Yehova Amatipatsa Zimene Timafunikira Tsiku Lililonse
“Musakayike mtima. Pakuti . . . Atate wanu adziŵa kuti musoŵa zimenezi.”—LUKA 12:29, 30.
1. Kodi Yehova amasamalira bwanji nyama?
KODI munaonapo mpheta kapena mbalame ina ikujomphajompha pa zinthu zooneka ngati dothi chabe? Mwina munadzifunsapo kuti ipeza chakudya chotani mwa kujomphajompha padothipo. Pa Ulaliki wa pa Phiri, Yesu anasonyeza kuti tingaphunzirepo kanthu poona mmene Yehova amadyetsera mbalame. Iye anati: “Yang’anirani mbalame za kumwamba, kuti sizimafesa ayi, kapena sizimatema ayi, kapena sizimatutira m’nkhokwe; ndipo Atate wanu wa Kumwamba azidyetsa. Nanga inu mulibe kusiyana nazo kuziposa kodi?” (Mateyu 6:26) Yehova amapereka chakudya kwa zolengedwa zake zonse m’njira zodabwitsa kwambiri.—Salmo 104:14, 21; 147:9.
2, 3. Kodi tingaphunzire zinthu ziti zauzimu pa mfundo yopempherera chakudya cha tsiku lililonse imene Yesu anatiphunzitsa?
2 Nanga, n’chifukwa chiyani Yesu m’pemphero lachitsanzo anaphatikizamo pempho lakuti: “Mutipatse ife lero chakudya chathu chalero”? (Mateyu 6:11) Tikhoza kuphunzira zambiri pa pempho lochepa limeneli. Poyamba, likutikumbutsa kuti Yehova ndiye Wopatsa Wamkulu. (Salmo 145:15, 16) Anthu angadzale ndi kulima, koma Mulungu yekha ndiye angakulitse zinthu, ngakhalenso kukulitsa zinthu mwauzimu. (1 Akorinto 3:7) Zimene timadya ndi kumwa ndi mphatso zochokera kwa Mulungu. (Machitidwe 14:17) Kupempha Mulungu kuti atipatse zimene tikufuna tsiku lililonse kumamusonyeza kuti sitipeputsa zinthu zimene amatipatsa. Komabe, mapemphero amenewo satichititsa kuti tisamagwire ntchito ngati tingathe kutero.—Aefeso 4:28; 2 Atesalonika 3:10.
3 Chachiŵiri, kupempherera kwathu “chakudya chathu cha lero” kumasonyeza kuti sitiyenera kudera nkhaŵa mopambanitsa za m’tsogolo. Yesu anapitiriza kunena kuti: “Musadere nkhaŵa, ndi kuti, Tidzadya chiyani? kapena, Tidzamwa chiyani? kapena, Tidzavala chiyani? Pakuti anthu akunja azifunitsa zonse zimenezo; pakuti Atate wanu wa Kumwamba adziŵa kuti musoŵa zonse zimenezo. Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu. Chifukwa chake musadere nkhaŵa za maŵa; pakuti maŵa adzadzidera nkhaŵa iwo okha.” (Mateyu 6:31-34) Kupempherera “chakudya chathu cha lero” kukutipatsa chitsanzo chokhala ndi moyo wosalira zambiri “wodzipereka kwa Mulungu.”—1 Timoteo 6:6-8, NW.
Chakudya Chauzimu cha Tsiku Lililonse
4. Kodi ndi zochitika ziti pa moyo wa Yesu ndi wa Aisrayeli zimene zikutsindika kufunika kwa kudya mwauzimu?
4 Kupempherera kwathu chakudya cha tsiku lililonse kuyenera kutikumbutsanso kuti timafunikira chakudya chauzimu tsiku lililonse. Ngakhale kuti Yesu anali ndi njala atasala chakudya kwa nthaŵi yaitali, iye anakana chiyeso cha Satana choti asandutse miyala kukhala chakudya, ponena kuti: “Kwalembedwa, Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse akutuluka mkamwa mwa Mulungu.” (Mateyu 4:4) Pano Yesu anagwira mawu a mneneri Mose, amene anauza Aisrayeli kuti: “[Yehova] anakuchepetsani, nakumvetsani njala, nakudyetsani ndi mana, amene simunawadziŵa, angakhale makolo anu sanawadziŵa; kuti akudziŵitseni kuti munthu sakhala wamoyo ndi mkate wokha, koma munthu akhala wamoyo ndi zonse zakutuluka mkamwa mwa Yehova.” (Deuteronomo 8:3) Mmene Yehova ankawapatsira mana Aisrayeli sikunali kungowapatsa chakudya chenicheni chokha komanso maphunziro auzimu. Phunziro limodzi lauzimu ndi lakuti, ankafunika “kuwola muyeso wa tsiku pa tsiku lake.” Akatola zoposa zimene akanadya tsiku limenelo, zotsalazo zinkayamba kununkha ndi kugwa mphutsi. (Eksodo 16:4, 20) Koma zimenezi sizinkachitika tsiku lachisanu ndi chimodzi pamene amafunika kutola chakudya cha masiku aŵiri kuti adzadye tsiku la Sabata. (Eksodo 16:5, 23, 24) Motero mana ankawakumbutsa nthaŵi zonse kuti ankafunika kukhala omvera ndiponso kuti miyoyo yawo inkadalira osati pa chakudya chokha koma pa “zonse zakutuluka mkamwa mwa Yehova.”
5. Kodi Yehova amatipatsa bwanji chakudya chauzimu cha tsiku lililonse?
5 Ifenso tifunika kudya chakudya chauzimu tsiku lililonse chimene Yehova amatipatsa kudzera mwa Mwana wake. N’chifukwa chake Yesu anasankha “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kuti apereke pa banja lachikhulupiriro “zakudya pa nthaŵi yake.” (Mateyu 24:45) Gulu la kapolo wokhulupirika limeneli sikuti limangopereka chakudya chochuluka kudzera mu zinthu zothandiza kuphunzira Baibulo komanso limatilimbikitsa kuti tiziŵerenga Baibulo tsiku lililonse. (Yoswa 1:8; Salmo 1:1-3) Mofanana ndi Yesu, ifenso tikhoza kupindula mwauzimu ngati tichita khama kuphunzira ndiponso kuchita zimene Yehova amafuna tsiku lililonse.—Yohane 4:34.
Kukhululukira Machimo
6. Kodi ndi mangawa ati amene tiyenera kupempherera kuti atikhululukire, ndipo kodi Yehova angafafanize machimo athu titachita zinthu ziti?
6 Pempho lotsatira mu pemphero lachitsanzo ndi lakuti: “Mutikhululukire mangawa athu, monga ifenso takhululukira amangawa athu.” (Mateyu 6:12) Pano Yesu sankalankhula za mangawa a ndalama. Iye anali kunena za kukhululukidwa kwa machimo athu. M’pemphero lachitsanzo limene Luka analemba, pempho limeneli limati: “Mutikhululukire ife machimo athu; pakuti ifenso tikhululukira munthu yense wa mangawa athu.” (Luka 11:4) Motero, tikachimwa, zimakhala ngati tili ndi mangawa kwa Yehova. Koma Mulungu wathu wachikondi ndi wokonzeka ‘kufafaniza’ mangawa amenewo ngati tilapa moona mtima, ndi ‘kubwerera,’ ndiponso kumupempha kuti atikhululukire pamaziko a nsembe ya dipo ya Kristu.—Machitidwe 3:19; 10:43; 1 Timoteo 2:5, 6.
7. N’chifukwa chiyani tiyenera kupemphera kuti atikhululukire tsiku ndi tsiku?
7 Nthaŵi zina timachimwa tikalephera kutsatira mfundo za Yehova zachilungamo. Chifukwa cha uchimo wotengera kwa makolo athu, tonse timachimwa pa mawu, zochita, ndi maganizo kapena timalephera kuchita zimene timafunika kuchita. (Mlaliki 7:20; Aroma 3:23; Yakobo 3:2; 4:17) Choncho, kaya tikudziŵa kapena sitikudziŵa kuti tachimwa tsiku limenelo, tiyenera kuphatikiza m’mapemphero athu tsiku lililonse pempho loti atikhululukire machimo athu.—Salmo 19:12; 40:12.
8. Kodi pemphero loti atikhululukire machimo athu liyenera kutilimbikitsa kuchita chiyani, ndipo pangakhale zotsatira zotani zothandiza?
8 Pamene tikupemphera kuti Mulungu atikhululukire machimo athu tiyenera kudzipenda moona mtima, kulapa, kuvomereza machimo athu, komanso tizikhala ndi chikhulupiriro mu mphamvu yopulumutsa ya mwazi wa Kristu. (1 Yohane 1:7-9) Kuti tisonyeze kuona mtima m’mapemphero athu, tiyenera kuchita “ntchito zoyenera kutembenuka mtima.” (Machitidwe 26:20) Tikatero tikhoza kukhala ndi chikhulupiriro kuti Yehova ndi wokonzeka kutikhululukira machimo athu. (Salmo 86:5; 103:8-14) Zotsatira zake zimakhala mtendere wosasimbika wa m’maganizo, “mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse,” umene “udzasunga mitima [yathu] ndi maganizo [athu] mwa Kristu Yesu.” (Afilipi 4:7) Koma pemphero lachitsanzo la Yesu limatiphunzitsanso zambiri zokhudza zimene tiyenera kuchita kuti machimo athu akhululukidwe.
Kuti Atikhululukire Tiyenera Kukhululukira Ena
9, 10. (a) Kodi Yesu anawonjezera ndemanga yotani mu pemphero lachitsanzo, ndipo kodi zimenezi zinatsimikizira chiyani? (b) Kodi Yesu anapereka fanizo lotani losonyeza kufunika kokhululukira ena?
9 Chochititsa chidwi n’chakuti, pempho loti “mutikhululukire mangawa athu, monga ifenso takhululukira amangawa athu,” ndi mbali yokhayo ya pemphero lachitsanzo imene Yesu anaifotokoza. Atamaliza pempherolo, anawonjezera kuti: “Pakuti ngati mukhululukira anthu zolakwa zawo adzakhululukira inunso Atate wanu wa Kumwamba. Koma ngati simukhululukira anthu zolakwa zawo, Atate wanunso sadzakhululukira zolakwa zanu.” (Mateyu 6:14, 15) Motero, Yesu anasonyeza bwino kuti kukhululukidwa kwathu ndi Yehova kumadalira mmene ifeyo tilili okonzeka kukhululukira ena.—Marko 11:25.
10 Nthaŵi ina, Yesu anapereka chitsanzo chosonyeza kufunika koti tizikhala okhululukira ngati tikuyembekezera kuti Yehova atikhululukire. Anafotokoza za mfumu imene inakhululukira mangawa aakulu amene kapolo anali nawo. Kenaka mfumuyi inalanga modetsa nkhaŵa munthu yemweyu pamene anakana kukhululukira mangawa ochepa kwambiri a kapolo mnzake. Yesu anamaliza fanizo lake ponena kuti: “Chomwechonso Atate wanga adzachitira inu, ngati inu simukhululukira yense mbale wake ndi mitima yanu.” (Mateyu 18:23-35) Phunziro lake n’loonekeratu: Mangawa a uchimo amene Yehova wakhululukira aliyense wa ife ndi aakulu kwambiri kusiyana ndi machimo alionse amene wina angatichimwire. Kuwonjezera apo, Yehova amatikhululukira tsiku lililonse. Motero, ifenso tikhoza kukhululuka zochimwa zimene ena amatichimwira nthaŵi zina.
11. Kodi ndi malangizo ati amene mtumwi Paulo ananena omwe tingatsatire ngati tikufuna kuti Yehova atikhululukire, ndipo pangakhale zotsatirapo zabwino zotani?
11 Mtumwi Paulo analemba kuti: “Mukhalirane okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Kristu anakhululukira inu.” (Aefeso 4:32) Kukhululukirana kumabweretsa mtendere pakati pa Akristu. Paulo anapitiriza kunena kuti: “Valani monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima; kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso; koma koposa izi zonse khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.” (Akolose 3:12-14) Zonsezi ndizo tanthauzo la pemphero limene Yesu anatiphunzitsa lakuti: “Mutikhululukire mangawa athu, monga ifenso takhululukira amangawa athu.”
Kutetezedwa Tikamayesedwa
12, 13. (a) Kodi pempho lotsatana ndi lomalizira limene lili m’pemphero lachitsanzo silikutanthauzanji? (b) Kodi Woyesa wamkulu ndani, ndipo kodi zimatanthauzanji tikamapemphera kuti asatitengere kokatiyesa?
12 Pempho lotsatana ndi lomalizira m’pemphero lachitsanzo la Yesu ndi lakuti: “Musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo.” (Mateyu 6:13) Kodi Yesu ankatanthauza kuti tizipempha Yehova kuti asamatiyese? Zimenezo sizingakhale choncho, chifukwa wophunzira Yakobo anauziridwa kulemba kuti: “Munthu poyesedwa, asanena, ndiyesedwa ndi Mulungu; pakuti Mulungu sakhoza kuyesedwa ndi zoipa, ndipo Iye mwini sayesa munthu.” (Yakobo 1:13) Komanso wamasalmo analemba kuti: “Mukasunga mphulupulu, Yehova, adzakhala chilili ndani, Ambuye?” (Salmo 130:3) Yehova sachita kudikirira kuti aone zimene tilakwitse, ndipotu sachita zinthu zotiyesa kuti tilakwe. Nanga mbali imeneyi ya pemphero lachitsanzoli ikutanthauzanji?
13 Satana Mdyerekezi ndi amene akuchita zinthu zotiyesa, kutichititsa kuti tigwe pogwiritsa ntchito machenjerero ake, ndiponso ngakhale kufuna kutilikwira. (Aefeso 6:11) Iyeyu ndiye Woyesa wamkulu. (1 Atesalonika 3:5) Tikamapemphera kuti asatitengere kokatiyesa, timakhala tikupempha Yehova kuti asalole zoti tigwe tikamayesedwa. Timakhala tikumupempha kuti atithandize kuti “asatichenjerere Satana,” ndipo tisafike pokopeka ndi mayesero. (2 Akorinto 2:11) Pemphero lathu ndi lakuti ifeyo tikhalebe “m’ngaka yake ya Wam’mwambamwamba,” kuti tipeze chitetezo chauzimu chimene chinalonjezedwa kwa anthu amene amazindikira kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira zonse zimene anthuwo amachita.—Salmo 91:1-3.
14. Kodi mtumwi Paulo akutitsimikizira motani kuti Yehova sadzatisiya ngati titayang’ana kwa Iye tikamayesedwa?
14 Tingakhale otsimikiza kuti ngati zimene timanena m’mapemphero athu ndiponso zimene timachita n’zochokeradi pansi pamtima, Yehova sadzatisiya. Mtumwi Paulo akutitsimikizira kuti: “Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.”—1 Akorinto 10:13.
“Mutipulumutse kwa Woipayo”
15. Kodi n’chifukwa chiyani tikufunika kupemphera kwambiri panopa kuti tipulumutsidwe kwa woipayo kusiyana ndi kale lonse?
15 Malinga ndi Malemba odalirika Achigiriki Achikristu olembedwa pamanja, pemphero la chitsanzo la Yesu limamaliza ndi mawu akuti: “Mutipulumutse kwa woipayo.”a (Mateyu 6:13) Kutetezedwa kwa Mdyerekezi n’kofunika kwambiri panthaŵi ino yamapeto. Satana pamodzi ndi ziwanda zake akuchita nkhondo ndi otsalira odzozedwa, “amene asunga malamulo a Mulungu, nakhala nawo umboni wa Yesu,” pamodzi ndi anzawo a “khamu lalikulu.” (Chivumbulutso 7:9; 12:9, 17) Mtumwi Petro analimbikitsa Akristu kuti: “Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdyerekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akam’likwire; ameneyo mum’kanize okhazikika m’chikhulupiriro.” (1 Petro 5:8, 9) Satana akufuna kuti aletse ntchito yathu yolalikira, ndipo amatiopseza pogwiritsa ntchito anthu ake padzikoli omwe ndi achipembedzo, a zamalonda, kapena a ndale. Komabe, ngati tikhalabe olimba, Yehova adzatipulumutsa. Mtumwi Yakobo analemba kuti: “Potero mverani Mulungu; koma kanizani mdyerekezi, ndipo adzakuthaŵani inu.”—Yakobo 4:7.
16. Kodi Yehova ali ndi njira zotani zimene angagwiritse ntchito kuti athandize atumiki ake amene akuyesedwa?
16 Yehova analola kuti Mwana wake ayesedwe. Koma Yesu atatsutsa Mdyerekezi, pogwiritsa ntchito Mawu a Mulungu monga chitetezo, Yehova anamutumizira angelo ake kuti akamulimbikitse. (Mateyu 4:1-11) Yehova amagwiritsanso ntchito angelo ake kuti atithandize ngati tipemphera ndi chikhulupiriro ndiponso ngati timutenga kukhala pothaŵirapo pathu. (Salmo 34:7; 91:9-11) Mtumwi Petro analemba kuti: “Ambuye adziŵa kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo, ndi kusunga osalungama kufikira tsiku loŵeruza akalangidwe.”—2 Petro 2:9.
Tatsala Pang’ono Kuwomboledwa Kotheratu
17. Potipatsa pemphero lachitsanzo, kodi Yesu anaika bwanji zinthu pa malo ake?
17 M’pemphero lachitsanzo, Yesu anaika zinthu pa malo ake. Nkhaŵa yathu yaikulu iyenera kukhala yoyeretsa dzina lalikulu ndi loyera la Yehova. Chifukwa chakuti chida chokwaniritsira zimenezi ndi Ufumu wa Mesiya, tikupempherera kuti Ufumuwo udze kudzawononga maufumu onse a anthu opanda ungwiro, kapena maboma, ndi kutsimikizira kuti cholinga cha Mulungu chachitika mokwanira monga kumwamba momwemonso padziko lapansi. Chiyembekezo chathu cha moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso chimadalira pa kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova ndiponso kuzindikira kuti iye ndiye woyenera kulamulira m’chilengedwe chonse. Tikamaliza kupempherera zinthu zonse zofunika kwambiri zimenezi, tikhoza kupempherera zinthu zimene timafuna tsiku lililonse, kuti atikhululukire machimo athu, ndiponso kuti atipulumutse ku ziyeso ndi machenjera a woipayo, Satana Mdyerekezi.
18, 19. Kodi pemphero lachitsanzo la Yesu likutithandiza bwanji kukhalabe odikira ndiponso kukhala ndi chiyembekezo “kufikira chitsiriziro”?
18 Kuwomboledwa kwathu kotheratu kwa woipayo ndiponso ku dongosolo lake la zinthu loipali kwayandikira. Satana akudziŵa bwino kwambiri kuti “kam’tsalira kanthaŵi” koti asonyeze “udani waukulu” padziko lapansi, makamaka kwa atumiki a Yehova okhulupirika. (Chivumbulutso 12:12, 17) Mu chizindikiro chokhala ndi zochitika zosiyanasiyana “cha mathedwe a nthaŵi ya pansi pano,” Yesu analosera zinthu zochititsa chidwi, zimene zina zidzachitika mtsogolo. (Mateyu 24:3, 29-31) Pamene tikuona zimenezi zikuchitika, chiyembekezo chathu chowomboledwa chimalimba. Yesu anafotokoza kuti: “Poyamba kuchitika izi weramukani, tukulani mitu yanu; chifukwa chiwomboledwe chanu chayandikira.”—Luka 21:25-28.
19 Pemphero lachitsanzo lachidule limene Yesu anauza ophunzira ake likutithandiza kuona zinthu zoyenera kuziphatikiza m’mapemphero athu pamene mapeto akuyandikira. Tikhalebe ndi chikhulupiriro kuti mpaka mapeto, Yehova adzapitiriza kutipatsa zimene timafuna tsiku lililonse, zauzimu ndiponso za moyo wa tsiku ndi tsiku. Kupitirizabe kudikira m’mapemphero kudzatithandiza ‘kugwiritsa chiyambi cha kutama kwathu [“chidaliro chathu,” NW] kuchigwira kufikira chitsiriziro.’—Ahebri 3:14; 1 Petro 4:7.
[Mawu a M’munsi]
a Mabaibulo ena, monga la Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono, limamaliza Pemphero la Ambuye ndi mawu otamanda Mulungu akuti: “Pakuti ufumu, mphamvu ndi ulemerero nzanu kwamuyaya. Amen.” Buku la The Jerome Biblical Commentary limati: “Mawu otamanda Mulungu ameneŵa . . . sapezeka mu [zolemba zapamanja] zodalirika.”
Kubwereza
• Kodi tikamapempha “chakudya chathu cha lero” timakhala tikutanthauza chiyani?
• Fotokozani tanthauzo la pempho lakuti “mutikhululukire mangawa athu, monga ifenso takhululukira amangawa athu.”
• Kodi zimatanthauzanji tikamapempha Yehova kuti asatitengere kokatiyesa?
• N’chifukwa chiyani tifunika kupemphera kuti “mutipulumutse kwa woipayo”?
[Zithunzi patsamba 15]
Tiyenera kukhululukira ena ngati tikufuna kuti Mulungu atikhululukire
[Mawu a Chithunzi patsamba 13]
Lydekker