera ndi kudzachiritsidwa matenda awo.” Ndipo n’zomwe zinachitikadi chifukwa Yesu ‘anawachiritsa onsewo.’ Ndiye tangoganizani, anthu ‘onse’ odwala anachiritsidwa. Yesu analalikiranso anthu amene “anali kusautsidwa ndi mizimu yonyansa,” omwe ankaponderezedwa ndi angelo oipa a Satana.—Luka 6:17-19.
Kenako Yesu anapeza malo ena abwino m’mbali mwa phirilo ndipo anthu ambiri anabwera n’kukhala momuzungulira. Pa nthawiyi atumwi ake 12 aja ayenera kuti anakhala naye pafupi. Anthu onsewo anali ndi chidwi kuti aphunzitsidwe ndi Yesu, yemwe analinso ndi mphamvu yochita zozizwitsa. Mfundo zimene anaphunzitsa pa nthawi imeneyo zinali zothandiza kwambiri kwa anthuwo ndipo zathandizanso anthu ena ambiri. Ifenso tingapindule kwambiri chifukwa anaphunzitsa mfundo zozama zauzimu m’njira yomveka bwino komanso yosavuta kumva. Yesu ankaphunzitsa pogwiritsa ntchito mafanizo komanso zinthu zimene anthuwo ankazidziwa bwino. Zimenezi zinathandiza kuti anthu amene ankafuna kuchita zinthu zosangalatsa Mulungu amvetse bwino mfundo zake. Kodi ndi mfundo zina ziti zimene zinachititsa kuti ulaliki wa Yesu wa paphiri ukhale wapadera kwambiri?
KODI NDI ANTHU OTANI AMENE AMAKHALA OSANGALALA?
Aliyense amafuna kukhala wosangalala. Yesu ankadziwa zimenezi, n’chifukwa chake anayamba ndi kufotokoza zimene anthu osangalala kapena kuti odala amachita. Anthu ambiri ayenera kuti anachita chidwi ndi nkhani imeneyi koma anadabwa ndi zinthu zina zimene Yesu ananena.
Iye anati: “Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu, chifukwa ufumu wakumwamba ndi wawo. Odala ndi anthu amene akumva chisoni, chifukwa adzasangalatsidwa. . . . Odala ndi anthu amene akumva njala ndi ludzu la chilungamo, chifukwa adzakhuta. . . . Odala ndi anthu amene akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo, pakuti ufumu wakumwamba ndi wawo. Ndinu odala pamene anthu akukunyozani ndi kukuzunzani, . . chifukwa cha ine. Kondwerani, dumphani ndi chimwemwe.”—Mateyu 5:3-12.
Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti “odala”? Iye sankanena za anthu omwe amadumphadumpha kapena kusangalala chifukwa chakuti pachitika zinazake zosangalatsa. Munthu wodala amasangalala kuchokera mumtima. Munthuyo amakhutira ndi zimene ali nazo komanso amaona kuti ali ndi zonse zomwe munthu amafunikira pa moyo wake.
Yesu ananena kuti anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu, amene amadzimvera chisoni chifukwa chakuti ndi ochimwa komanso amene amafuna kumudziwadi Mulungu ndi kumutumikira, amenewo ndi amene amakhaladi osangalala kapena kuti odala. Akamazunzidwa kapena anthu ena akamadana nawo chifukwa chochita zimene Mulungu amafuna, amakhalabe osangalala chifukwa amadziwa kuti akuchita zinthu zosangalatsa Mulungu komanso kuti adzawadalitsa powapatsa moyo wosatha.
Anthu ambiri amaganiza kuti munthu amakhala wosangalala ngati ali wotchuka komanso ngati ali ndi chuma. Koma Yesu ananena zosiyana ndi zimenezi. Pofuna kuthandiza anthuwo kuti amvetse mfundo yake, iye ananena kuti: “Koma tsoka inu anthu achuma, chifukwa mwalandiriratu zonse zokusangalatsani. Tsoka inu amene mukukhuta tsopano, chifukwa mudzamva njala. Tsoka inu amene mukuseka tsopano, chifukwa mudzamva chisoni ndi kulira. Muli ndi tsoka, anthu onse akamanena zabwino za inu, pakuti zoterezi n’zimene makolo awo akale anachitira aneneri onyenga.”—Luka 6:24-26.
Kodi kukhala ndi chuma, kuseka komanso kusangalala chifukwa chakuti anthu ena akunena zabwino za munthu kungamubweretsere bwanji tsoka? Kungamubweretsere tsoka chifukwa chakuti munthu akakhala ndi zinthu zimenezi n’kumaziona kuti ndi zofunika kwambiri amasiya kutumikira Yehova zomwe zimamuchititsa kuti asamakhalenso wosangalala. Yesu sankatanthauza kuti ngati munthu ali ndi njala kapena ngati ali wosauka ndiye kuti angakhale wosangalala. Komabe, nthawi zambiri anthu amene amakumana ndi mavuto ngati amenewa ndi amene amatsatira zimene Yesu anaphunzitsa. Kutsatira mfundo zimenezi n’kumene kumawathandiza kuti azikhaladi osangalala.
Kenako poganizira za ophunzira ake, Yesu ananena kuti: “Inu ndinu mchere wa dziko lapansi.” (Mateyu 5:13) N’chifukwa chiyani Yesu anayerekezera ophunzira ake ndi mchere? Mchere umathandiza kuti zinthu zisawonongeke kapena kuti zisawole. Komanso m’kachisi wa Mulungu, pambali pa guwa la nsembe pankakhala mchere wambiri womwe ankauthira pa nyama zoperekedwa nsembe. Zimenezi zinkasonyezanso kuti nsembeyo ndi yoyera komanso yosawonongeka. (Levitiko 2:13; Ezekieli 43:23, 24) Choncho, ophunzira a Yesu anali ngati “mchere wa dziko” chifukwa zochita zawo zinkathandiza anthu kuti apitirizebe kukhala pa ubwenzi ndi Yehova komanso kuti azikhala ndi makhalidwe abwino. Ndipo uthenga umene ophunzirawo ankalalikira unkathandiza komanso kuteteza moyo wa anthu amene ankamvetsera.
Yesu anauzanso ophunzira ake kuti: “Inu ndinu kuwala kwa dziko.” Munthu akayatsa nyale saivundikira ndi dengu koma amaiika pa choikapo nyale kuti iziwala. N’chifukwa chake Yesu ananena kuti: “Onetsani kuwala kwanu pamaso pa anthu, kuti aone ntchito zanu zabwino ndi kuti alemekeze Atate wanu wakumwamba.”—Mateyu 5:14-16.
MFUNDO ZIMENE OTSATIRA AKE ONSE AYENERA KUTSATIRA
Atsogoleri achipembedzo achiyuda ankadana ndi Yesu chifukwa chomuganizira kuti ankaphwanya Chilamulo cha Mulungu moti anayamba kukonza zoti amuphe. Choncho Yesu anawauza mosabisa kuti: “Musaganize kuti ndinabwera kudzawononga Chilamulo kapena Zolemba za aneneri. Sindinabwere kudzaziwononga koma kudzazikwaniritsa.”—Mateyu 5:17.
Yesu ankalemekeza kwambiri Chilamulo cha Mulungu ndipo ankalimbikitsanso anthu ena kuti azichita chimodzimodzi. Ndipotu ananena kuti: “Aliyense wophwanya lililonse la malamulo aang’ono awa ndi kuphunzitsa anthu kuphwanya malamulowo, adzakhala ‘wosayenera kulowa’ mu ufumu wakumwamba.” Ponena mawu amenewa ankatanthauza kuti munthu wochita zimenezi sadzalowa mu Ufumu wa Mulungu. Anapitirizanso kuti: “Koma aliyense wotsatira ndi kuphunzitsa malamulowa, ameneyo adzakhala ‘woyenera kulowa’ mu ufumu wakumwamba.”—Mateyu 5:19.
Yesu anawachenjezanso kuti ayenera kupewa makhalidwe amene akanawachititsa kuphwanya Chilamulo cha Mulungu. Popeza Yesu ankadziwa kuti Chilamulo chinkanena kuti “Usaphe munthu,” iye ananena kuti: “Aliyense wopitiriza kupsera mtima m’bale wake wapalamula mlandu wa kukhoti.” (Mateyu 5:21, 22) Kupitiriza kupsera mtima mnzathu ndi koopsa ndipo kukhoza kutichititsa kuti timuphe. Choncho Yesu anafotokoza zimene munthu ayenera kuchita kuti akhale pa mtendere ndi mnzake. Iye anati: “Choncho ngati wabweretsa mphatso yako paguwa lansembe, ndipo uli pomwepo wakumbukira kuti m’bale wako ali nawe chifukwa, siya mphatso yako patsogolo pa guwa lansembe pomwepo. Pita ukayanjane ndi m’bale wako choyamba, ndipo ukabwerako, pereka mphatso yako.”—Mateyu 5:23, 24.
Lamulo lina lomwe linali mu Chilamulo linali loletsa chigololo. Yesu ananena kuti: “Inu munamva kuti anati, ‘Usachite chigololo.’ Koma ine ndikukuuzani kuti aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kumulakalaka, wachita naye kale chigololo mumtima mwake.” (Mateyu 5:27, 28) Yesu sankanena za maganizo oipa amene nthawi zina munthu akhoza kukhala nawo, koma ankanena za kuopsa ‘koyang’anitsitsa.’ Ngati munthu akuyang’anitsitsa mkazi kapena mwamuna amayamba kulakalaka atagona naye ndiyeno akapeza mpata akhoza kuchita chigololo. Ndiye kodi munthu angatani kuti asafike pochita khalidwe loipali? Munthu afunika kukhala wosamala kwambiri komanso kukhala ndi mfundo zoti azizitsatira pa moyo wake. Yesu ananena kuti: “Tsopano ngati diso lako lakumanja limakuchimwitsa, ulikolowole ndi kulitaya. . . . Ngati dzanja lako lamanja limakuchimwitsa, ulidule ndi kulitaya.”—Mateyu 5:29, 30.
Anthu ena amalolera kuti dzanja kapena mwendo wawo womwe uli ndi matenda udulidwe kuti apulumutse moyo wawo. Choncho, m’pomveka kuti Yesu ananena kuti munthu afunika ‘kutaya’ chilichonse, kuti apewe kuganizira zinthu zoipa komanso kuti apewe zotsatirapo zake. Munthu afunika kutaya chilichonse ngakhale zinthu zooneka kuti ndi zofunika kwambiri ngati dzanja kapena diso. Yesu anati: “Pakuti n’kwabwino kuti ukhale wopanda chiwalo chimodzi kusiyana n’kuti thupi lako lonse lidzaponyedwe m’Gehenaa,” zomwe zikutanthauza kuti munthuyo adzawonongedwa ndipo sadzakhalanso ndi moyo.
Yesu anaperekanso malangizo omwe tingatsatire ngati munthu wina wachita zinthu zomwe zatikhumudwitsa. Iye ananena kuti: “Usalimbane ndi munthu woipa, koma wina akakumenya mbama patsaya lakumanja, umutembenuzirenso linalo.” (Mateyu 5:39) Zimenezi sizikutanthauza kuti munthu sangadziteteze kapena kuteteza banja lake ngati atakumana ndi achifwamba. Yesu ananena za kumenyedwa mbama yomwe cholinga chake sichikhala kuvulaza kapena kupha munthuyo, koma chimakhala kumuchititsa manyazi. Choncho mfundo ya Yesu inali yakuti, ngati munthu atafuna kuyambitsa ndewu kapena mkangano, pomenya mnzakeyo mbama kapena polankhula mawu achipongwe, woputidwayo sayenera kubwezera.
Mfundo imeneyi ndi yogwirizana ndi lamulo lonena za kukondana lomwe linali mu Chilamulo cha Mulungu. Choncho Yesu anauza anthu omwe ankamumvetsera kuti: “Pitirizani kukonda adani anu ndi kupempherera amene akukuzunzani.” Yesu ananenanso chifukwa chomveka chochitira zimenezi. Iye anati: “Kuti musonyeze kuti ndinudi ana a Atate wanu wakumwamba. Chifukwa iye amawalitsira dzuwa lake pa anthu oipa ndi abwino.”—Mateyu 5:44, 45.
Pofuna kuwathandiza anthuwo kumvetsa mfundo yaikulu ya nkhaniyi, Yesu anati: “Khalani angwiro, monga mmene Atate wanu wakumwamba alili wangwiro.” (Mateyu 5:48) Yesu sankatanthauza kuti anthu angakhaledi angwiro. Komabe ngati timatsanzira Mulungu tikhoza kusonyeza chikondi ngakhale kwa adani athu. M’mawu ena tinganene kuti: “Pitirizani kukhala achifundo, potengera Atate wanu amenenso ali wachifundo.”—Luka 6:36.
NKHANI YA PEMPHERO KOMANSO KUKHULUPIRIRA MULUNGU
Yesu anapitiriza kuphunzitsa anthuwo powalimbikitsa kuti: “Samalani kuti musamachite chilungamo chanu pamaso pa anthu ndi cholinga chakuti akuoneni.” Ponena zimenezi Yesu ankachenjeza anthu amene ankachita zinthu zachinyengo n’kumadzionetsera ngati akutumikira Mulungu. Iye ananenanso kuti: “Pamene ukupereka mphatso zachifundo, usalize lipenga muja amachitira onyenga.” (Mateyu 6:1, 2) Choncho ndi bwino kupereka mphatso zachifundo mosaonetsera kwa anthu ena.
Kenako Yesu ananena kuti: “Pamene mukupemphera, musamachite ngati anthu onyenga. Pakuti iwo amakonda kuimirira m’masunagoge ndi m’mphambano za misewu ikuluikulu kuti anthu aziwaona.” Ananenanso kuti: “Koma iwe popemphera, lowa m’chipinda chako pawekha ndi kutseka chitseko, ndipo pemphera kwa Atate wako amene ali kosaoneka.” (Mateyu 6:5, 6) Sikuti Yesu ankaletsa zopemphera pagulu chifukwa iyenso anaperekapo mapemphero oterowo. Koma ankaletsa zoti anthu azipemphera pagulu n’cholinga chofuna kugometsa anthu komanso kuti aziwapatsa ulemu.
Anauzanso anthuwo kuti: ‘Popemphera, musamanene zinthu mobwerezabwereza ngati mmene amachitira anthu a mitundu ina.’ (Mateyu 6:7) Yesu sankatanthauza kuti kupempherera nkhani yomweyomweyo n’kulakwa. Koma zomwe ananenazi zikusonyeza kuti sankagwirizana ndi zoti munthu azipereka “mobwerezabwereza” mapemphero ochita kuloweza. Kenako anapereka pemphero lachitsanzo lokhala ndi mfundo 7. Mfundo zitatu zoyambirira zimanena za cholinga cha Mulungu komanso kuti iye ndiye woyenera kulamulira. Mfundo zake ndi zakuti: Dzina la Mulungu liyeretsedwe, Ufumu wa Mulungu ubwere komanso chifuniro chake chichitike. Choncho tiziyamba kaye tatchula mfundo zimenezi kenako n’kutchula zinthu ngati izi: kuti atipatse chakudya cha tsiku ndi tsiku, kuti atikhululukire machimo athu, kuti tisalowe m’mayesero komanso kuti atipulumutse kwa woipayo.
Kodi tiziona bwanji chuma komanso katundu amene tili naye? Yesu analimbikitsa anthu aja kuti: “Lekani kudziunjikira chuma padziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri zimawononga, ndiponso pamene mbala zimathyola ndi kuba.” Zimenezi n’zomveka chifukwa katundu komanso chuma chikhoza kutha nthawi iliyonse. Ndipotu kukhala ndi chuma komanso katundu wambiri sikuchititsa kuti Mulungu azitiona kuti ndife ofunika kwambiri. N’chifukwa chake Yesu ananena kuti: “Unjikani chuma chanu kumwamba.” Tingachite zimenezi ngati timafunafuna Ufumu choyamba. Palibe amene angatilande mwayi wodzapeza moyo wosatha kapena kutilanda ubwenzi wathu ndi Mulungu. Choncho Yesu ananena zoona pamene ananena kuti: “Kumene kuli chuma chako, mtima wako umakhalanso komweko.”—Mateyu 6:19-21.
Pofuna kuwathandiza kumvetsa mfundoyi, Yesu anafotokoza fanizo lakuti: “Nyale ya thupi ndi diso. Chotero ngati diso lako lili lolunjika pa chinthu chimodzi, thupi lako lonse lidzakhala lowala. Koma ngati diso lako lili loipa, thupi lako lonse lidzachita mdima.” (Mateyu 6:22, 23) Ngati diso lathu lophiphiritsa limaona bwinobwino, limakhala ngati nyale imene ikuunikira thupi lonse. Koma kuti zimenezi zitheke, diso lathu liyenera kuyang’ana pa chinthu chimodzi, apo ayi tikhoza kumasankha zinthu zolakwika pa moyo wathu. Tikamangoganizira kwambiri za chuma komanso katundu wathu m’malo moganizira zotumikira Mulungu, tikhoza kuyamba kuchita zachinyengo zomwe zingatanthauze kuti ‘thupi lathu lonse lachita mdima.’
Kenako Yesu ananena mfundo yosatsutsika yakuti: “Kapolo sangatumikire ambuye awiri, pakuti adzadana ndi mmodzi ndi kukonda winayo, kapena adzakhulupirika kwa mmodzi ndi kunyoza winayo. Simungathe kutumikira Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.”—Mateyu 6:24.
Anthu ena amene ankamvetsera ulaliki wa Yesu ayenera kuti ankadera nkhawa mmene angapezere zinthu zofunikira pa moyo wawo. Choncho Yesu anawakhazika mtima pansi powauza kuti sayenera kudera nkhawa zinthu zimenezi ngati amafunafuna Ufumu choyamba. Anawauza kuti: “Onetsetsani mbalame zam’mlengalenga, pajatu sizifesa mbewu kapena kukolola, kapenanso kusunga chakudya m’nkhokwe. Koma Atate wanu wakumwamba amazidyetsa.”—Mateyu 6:26.
Ponena za maluwa akutchire amene anali paphiri limene anthu aja anakhala, Yesu ananena kuti: “Ngakhale Solomo mu ulemerero wake wonse sanavalepo zokongola ngati lililonse la maluwa amenewa.” Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Tikuphunzira kuti: ‘Ngati Mulungu amaveka chotero zomera zakutchire, zimene zimangokhalapo lero lokha, mawa n’kuzisonkheza pamoto, kodi iye sangativeke kuposa pamenepo?’ (Mateyu 6:29, 30) N’chifukwa chake Yesu ananena kuti: “Musamade nkhawa n’kumanena kuti, ‘Tidya chiyani?’ kapena, ‘Timwa chiyani?’ kapena, ‘Tivala chiyani?’ . . . Koma Atate wanu wakumwamba akudziwa kuti inuyo mumafunikira zinthu zonsezi. Chotero pitirizani kufunafuna ufumu choyamba ndi chilungamo chake, ndipo zina zonsezi zidzawonjezedwa kwa inu.”—Mateyu 6:31-33.
KODI MUNTHU ANGATANI KUTI APEZE MOYO?
Atumwi komanso anthu ena amtima wabwino ankafuna kusangalatsa Mulungu koma zimenezi sizinali zophweka chifukwa cha mmene zinthu zinalili. Mwachitsanzo, Afarisi ambiri ankakonda kupezera ena zifukwa komanso ankapupuluma kuweruza anthu ena. Choncho Yesu anachenjeza anthu amene ankamvetsera ulaliki wake kuti: “Lekani kuweruza ena kuti inunso musaweruzidwe, pakuti chiweruzo chimene mukuweruza nacho ena inunso mudzaweruzidwa nacho.”—Mateyu 7:1, 2.
Yesu anasonyeza kuti kutsatira zimene Afarisiwo ankachita kunali koopsa kwambiri. Pofuna kuthandiza anthuwo kumvetsa mfundo imeneyi ananena fanizo lakuti: “Wakhungu sangatsogolere wakhungu mnzake, angatero ngati? Ngati atatero onse awiri angagwere m’dzenje, si choncho kodi?” Ndiye kodi pamenepa Yesu ankawaphunzitsa kuti aziwaona bwanji anzawo? Sankafunika kumangoona zochita za anzawo n’cholinga choti awapezere zifukwa poti kuchita zimenezi unali mlandu waukulu. Ndiyeno Yesu anawafunsa kuti: “Ungauze bwanji m’bale wako kuti, ‘M’bale, taima ndikuchotse kachitsotso kamene kali m’diso lakoka,’ koma iwe osaona mtanda wa denga la nyumba umene uli m’diso lako? Wonyenga iwe! Yamba wachotsa mtanda wa denga la nyumba uli m’diso lakowo, ndipo ukatero udzatha kuona bwinobwino mmene ungachotsere kachitsotso kamene kali m’diso la m’bale wako.”—Luka 6:39-42.
Zimenezi si zinkatanthauza kuti ophunzira a Yesu analibiretu ufulu woweruza chifukwa pa nthawi ina Yesu anawauza kuti: “Musamapatse agalu zinthu zopatulika, kapena kuponyera nkhumba ngale zanu.” (Mateyu 7:6) Mfundo za choonadi zopezeka m’Mawu a Mulungu ndi zamtengo wapatali ngati ngale. Choncho ngati anthu ena atachita zinthu zosonyeza kusayamikira choonadi chamtengo wapatalichi ngati mmene agalu kapena nkhumba zimachitira, ophunzira a Yesu ankafunika kungowasiya n’kumakafunafuna anthu ofuna kudziwa Mulungu.
Kenako Yesu anapitiriza nkhani ya pemphero ija pofotokoza kufunika kolimbikira kupemphera. Ananena kuti: “Pemphanibe, ndipo adzakupatsani.” Mulungu ndi wokonzeka kuyankha mapemphero athu ndipo Yesu anasonyeza zimenezi powafunsa anthuwo kuti: “Ndani pakati panu amene mwana wake atamupempha mkate, iye angamupatse mwala? . . . Chotero ngati inuyo, ngakhale kuti ndinu oipa, mumadziwa kupereka mphatso zabwino kwa ana anu, kuli bwanji Atate wanu wakumwamba? Ndithudi, iye adzapereka zinthu zabwino kwa onse om’pempha!”—Mateyu 7:7-11.
Ndiyeno Yesu ananena mfundo yomwe ndi yofunika komanso yodziwika kwambiri pa nkhani yochita zinthu ndi anthu ena. Mfundoyo ndi yakuti: “Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zomwezo.” Tonse tingachite bwino kumaganizira mfundo yolimbikitsayi komanso kumaitsatira pochita zinthu ndi anthu ena. Komabe, kuchita zimenezi sikophweka, poganiziranso zimene Yesu ananena kuti: “Lowani pachipata chopapatiza. Pakuti msewu waukulu ndi wotakasuka ukupita kuchiwonongeko, ndipo anthu ambiri akuyenda mmenemo. Koma chipata cholowera ku moyo n’chopapatiza komanso msewu wake ndi wopanikiza, ndipo amene akuupeza ndi owerengeka.”—Mateyu 7:12-14.
Nthawi imeneyo panali anthu ena omwe ankafuna kusokoneza ophunzira a Yesu kuti asiye kutsatira mfundo zomwe zikanawathandiza kudzapeza moyo wosatha. Choncho Yesu anachenjeza ophunzirawo kuti: “Chenjerani ndi aneneri onyenga amene amabwera kwa inu atavala ngati nkhosa, koma mkati mwawo ali mimbulu yolusa.” (Mateyu 7:15) Yesu ananenanso kuti anthu amadziwa ngati mtengo uli wabwino kapena woipa akaona zipatso zake. Ndi mmene zililinso ndi anthu. Tikhoza kuzindikira aneneri onyenga poona zochita zawo komanso zimene amaphunzitsa. Ndipo Yesu anafotokozanso kuti munthu amadziwika kuti ndi wophunzira wake osati ndi zolankhula zake zokha, komanso ndi zochita zake. Anthu ena amanena kuti Yesu ndi Mbuye wawo. Koma bwanji ngati anthuwo sachita zimene Mulungu amafuna? Yesu ananena kuti: “Ine ndidzawauza momveka bwino kuti: ‘Sindikukudziwani ngakhale pang’ono! Chokani pamaso panga, anthu osamvera malamulo inu.’”—Mateyu 7:23.
Pomaliza ulaliki wake wa paphiri, Yesu ananena kuti: “Aliyense wakumva mawu angawa ndi kuwachita adzafanizidwa ndi munthu wochenjera, amene anamanga nyumba yake pathanthwe. Ndiyeno kunagwa chimvula champhamvu ndipo madzi anasefukira. Kenako chimphepo chinafika n’kuwomba nyumbayo, koma sinagwe chifukwa chakuti inakhazikika pathanthwepo.” (Mateyu 7:24, 25) Koma n’chiyani chinathandiza kuti nyumbayo isagwe? Chifukwa chakuti munthuyo “anakumba mozama kwambiri ndi kuyala maziko pathanthwe.” (Luka 6:48) Choncho kungomva zimene Yesu anaphunzitsa sikokwanira. Tiyenera kuyesetsa ‘kumachita’ zimene taphunzirazo.
Nanga bwanji za munthu amene ‘amamva mawu’ a Yesu koma “osawachita”? Munthu woteroyo ali ngati ‘munthu wopusa amene amamanga nyumba yake pamchenga.’ (Mateyu 7:26) Nyumbayo ikhoza kugwa ngati kutabwera mvula, madzi osefukira kapena mphepo yamphamvu.
Anthuwo anadabwa kwambiri ndi mmene Yesu anawaphunzitsira pa ulaliki umenewu. Iye anawaphunzitsa monga munthu waulamuliro osati ngati atsogoleri achipembedzo aja. N’kutheka kuti anthu ambiri amene anamvetsera zimene Yesu anaphunzitsa anakhala ophunzira ake.
a Malo amene ankatayako komanso kuwotcherako zinyalala omwe anali kunja kwa mpanda wa Yerusalemu