“Tiphunzitseni Ife Kupemphera”
“Wina wa ophunzira ake anati kwa iye, Ambuye, tiphunzitseni ife kupemphera.”—LUKA 11:1.
1-3. (a) Kodi nchifukwa ninji ophunzira a Yesu anafunafuna malangizo a pemphero? (b) Kodi ndi mafunso otani a pemphero omwe amabuka?
ANTHU ena ali ndi mphatso ya liwu labwino la kuimba. Ena ali ndi maluso achibadwa monga akatswiri oimba ndi zoimbira. Koma kuti afikire kukhala aluso kwambiri, ngakhale oimba ndi oliza malimba ameneŵa amafunikira malangizo. Nzofanana ndi pemphero. Ophunzira a Yesu Kristu anafikira pakuzindikira kuti anafunikira malangizo ngati Mulungu anali kudzamva mapemphero awo.
2 Kaŵirikaŵiri Yesu anapita mwamtseri kwa Atate ŵake m’pemphero, monga mmene anachitira usiku wonse asanasankhe atumwi 12. (Luka 6:12-16) Ngakhale kuti anafulumizanso ophunzira ake kupemphera mwamtseri, iwo anamumva akupemphera poyera ndipo anawona kuti anali wosafanana ndi onyenga achipembedzo amene anapemphera kuti awonedwe ndi anthu. (Mateyu 6:5, 6) Pamenepo, mwachiwonekere, otsatira a Yesu anafuna malangizo ake apamwamba onena za pemphero. Chotero, timaŵerenga kuti: “Ndipo kunali, pakukhala iye pamalo pena ndi kupemphera, mmene analeka, wina wa ophunzira ake anati kwa iye, Ambuye, tiphunzitseni ife kupemphera, monganso Yohane [m’Batizi] anaphunzitsira ophunzira ake.”—Luka 11:1.
3 Kodi Yesu anayankha motani? Kodi tingaphunzirenji kuchokera m’chitsanzo chake? Ndipo kodi tingapindulire motani kumalangizo ake onena za pemphero?
Phunziro kwa Ife
4. Kodi nchifukwa ninji tiyenera “kupemphera mosalekeza,” ndipo kutero kumatanthauzanji?
4 Tingaphunzire zambiri m’mawu ndi chitsanzo cha Yesu monga munthu wodziŵa kupemphera. Phunziro limodzi nlakuti ngati Mwana wangwiro wa Mulungu anafunikira kupemphera mokhazikika, ndiko kuti ophunzira ake opanda ungwirowo afunikira kwakukulukulu kuyang’ana kwa Mulungu mosalekeza kaamba ka chitsogozo, chitonthozo, ndi chichirikizo chauzimu. Motero, tiyenera “kupemphera osaleka.” (1 Atesalonika 5:17) Ndithudi, ichi sichimatanthauza kuti nthaŵi zonse tiyenera kukhala ogwada. Mmalo mwake, tiyenera kukhala ndi mkhalidwe wapemphero nthaŵi zonse. Tiyenera kuyang’ana kwa Mulungu kaamba ka chitsogozo m’njira zonse za moyo kotero kuti tikachite mwanzeru ndi kukhala ndi chivomerezo chake nthaŵi zonse.—Miyambo 15:24.
5. Kodi nchiyani chimene chingabe nthaŵi imene tiyenera kupereka ku pemphero, ndipo kodi tiyenera kuchitanji za ichi?
5 ‘M’masiku otsiriza’ ano, zinthu zambiri zingatibere nthaŵi imene tiyenera kuthera m’pemphero. (2 Timoteo 3:1) Koma ngati nkhaŵa zapanyumba, kusamalira bizinesi, ndi zina zotero zikudodometsa kupemphera mokhazikika kwa Atate wathu wakumwamba, ndiko kuti talemetsedwa koposa ndi nkhaŵa zamoyo uno. Mkhalidwe woterowo uyenera kuwongoleredwa mwamsanga, popeza kuti kulephera kupemphera kumatsogolera kukutaikiridwa chikhulupiriro. Ndiko kuti tiyenera kuchepetsa mathayo athu antchito zakuthupi kapena kulinganiza zofunika zamoyo ndi kupereka mitima yathu mowona mtima ndi mobwerezabwereza kwa Mulungu kaamba ka chitsogozo. Tiyenera “kudikira m’pemphero.”—1 Petro 4:7.
6. Kodi ndipemphero liti limene tidzapenda tsopano, ndipo ndi cholinga chotani?
6 M’pemphero lotchedwa lachitsanzo, Yesu anaphunzitsa ophunzira ake mmene angapempherere, osati kwenikweni chimene anganene. Cholembedwa cha Luka chimasiyana pang’ono ndi chija cha Mateyu chifukwa chakuti zochitika zosiyana zinaphatikizidwa. Tidzapenda pemphero limeneli monga chitsanzo cha mpangidwe wa mapemphero athu monga otsatira a Yesu ndi Mboni za Yehova.
Atate Wathu ndi Dzina Lake
7. Kodi ndani omwe ali ndi mwaŵi wa kutchula Yehova kuti “Atate wathu”?
7 “Atate wathu wakumwamba.” (Mateyu 6:9; Luka 11:2) Popeza kuti Yehova ndiye Mlengi wa anthu ndipo amakhala kumwamba, nkoyenera kumutcha “Atate wathu wakumwamba.” (1 Mafumu 8:49; Machitidwe 17:24, 28) Kugwiritsira ntchito liwu lakuti “wathu” kumavomereza kuti enanso ali ndi unansi wathithithi ndi Mulungu. Koma kodi ndani omwe ali ndi mwaŵi wopanda malire wa kumutcha iye Atate wawo? Ndianthu odzipereka ndi obatizidwa okha, m’banja lake la olambira. Kutcha Yehova “Atate wathu” kumasonyeza kuti timakhulupirira Mulungu ndi kuzindikira kuti maziko okha a kuyanjanitsidwira naye ndiwo kuvomereza kotheratu nsembe la dipo ya Yesu.—Ahebri 4:14-16; 11:6.
8. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kulakalaka kuthera nthaŵi m’pemphero kwa Yehova?
8 Ha tiyenera kudzilingalira kukhala oyandikana chotani nanga kwa Atate wathu wakumwamba! Monga ana amene samatopa konse kupita kwa atate wawo, tiyenera kulakalaka kuthera nthaŵi tikupemphera kwa Mulungu. Chiyamikiro chochokera mumtima kaamba ka madalitso ake auzimu ndi akuthupi chiyenera kutifulumiza kumthokoza kaamba ka ubwino wake. Tiyenera kukhala okhoterera ku kupereka kwa iye mavuto omwe amatithodwetsa, ndikudalira kuti iye adzatichilikiza. (Salmo 55:22) Tingatsimikizire kuti ngati tikhala okhulupirika, chirichonse pomalizira pake chidzatikomera chifukwa chakuti iye amatisamalira.—1 Petro 5:6, 7.
9. Kodi pemphero la kuyeretsedwa kwa dzina la Mulungu ndiro pempho la chiyani?
9 “Dzina lanu liyeretsedwe.” (Mateyu 6:9; Luka 11:2) Liwu lakuti “dzina” nthaŵi zina limatanthauza munthu iye mwiniyo, ndipo “kuyeretsa” kumatanthauza “kudalitsa, kupatulikitsa kapena kusunga kukhala chopatulika.” (Yerekezerani ndi Chivumbulutso 3:4.) Motero, kwenikweni, pemphero la kuyeretsa dzina la Mulungu ndilo pempho lakuti Yehova achitepo kanthu kudziyeretsa iye mwiniyo. Motani? Mwakuchotsa chitonzo chonse chimene chinawunjikidwa padzina lake. (Salmo 135:13) Chifukwa cha chimenecho, Mulungu adzachotsa kuipa, kudzikweza iye mwini, ndikupangitsa mitundu kudziŵa kuti iye ndiye Yehova. (Ezekieli 36:23; 38:23) Ngati tilakalaka kuwona tsiku limenelo ndi kuzindikiradi ukulu wa Yehova, nthaŵi zonse tidzamfikira mumkhalidwe waulemu womveketsedwa m’mawu akutiwo “dzina lanu liyeretsedwe.”
Ufumu wa Mulungu ndi Chifuniro Chake
10. Kodi nchiyani chomwe chikutanthauzidwa pamene tipemphera kuti Ufumu wa Mulungu udze?
10 “Ufumu wanu udze.” (Mateyu 6:10; Luka 11:2) Ufumu wotanthauzidwa panopa ndiwo kulamulira kwa ufumu wa Yehova, monga momwe wasonyezedwera kupyolera m’boma Laumesiya la kumwamba m’manja mwa Yesu Kristu ndi “oyera” ogwirizana naye. (Daniel 7:13, 14, 18, 27; Yesaya 9:6, 7; 11:1-5) Kodi kuupempherera kuti “udze” kumatanthauzanji? Iko kumatanthauza kuti tikupempha kuti Ufumu wa Mulungu udze kudzawononga otsutsa onse apadziko lapansi a ulamuliro waumulungu. Pambuyo pakuti Ufumuwo ‘waphwanya ndi kutha maufumu onse a padziko lapansi,’ iwo udzasanduliza dziko lapansi kukhala paradaiso wapadziko lonse.—Danieli 2:44; Luka 23:43.
11. Ngati tilakalaka kuwona chifuniro cha Yehova chikuchitidwa m’chilengedwe cha ponseponse chonse, kodi tidzachitanji?
11 “Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:10) Iri ndi pempho lakuti Mulungu achite chifuniro chake padziko lapansi, chomwe chiphatikizapo kuchotsa adani ake. (Salmo 83:9-18; 135:6-10) Kwenikweni, zitanthauza kuti timalakalaka kuwona chifuniro cha Mulungu chikuchitidwa m’chilengedwe chaponseponse chonse. Ngati chimenechi chiri mumtima mwathu, nthaŵi zonse tidzachita chifuniro cha Yehova kumlingo wothekera kwa ife. Sitikanapereka pempho loterolo mowona mtima ngati sitinayeseyese mwamphamvu kupangitsa chifuniro cha Mulungu kuchitidwa kwa ife eni. Ngati tikupemphera mwanjirayi, pamenepo, tiyenera kutsimikizira kuti sitikuchita zinthu zosiyana ndi chifunirocho, monga ngati kutomerana ndi wosakhulupilira kapena kutsatira njira zaudziko. (1 Akorinto 7:39; 1 Yohane 2:15-17) Mmalo mwake, nthaŵi zonse tiyenera kukumbukira lingaliro lakuti, ‘Kodi nchiyani chimene chiri chifuniro cha Yehova pankhaniyi?’ Inde, ngati tikonda Mulungu ndi mtima wathu wonse, tidzafunafuna chitsogozo chake m’zochita zonse zamoyo.—Mateyu 22:37.
Chakudya Chathu cha Tsiku ndi Tsiku
12. Kupempha ‘chakudya chatsiku ndi tsiku’ chokha kuli ndi chiyambukiro chabwino chotani pa ife?
12 “Mutipatse ife lero chakudya chathu chalero.” (Mateyu 6:11) Cholembedwa cha Luka chimati: “Tipatseni ife tsiku ndi tsiku chakudya chapatsiku.” (Luka 11:3) Kupempha Mulungu kuti apereke chakudya choyenerera cha “patsiku” kumakulitsa chikhulupiriro mu nzeru zake zosamalira zosoŵa zathu za tsiku ndi tsiku. Aisrayeli ankasonkhanitsa “muyeso watsiku patsiku lake,” wa mana osati wamlungu kapena kuposerapo. (Eksodo 16:4) Ili sipemphero lopempha zakudya zonona ndi za mwana alirenji koma la zosoŵa zathu za tsiku ndi tsiku pamene zibuka. Kupempha chakudya chatsiku ndi tsiku chokha kumatithandizanso kusakhala adyera.—1 Akorinto 6:9, 10.
13. (a) M’lingaliro lotakata, kodi nchiyani chomwe chikutanthauzidwa mwa kupempha chakudya cha tsiku ndi tsiku? (b) Kodi nchiyani chomwe chiyenera kukhala kaimidwe kathu kamaganizo, ngakhale ngati tigwira ntchito mwamphamvu koma sitipezabe zokwanira zochirirapo?
13 M’lingaliro lotakataka, kupempha chakudya chatsiku ndi tsiku kumasonyeza kuti sitimadzilingalira kukhala odzidalira koma nthaŵi zonse kuyang’ana kwa Mulungu kaamba ka chakudya, chakumwa, zovala, ndi zofunika zina. Monga ziŵalo zodzipereka za banja lake la olambira, timadalira Atate wathu koma sitimakhala manja lende mwa kumuyembekezera kutigaŵira mozizwitsa. Timagwira ntchito ndi kugwiritsira ntchito njira iriyonse imene tiri nayo kupezera zakudya ndi zofunika zina. Komabe, moyenelera timathokoza Mulungu m’pemphero chifukwa chakuti timawona m’makonzedwe amenewa chikondi, nzeru, ndi mphamvu za Atate wathu wakumwamba. (Machitidwe 14:15-17; yerekezerani ndi Luka 22:19.) Khama lathu lingatichitse kulemerera. Koma ngakhale ngati tigwira ntchito mwamphamvu ndipo sitipezabe zokwanira, tikhaletu oyamikira ndi okhutira. (Afilipi 4:12; 1 Timoteo 6:6-8) Kwenikweni, munthu wa Mulungu wokhala ndi zakudya wamba ndi zovala wamba angakhale wachimwemwe kwenikweni kuposa ena amene ali olemera kuthupi. Motero ngakhale pamene tiri ndi zochepa chifukwa cha mikhalidwe imene tiri osakhoza kulamulira, tisalefuke. Ife tingakhalebe olemera mwauzimu. Ndithudi, sitiyenera kukhala anjala m’chikhulupiriro, m’chiyembekezo, ndi m’chikondi cha pa Yehova, kwa amene chitamando chathu ndi chithokozo zimapitako m’pemphero lochokera mumtima.
Kukhululukira Mangaŵa Athu
14. Kodi ndi mangaŵa ati amene timapempherera chikhululukiro, ndipo kodi Mulungu amachitanji nawo?
14 “Ndipo mutikhululukire mangaŵa athu, monga ifenso takhululukira amangaŵa athu.” (Mateyu 6:12) Cholembedwa cha Luka chimasonyeza kuti mangaŵa amenewo ndiwo machimo. (Luka 11:4) Uchimo wobadwa nawo umatilepheretsa kuchita zinthu zonse mogwirizana ndi chifuniro changwiro cha Atate wathu. Motero, m’lingaliro lina, ndiko kuti, zophophonya zimenezi zakhala mangaŵa athu, kapena mathayo kwa Mulungu, kuyambira pamene ‘tinayamba kukhala ndi moyo ndi kuyenda mwa mzimu.’ (Agalatiya 5:16-25; yerekezerani ndi Aroma 7:21-25.) Tiri ndi mangaŵa ameneŵa chifukwa chakuti ndife opanda ungwiro ndipo pakali pano sitingayenelere mokwanira miyezo ya Mulungu. Ndiko kukhululukidwa kwa machimowa kumene tiri ndi mwaŵi wa kupempherera. Mwachimwemwe, Mulungu angagwiritsire ntchito mphamvu ya nsembe ya dipo la Yesu kumangaŵa ameneŵa, kapena machimo.—Aroma 5:8; 6:23.
15. Kodi ndilingaliro lotani limene tiyenera kukhala nalo kulinga kuchilango chofunika?
15 Ngati tiyembekezera Mulungu kutikhululukira mangaŵa athu, kapena machimo, tiyenera kulapa ndi kukhala ofunitsitsa kulandira chilango. (Miyambo 28:13; Machitidwe 3:19) Chifukwa chakuti Yehova amatikonda, iye amatipatsa chilango chimene aliyense wa ife timafunikira kotero kuti tiwongolere zofooka zathu. (Miyambo 6:23; Ahebri 12:4-6) Ndithudi, tingakhale achimwemwe, ngati kukula msinkhu m’chikhulupiriro ndi chidziŵitso zipeza mtima wathu uli wogwirizana kotheratu ndi malamulo a Mulungu ndi miyezo kotero kuti sitimachimwa konse pamlingo wadala. Koma bwanji ngati tiwona kuchita dala kulikonse m’kuchita kwathu cholakwa? Pamenepo tiyenera kumva chisoni kwambiri ndipo tiyenera kupemphera mwamphamvu kaamba ka chikhululukiro. (Ahebri 10:26-31) Mwa kugwiritsira ntchito uphungu umene talandira, tiyenera kuwongolera njira yathu mofulumira.
16. Kodi nchifukwa ninji kuli kopindulitsa kupitirizabe kupempha Mulungu kutikhululukira machimo athu?
16 Kupempha Mulungu nthaŵi zonse kukhululukira machimo athu nkopindulitsa. Kuchita zimenezi kumapangitsa kuwona mosalekeza kulakwa kwathu ndipo kumatichititsa kukhala odzichepetsa. (Salmo 51:3, 4, 7) Tifunikira Atate wathu wakumwamba “kutikhululukira machimo athu, ndi kutisambitsa . . . chosalungama chirichonse.” (1 Yohane 1:8, 9) Ndiponso, kutchula mangaŵa athu m’pemphero kumatithandiza kupitirizabe kusaleka kuchita nkhondo yolimbana nawo. Motero timakumbutsidwanso mosalekeza za kufunikira kwathu dipo ndi mphamvu ya mwazi wokhetsedwa wa Yesu.—1 Yohane 2:1, 2; Chivumbulutso 7:9, 14.
17. Kodi kupempherera chikhululukiro kumatithandiza motani muunansi wathu ndi ena?
17 Kupempherera chikhululukiro kumatithandizanso kukhala achifundo, okoma mtima, ndi owolowa manja kwa awo amene angakhale amangaŵa athu m’zinthu zazikulu ndi zazing’ono. Cholembedwa cha Luka chikuti: “Mutikhululukire ife machimo athu; pakuti ifenso tikhululukira munthu yense wamangaŵa athu.” (Luka 11:4) Kwenikweni, tingafikire pakukhululukidwa ndi Mulungu pokhapokha ngati ife ‘taŵakhululukira kale amangaŵa athu,’ anthu otichimwira. (Mateyu 6:12; Marko 11:25) Yesu anawonjezera kuti: “Pakuti ngati mukhululukira anthu zolakwa zawo adzakhululukira inunso Atate wanu wakumwamba. Koma ngati simukhululukira anthu zolakwa zawo, Atate wanunso sadzakhululukira zolakwa zanu.” (Mateyu 6:14, 15) Kupempherera kukhululukidwa machimo athu kuyenera kutisonkhezera kupirira ndi ena ndi kuwakhululukira. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Monga Yehova anakukhululukirani, teroni inunso.”—Akolose 3:13; Aefeso 4:32.
Chiyeso ndi Woipayo
18. Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kuimba Mulungu mlandu kaamba ka mayeso ndi ziyeso zathu?
18 “Ndipo musatitengere ife kokatiyesa.” (Mateyu 6:13; Luka 11:4) Mawu ameneŵa samatanthuza kuti Yehova amatiyesa kuchita tchimo. Nthaŵi zina Malemba amanena za Yehova kukhala akuchita kapena kupangitsa zinthu kuchitika zimene iye wangozilola. (Rute 1:20, 21; yerekezerani ndi Mlaliki 11:5.) Koma “Mulungu sakhoza kuyesedwa ndi zoipa, ndipo iyemwini sayesa munthu,” analemba motero wophunzira Yakobo. (Yakobo 1:13) Chotero, tisaike liwongo pa Atate wathu wakumwamba kaamba ka mayeso ndi ziyeso za zinthu zoipa, pakuti Satana ndiye Woyesa amene amayesayesa kutichititsa kuchimwira Mulungu.—Mateyu 4:3; 1 Atesalonika 3:5.
19. Kodi ndimotani mmene tingapempherere ponena za chiyeso?
19 Mwa kupempha kuti, “Musatitengere ife kokatiyesa,” kwenikweni ife tikupempha Yehova kusatilola kugonja pamene tayesedwa kapena kutsenderezedwa kusamumvera iye. Tingapembedzere Atate wathu kutsogoza mapazi athu kotero kuti palibe chiyeso chomwe chidzatigwera chimene chidzakhala chonkitsa kwa ife. Pankhaniyi, Paulo analemba kuti: “Sichinakugwereni inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.” (1 Akorinto 10:13) Tingapemphere kuti Yehova atitsogolere kotero kuti sitikuyesedwa koposa kumene tikhoza kupirira ndi kuti atipatse njira yopulumukira pamene tatsenderezedwa kotheratu. Ziyeso zimachokera kwa Mdyerekezi, thupi lathu lochimwa, ndi zofooka za ena, koma Atate wathu wachikondi angatitsogolere kotero kuti sitikulakidwa.
20. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kupempherera kupulumutsidwa kwa “woipayo”?
20 “Koma mutipulumutse kwa woipayo.” (Mateyu 6:13) Motsimikizirika Mulungu angaletse Satana, “woipayo,” kuti asatilake. (2 Petro 2:9) Ndipo palibe nthaŵi ina pamene kupulumutsidwa kwa Mdyerekezi kunakhala kwakukulu kwambiri kuposa tsopano, popeza ‘iye ali ndi mkwiyo waukulu, podziŵa kuti kamtsalira kanthaŵi.’ (Chivumbulutso 12:12) Sitiri osadziŵa ponena za machenjera a Satana, komanso iye saali wosadziŵa ponena za zofooka zathu. Chotero, tifunikira kupemphera kuti Yehova atipulumutse kuti tisagwidwe ndi Mdaniyu wofanana ndi mkango. (2 Akorinto 2:11; 1 Petro 5:8, 9; yerekezerani ndi Salmo 141:8, 9.) Mwachitsanzo, ngati tiri ndi chikhumbo cha kukwatira, tingafunikire kupempha Yehova kutipulumutsa kumachenjera a Satana ndi ku ziyeso za kukulitsa unansi waudziko umene ungatsogolere kuchisembwere kapena ku kusamvera Mulungu mwa kukwatirana ndi wosakhulupirira. (Deuteronomo 7:3, 4; 1 Akorinto 7:39) Kodi timalakalaka chuma? Pamenepo pemphero lingafunike kutithandiza kukaniza ziyeso za kutchova juga kapena kuba ndalama mwa kuchita chinyengo. Pokhala wolakalaka kuwononga unansi wathu ndi Yehova, Satana adzagwiritsira ntchito chida chirichonse chopezeka m’nkhokwe yake ya zida za ziyeso. Motero tipempheretu mosalekeza kwa Atate wathu wakumwamba, yemwe samasiya olungama kuchiyeso ndi yemwe amapereka chilanditso kwa woipayo.
Pemphero Limalimbikitsa Chikhulupiriro ndi Chiyembekezo
21. Kodi ndimotani mmene tapindulira mwa kupempherera Ufumu?
21 Atate wathu wakumwamba, yemwe amatipulumutsa kwa woipayo, amasangalala m’kutidalitsa molemerera. Komabe, kodi nchifukwa ninji iye kwa nthaŵi yaitali motere walola anthu ake okondedwa kupempherera kuti, “Ufumu wanu udze”? Eya, kwazaka zambiri zapitazo kupemphera mwanjirayi kwawonjezera chikhumbo chathu ndi kuyamikira Ufumuwo. Pemphero loterolo limatikumbutsa za kufunika kwambiri kwa boma lakumwamba labwino koposalo. Limatisungitsanso mosalekeza chiyembekezo cha moyo pansi pa kulamulira kwa Ufumuwo chiri pamaso pathu.—Chivumbulutso 21:1-5.
22. Kodi nchiyani chimene chiyenera kukhala lingaliro lathu la maganizo losalekeza kulinga kupemphero kwa Atate wathu wa kumwamba, Yehova?
22 Mosakaikira pemphero limalimbikitsa chikhulupiriro mwa Yehova. Chomangira chathu ndi iye chimalimbikitsidwa pamene ayankha mapemphero athu. Motero, tisaleme kutembenukira kwa iye tsiku ndi tsiku ndi chitamando, chiyamiko, ndi pembedzero. Ndipo tiyeni tikhaletu oyamikira kuyankho lothandiza la Yesu kupempho la otsatira ake: “Ambuye, tiphunzitseni kupemphera.”
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi ndiphunziro lotani limene tingaphunzire kumawu ndi chitsanzo za Yesu monga munthu wodziŵa kupereka pemphero?
◻ Kodi tiyenera kupempherera chiyani ponena za Atate wathu wakumwamba ndi dzina lake?
◻ Kodi timapemphanji pamene tipempherera Ufumu wa Mulungu kudza ndi chifuniro chake kuchitika?
◻ Kodi timapemphanji pamene tipempherera chakudya chathu cha tsiku ndi tsiku?
◻ Kodi nchiyani chomwe chimatanthauzidwa pamene tipempherera kukhululukidwa kwa mangaŵa athu?
◻ Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika koposa kupemphera ponena za chiyeso ndi kupulumutsidwa kwa Satana, woipayo?
[Chithunzi patsamba 16]
Otsatira a Yesu anampempha kuwaphunzitsa mmene angapempherere. Kodi mukudziŵa mmene tingapindulire m’malangizo ake onena za pemphero?