Kodi Mzimu wa Dziko Ukukuipitsani?
PA September 12, 1990, fakitale ina ya ku Kazakstan inaphulika. Mpweya woipa [radioactivity] umene unatuluka m’fakitalemo unafalikira m’dera lonselo, ukumaika pangozi moyo wa anthu 120,000 akumeneko, ndipo ambiri a iwo anachita zionetsero m’makwalala zosonyeza kukwiya ponena za poizoni wakuphayo.
Koma pamene nkhaniyi inavumbulidwa yonse, anapeza kuti iwo anazingidwa ndi mpweya woipawo kwa zaka makumi ambiri. M’zaka zonsezo, matani 100,000 a zinyalala zapoizoni anatayidwa pamtetete, malo osasamalika. Ngakhale kuti anayandikana ndi malo angoziwo, panalibe amene ankada nazo nkhaŵa. Nchifukwa ninji sanade nkhaŵa?
Tsiku lililonse, akuluakulu a fakitaleyo ankasonyeza kuchuluka kwa mpweya woipawo m’bwalo la maseŵero kumene kunasonyeza kuti panalibe ngozi iliyonse. Manambalawo analidi oona, koma ankasonyeza chabe kutuluka kwa cheza cha gamma. Cheza cha alpha, chimene sanapime kuchuluka kwake, nchofanana kuopsa kwake ndi cheza cha gamma. Amayi ambiri anazindikira kuti nchifukwa chake ana awo ankadwaladwala.
Kumbali yauzimu, tingathenso kuipitsidwa ndi zoipitsa zosaoneka. Ndiponso mofanana ndi anthu atsoka a ku Kazakstan, ambiri sakudziŵanso za kuipitsa koika moyo pangoziku. Baibulo limatcha kuipitsa kumeneku “mzimu wa dziko,” umene umasonkhezeredwa ndi Satana Mdyerekezi. (1 Akorinto 2:12) Mdani wa Mulungu ameneyu mwanjiru amagwiritsira ntchito mzimu umenewu—kapena kuti maganizo owanda—a dziko kuti afooketse kudzipatulira kwathu kwa Mulungu.
Kodi mzimu wa dziko ungafooketse bwanji mphamvu yathu yauzimu? Mwa kukulitsa chikhumbo cha maso komanso kugwiritsira ntchito dyera lathu lachibadwa. (Aefeso 2:1-3; 1 Yohane 2:16) Mwachitsanzo, tidzafotokoza mbali zitatu zosiyanasiyana pa zimene maganizo a dzikoli angaipitsire makhalidwe athu auzimu pang’onopang’ono.
Kufunafuna Ufumu Choyamba
Yesu analimbikitsa Akristu ‘kufunafuna Ufumu choyamba ndi chilungamo cha Mulungu.’ (Mateyu 6:33) Kumbali ina, mzimu wa dziko ungatipangitse kuona zilakolako zathu ndi zisangalalo zathu kukhala zinthu zofunika kwambiri. Ngozi yoyamba sindiyo kusiyiratu kutsata zinthu zauzimu, koma kuziika pambuyo m’moyo wathu. Tingathe kunyalanyaza ngoziyo—monga momwe anachitira anthu a ku Kazakstan—chifukwa chopusitsidwa kuti tili otetezereka. Poona kuti takhala zaka zambiri tikutumikira mokhulupirika ndiponso poona kuti timayamikira abale athu ndi alongo athu auzimu tingapusitsidwe ndi kuganiza kuti sitinganyalanyaze choonadi. Nkutheka kuti anthu ambiri a kumpingo wa Efeso ankaganiza chimodzimodzi.
Cha m’chaka cha 96 C.E., Yesu anawapatsa uphungu wotsatirawu: “Ndili nako kanthu kotsutsana ndi iwe, kuti unataya chikondi chako choyamba.” (Chivumbulutso 2:4) Akristu amene anatumikira kwa nthaŵi yaitaliwa anapirira zovuta zambiri. (Chivumbulutso 2:2, 3) Anaphunzitsidwa ndi akulu okhulupirika, kuphatikizapo mtumwi Paulo. (Machitidwe 20:17-21, 27) Komabe, patapita zaka zambiri, kukonda kwawo Yehova kunazirala, ndipo anasiya kupita kwawo patsogolo mwauzimu.—Chivumbulutso 2:5.
Mwinamwake, ena mwa Aefesowo anakhudzidwa ndi kukondetsa chuma ndi chitukuko cha mumzindamo. Mwachisoni, kukondetsa chuma kwa anthu amakono kwagwetsanso Akristu ena. Kulimbikira kufunafuna moyo wapamwamba mosapeŵeka konse kudzatitayitsa zolinga zathu zauzimu.—Yerekezerani ndi Mateyu 6:24.
Pochenjeza za ngozi imeneyi, Yesu anati: “Diso ndilo nyali ya thupi; chifukwa chake ngati diso lako lili lakumodzi, thupi lako lonse lidzakhala loŵalitsidwa. Koma ngati diso lako lili loipa [“losirira,” mawu a m’tsinde, NW], thupi lako lonse lidzakhala lodetsedwa.” (Mateyu 6:22, 23) Diso “lakumodzi” ndi diso loona bwino mwauzimu, diso losumikidwa pa Ufumu wa Mulungu. Kumbali ina, diso “loipa” kapena diso “losirira” ndi diso loona pafupi, losumika chabe pa zilakolako zathupi zalero. Silitha kuona zinthu zauzimu ndi mapindu ake amtsogolo.
M’vesi lake loyambirira, Yesu anati: “Kumene kuli chuma chako, komwe udzakhala mtima wakonso.” (Mateyu 6:21) Kodi tingadziŵe bwanji kuti mtima wathu ukusumika pa zinthu zauzimu kapena pa zinthu zakuthupi? Mwinamwake chingatidziŵitse bwino ndi nkhani zathu, pakuti ‘mkamwa mungolankhula mwa kuchuluka kwa mtima.’ (Luka 6:45) Ngati nthaŵi zonse timakamba za zinthu zakuthupi kapena zipambano zakudziko, ndiwo umboni wakuti mtima wathu wagaŵanika ndiponso kuona kwathu kwauzimu kwawonongeka.
Carmen,a mlongo wachisipanya, analimbana ndi vuto limeneli. “Ndinaleredwa m’banja la choonadi,” akufotokoza motero Carmen, “koma pamene ndinali ndi zaka 18, ndinayamba ntchito yanga ya sukulu ya mkaka. Patapita zaka zitatu ndinali nditalemba antchito anayi, ntchitoyo inkayenda bwino, ndipo ndinkapeza ndalama zambiri. Mwinamwake chimene chinandisangalatsa kwambiri chinali chakuti ndinali kudzipezera ndalama zanga choncho ndinali ‘wachipambano.’ Kunena zoona, mtima wanga unasumika pa ntchitoyo—inali bwenzi langa lapamtima.
“Ndinaganiza kuti ndingakhalebe Mboni pamene ndikuthera nthaŵi yanga yambiri m’ntchitoyi. Kumbali ina, ndinkafunitsitsanso kutumikira Yehova mowonjezereka. Chimene pomaliza chinandilimbikitsa kuti ndiike Ufumu pamalo oyamba chinali chitsanzo cha mabwenzi anga aŵiri amene anali apainiya. Mmodzi wa iwo, Juliana, anali mumpingo wanga. Sanandikakamize kuti ndiyambe kuchita upainiya, koma zimene ankakamba ndi chisangalalo chimene ankapeza mu utumiki wake zinandipangitsa kuganizanso mofatsa za kufunika kwa zinthu zauzimu m’moyo wanga.
“Patapita nthaŵi, pamene ndinali patchuti ku United States, ndinkakhala ndi Gloria, mlongo mpainiya. Panali pasanapite nthaŵi yaitali chimwalirire cha mwamuna wake, ndipo ankasamalira mwana wake wamkazi wazaka zisanu ndi amayi ake amene ankadwala matenda a kansa. Koma ankachitabe upainiya. Chitsanzo chake ndi kuyamikira kwake utumiki kuchokera pansi pamtima zinandigwira mtima. Masiku anayi okha amene ndinakhala panyumba pake anandilimbitsa mtima kuti ndipatse Yehova maluso anga. Choyamba ndinakhala mpainiya wokhazikika, ndipo patapita zaka zingapo, ineyo ndi mwamuna wanga tinaitanidwa kuti tikatumikire pa Beteli. Ndinasiya ntchito yangayo—cholepheretsa kukula kwanga kwauzimu—ndipo tsopano ndikuona kuti moyo wanga ngwachipambano pamaso pa Yehova, chimene chili chinthu chofunika kwambiri.”—Luka 14:33.
Kuphunzira ‘kutsimikizira zinthu zofunika kwambiri,’ monga momwe anachitira Carmen, kudzatithandiza kupanga zosankha zanzeru pofuna ntchito, maphunziro, nyumba, ndi njira ya moyo. (Afilipi 1:10, NW) Koma kodi timatsimikiziranso zinthu zofunika kwambiri pamene tilingalira za zosangulutsa? Iyi ndi mbali ina imene mzimu wa dziko ulinso wamphamvu kwambiri.
Ikani Zosangulutsa Pamalo Ake Oyenera
Mzimu wa dziko umagwiritsira ntchito mochenjera kwambiri chilakolako chachibadwa cha anthu chofuna kupuma ndi kusanguluka. Popeza kuti anthu ambiri alibe chiyembekezo chenicheni cha mtsogolo, iwo amafunadi zosangulutsa ndi chikondwerero chonse nthaŵi ino. (Yerekezerani ndi Yesaya 22:13; 1 Akorinto 15:32.) Kodi ifeyo timaona zosangulutsa kukhala zinthu zofunika kwambiri? Umenewo ungakhale umboni wakuti maganizo a dziko akuipitsa kaonedwe kathu.
Baibulo limachenjeza kuti: “Wokonda zoseketsa [“zosangulutsa,” Lamsa] adzasauka.” (Miyambo 21:17) Zosangulutsa sizoipa, koma kuzikonda, kapena kuziika pamalo oyamba, kudzatisaukitsa mwauzimu. Chilakolako chathu cha zinthu zauzimu mosakayikira konse chidzaloŵa pansi, ndipo sitidzakhala ndi nthaŵi yokalalikira uthenga wabwino.
Choncho, Mawu a Mulungu amatilangiza kuti “khalani okonzekera m’maganizo kugwira ntchito, odziletsa kotheratu.” (1 Petro 1:13, The New English Bible) Kudziletsa nkofunika kuti tiike zosangulutsa zathu pamalo ake. Kukhala okonzekera kugwira ntchito kumatanthauza kukhala okonzekera kugwira ntchito yauzimu, kaya ndi phunziro, misonkhano, kapena utumiki wakumunda.
Nanga bwanji ponena za kupuma kofunikako? Kodi tiyenera kudziimba mlandu pamene tipatula nthaŵi yopuma? Kutalitali. Kupuma nkofunika, makamaka lerolino pamene dziko lili lodzaza ndi zopsinja maganizo. Komabe, monga Akristu odzipatulira sitingalole kuti miyoyo yathu isumikidwe kwambiri pa zosangulutsa. Kukondetsa zosangulutsa pang’ono ndi pang’ono kungatipusitse kuti tichite ulesi ndi kuchita zinthu zofunika. Zosangulutsa zingapangitse chisamaliro chathu pa zinthu zofunika kuzirala, ndiponso zingatipangitse kumwerekera ndi kudzikhutiritsa. Nanga tingatani kuti tikhale ndi kaonedwe kabwino ka zosangulutsa?
Baibulo limati kupumula pang’ono kuli bwino kuposa kugwira ntchito modzipanikiza—makamaka ngati ntchito yake ili yosafunikira kwenikweni. (Mlaliki 4:6) Ngakhale kuti kupuma kumathandiza matupi athu kupezanso mphamvu, mphamvu yauzimu imadza ndi mphamvu ya Mulungu yogwira ntchito. (Yesaya 40:29-31) Timalandira mzimu woyerawu pamene tichita ntchito zathu zachikristu. Phunziro laumwini limadyetsa maganizo athu ndipo limakulitsa zilakolako zoyenera. Kupezeka pamisonkhano kumakulitsa chiyamikiro chathu kwa Mlengi wathu. Kutenga nawo mbali mu utumiki wachikristu kumakulitsa mtima woganizira ena. (1 Akorinto 9:22, 23) Mongadi momwe Paulo anafotokozera molondola kuti, “munthu wakunja anyonyotsokadi, koma tsiku lililonse munthu wamkati alandira mphamvu zatsopano.”—2 Akorinto 4:16, Phillips.
Ileana, mayi wa ana asanu ndi mmodzi amenenso ndi mkazi wa mwamuna wosakhulupirira, amakhala wotangwanika nthaŵi zonse. Ali ndi udindo wosamalira zinthu za pabanja lake ndi achibale ena angapo, zimene zimampangitsa kukhala wotangwanika nthaŵi zonse. Komabe, iye amapereka chitsanzo chabwino cha kulalikira ndi kukonzekera misonkhano. Kodi amatha bwanji kugwira ntchito zina zambirizo?
“Misonkhano ndi utumiki wakumunda zimandithandiza kwambiri kuti ndizitha kugwira ntchito zinazo bwinobwino,” akufotokoza motero Ileana. “Mwachitsanzo, nditatha kulalikira, ndimakhala ndi zambiri zoganizira pamene ndikugwira ntchito yanga yapanyumba. Kaŵirikaŵiri ndimaimba nyimbo pamene ndikugwira ntchitoyo. Komano, ndikaphonya msonkhano kapena ngati ndangolalikira pang’ono, ntchito zapanyumba zimakhala zoŵaŵa kwambiri.”
Nzosiyana chotani nanga ndi kukondetsa zosangulutsa!
Kukongola Kwauzimu Kumasangalatsa Yehova
Tikukhala m’dziko limene mopitirizabe limadera nkhaŵa kwambiri maonekedwe akuthupi. Anthu amawononga ndalama zambiri pofuna kuti maonekedwe awo asinthidwe ndi kuchepetsa zotulukapo zaukalamba. Izi zimaphatikizapo kuika tsitsi m’malo opanda tsitsi ndi kusinthanso maonekedwe ake, kuika zipangizo zokuza maŵere, ndiponso kuchitidwa opaleshoni pofuna kuti akongoletsedwe. Anthu miyandamiyanda amapita kumalo ochepetsera kunenepa, kunyumba zamaseŵero olimbitsa thupi, ndi kumaphunziro a maseŵero othandiza kapumidwe kabwino, kapena kugula mavidiyo ophunzitsa maseŵero olimbitsa thupi ndi mabuku ofotokoza za zakudya zothandiza kuchepetsa thupi. Dziko limafuna kutichititsa kukhulupirira kuti chimwemwe chimadza kokha mwa maonekedwe athu, kuti “maonekedwe” athu ndiwo chinthu chofunika kwambiri.
Ku United States, malinga ndi kufufuza kolembedwa m’magazini ya Newsweek, kunapezeka kuti 90 peresenti ya Aamereka achiyera achinyamata “anali osakhutira ndi maonekedwe a matupi awo.” Kufunitsitsa kuoneka bwino kungakhudze makhalidwe athu auzimu. Pamene anali Mboni ya Yehova yachitsikana, Dora ankachita manyazi ndi maonekedwe ake akuthupi chifukwa chakuti anali wonenepa kwambiri. “Ndikapita kokagula zinthu, kunali kovuta kupeza zovala zoti zingandikwane,” iye akufotokoza motero. “Zinaoneka monga kuti zovala zooneka bwino anazipangira atsikana ochepa matupi okha basi. Choipitsitsa chinali chakuti, anthu ankandinyoza kwambiri chifukwa cha kunenepa kwangaku, zimene zinkandikhumudwitsa kwambiri, makamaka ngati akuchita zimenezi anali abale anga ndi alongo anga auzimu.
“Chotsatirapo chake, ndinayamba kusamala mopambanitsa za maonekedwe anga, kwakuti zinthu zauzimu ndinayamba kuziika pambuyo m’moyo wanga. Zinali monga ngati kuti chisangalalo changa chinkadalira pa ukulu wa chiuno changa. Papita zaka zingapo tsopano, ndipo tsopano popeza kuti ndine mayi wokhwima m’maganizo ndiponso Mkristu, ndinasintha malingaliro. Ngakhale kuti ndimasamala za maonekedwe anga, ndimadziŵa kuti ndi kukongola kwauzimu kumene kuli kofunika kwambiri, ndiponso zimenezo ndizo zimandipatsa chikhutiro chachikulu. Pamene ndinazindikira zimenezi, ndinayamba kuika zinthu za Ufumu pamalo ake oyenera.”
Sara anali mkazi wokhulupirika wakale amene anali ndi malingaliro ameneŵa achikatikati. Ngakhale kuti Baibulo limanena za kukongola kwake kwakuthupi pamene anali ndi zaka zoposa 60, kwakukulukulu limanena za mikhalidwe yake yabwino—munthu wobisika wamtima. (Genesis 12:11; 1 Petro 3:4-6) Iye anali ndi mzimu wodekha ndi wofatsa, ndipo anamvera kotheratu mwamuna wake. Sara analibe nkhaŵa yosayenera ponena za mmene ena ankamuonera. Ngakhale kuti anachokera m’banja lolemera, iye mofunitsitsa anakhala m’mahema kwa zaka zoposa 60. Iye anathandiza mwamuna wake mofatsa ndiponso mosadzikonda; anali mkazi wachikhulupiriro. Zimenezo nzimene zinampangitsa kukhala mkazi wokongola kwambiri.—Miyambo 31:30; Ahebri 11:11.
Monga Akristu, timafuna kuwonjezera kukongola kwathu kwauzimu, kukongola kumene ngati kuwonjezeredwa mobwerezabwereza, kudzakula kwambiri ndi kukhalitsa. (Akolose 1:9, 10) Tingakulitse maonekedwe athu auzimu m’njira zazikulu ziŵiri.
Timakhala okongola kwambiri pamaso pa Yehova pamene timatenga nawo mbali mu utumiki wathu wopulumutsa miyoyo. (Yesaya 52:7; 2 Akorinto 3:18–4:2) Ndiponso, pamene tiphunzira kuonetsa mikhalidwe yachikristu, kukongola kwathu kumakulitsidwa. Mwaŵi wowonjezera kukongola kwathu kwauzimu ulipo waukulu: “Mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu; . . . khalani achangu mumzimu, . . . cherezani aulendo. . . . Kondwani nawo iwo akukondwera; lirani nawo akulira. . . . Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. . . . Khalani ndi mtendere ndi anthu onse.” (Aroma 12:10-18) Kukulitsa makhalidwe ameneŵa kudzatipangitsa kukhala paubwenzi ndi onse aŵiri Mulungu ndi anthu anzathu, ndiponso kudzachepetsa malingaliro auchimo a choloŵa.—Agalatiya 5:22, 23; 2 Petro 1:5-8.
Tingagonjetse Mzimu wa Dziko!
M’njira zambiri zosazindikirika msanga, mzimu woipa wa dziko ungafooketse kukhulupirika kwathu. Ungatipangitse kusakhutira ndi zimene tili nazo ndi kutipangitsa kudera nkhaŵa kwambiri zofuna ndi zinthu zathu choyamba m’malo motsogoza za Mulungu. Mwinanso ungatipangitse kukhala ndi maganizo a anthu m’malo mwa maganizo a Mulungu, kuona zosangulutsa kapena maonekedwe akuthupi ngati zinthu zofunika kwambiri.—Yerekezerani ndi Mateyu 16:21-23.
Satana akufunitsitsa kusakaza makhalidwe athu auzimu, ndipo mzimu wa dziko ndi chimodzi mwa zida zake zazikulu. Kumbukirani kuti Mdyerekezi angasinthe njira zake zochitira zinthu, kuleka kukhala mkango wobuma, m’malo mwake nkukhala wochenjera ngati njoka. (Genesis 3:1; 1 Petro 5:8) Nthaŵi zina, dziko limagonjetsa Mkristu kupyolera m’chizunzo chachikulu, koma kaŵirikaŵiri limamugonjetsa pomuipitsa pang’onopang’ono. Paulo anada nkhaŵa kwambiri ndi vuto lachiŵirili pamene anati: “Ndiopa, kuti pena, monga njoka inanyenga Heva ndi kuchenjerera kwake, maganizo anu angaipsidwe kusiyana nako kuona mtima ndi kuyera mtima zili kwa Kristu.”—2 Akorinto 11:3.
Kuti tidzichinjirize ku machenjera a njokayi, tiyenera kuzindikira njira zoipa zimene ‘zimachokera ku dziko’ ndipo tiyenera kuzikana kotheratu. (1 Yohane 2:16) Sitiyenera kusochezedwa pokhulupirira kuti kalingaliridwe ka dzikoli nkosavulaza. Mpweya wapoizoni wa dongosolo la Satana wafika poipa kwambiri.—Aefeso 2:2.
Titazindikira kulingalira kwa dziko, tingathe kukugonjetsa mwa kudzaza maganizo athu ndi mtima wathu ndi chiphunzitso choyera cha Yehova. Mogwirizana ndi Mfumu Davide, tiyeni tinene kuti: “Mundidziŵitse njira zanu, Yehova; mundiphunzitse mayendedwe anu. Munditsogolere m’choonadi chanu, ndipo mundiphunzitse; pakuti Inu ndinu Mulungu wa chipulumutso changa.”—Salmo 25:4, 5.
[Mawu a M’munsi]
a Maina asinthidwa.
[Chithunzi patsamba 26]
Kulimbikira kufunafuna moyo wapamwamba kungatitayitse zolinga zathu zauzimu