Mzimu Woyera Umatipatsa Mphamvu Yolimbana ndi Mayesero Ndiponso Zofooketsa
“Mzimu woyera ukadzafika pa inu, mudzalandira mphamvu.”—MAC. 1:8.
1, 2. Kodi Yesu analonjeza ophunzira ake za thandizo liti, ndipo n’chifukwa chiyani thandizoli lili lofunika kwambiri?
YESU ankadziwa kuti ophunzira ake sangathe mwa mphamvu yawo yokha kutsatira zinthu zonse zimene anawalamulira. Zinali zoonekeratu kuti ankafunikira mphamvu yoposa yachibadwa chifukwa ntchito yolalikira inali yaikulu, adani awo anali amphamvu komanso anali ndi zofooka monga anthu opanda ungwiro. Choncho, Yesu asanapite kumwamba, anatsimikizira ophunzira ake kuti: “Mzimu woyera ukadzafika pa inu, mudzalandira mphamvu. Pamenepo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka kumalekezero a dziko lapansi.”—Mac. 1:8.
2 Lonjezo limeneli linayamba kukwaniritsidwa pa Pentekosite mu 33 C.E., pamene mzimu woyera unapatsa mphamvu otsatira a Yesu Khristu kuti alalikire mu Yerusalemu monse. Palibe chilichonse chimene chikanaletsa ntchitoyi. (Mac. 4:20) Otsatira a Yesu okhulupirika, kuphatikizapo ifeyo, akufunikira kwambiri mphamvu yochokera kwa Mulungu “masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.”—Mat. 28:20.
3. (a) Fotokozani kusiyana kwa mzimu woyera ndi mphamvu. (b) Kodi mphamvu imene Yehova amapereka kudzera mwa mzimu woyera imatithandiza kuchita chiyani?
3 Yesu analonjeza ophunzira ake kuti ‘mzimu woyera ukadzafika pa iwo adzalandira mphamvu.’ Kodi pa lonjezoli pali kusiyana kotani pakati pa “mzimu woyera” ndi “mphamvu”? Mzimu wa Mulungu ndiwo mphamvu yake yogwira ntchito imene iye amagwiritsa ntchito pa anthu kapena zinthu kuti chifuniro chake chichitike. Koma imasiyana ndi mphamvu wamba imene ingakhale mwa chinthu kapena munthu. Mphamvu imene ingakhale mwa munthu sigwira ntchito mpaka nthawi imene munthuyo akufuna kuchita chinachake. Choncho tingayerekezere mzimu woyera ndi mphamvu ya magetsi imene ikulowa m’batire politchaja. Koma mphamvu imene ili mwa munthu ili ngati mphamvu imene yasungidwa m’batire. Mphamvu imene Yehova amapereka kwa anthu kudzera mwa mzimu woyera imatithandiza kukwaniritsa udindo wathu monga Akhristu odzipereka komanso kulimbana ndi mavuto ndi mayesero.—Werengani Mika 3:8; Akolose 1:29.
4. Kodi tikambirana chiyani m’nkhani ino, ndipo chifukwa chiyani?
4 Kodi mphamvu imene timalandira kudzera mwa mzimu woyera imatithandiza bwanji? Kodi ndi zinthu ziti zimene tingachite mothandizidwa ndi mzimu woyera? Tikamayesetsa kutumikira Mulungu mokhulupirika timakumana ndi mavuto kuchokera kwa Satana, dziko lakeli, kapena chifukwa cha kupanda kwathu ungwiro. Akhristufe timafunika kulimbana ndi mavuto amenewa n’cholinga choti tisafooke koma tizilalikira mwakhama ndiponso kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Tiyeni tsopano tikambirane mmene mzimu woyera umatithandizira kulimbana ndi mayesero, kutopa ndiponso kufooka.
Mphamvu Yolimbana ndi Mayesero
5. Kodi pemphero lingatithandize bwanji kupeza mphamvu?
5 Yesu anaphunzitsa otsatira ake kupemphera kuti: “Musatilowetse m’mayesero, koma mutilanditse kwa woipayo.” (Mat. 6:13) Yehova sadzasiya atumiki ake okhulupirika amene amapempha zimenezi. Pa nthawi ina, Yesu ananena kuti: “Atate wakumwamba . . . adzapereka mowolowa manja mzimu woyera kwa amene akum’pempha.” (Luka 11:13) Lonjezo lakuti Yehova adzatipatsa mphamvu yotithandiza kuchita zabwino ndi lolimbikitsa kwambiri. Koma izi sizikutanthauza kuti Yehova adzatiteteza kuti tisamakumane ndi mayesero. (1 Akor. 10:13) Choncho tiyenera kupemphera mwakhama kwambiri makamaka pa nthawi imene tikukumana ndi mayesero.—Mat. 26:42.
6. Kodi Yesu anayankha Satana pogwiritsa ntchito chiyani?
6 Pa nthawi imene ankayesedwa, Yesu anayankha Mdyerekezi pogwiritsa ntchito malemba. Yesu ankadziwa bwino Mawu a Mulungu ndipo n’chifukwa chake anayankha kuti: “Malemba amati . . . Malemba amatinso . . . Choka Satana! Pakuti Malemba amati, ‘Yehova Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira, ndipo uyenera kutumikira iye yekha basi.’” Kukonda Yehova ndiponso Mawu ake kunathandiza Yesu kuti asakopedwe ndi Woyesayo. (Mat. 4:1-10) Yesu atapambana mayesero onse, Satana anamusiya.
7. Kodi Baibulo lingatithandize bwanji kukana mayesero?
7 Ngati Yesu ankadalira Malemba pokana zimene Mdyerekezi anamuuza, kuli bwanji ifeyo? Kuti tithe kukana Mdyerekezi ndi mayesero ake, choyamba tiyenera kukhala ndi mtima wofuna kudziwa bwino mfundo za Mulungu n’kumayesetsa kwambiri kuzitsatira. Kuphunzira Malemba kwathandiza anthu ambiri kumvetsa bwino nzeru ndi chilungamo cha Mulungu ndipo zimenezi zawalimbikitsa kutsatira mfundo za m’Baibulo. “Mawu a Mulungu” ndi amphamvu ndipo amatha kuzindikira “zimene munthu akuganiza komanso zolinga za mtima wake.” (Aheb. 4:12) Munthu akamachita khama kuwerenga ndi kusinkhasinkha Malemba, amamvetsa bwino kuti ‘m’njira zonse za Yehova muli choonadi.’ (Sal. 25:10) Choncho ndi bwino kusinkhasinkha malemba amene angatithandize pa zofooka zathu.
8. Kodi tingatani kuti tilandire mzimu woyera?
8 Yesu anatha kukana mayesero osati chifukwa chongodziwa Malemba basi, komanso chifukwa chakuti ‘anadzazidwa ndi mzimu woyera.’ (Luka 4:1) Kuti nafenso tikhale ndi mphamvu komanso luso limene Yesu anali nalo, tiyenera kuyandikira Yehova mwa kugwiritsa ntchito zinthu zonse zimene wapereka zotithandiza kuti tipeze mzimu woyera. (Yak. 4:7, 8) Zina mwa zinthu zimenezi ndi kuphunzira Baibulo, kupemphera, kusonkhana ndiponso kucheza ndi okhulupirira anzathu. Anthu ambiri aona kuti kukhala ndi ndandanda yabwino yochitira zimenezi kumawathandiza kuika maganizo awo pa zinthu zauzimu zomwe ndi zolimbikitsa.
9, 10. (a) Kodi m’dera lanu mumakumana ndi mayesero ati? (b) Pamene mwatopa, kodi kupemphera ndiponso kuganiza mofatsa kungakuthandizeni bwanji kuti musagonje pa mayesero?
9 Kodi inuyo mukulimbana ndi mayesero ati? Kodi munayesedwapo kuti muyambe kukopana ndi munthu wina yemwe si mwamuna kapena mkazi wanu? Ngati simuli pa banja kodi munayesedwapo kuti muyambe chibwenzi ndi munthu wosakhulupirira? Nthawi zina Akhristu akamaonera TV kapena akamagwiritsa ntchito Intaneti, mwadzidzidzi angayesedwe kuti aone zinthu zoipa. Ngati izi zinakuchitikiranipo, kodi munachita chiyani? Ndi bwino kusinkhasinkha kapena kuganizira mofatsa mfundo yakuti kugonja pa chinthu chimodzi kungachititse kuti munthu adzagonjenso pa zinthu zina mpaka kufika pochita tchimo lalikulu. (Yak. 1:14, 15) Ndi bwinonso kuganizira mmene izi zingakhumudwitsire Yehova, mpingo ndiponso banja lanu. Koma munthu akamatsatira mfundo za Mulungu mokhulupirika amakhala ndi chikumbumtima chabwino. (Werengani Salimo 119:37; Miyambo 22:3.) Mukamakumana ndi mayesero ngati amenewa, muzipemphera kuti mupeze mphamvu zokanira.
10 Pali mfundo inanso yokhudza kuyesedwa kwa Yesu imene tiyenera kuikumbukira. Pa nthawi imene Satana ankamuyesa, Yesu anali atakhala m’chipululu kwa masiku 40 osadya kalikonse. N’zosakayikitsa kuti Mdyerekezi anaona kuti iyi inali ‘nthawi yabwino’ kuyesa Yesu. (Luka 4:13) Satana amayesetsanso kupeza nthawi yabwino yoti atiyese. Choncho, m’pofunika kuyesetsa kuti tikhalebe olimba mwauzimu. Satana amayesa anthu pa nthawi imene akuona kuti anthuwo afooka kwambiri. Ndiyetu ngati tatopa kapena kufooka m’pamene tiyenera kuchonderera Yehova kuti atiteteze ndiponso kutipatsa mzimu woyera.—2 Akor. 12:8-10.
Mphamvu Yotithandiza Tikatopa Kapena Tikafooka
11, 12. (a) N’chifukwa chiyani anthu ambiri amafooka masiku ano? (b) Kodi tingapeze bwanji mphamvu zotithandiza kuti tisafooke?
11 Anthu opanda ungwirofe timafooka nthawi ndi nthawi. Izi zikuchitikachitika masiku ano chifukwa chakuti tikukhala m’masiku ovuta. Mwina tinganene kuti ino ndi nthawi yovuta kwambiri kuposa kale lonse. (2 Tim. 3:1-5) Pamene Armagedo ikuyandikira, mavuto a zachuma, kuvutika maganizo ndiponso mavuto ena akuwonjezereka. Choncho n’zosadabwitsa kuti anthu ena amavutika kukwaniritsa udindo wawo wosamalira banja. Anthu amatopa, kufooka, kupanikizika mpaka ena kufika pothedwa nzeru. Ngati umu ndi mmene zilili ndi inuyo kodi mungatani?
12 Kumbukirani kuti Yesu anatsimikizira ophunzira ake kuti adzawapatsa mthandizi, womwe ndi mzimu woyera wa Mulungu. (Werengani Yohane 14:16, 17.) Mzimu umenewu ndi wamphamvu kwambiri kuposa mphamvu ina iliyonse m’chilengedwechi. Yehova angagwiritse ntchito mzimuwu “kuchita zazikulu kwambiri” potipatsa mphamvu zotithandiza kupirira vuto lililonse limene tingakumane nalo. (Aef. 3:20) Mtumwi Paulo ananena kuti tikamadalira mzimuwu timapeza “mphamvu yoposa yachibadwa,” ngakhale kuti “timapanikizidwa mwamtundu uliwonse.” (2 Akor. 4:7, 8) Yehova sakulonjeza kutichotsera mavuto onse koma akutitsimikizira kuti kudzera mwa mzimu wake, iye azitipatsa mphamvu yotithandiza kulimbana nawo.—Afil. 4:13.
13. (a) Kodi mtsikana wina wapatsidwa mphamvu m’njira ziti kuti apirire vuto lake? (b) Perekani chitsanzo cha munthu amene mukum’dziwa yemwe wapatsidwanso mphamvu pa mavuto ake.
13 Taganizirani za mpainiya wokhazikika wina wa zaka 19, dzina lake Stephanie. Pamene anali ndi zaka 12 anadwala matenda opha ziwalo ndipo kuchipatala anamuuzanso kuti ali ndi chotupa mu ubongo. Kuchokera nthawi imeneyi, wachitidwa maopaleshoni awiri komanso wapatsidwa chithandizo china champhamvu kuchipatala. Koma kenako anadwalanso kawiri ndipo zimenezi zinachititsa kuti asamagwiritse ntchito bwinobwino ziwalozake zakumanzere ndiposo kuti asamaone bwinobwino. Stephanie amayesetsa kuti asatope n’cholinga choti athe kuchita zinthu zofunika kwambiri monga kupita ku misonkhano ndi kulowa mu utumiki wakumunda. Iye amaona kuti Yehova amamuthandiza m’njira zosiyanasiyana kuti apirire. Nkhani zimene amawerenga m’mabuku ofotokoza Baibulo, zokhudza zimene Akhristu anzake akumana nazo, zimamulimbikitsa kwambiri akafooka. Abale ndi alongo amamuthandizanso mwa kumulembera makalata kapena kumulimbikitsa misonkhano isanayambe ndiponso ikatha. Anthu achidwi amasonyezanso kuyamikira zimene Stephanie amawaphunzitsa mwa kupita kunyumba kwa Stephanie kuti iye akawaphunzitse Baibulo. Stephanie amathokoza kwambiri Yehova chifukwa cha zonsezi. Iye amakonda kwambiri lemba la Masalimo 41:3 ndipo amaona kuti lembali lakwaniritsidwa pa iye.
14. Kodi tiyenera kupewa chiyani tikafooka ndipo chifukwa chiyani?
14 Tikatopa kapena kupanikizika, si bwino kuganiza zosiya kuchita zinthu zina zauzimu poganiza kuti tipeza mpumulo. Kuchita zimenezi kungakhale kulakwitsa kwambiri. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chakuti zinthu monga kuphunzira Baibulo patokha kapena ndi banja, kulalikira ndiponso kupezeka pa misonkhano zimathandiza kuti mzimu woyera utipatse mphamvu. Nthawi zonse zinthu zauzimu zimatitsitsimula. (Werengani Mateyu 11:28, 29.) Kawirikawiri, abale ndi alongo amene amafika ku misonkhano ali otopa amabwerera kwawo atalimbikitsidwa kwambiri ndipo amakhala ngati batire limene latchajidwa.
15. (a) Kodi Yehova analonjeza kuti moyo wachikhristu udzakhala wosavuta? Fotokozani mogwirizana ndi Malemba. (b) Kodi Mulungu watilonjeza chiyani ndipo tingadzifunse funso liti?
15 Koma sikuti kukhala Mkhristu n’kosavuta. Kuti munthu akhale Mkhristu wokhulupirika pamafunika khama. (Mat. 16:24-26; Luka 13:24) Pogwiritsa ntchito mzimu woyera, Yehova angapereke mphamvu kwa munthu wotopa. Mneneri Yesaya analemba kuti: “Anthu odalira Yehova adzapezanso mphamvu. Iwo adzaulukira m’mwamba ngati ali ndi mapiko a chiwombankhanga. Adzathamanga koma osafooka. Adzayenda koma osatopa.” (Yes. 40:29-31) Ngati Mulungu amatipatsa mphamvu, ndi bwino kudzifunsa kuti, N’chifukwa chiyani anthufe timatopa mwauzimu?
16. Kodi tingapewe bwanji zinthu zimene zingatitopetse kapena kutifooketsa?
16 Mawu a Yehova amatilimbikitsa ‘kutsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.’ (Afil. 1:10) Poyerekezera moyo wachikhristu ndi mpikisano wothamanga mtunda wautali, Paulo anauziridwa kulemba kuti: “Tiyeninso tivule cholemera chilichonse . . . Ndipo tithamange mopirira mpikisano umene atiikirawu.” (Aheb. 12:1) Apa ankatanthauza kuti tiyenera kupewa zinthu zosafunika zimene zingatilemetse n’kutitopetsa. N’kutheka kuti ena mwa ife tikudzikakamiza kuchita zinthu zina pamene ndife otanganidwa kale. Ngati nthawi zambiri mumaona kuti mwatopa ndipo ndinu opanikizika ndi bwino kuonanso nthawi imene mumathera pa ntchito yanu, pa maulendo okasangalala ndiponso pa masewera kapena zinthu zina zimene mumachita pa nthawi yopuma. Tiyenera kuchita zinthu mwanzeru ndiponso modzichepetsa, kuzindikira zimene sitingakwanitse komanso kupewa zinthu zosafunika.
17. N’chifukwa chiyani ena afooka, nanga kodi Yehova akutitsimikizira chiyani pa nkhani imeneyi?
17 Mwina enafe tafookanso chifukwa chakuti mapeto a dongosolo lino sanafike pa nthawi imene tinkayembekezera. (Miy. 13:12) Aliyense amene ali ndi maganizo amenewa akhoza kulimbikitsidwa ndi mawu a pa Habakuku 2:3 akuti: “Masomphenyawa akuyembekezera nthawi yake yoikidwiratu ndipo akuthamangira kumapeto kwake. Zimene zili m’masomphenyazi si zonama. Ngakhale masomphenyawa atazengereza, uziwayembekezerabe chifukwa adzakwaniritsidwa ndithu. Iwo sadzachedwa.” Pamenepa, Yehova akutitsimikizira kuti mapeto a dongosolo lino afika pa nthawi yake.
18. (a) Kodi ndi malonjezo ati amene amakulimbikitsani? (b) Kodi nkhani yotsatira idzatithandiza bwanji?
18 Mtumiki aliyense wokhulupirika wa Yehova amalakalaka nthawi pamene kutopa ndi kufooka zidzatha n’kumasangalala ndi mphamvu imene anali nayo “masiku ake aunyamata.” (Yobu 33:25) Koma ngakhale masiku ano, munthu wathu wamkati angakhale wamphamvu chifukwa chothandizidwa ndi mzimu woyera tikamachita zinthu zauzimu zomwe ndi zolimbikitsa. (2 Akor. 4:16; Aef. 3:16) Musalole kuti kutopa kukulepheretseni kupeza madalitso osatha. Vuto lililonse limene tingakumane nalo, kaya likhale mayesero, kutopa kapena kufooka, lidzatha posachedwapa apo ayi m’dziko latsopano limene Mulungu walonjeza. M’nkhani yotsatira tidzakambirana mmene mzimu woyera umaperekera mphamvu kwa Akhristu kuti athe kupirira pozunzidwa, kupewa kumangotsatira zofuna za anzawo ndiponso kupirira mavuto ena.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi kuwerenga Baibulo kumatipatsa bwanji mphamvu?
• Kodi kupemphera ndi kusinkhasinkha kumatipatsa bwanji mphamvu?
• Kodi mungapewe bwanji zinthu zimene zingakufooketseni?
[Chithunzi patsamba 24]
Misonkhano yachikhristu imatipatsa mphamvu mwauzimu