Kodi Chipembedzo Chingakhutiritse Zosowa Zathu?
NCHIYANI chimene tidzadya? Nchiyani chimene tidzamwa? Nchiyani chimene tidzavala? Pali chisonkhezero chofulumira ponena za mafunso amenewa, makamaka ngati chiri chovuta kupeza zosowa zofunika za moyo. Komabe, zindikirani chimene Yesu Kristu ananena: “Musadere nkhaŵa moyo wanu, chimene mudzadya ndi chimene mudzamwa; kapena thupi lanu, chimene mudzavala.” (Mateyu 6:25) Kodi chimenechi chikuwoneka chachilendo? Ndiko nkomwe, ngati wina asowa chakudya, chovala, ndi malo ogona, chomwe amafuna ndi thandizo lokhoza kugwira ntchito, osati chimene ena amachiwona monga thandizo la chipembedzo.
Yesu sanali wosamverera chifundo, ndiponso iye sanali kuyesa kuthaŵa nkhaniyo. Iye anali wodziŵa za zosowa za anthu. Mosasamala kanthu za chimenecho, iye anadziŵanso za tsoka lenileni lalikulu. Pamene chibwera ku kukhutiritsa zosowa zathu, chiri chapafupi kuzika miyoyo yathu mozungulira pa zinthu zakuthupi ndi kudzimva kuti Mulungu sali wofunika koposa. Chotero, tiyenera kupeza zinthu zathu zoyambirira molondola.
Tingakhale tikupeza zinthu zathu zoyambirira molondola ngati titsatira uphungu wa Yesu: “Muthange mwafuna choyamba Ufumu ndi chilungamo [cha Mulungu], ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.” (Mateyu 6:33) Ngati titsatira uphungu umenewo, chipembedzo—chipembedzo chowona chozikidwa pa chowonadi cha Baibulo—chingakhutiritse zosowa zathu.
Yesu sanali wosalingalira zenizeni pa kulingalira kuti, ngakhale kuli tero, kungokhala kokha mmodzi wa ophunzira ake ndi kutsatira ziphunzitso zake za chipembedzo mwamsanga kungathetse mavuto athu ndiponso iye sanatanthauze kuti ophunzira ake ayenera kungokhala ndi kudikira kaamba ka Mulungu kupereka zosowa zawo mozizwitsa. Nkulekelanji, popeza aliyense angakhale Mkristu ngati chimenecho chinatanthauza ufulu wa mwadzidzidzi ku zovuta zonse za moyo! Chimene Yesu anatanthauza chinali chakuti Atate wake, Yehova Mulungu, amapereka chirichonse choyenera kukhutiritsa zosowa zathu zonse. Chimenecho ndicho chifukwa chake Yesu ananenanso kuti: “Atate wanu wa kumwamba adziŵa kuti musowa zonse zimenezo.”—Mateyu 6:32.
Yehova amakhutiritsa zosowa zathu zofunika kwambiri zauzimu. Kupyolera m’Malemba Oyera, iye watipatsa ife chitsogozo chouziridwa kutsogoza miyoyo yathu m’mkhalidwe wabwino koposa wothekera. (Yesaya 48:17) Mulungu wakhazikitsa mayanjano a olambira omwe amapereka chirikizo pamene lifunika. (Machitidwe 4:34) Iye amagweramonso kuthandiza atumiki ake kupyolera mwa mzimu wake woyera, kapena mphamvu yogwira ntchito. (Luka 11:13; Agalatiya 5:22-25) Kuwonjezerapo, Mulungu wapanga makonzedwe a kubwezeretsa Paradaiso kudziko lapansi.—Luka 23:43; Chivumbulutso 21:1-4.
Kukhutiritsa Zosowa Zathu Zakuthupi
Tsopano lingalirani ena a maprinsipulo a Baibulo omwe athandiza anthu kukhutiritsa zosowa zawo zakuthupi. Mtumwi wa Chikristu Paulo analemba kuti:
“Tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu.” (2 Akorinto 7:1)
Lingalirani za mavuto onse omwe tingapulumuke ngati tipewa chidetso cha fodya, anamgoneka oletsedwa ndi zinthu zina zomwe zimaipitsa thupi. Ndipo tingakhale abwinopo chotani nanga ngati sitisakaza ndalama, nthaŵi ndi malingaliro pa mabukhu a mkhalidwe woipa ndi zosangulutsa zomwe zingadetse uzimu wathu!
Malemba amanenanso kuti:
“Usakhale mwa akumwaimwa vinyo, ndi ankhuli osusuka. Pakuti wakumwaimwa ndi wosusukayo adzasauka; Ndipo kusinza kudzaveka munthu nsanza.” (Miyambo 23:20, 21)
Dziŵani zotulukapo zomalizira za kumwaimwa ndi kususuka—umphaŵi ndi nsanza. Ambiri lerolino—ngakhale anthu a chipembedzo kwambiri—amakhalabe aumphaŵi chifukwa iwo amamwerekera mu zakumwa zoledzeretsa kapena ali omwerekera ku zinthu zomwe zimadetsa thupi. Kupewa zinthu zoterozo kuti timamatire ku miyezo ya Baibulo kumachita zambiri kuthandiza kukhutiritsa zosowa zathu kaamba ka chakudya, zovala, ndi malo ogona.
Prinsipulo lina lomwe lathandiza Akristu kukhutiritsa zosowa zawo likuwonedwa mu mawu a mtumwi Paulo:
“Takopeka mtima kuti tiri nacho chikumbumtima chokoma m’zonse, pofuna kukhala nawo makhalidwe abwino.” (Ahebri 13:18)
Kuwona mtima mu machitidwe awo onse kwatheketsa Akristu ambiri kupereka bwino kaamba ka iwo eni ndi mabanja awo. Kuwapezera iwo chiyamikiro chabwino, ndipo ena ali okhoza kuchita malonda ndi iwo. Munthu wowona mtima nthaŵi zonse sangakhale ndi zambiri m’njira ya kuthupi, koma iye kaŵirikaŵiri ali ndi zosowa zofunika za moyo ndipo amasungilira ulemu wake.
Wogwirizana kotheratu ndi ichi uli uphungu wakuti:
“Wakubayo asabenso; koma makamaka agwiritse ntchito, nagwire ntchito yokoma ndi manja ake.” (Aefeso 4:28)
Kugwiritsira ntchito prinsipulo limeneli kwathandiza ambiri kupeza ndi kusungabe ntchito chifukwa iwo ali odalirika. Mofananamo, iwo ali okhoza kupereka kaamba ka iwo eni ndi mabanja awo. M’malo mwa kukhala oyambukiridwa ndi mzimu wa dziko lino, womwe umatembenuzira diso lakhungu ku machitachita ambiri akusawona mtima, Akristu ali owona mtima, ndipo ichi chimabweretsa zotulukapo zabwino.
Kuti tichitire chitsanzo: Mmodzi wa Mboni za Yehova mu Japan anafuna kugwira ntchito maora ochepa mlungu uliwonse kotero kuti akhale ndi nthaŵi yokwanira kaamba ka zolondola zauzimu. Pamene iye anapanga chifunsirochi, ngakhale kuli tero, womlemba ntchito wake anamuchotsa ntchito. Pa chimenecho, mayi wake wa wolemba ntchitoyo anafunsa kuti: “Kodi unachotsa ntchito munthu wodalirika koposa?” Zinthu zinaipa koposa kwa Mboniyo pamene anavulaza msana wake pamene anali kuchita ntchito ina. Mwamsanga pambuyo pake, iye anakumana ndi womlemba ntchito wake woyambirira, yemwe anali wokhumudwitsidwa chifukwa iye anali atangodziŵa kumene kuti mmodzi wa olembedwa ntchito ake anali kuba golidi, platinum, ndi mphete kuchokera ku kampani yake ya miyala yokometsera. Wolemba ntchitoyo mwamsanga anafunsa Mboniyo kubwereranso ku ntchito, panthaŵi ino wolamuliridwa ndi zofuna za mboniyo. Munthuyo anafuna wogwira ntchito wowona mtima.
Molingana ndi mtumwi Paulo, Mkristu ayenera “kuchita ntchito molimbika” osati kokha kuti apereke kaamba ka iyemwini komanso “kuti akhale nacho china chakugawira kwa osowa.” (Aefeso 4:28) M’nthaŵi zosowa, Akristu owona nthaŵi zonse amakhala ofunitsitsa kuthandiza ena. Banja lina mu Fiji linakumana ndi ichi pamene nyumba yawo inawonongedwa kwambiri ndi mphepo yolimba pamene anali ku msonkhano Wachikristu. Pamene anabwerera kunyumba anapeza chiwonetsero cha kusakaza. Koma anapezanso akhulupiriri anzawo omwe mwachimwemwe anagwiritsira ntchito magwero awo kupereka kwa banjalo malo ogona ndi thandizo m’kumanganso nyumba yawo. “Chinali chitonthozo,” akutero tateyo, “pamene udziŵa kuti pali Akristu omwe amasamaliradi ponena za iwe.”
Yesu Kristu anamva chisoni chachikulu kaamba ka osowa. Pa zochitika zambiri, iye mwaumwini anathandiza awo opanda mwaŵi m’njira imodzi kapena inzake. Ndithudi, Yesu anadziŵa kuti kufikira ku utali umene dongosolo loipa iri la kachitidwe ka zinthu lidzaloledwa kukhalapo, umphaŵi ndi mavuto ena amayanjano adzakhalirira. (Yohane 12:8) Chotero, ngakhale kuti iye anachita zambiri kuthandiza anthu mwakuthupi, mphamvu yeniyeni ya utumiki wake inali kukhutiritsa zosowa zawo zauzimu.
Pamene khamu limene njala yake inakhutiritsidwa linatsatira Yesu ku Kapernao, iye anapanga ndemanga yodziŵikayi: “Mundifunafuna, osati chifukwa munawona zizindikiro, koma chifukwa munadya kuchokera ku mikate nimukhutiritsidwa. Gwirani ntchito, si kaamba ka chakudya chomwe chimatha, koma chakudya chomwe chimakhalira ku moyo wosatha, chimene Mwana wa munthu akupatsani inu.” (Yohane 6:26, 27) Nchiyani chimene Yesu anatanthauza?
Yesu anatanthauza kuti pali tsoka lakuti anthu angayanjane ndi iye ndi atumwi ake kokha chifukwa cha mwaŵi wa zinthu zakuthupi. Koma iye anadziŵa kuti ichi sichidzawabweretsera mapindu osatha. Chotero iye ananena kuti: “Odala ali osauka mu mzimu; chifukwa uli wawo ufumu wakumwamba. Odala ali akumva njala ndi ludzu la chilungamo; chifukwa adzakhuta.”—Mateyu 5:3, 6.
Pambali pa njala kaamba ka chakudya chakuthupi, pali njala kaamba ka chowonadi ndi chikwaniritso chauzimu. Chimwemwe chenicheni chimatulukapo pamene njala yauzimu imeneyi ikhutiritsidwa. Dziko la chipembedzo latulutsa chitaganya cha maganizo ozikidwa pa zinthu zakuthupi. Zipembedzo za Kum’mawa zasiya anthu m’mdima wauzimu. Koma kulambira kowona—chipembedzo cha Yesu Kristu—chakhutiritsa zosowa zauzimu za anthu. Chingachite zofananazo kwa inu. Makonzedwe amenewa angakhale anu ngati mudziyeneretsa inu eni kaamba ka iwo.
Mwachitsanzo, kuchokera kwa Mkristu wodzilowetsa m’kuchitira umboni m’khwalala mwamuna wachichepere mmodzi wa ku Mauritius analandira makope a Nsanja ya Olonda ndi magazini inzake ya Galamukani! Mlungu wotsatira, iye anabwera kaamba ka makope owonjezereka. Iye analongosola kuti iye anali atafuna kudzipha chifukwa cha mavuto ake a zachuma, koma magaziniwo anamthandiza iye kuzindikira kuti panali Mulungu yemwe amasamalira kaamba ka ife. Njala yauzimu ya mwamuna wachichepereyo inayamba kukhutiritsidwa.
Kodi ife tidzawona nthaŵi pamene zosowa zathu zonse zidzakhutiritsidwa kotheratu? Baibulo limalonjeza kuti tidzatero. Zowona, anthu atopetsedwa ndi kumva lonjezo pambuyo pa lonjezo kaamba ka zinthu zabwino zodzabwera. Iwo akhala okhumudwitsidwa kaŵirikaŵiri. Koma tingakhale ndi chidaliro m’malonjezo a Baibulo. Mkonzi wake, Yehova Mulungu, amakwaniritsa lonjezo lirilonse limene iye amapanga. Yoswa analongosola bwino ichi pamene iye anakumbutsa Aisrayeli anzake: “Mumadziŵa m’mitima yanu yonse ndi m’moyo wanu wonse kuti pa mawu okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwa padera mawu amodzi. Onse anachitikira inu. Sanasowapo mawu amodzi.”—Yoswa 23:14.
Yankho lenileni ku mavuto athu onse limakhala mu kukwaniritsidwa kwa malonjezo ozizwitsa a Mulungu akuyeretsa dziko lonse lapansi. (Chivumbulutso 11:18) Zosowa zathu zonse zidzakhutiritsidwa pamene Ufumu wake udzabwezeretsa Paradaiso wa padziko lapansi, kukwaniritsa chifuno chake choyamba kaamba ka mtundu wathu. (Mateyu 6:9, 10) Kenaka sitidzamvanso ‘mawu akulira kapena kulira kwa njala’ kuchokera kwa anthu amene zosowa zawo sizingakhutiritsidwe. Kuchokera mu ntchito yowona mtima ndi kugwiritsira ntchito maprinsipulo aumulungu, iwo adzasangalala ndi moyo weniweni, wokhutiritsa.—Yesaya 65:17-25.
Maria, m’virigo wa Chikatolika wotchulidwa poyambirirayo, anapeza chikhutiritso chimenechi. Iye anazindikira kuti iye anakhala m’mdima wauzimu kwa zaka zambiri, kukanthidwa ndi mantha ponena za mtsogolo ndipo wosakhoza kuwona tanthauzo lenileni la moyo. Koma kuphunzira chowonadi cha Baibulo kunasintha zonsezo. “Ndinachoka m’mdima kupita m’kuwunika komawala,” iye anatero. (Masalmo 43:3; Miyambo 4:18) Ichi sichinangomthandiza iye kukumana ndi zosowa zake za mwamsanga zakuthupi komanso kunakhutiritsa njala ndi ludzu lake lauzimu. Inde, chipembedzo—chipembedzo chowona—chingakhutiritse zosowa zathu.
[Chithunzi patsamba 7]
Chipembedzo chowona chidzakhutiritsa zosowa zathu zonse