Mungakhale ndi Khalidwe Labwino mwa Kutsatira Zimene Yesu Anaphunzitsa
“Wotumidwa ndi Mulungu amalankhula mawu a Mulungu.”—YOH. 3:34.
1, 2. N’chifukwa chiyani tinganene kuti ulaliki wonse wa pa phiri unali “mawu a Mulungu”?
PA ULALIKI wake wa pa phiri, Yesu anaphunzitsa mfundo zochuluka zofunika kwambiri. Zimenezi n’zosadabwitsa chifukwa Khristu ankaphunzitsa mawu ochokera kwa Yehova. Pofotokoza mmene Yesu ankaphunzitsira, Baibulo limati: “Wotumidwa ndi Mulungu amalankhula mawu a Mulungu.”—Yoh. 3:34-36.
2 Ngakhale kuti Yesu anakamba ulaliki wa pa phiriwu mwina kwa mphindi zosakwana 30, iye anagwira mawu Malemba Achiheberi maulendo 21, m’mabuku 8. Choncho, ulaliki wonsewu unalidi “mawu a Mulungu.” Tsopano tiyeni tione mmene tingagwiritsire ntchito zina mwa mfundo zamtengo wapatali zopezeka mu ulaliki wogwira mtima umenewu, wa Mwana wokondedwa wa Mulungu.
“Ukayanjane ndi M’bale Wako Choyamba”
3. Atachenjeza ophunzira ake za kuopsa kwa mkwiyo, kodi Yesu anawalangiza chiyani?
3 Monga Akhristu, timakhala osangalala ndiponso timadzetsa mtendere chifukwa choti tili ndi mzimu woyera wa Mulungu. Ndipo chimwemwe ndi mtendere ndi zina mwa zipatso za mzimuwu. (Agal. 5:22, 23) Yesu ankafuna kuti ophunzira ake apitirize kukhala mwamtendere ndiponso mosangalala, choncho iye anawachenjeza za kuopsa kopitiriza kukhala ndi mkwiyo, komwe kungachititse imfa. (Werengani Mateyo 5:21, 22.) Kenako anati: “Chotero ngati wabweretsa mphatso yako paguwa la nsembe, ndipo uli pomwepo wakumbukira kuti m’bale wako ali nawe chifukwa, siya mphatso yako patsogolo pa guwa la nsembe pomwepo. Pita ukayanjane ndi m’bale wako choyamba, ndipo ukabwerako, pereka mphatso yako.”—Mat. 5:23, 24.
4, 5. (a) Kodi “mphatso” imene Yesu ananena pa Mateyo 5:23, 24 inali chiyani? (b) Kodi kuyanjana ndi m’bale wathu amene tamulakwira n’kofunika motani?
4 “Mphatso” imene Yesu anatchula inali nsembe yamtundu uliwonse yoperekedwa pakachisi ku Yerusalemu. Mwachitsanzo, kupereka nsembe za nyama kunali kofunika kwambiri panthawiyo chifukwa chakuti inali mbali ya kulambira Yehova. Komabe, Yesu anasonyeza kuti kuyanjana ndi munthu amene tamulakwira, tisanapereke mphatso kwa Mulungu ndiko chinthu chofunika kwambiri.
5 Choncho, kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Yesu ananena? Tikuphunzirapo kuti zimene timachitira anthu ena zimakhudza kwambiri ubwenzi wathu ndi Yehova. (1 Yoh. 4:20) Nsembe zimene anthu akale ankapereka kwa Mulungu zinali zopanda ntchito ngati woperekayo sankakhala bwino ndi ena.—Werengani Mika 6:6-8.
Kudzichepetsa N’kofunika Kwambiri
6, 7. Kuti tiyanjanenso ndi m’bale wathu amene tamulakwira, n’chifukwa chiyani pamafunika kudzichepetsa?
6 Pamafunika kukhala wodzichepetsa kwambiri kuti tiyanjanenso ndi m’bale wathu. Anthu odzichepetsa sakangana kapena kulimbana ndi Akhristu anzawo poyesa kuteteza ufulu wawo. Kulimbana kapena kukangana ndi abale athu kungabweretse mavuto ngati mmene zinalili mu mpingo wa ku Korinto. Chifukwa cha mavuto amenewo, mtumwi Paulo anauza mpingowo kuti: “Ndiye kuti mwalephereratu ngati mukutengerana wina ndi mnzake ku khoti. Bwanji osangolola kulakwiridwa? Bwanji osalola kuberedwa?”—1 Akor. 6:7.
7 Yesu sananene kuti cholinga chopitira kwa m’bale wathu ndicho kukam’sonyeza kuti ifeyo sitinalakwe koma iyeyo ndiye wolakwa. Cholinga chathu chizikhala kukayanjananso ndi m’bale wathuyo. Kuti zimenezi zitheke tifunika kufotokoza moona mtima zimene zili kukhosi kwathu. Tifunikanso kuzindikira kuti mnzathuyo wakhumudwa. Ndipo ngati talakwa, tiyenera kupepesa modzichepetsa.
“Ngati Diso Lako Lakumanja Limakupunthwitsa”
8. Fotokozani mwachidule zimene Yesu ananena pa Mateyo 5:29, 30.
8 Pa ulaliki wake wa pa phiri, Yesu anapereka malangizo abwino pankhani ya makhalidwe. Iye ankadziwa kuti munthu angachite zinthu zolakwika kwambiri chifukwa cha thupi lake lopanda ungwiro. N’chifukwa chake anati: “Ngati diso lako lakumanja limakupunthwitsa, ulikolowole ndi kulitaya. Pakuti n’kwabwino kuti ukhale wopanda chiwalo chimodzi kusiyana n’kuti thupi lako lonse liponyedwe m’Gehena. Komanso ngati dzanja lako lamanja limakulakwitsa, ulidule ndi kulitaya. Pakuti n’kwabwino kuti ukhale wopanda chiwalo chimodzi kusiyana n’kuti thupi lako lonse liponyedwe m’Gehena.”—Mat. 5:29, 30.
9. Kodi “diso” kapena “dzanja” lathu ‘lingatipunthwitse’ motani?
9 “Diso” limene Yesu ananena likutanthauza mphamvu ya kuonetsetsa ndi kuganizira kwambiri chinthu chinachake, ndipo “dzanja” likutanthauza zimene timachita ndi manja athu. Tikapanda kusamala, ziwalo zimenezi zingathe ‘kutipunthwitsa’ n’kusiya ‘kuyenda ndi Mulungu.’ (Gen. 5:22; 6:9) Choncho tikamayesedwa kuti tichite choipa, tifunika kuchita chilichonse chimene tingathe kuti tipewe choipacho, ndipo zimenezi zili ngati kukolowola diso kapena kudula dzanja.
10, 11. N’chiyani chingatithandize kupewa chiwerewere?
10 Kodi tingatani kuti tiletse maso athu kuyang’anitsitsa zinthu zoipa? Yobu, yemwe anali munthu woopa Mulungu anati: “Ndinapangana ndi maso anga, potero ndipenyerenji namwali?” (Yobu 31:1) Yobu anali munthu wokwatira ndipo anatsimikiza mtima kuti asaswe malamulo a Mulungu okhudza makhalidwe abwino. Ifenso tiyenera kukhala ndi maganizo ngati amenewa, kaya tili pabanja kapena ayi. Kuti tipewe kuchita chiwerewere, timafunika kutsogoleredwa ndi mzimu woyera, umene umathandiza anthu okonda Mulungu kukhala odziletsa.—Agal. 5:22-25.
11 Kuti tipewe kuchita chiwerewere, tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndimalola maso anga kundichititsa kukhala ndi chilakolako choona zinthu zolaula zimene zimapezeka m’mabuku, pa TV, kapena pa Intaneti?’ Ndi bwino kuti tizikumbukiranso mawu amene wophunzira Yakobe analemba, kuti: “Munthu aliyense amayesedwa mwa kukopedwa ndi kukodwa m’chilakolako cha iye mwini. Ndiye chilakolako chikatenga pathupi, chimabala tchimo; nalonso tchimo likakwaniritsidwa, limabweretsa imfa.” (Yak. 1:14, 15) Ndipo ngati munthu wodzipereka kwa Mulungu ‘amayang’anitsitsa’ munthu yemwe si mwamuna kapena mkazi mnzake momulakalaka, ayenera kuyesetsa kusiya khalidwe lakelo, ndipo zimenezi zikufanana ndi kukolowola diso n’kulitaya.—Werengani Mateyo 5:27, 28.
12. Kodi Paulo anapereka malangizo otani amene angatithandize kupewa zilakolako zoipa?
12 Kugwiritsa ntchito manja athu molakwika kungatichititse kuswa mfundo za Yehova za makhalidwe abwino. Ndipo tiyenera kutsimikiza mtima kuti tisakhale ndi makhalidwe oipa. Choncho, tiyenera kutsatira malangizo a mtumwi Paulo akuti: “Chititsani ziwalo za thupi lanu pa dziko lapansi kukhala zakufa ku dama, chonyansa, chilakolako cha kugonana, chikhumbo choipa, ndi kusirira kwa nsanje, kumene ndiko kulambira mafano.” (Akol. 3:5) Mawu akuti ‘chititsani kukhala zakufa’ akusonyeza kuti m’pofunika kuyesetsa kuchita chilichonse chimene tingathe kuti tipewe zilakolako zoipa.
13, 14. N’chifukwa chiyani kupewa maganizo ndi makhalidwe oipa kuli kofunika?
13 Pofuna kupulumutsa moyo wake, munthu akhoza kuvomereza kuti adokotala amudule mwendo kapena dzanja limene lili ndi vuto. ‘Kutaya’ diso kapena dzanja lathu mophiphiritsa n’kofunika chifukwa kungatithandize kupewa kuganizira ndiponso kuchita zinthu zolakwika zimene zingawonongetse moyo wathu wauzimu. Kukhala oyera mwamaganizo, mwamakhalidwe ndiponso mwauzimu ndi njira yokhayo imene ingatithandize kupewa Gehena, yemwe ndi chiwonongeko chotheratu.
14 M’pofunika kuchita khama kwambiri kuti tipitirize kukhala ndi makhalidwe abwino, chifukwa ndife ochimwa ndiponso opanda ungwiro. N’chifukwa chake Paulo anati: “Ndipumphuntha thupi langa ndi kulitsogolera ngati kapolo, kuopera kuti, pambuyo poti ndalalikira kwa ena, ine ndemwe ndingakhale wosayenera m’njira inayake.” (1 Akor. 9:27) Choncho, tiyeni tiyesetse kutsatira malangizo a Yesu pankhani yokhudza makhalidwe abwino, ndipo tipewe kuchita chilichonse chosonyeza kusayamikira nsembe yake yadipo.—Mat. 20:28; Aheb. 6:4-6.
“Khalani Opatsa”
15, 16. (a) Kodi Yesu anasonyeza motani chitsanzo pankhani ya kupatsa? (b) Kodi mawu a Yesu a pa Luka 6:38 amatanthauza chiyani?
15 Chitsanzo chabwino kwambiri cha Yesu pankhani ya kupatsa ndiponso zimene anaphunzitsa, zimatilimbikitsa nafenso kukhala opatsa. Iye anasonyeza kuti ndi wowolowa m’manja kwambiri pamene anabwera padziko lapansi kudzathandiza anthu ochimwa. (Werengani 2 Akorinto 8:9.) Yesu anasiya ulemerero wake kumwamba n’kudzakhala monga munthu padziko lapansi ndiponso kudzafera anthu ochimwa. Ena mwa anthu amenewa anadzapeza chuma kumwamba monga olamulira anzake mu Ufumu wa Mulungu. (Aroma 8:16, 17) Ndipo Yesu analimbikitsa anthu kukhala opatsa pamene ananena kuti:
16 “Khalani opatsa, inunso anthu adzakupatsani. Adzakhuthulira m’matumba anu muyeso wabwino, wotsendereka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Pakuti muyeso umene mukupimira ena, iwonso adzakupimirani womwewo.” (Luka 6:38) Mawu akuti ‘kukhuthulira m’matumba’ palembali akunena zomwe zinkachitika kale m’misika. Nthawi imeneyo, munthu wogula malonda ankapinda chovala chake chakumtunda kuti chikhale ngati thumba ndipo wogulitsa malonda ankathira zinthu m’menemo. Ngati ndife owolowa manja, anthu enanso angatipatse zinthu mowolowa manja, mwina panthawi imene tili m’mavuto.—Mlal. 11:2.
17. Kodi Yehova anatisonyeza motani chitsanzo chabwino pankhani ya kupatsa, ndipo n’kupatsa kotani kumene kungatibweretsere chimwemwe?
17 Yehova amakonda anthu amtima wopatsa ndipo amawadalitsa. Iye anatisonyeza chitsanzo chabwino pankhani imeneyi pamene anatipatsa Mwana wake wobadwa yekha, “kuti aliyense wokhulupirira mwa iye asawonongeke, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yoh. 3:16) Paulo analemba kuti: “Wobzala mowolowa manja adzakololanso zochuluka. Aliyense achite mwa kutsimikiza kwa mtima wake, osati monyinyirika kapena mokakamizika ayi, pakuti Mulungu amakonda wopereka mokondwera.” (2 Akor. 9:6, 7) Kukhala wopatsa pa zinthu zathu monga nthawi, mphamvu ndiponso chuma, pothandiza kupititsa patsogolo kulambira koona, kumatithandiza kukhala ndi chimwemwe komanso timalandira madalitso ambiri.—Werengani Miyambo 19:17; Luka 16:9.
“Usalize Lipenga”
18. Kodi ndi zinthu ziti zimene zingachititse kuti ‘tisadzalandire mphoto’ kwa Atate wathu wakumwamba?
18 “Samalani kuti musamachite chilungamo chanu pamaso pa anthu ndi cholinga chakuti akuoneni; chifukwa mukatero simudzalandira mphoto kwa Atate wanu amene ali kumwamba.” (Mat. 6:1) Ponena kuti “chilungamo,” Yesu ankatanthauza khalidwe logwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Iye sankatanthauza kuti tisamaonetse khalidwe limeneli pagulu, chifukwa anali atauza ophunzira ake kuti: “Onetsani kuwala kwanu pamaso pa anthu.” (Mat. 5:14-16) Koma ‘sitidzalandira mphoto’ kwa Atate wathu wakumwamba ngati timachita zinthu ‘n’cholinga choti anthu atione,’ ngati mmene amachitira akatswiri azisudzo pochita sewero. Tikakhala ndi maganizo odzionetsera, sitingakhale paubwenzi ndi Mulungu ndiponso sitidzalandira madalitso osatha mu Ufumu wake.
19, 20. (a) Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti ‘tisalize lipenga’ tikafuna kupereka “mphatso za chifundo”? (b) Kodi tingatani kuti dzanja lathu lamanzere lisadziwe zimene dzanja lamanja likuchita?
19 Ngati tili ndi maganizo abwino tidzatsatira malangizo a Yesu akuti: “Pamene ukupereka mphatso za chifundo, usalize lipenga muja amachitira onyenga m’masunagoge ndi m’misewu, kuti anthu awatamande. Ndithu ndikukuuzani, Amenewo akulandiriratu mphoto yawo yonse.” (Mat. 6:2) “Mphatso za chifundo” zimenezi zinali zinthu zomwe anthu ankapereka pothandiza osauka. (Werengani Yesaya 58:6, 7.) Yesu ndi ophunzira ake anali ndi thumba la ndalama zothandizira osauka. (Yoh. 12:5-8; 13:29) Popeza kuti anthu sankachita kulizadi lipenga pofuna kuthandiza osauka, n’zoonekeratu kuti Yesu anagwiritsa ntchito mawu okokomeza pamene ananena kuti ‘tisalize lipenga’ tikafuna kupereka “mphatso za chifundo.” Mosiyana ndi Afarisi, sitiyenera kulengeza tikathandiza anthu osauka. Yesu anawatchula kuti ndi onyenga chifukwa ankalengeza “m’masunagoge ndi m’misewu” akathandiza anthu. Anthu onyenga amenewo anali ‘kulandiriratu mphoto yawo yonse.’ Kutamandidwa ndi anthu komanso mwina kukhala limodzi ndi arabi otchuka pamipando yakutsogolo m’masunagoge, inali mphoto imene iwo ankalandiriratu. Ndipo anthu amenewa sakanayembekezera kulandira chinthu chilichonse kwa Yehova. (Mat. 23:6) Nanga ophunzira a Khristu anayenera kumachita zinthu motani? Yesu anawauza mawu amene akugwiranso ntchito kwa ife, akuti:
20 “Koma iwe, pamene ukupereka mphatso za chifundo, dzanja lako lamanzere lisadziwe zimene dzanja lako lamanja likuchita, kuti mphatso zako za chifundo zikhale zamseri; ukatero Atate wako amene akuyang’ana kuseriko adzakubwezera.” (Mat. 6:3, 4) Nthawi zambiri manja athu amagwira ntchito pamodzi. Choncho, mfundo yakuti dzanja lathu lamanzere lisadziwe zimene dzanja lathu lamanja likuchita ikutanthauza kuti tikathandiza ena, sitiyenera kulengeza zimenezo, ngakhale kwa anzathu apamtima kwambiri.
21. Kodi Yehova, ‘amene amayang’ana kuseri,’ angatibwezere zinthu monga ziti?
21 ‘Mphatso zathu zachifundo’ zimakhala zamseri, ngati sitidzitamandira tikathandiza ena. Motero Atate wathu, amene ‘amayang’ana kuseriko’ adzatibwezera. Popeza Atate wathu amakhala kumwamba ndipo sitingathe kumuona, tinganene kuti iye amakhala ‘kuseri.’ (Yoh. 1:18) Kubwezera kumene Yehova, ‘amene amayang’ana kuseri,’ angatichitire kukuphatikizapo kutilola kukhala naye paubwenzi, kutikhululukira machimo ndiponso kutipatsa moyo wosatha. (Miy. 3:32; Yoh. 17:3; Aef. 1:7) Amenewatu ndi madalitso abwino kwambiri kuposa kutamandidwa ndi anthu.
Yamikirani Mfundo Zamtengo Wapatali Zimene Yesu Anaphunzitsa
22, 23. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyamikira zimene Yesu anaphunzitsa?
22 Ulaliki wa pa phiri uli ndi mfundo zambiri zamtengo wapatali zothandiza pamoyo wathu wauzimu, zomwenso zingatithandize kukhala achimwemwe m’dziko lamavutoli. Timakhala osangalala tikamayamikira ndiponso kugwiritsa ntchito mfundo zimene Yesu anaphunzitsa.
23 Aliyense “wakumva” ndi ‘kuchita’ zimene Yesu anaphunzitsa adzadalitsidwa kwambiri. (Werengani Mateyo 7:24, 25.) Choncho, tiyeni tikhale otsimikiza mtima kutsatira malangizo a Yesu. Mfundo zina zimene iye anaphunzitsa pa ulaliki wake wa pa phiri tizikambirana m’nkhani yotsatirayi.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi kuyanjana ndi m’bale wathu amene tamulakwira n’kofunika chifukwa chiyani?
• Kodi tingatani kuti ‘diso lathu lakumanja’ lisamatipunthwitse?
• Kodi tiyenera kukhala otani pankhani ya kupatsa?
[Chithunzi patsamba 11]
Ndi bwino kwambiri ‘kuyanjananso’ ndi Mkhristu mnzathu amene tamulakwira
[Zithunzi pamasamba 12, 13]
Yehova amadalitsa anthu amtima wopatsa