Kodi Tiyenera Kupemphera Motani kwa Mulungu?
PAMENE wophunzira anapempha malangizo onena za pemphero, Yesu sanakane kumpatsa. Malinga ndi Luka 11:2-4, iye anayankha kuti: “Mmene mupemphera nenani, Atate, dzina lanu liyeretsedwe; ufumu wanu udze; tipatseni ife tsiku ndi tsiku chakudya cha patsiku. Ndipo mutikhululukire ife machimo athu; pakuti ifenso tikhululukira munthu yense wa mangawa athu. Ndipo musatitengere ife kokatiyesa.” Limeneli ambiri amalidziŵa kukhala Pemphero la Ambuye. Limapereka chidziŵitso chochuluka.
Choyamba, liwu loyambirira lenilenilo likutiuza kumene tiyenera kupereka mapemphero athu—kwa Atate wathu. Taonani kuti Yesu sanapereke mpata uliwonse wa kupemphera kwa munthu wina wake, fano, “woyera mtima,” kapena ngakhale kwa iye. Ndipotu Mulungu analengeza kuti: “Ulemerero wanga ine sindidzapereka kwa wina, ngakhale kunditamanda kwa mafano osemedwa.” (Yesaya 42:8) Motero mapemphero operekedwa ku chilichonse kapena kwa aliyense koma osati kwa Atate wathu wakumwamba samamvedwa ndi iye, kaya wolambirayo akhale woona mtima motani. M’Baibulo, Yehova Mulungu yekha ndiye amatchedwa “Wakumva pemphero.”—Salmo 65:2.
Ena anganene kuti “oyera mtima” amangokhala ngati atetezi kwa Mulungu. Koma Yesu iye mwini analangiza kuti: “Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa ine. Ndipo chimene chilichonse mukafunse m’dzina langa, ndidzachichita, kuti Atate akalemekezedwe mwa Mwana.” (Yohane 14:6, 13) Motero Yesu anachotsapo lingaliro lakuti aliyense wotchedwa woyera mtima angakhale mtetezi. Taonaninso zimene mtumwi Paulo ananena pa Kristu: “Sanangotifera—adauka kwa akufa, ndipo amaimirira kudzanja lamanja la Mulungu ndi kutipembedzera ife komweko.” “Akhala ndi moyo kosatha kuteteza onse amene adza kwa Mulungu mwa iye.”—Aroma 8:34; Ahebri 7:25, Jesuralem Bible yachikatolika.
Dzina Limene Liyenera Kuyeretsedwa
Mawu otsatira a pemphero la Yesu anali akuti: “Dzina lanu liyeretsedwe.” Kodi munthu angayeretsere motani, kapena kupatula, dzina la Mulungu ngati sakulidziŵa ndipo saligwiritsira ntchito? Mulungu akutchulidwa ndi dzina lake lakuti Yehova nthaŵi zoposa 6,000 mu “Chipangano Chakale.”
Mawu amtsinde pa Eksodo 6:3 mu Douay Version yachikatolika amati ponena za dzina la Mulungu: “Anthu ena amakono apanga dzina lakuti Yehova . . . , kukhala matchulidwe enieni a dzina [la Mulungu], limene lili m’malemba achihebri, amene sakudziŵika bwino tsopano chifukwa cha kusagwiritsiridwa ntchito kwa nthaŵi yaitali.” Motero New Jerusalem Bible yachikatolika imagwiritsira ntchito dzina lakuti Yahweh. Ngakhale kuti akatswiri ena amakonda matchulidwe amenewo, “Yehova” ndi matchulidwe oyenera ndipo odziŵika kwa nthaŵi yaitali a dzina la Mulungu m’Chicheŵa. Zinenero zina zili ndi matchulidwe awo a dzina la Mulungu. Chofunika koposa ndicho chakuti tizigwiritsira ntchito dzinalo kuti tiliyeretse. Kodi tchalitchi chanu chakuphunzitsani kugwiritsira ntchito dzina lakuti Yehova m’pemphero?
Nkhani Zoyenera Zotchula m’Pemphero
Ndiyeno Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kupemphera kuti: “Ufumu wanu udze.” Uthenga Wabwino wa Mateyu umawonjezera mawu akuti: “Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:10) Ufumu wa Mulungu ndi boma lokhala m’manja mwa Yesu Kristu. (Yesaya 9:6, 7) Malinga ndi ulosi wa Baibulo, posachedwapa udzaloŵa m’malo maboma onse a anthu ndi kudzetsa nyengo ya mtendere wa padziko lonse. (Salmo 72:1-7; Danieli 2:44; Chivumbulutso 21:3-5) Chotero Akristu oona kaŵirikaŵiri amatchula nkhani ya kudza kwa Ufumu m’mapemphero awo. Kodi tchalitchi chanu chakuphunzitsani kuchita motero?
Chokondweretsa ndicho chakuti Yesu anasonyezanso kuti mapemphero athu angaphatikizepo nkhani zaumwini zimene zimatikhudza. Iye anati: “Tipatseni ife tsiku ndi tsiku chakudya cha patsiku. Ndipo mutikhululukire ife machimo athu; pakuti ifenso tikhululukira munthu yense wa mangawa athu. Ndipo musatitengere ife kokatiyesa.” (Luka 11:3, 4) Mawu a Yesu amatanthauza kuti m’zochitika za tsiku ndi tsiku tingapemphe chifuniro cha Mulungu, kuti tingafikire Yehova pa chilichonse chimene chingatidetse nkhaŵa kapena kusokoneza mtendere wathu wamaganizo. Kuchonderera Mulungu m’njira imeneyi nthaŵi zonse kumatithandiza kuzindikira kuti timadalira pa iye. Motero timazindikira bwino lomwe kuti amalamulira moyo wathu. Mofananamo nkopindulitsa kupempha Mulungu tsiku ndi tsiku kuti atikhululukire zolakwa zathu. Chotero timazindikira bwino lomwe zofooka zathu—ndi kukhala ololera kwambiri zophophonya za ena. Chilimbikitso cha Yesu chakuti tizipempherera kulanditsidwa kwathu pa ziyeso nchoyenereranso, makamaka chifukwa cha makhalidwe omaluluzika a dziko lino. Mogwirizana ndi pemphero limenelo, timasamala kupeŵa mikhalidwe imene ingatichititse kulakwa.
Chotero, nkosakayikiritsa kuti Pemphero la Ambuye limatiuza zambiri ponena za kupereka mapemphero amene amakondweretsa Mulungu. Koma kodi Yesu anafuna kuti tiphunzire pemphero limeneli ndi kumangolitchula pamtima nthaŵi zonse?
Uphungu Wowonjezereka pa Pemphero
Yesu anapereka malangizo owonjezereka pa pemphero. Pa Mateyu 6:5, 6, timaŵerenga kuti: “Pamene mupemphera, musakhale monga onyengawo; chifukwa iwo akonda kuimirira ndi kupemphera m’masunagoge, ndi pa mphambano za makwalala, kuti aonekere kwa anthu. . . . Koma iwe popemphera, loŵa m’chipinda chako, nutseke chitseko chako, nupemphere Atate wako ali mtseri, ndipo Atate wako wakuona mtseri adzakubwezera iwe.” Mawuŵa akutiphunzitsa kuti pemphero siliyenera kuperekedwa m’njira yodzionetsera ndi yodzitamanda kuti tikondweretse wina wake. Kodi mumatsanulira mtima wanu kwa Yehova mtseri, monga momwe Baibulo limalimbikitsira?—Salmo 62:8.
Yesu anachenjeza kuti: “Popemphera musabwerezebwereze chabe iyayi, monga amachita anthu akunja, chifukwa ayesa kuti adzamvedwa ndi kulankhulalankhula kwawo.” (Mateyu 6:7) Momvekera bwino, Yesu sanavomereze kuloŵeza mapemphero pamtima—ngakhale kuwaŵerenga m’buku lina lake. Mawu ake amaletsanso kugwiritsira ntchito korona.
Buku la mapemphero la Akatolika limavomereza kuti: “Pemphero lathu labwino koposa lingakhale malingaliro athu achibadwa ongobwera pamene titembenukira kwa iye ndi chiyamiko kapena pofuna thandizo, pa nthaŵi zachisoni, kapena pa kumtamanda kwathu kwa nthaŵi zonse.” Mapemphero a Yesu iye mwini anali achibadwa, osati oloŵeza pamtima. Mwachitsanzo, ŵerengani pemphero la Yesu lopezeka pa Yohane chaputala cha 17. Linamamatira kupemphero la chitsanzo, likumamveketsa chikhumbo cha Yesu cha kuona dzina la Yehova litayeretsedwa. Pemphero la Yesu linali lachibadwa ndipo lochokeradi mumtima.
Mapemphero Amene Mulungu Amamva
Ngati munaphunzitsidwa kupereka mapemphero oloŵeza pamtima, kupemphera kwa “oyera mtima” kapena ku mafano, kapena kugwiritsira ntchito zinthu zachipembedzo, zonga korona, kupemphera m’njira imene Yesu anasonyeza kungaoneke kukhala kovuta kwambiri panthaŵi yoyamba. Komabe, mfungulo yake ndiyo kudziŵa Mulungu—dzina lake, zifuno zake, umunthu wake. Mungachite zimenezi mwa kuphunzira Baibulo mosamalitsa kwambiri. (Yohane 17:3) Mboni za Yehova zili zokonzeka ndipo zikufunitsitsa kukuthandizani pa zimenezi. Inde, zathandiza anthu mamiliyoni kuzungulira dziko ‘kulawa, ndi kuona kuti Yehova ndiye wabwino!’ (Salmo 34:8) Pamene mudziŵa Mulungu kwambiri, ndi pamenenso mudzasonkhezeredwa kwambiri kumtamanda m’pemphero. Ndiponso pamene muyandikira kwambiri kwa Yehova m’mapemphero aulemu, ndi pamenenso unansi wanu ndi iye udzakhala wathithithi.
Motero alambiri onse oona a Mulungu akulimbikitsidwa ‘kupemphera kosaleka.’ (1 Atesalonika 5:17) Tsimikizirani kuti mapemphero anu ngogwirizanadi ndi Baibulo, kuphatikizapo malangizo a Yesu Kristu. Mwa njira imeneyo mungakhale otsimikiza kuti mapemphero anu adzayanjidwa ndi Mulungu.
[Chithunzi patsamba 7]
Pamene tiphunzira zambiri ponena za Yehova, ndi pamenenso timasonkhezeredwa kwambiri kupemphera kwa iye kuchokera mumtima