Muthange Mwafuna Ufumu ndi Chilungamo cha Mulungu
‘Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.’—MATEYU 6:33.
1, 2. Kodi alembi ndi Afarisi anatembenuza ntchito zimene zinali zabwino pazokha kukhala chiyani, ndipo kodi ndi chenjezo lotani limene Yesu anapereka kwa atsatiri ake?
ALEMBI ndi Afarisi anafunafuna chilungamo m’njira yawo, imene sinali njira ya Mulungu. Siizi zokha, komanso pamene anachita ntchito zimene zinali zabwino pazokha, anazitembenuza kukhala ntchito zachinyengo zochitidwira kuwonedwa ndi anthu. Iwo sankatumikira Mulungu ayi, koma uchabe wawo. Yesu anachenjeza ophunzira ake kutsutsa kachitidwe ka maseŵerawa kuti: ‘Yang’anirani kuti musachite zolungama zanu pamaso pa anthu kuti muonekere kwa iwo; pakuti ngati mutero mulibe mphotho ndi Atate wanu wa kumwamba.’—Mateyu 6:1.
2 Yehova amawayamikira anthu amene amapatsa zinthu osauka—koma osati anthu amene amapatsa monga mmene anachitira Afarisi. Yesu anachenjeza ophunzira ake kuti asawatsanzire mwakuti: ‘Chifukwa chake pamene paliponse upatsa mphatso zachifundo, usamaomba lipenga patsogolo pako, monga amachita onyenga m’masunagoge, ndi m’makwalala, kotero kuti atamandidwe ndi anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zawo.’—Mateyu 6:2.
3. (a) Kodi ndimnjira yotani mmene alembi ndi Afarisi analandiriratu kaamba ka zopereka zawo? (b) Kodi ndimotani mmene kaimidwe ka Yesu pa zopereka kanasiyanira?
3 Liwu Lachigiriki lomasuliridwa ndi mawu akuti “iwo alandiriratu” (a·peʹkho) linali liwu limene kaŵirikaŵiri linawonekera m’malisiti a bizinesi. Kuligwiritsira ntchito kwake mu Ulaliki wa pa Phiri kumasonyeza kuti “iwo azilandira mphotho zawo,” ndiko kuti, “iwo aisaina lisiti ya mphotho yawoyo: kuyenerera kwawo kwa kuilandira mphotho yawo kwakwaniritsidwa, ndendende monga kuti adaipereka kale lisiti yake.” (An Expository Dictionary of New Testament Words, yolembedwa ndi W. E. Vine) Mphatso za osauka zinapemphedwera poyera m’makwalala. M’masunagoge maina a osonkha zopereka ankalengezedwa. Anthu amene anapereka zinthu zambiri analemekezedwa mwapadera mwakuwaika pa mipando yoyandikana ndi arabi polambira. Ankapereka kuti awonedwe ndi anthu; iwo anawonedwa ndi kulemekezedwa ndi anthu; mwakutero, iwo anaisaina lisiti yamphotho imene inachokera m’kupatsa mphatso kwawoko “Alandiriratu.” Kaimidwe ka Yesu kanali kosiyana chotani nanga ndi aka! Patsani “zam’tseri; ndipo Atate wako wakuona m’tseri adzakubwezera iwe.”—Mateyu 6:3, 4; Miyambo 19:17.
Mapemphero Amene Amakondweretsa Mulungu
4. Kodi nchifukwa ninji mapemphero a Afarisi anachititsira Yesu kutcha amunawa kukhala onyenga?
4 Yehova amayamikira mapemphero amene amalunjikitsidwa kwa iye—koma osati monga mmene anapempherera Afarisi. Yesu anati kwa atsatiri ake: ‘Ndipo pamene mupemphera, musakhale monga onyengawo; chifukwa iwo akonda kuimirira ndi kupemphera m’masunagoge, ndi pa mphambano za makwalala, kuti aonekere kwa anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zawo.’ (Mateyu 6:5) Afarisi anali ndi mapemphero ambiri ofunikira kubwerezedwabwerezedwa tsiku lirilonse, panthaŵi zakutizakuti, mosasamala kanthu za kumene iwo anali. Mwalamulo, iwo anafunikira kuwapereka mseri. Komabe, mwamachenjera, iwo anakhoza kukhala “pa mphambano za makwalala,” owonekera kwa anthu odutsa m’njira zonse zinayi, pamene nthaŵi yopemphera inafika.
5. (a) Kodi ndi machitidwe ena ati amene anachititsa mapemphero a Afarisi kusamvedwa ndi Mulungu? (b) Kodi Yesu anaika zinthu ziti poyamba m’pemphero lake lachitsanzo, ndipo kodi anthu lerolino amavomerezana nalo?
5 Kuti asonyeze kuyera kwachinyengo, iwo akakhoza monyenga ‘kuchita mapemphero atali.’ (Luka 20:47) Mwambo wina wapakamwa unati: “Anthu achangu akale ankayembekezera kwa ola limodzi asanapereke Tefillah [pemphero].” (Mishnah) Panthaŵiyo aliyense akatsimikizira kuwona chifundo chawo ndikuzizwa nacho! Mapemphero oterowo sanapite kutali koma kuthera m’mutu mwawomo. Yesu anati komwe kunafunikira kunali kupempherera mseri, popanda kubwerezabwereza kopanda pake, ndipo iye anawapatsa chitsanzo chopepuka. (Mateyu 6:6-8; Yohane 14:6, 14; 1 Petro 3:12) Pemphero lachitsanzo la Yesu linaika zinthu zoyamba poyamba motere: ‘Atate wathu wa kumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe.’ (Mateyu 6:9-13) Ndi anthu ochepa amene amalidziŵa dzina la Mulungu lerolino, ngochepanso amene amafuna kuti liyeretsedwe. Chotero iwo amampanga kukhala mulungu wopanda dzina. Ufumu wa Mulungu udze eti? Ambiri amaganiza kuti uli kale pano, mkati mwawo. Iwo angapempherere chifuno chake kuchitika, komatu ambiri amachita chifuniro chawo.—Miyambo 14:12.
6. Kodi nchifukwa ninji Yesu anatsutsa kusala kudya Kwachiyuda kukhala kopanda pake?
6 Kusala kudya nkololeka kwa Yehova—koma osati monga mmene kunachitidwira ndi Afarisi. Monga mmene anachitira ndi kupatsa mphatso zaulere ndi kupemphera kochitidwa ndi alembi ndi Afarisi, Yesu anatsutsanso kusala kwawo kudya kukhala kopanda pake mwakuti: ‘Pamene ponse musala kudya, musakhale ndi nkhope yachisoni, ngati onyengawo; pakuti aipitsa nkhope zawo, kuti aonekere kwa anthu kuti alimkusala kudya. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zawo.’ (Mateyu 6:16) Miyambo yawo yapakamwa inasonyeza kuti m’nthaŵi ya kusala kudya Afarisi sankasamba konse kapena kudzola mafuta koma kupaka phulusa pamitu yawo. Pamene sankasala kudya, Ayuda anasamba ndi kudzola mafuta thupi lawo mokhazikika.
7. (a) Kodi atsatiri a Yesu anafunikira kudzisamalira okha motani pa kusala kudya? (b) Ponena za kusala kudya, kodi Yehova anafunanji m’tsiku la Yesaya?
7 Ponena za kusala kudya, Yesu anauza atsatiri ake kuti: ‘Dzola mutu wako, ndi kusamba nkhope yako: kuti usaonekere kwa anthu kuti ulikusala kudya, koma kwa Atate wako ali m’tseri.’ (Mateyu 6:17, 18) M’tsiku la Yesaya, Ayuda opanduka anasangalala ndi kusala kwawo kudya, akumavulaza miyoyo yawo, kuweramitsa mitu yawo, ndi kukhala pachiguduli ndi paphulusa. Koma Yehova anawafuna kuti amasule otsenderezedwa, adyeste akumva njala, apatse pogona opanda nyumba, ndi kuveka opanda zovala.—Yesaya 58:3-7.
Kundikani Chuma Chakumwamba
8. Kodi nchiyani chinapangitsa alembi ndi Afarisi kutaikiridwa mmene angapezere chiyanjo cha Mulungu, ndipo kodi ndi lamulo liti, pambuyo pake lofotokozedwa ndi Paulo, limene iwo ananyalanyaza?
8 M’kulondola kwawo chilungamo, alembi ndi Afarisi anataikiridwa mopezera chiyanjo cha Mulungu ndipo anasumika pa kukondweretsa anthu. Iwo anatanganitsidwa zedi ndi miyambo ya anthu kwakuti anakankhira pambali Mawu olembedwa a Mulungu. Iwo anasumika mitima yawo pamaudindo a padziko lapansi mmalo mwa chuma chakumwamba. Iwo ananyalanyaza chowonadi chopepuka ichi chimene Mfarisi wotembenuzidwa kukhala Mkristu anachilemba zaka zingapo pambuyo pake: ‘Chirichonse mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima, monga kwa [Yehova, NW], osati kwa anthu ai; podziŵa kuti mudzalandira kwa [Yehova, NW] mphotho ya cholowa.’—Akolose 3:23, 24.
9. Kodi ndi ngozi ziti zimene zingawopsyeze chuma chapadziko lapansi, koma kodi nchiyani chimene chidzasunga chuma chowona kukhala chosungika?
9 Yehova ngwokondweretsedwa m’kudzipereka kwanu kwa iye, osati mu akaunti yanu ya ku banki. Iye amadziŵa kuti kumene kuli mtima wanu ndiko kuli chuma chanu. Kodi dzimbiri ndi njenjete zingachidye chuma chanu? Kodi mbala zingaboole chipupa chadothi ndikuchiba? Kapena m’nthaŵi zamakonozi za m’gwedegwede wa chuma, kodi kutha mtengo kwa ndalama kungagwetse mphamvu yake ya kugula zinthu kapena kodi kugwa kwa misika yogulitsa chisungiko cha chuma kudzachithetseratu? Kodi kukula kwa upandu kudzapangitsa chuma chanu kubedwa? Izi sizingachitike ngati chasungidwira m’mwamba. Sichingachitikenso ngati diso lanu—nyali imene imaunikira thupi lanu lonse—nlopepuka, losumikidwa pa Ufumu wa Mulungu ndi chilungamo chake. Chuma chiri ndinjira yothera. ‘Usadzitopetse kuti ulemere; leka nzeru yako yako. Kodi upenyeranji chimene kulibe? Pakuti chuma chimera mapiko, ngati mphungu youluka mumlengalenga.’ (Miyambo 23:4, 5) Chotero nkuthedweranji tulo ndi chuma? “Kukhuta kwa wolemera sikumgonetsa tulo.” (Mlaliki 5:12) Kumbukirani chenjezo ili la Yesu: ‘Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.’—Mateyu 6:19-24.
Chikhulupiriro Chimene Chimachotsa Kuda Nkhaŵa
10. Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kuika chikhulupiriro chanu mwa Mulungu mmalo mwa chuma chakuthupi, ndipo kodi ndi uphungu wotani umene Yesu anapereka?
10 Yehova akufuna kuti chikhulupiriro chanu chikhale mwa iye, osati m’chuma chakuthupi. ‘Wopanda chikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna iye.’ (Ahebri 11:6) Yesu anati: ‘Chifukwa moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.’ (Luka 12:15) Mamiliyoni omwe mukuwasungira m’banki sadzapangitsa mapapo odwala kugwirabe ntchito kapena kupangitsa mtima wokalamba kupompabe mwazi. Chotero ‘chifukwa chake ndinena kwa inu,’ Yesu anapitiriza tero mu Ulaliki wake wa pa Phiri kuti: ‘Musadere nkhaŵa moyo wanu, chimene mudzadya ndi chimene mudzamwa; kapena thupi lanu, chimene mudzavala. Kodi moyo suli woposa chakudya, ndi thupi loposa chovala?’—Mateyu 6:25.
11. Kodi nkuti kumene Yesu anapeza mafanizo ake ambiri, ndipo kodi ndimotani mmene ichi chasonyezedwera mu Ulaliki wa pa Phiri?
11 Yesu anali katswiri wolankhula mafanizo. Iye anawalingalira paliponse pamene anapenya. Iye anawona mkazi akuika nyali yoyatsidwa pa choikapo nyali ndipo anachisintha ichi kukhala fanizo. Iye anawona mbusa akulekanitsa nkhosa ndi mbuzi; nachipanganso ichi kukhala fanizo. Iye anawona ana akuseŵera pamsika; nawatolanso kukhala fanizo. Ndipo zinali tero pa Ulaliki wa pa Phiri. Pamene analankhula za kuda nkhaŵa ponena za zosoŵa zakuthupi, iye anawona mafanizo m’mbalame zomaulukauluka ndi maluŵa okometsera m’mphepete mwa mapiri. Kodi mbalame zimafesa ndikututa? Ayi. Kodi maluŵa amapota ndi kuluka? Ayi. Mulungu ndiye anawapanga; iye amawasamalira. Komabe, inu ndinu wamtengo wapatali kuposa mbalame ndi maluŵa. (Mateyu 6:26, 28-30) Iye anampereka Mwana wake kaamba ka inu, osati izo.—Yohane 3:16.
12. (a) Kodi mafanizo a mbalame ndi maluwa anatanthauza kuti ophunzira a Yesu sanafunikire kugwira ntchito? (b) Kodi Yesu ankapanga mfundo iti ponena za ntchito ndi chikhulupiriro?
12 Yesu panopa sanali kuwuza atsatiri ake kuti sanafunikire kugwira ntchito kuti adzidyetse ndi kudziveka. (Onani Mlaliki 2:24; Aefeso 4:28; 2 Atesalonika 3:10-12.) Pa m’mawa mwa nyengo ya ngululu mmenemo, mbalame zinali zotanganitsidwa kutolatola zakudya, kupalana ubwenzi, kumanga zisa, kufungatira mazira, kudyetsa ana awo. Izo zinkagwira ntchito koma popanda kuda nkhaŵa. Maluwa nawonso anali otanganitsidwa kuika mizu yawo m’nthaka kufunafuna madzi ndi zakudya ndikutambasulira masamba awo kudzuŵa. Iwo anafunikira kukula ndikuphuka maluŵa ndikubala mbewu zawo asanafe. Iwo ankagwira ntchito koma popanda kuda nkhaŵa. Mulungu anazidyetsa mbalame ndi maluŵa. ‘Nanga siinu kopambana ndithu, inu akukhulupirira pang’ono?’—Mateyu 6:30.
13. (a) Kodi nchifukwa ninji kunali koyenerera kwa Yesu kugwiritsira ntchito kupima kwa mkono polankhula za kuwonjezera utali wa moyo wa munthu? (b) Kodi ndimotani kunena kwake titero, mmene mungatalikitsire moyo wanu makilomita opanda polekezera?
13 Chotero khalani nacho chikhulupiriro. Musade nkhaŵa. Nkhaŵa sizidzasintha chirichonse. ‘Ndani wa inu ndi kuda nkhawa angathe kuonjezera pa [utali wa moyo, NW] wake mkono umodzi?’ (Mateyu 6:27) Koma kodi nchifukwa ninji Yesu akugwiritsira ntchito kupima mtunda kwa kuthupi, mkono, kupimira nthaŵi ya utali wa moyo? Mwinamwake nchifukwa chakuti Baibulo kaŵirikaŵiri limafanizitsa utali wa moyo wa munthu ku ulendo, mwa kugwiritsira ntchito mawu onga ngati ‘njira ya ochimwa,’ “njira ya olungama,” ‘chipata chotakata chonka ku chiwonongeko,’ ndi ‘chipata chopapatiza chonka nacho ku moyo.’ (Salmo 1:1; Miyambo 4:18, NW; Mateyu 7:13, 14) Kudera nkhaŵa zosoŵa za tsiku ndi tsiku sikungawonjezere moyo wa munthu mpang’ono ponse, ngakhale “mkono umodzi,” kunena kwake titero. Koma ilipo njira yotalikitsira moyo wanu m’makilomita mamiliyoni ambirimbiri opanda mapeto, kunena kwake titero. Simwakukhala wodera nkhaŵa mwa kunena kuti: ‘Tidzadya chiyani?’ kapena kuti ‘Tidzamwa chiyani?’ kapena ‘Tidzavala chiyani?’ koma ndi mwa kukhala ndi chikhulupiriro ndikuchita ichi chimene Yesu akutiuza kuchita: ‘Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.’—Mateyu 6:31-33.
Kupeza Ufumu wa Mulungu ndi Chilungamo Chake
14. (a) Kodi ndiuti umene uli mutu wa Ulaliki wa pa Phiri? (b) Kodi alembi ndi Afarisi anafunafuna Ufumu ndi chilungamo m’njira yolakwika iti?
14 M’sentensi lotsegulira Ulaliki wake wa pa Phiri, Yesu analankhula za Ufumu wakumwamba kukhala wa odera nkhaŵa kusowa kwawo kwauzimu. M’sentensi lachinayi, iye anati akumva njala ndi ludzu lachilungamo adzakhuta. Panopa Yesu akuika ponse paŵiri Ufumu ndi chilungamo cha Yehova pamalo oyamba. Izi ndizo mutu wa Ulaliki wa pa Phiri. Ndiwo mayankho ku zosoŵa za anthu onse. Koma kodi Ufumu wa Mulungu ndi chilungamo cha Mulungu zingapezedwe bwanji? Kodi tingapitirize bwanji kuzifunafuna? Osati m’njira imene alembi ndi Afarisi anachitira. Iwo anafunafuna Ufumu ndi chilungamo kupyolera m’Chilamulo cha Mose, chimene iwo anati chinaphatikizapo miyambo yapakamwa, popeza kuti anakhulupirira kuti zonse ziŵiri Chilamulo cholembedwa ndi miyambo yapakamwa inapatsidwa kwa Mose ndi Mulungu pa Phiri la Sinai.
15. (a) Ponena za Ayuda, kodi ndiliti pamene miyambo yawo yapakamwa inayamba, ndipo kodi ndimotani mmene anaikwezera pamwamba pa Chilamulo cholembedwa cha Mose? (b) Kodi ndiliti pamene miyamboyi inayambadi, ndipo ndi chiyambukiro chotani pa Chilamulo cha Mose?
15 Mwambo wawo wonena za ichi unati: “Mose analandira Chilamulo [mawu amtsinde, ‘Chilamulo Chapakamwa’] pa Sinai ndikuchipereka kwa Yoswa, ndipo Yoswa anachipereka kwa akulu, ndipo akulu anachipereka kwa Aneneri; ndipo Aneneri anachipereka kwa amuna a m’Sunagoge Wamkulu.” M’kupita kwanthaŵi chilamulo chawo chapakamwa chinakwezedwa pamwamba pa ngakhale Chilamulo cholembedwa motere: “[Ngati] munthu achimwira mawu a Chilamulo [cholembedwa], samayenerera kupatsidwa chilango,” koma ngati “munthu awonjezera ku mawu a Alembi [miyambo yapakamwa], iye ayenerera kupatsidwa chilango.” (Mishnah) Miyambo yawo yapakamwa siinayambire pa Sinai. Kwenikweni, iyo inayamba kuwonjezeredwa mofulumira zaka mazana aŵiri Kristu asanadze. Iwo anawonjezera, kuchotsapo, ndikuthetsa mphamvu Chilamulo cholembedwa cha Mose.—Yerekezerani ndi Deuteronomo 4:2; 12:32.
16. Kodi chilungamo cha Mulungu chimabwera motani kaamba ka anthu?
16 Chilungamo cha Mulungu chimabwera osati kupyolera m’Chilamulo komatu popanda icho: ‘Chifukwa kuti pamaso pake palibe munthu adzayesedwa wolungama ndi ntchito za lamulo; pakuti uchimo udziwika ndi lamulo. Koma tsopano chilungamo cha Mulungu chaoneka chopanda lamulo, Chilamulo ndi Aneneri achitira ichi umboni; ndicho chilungamo cha Mulungu chimene chichokera mwa chikhulupiriro cha pa Yesu Kristu.’ (Aroma 3:20-22) Chotero chilungamo cha Mulungu chimabwera ndi kuika chikhulupiriro mwa Kristu Yesu—ichi ‘chinachitidwa umboni ndi Chilamulo ndi Aneneri’ bwino lomwe. Maulosi a Mesiya anakwaniritsidwa mwa Yesu. Iye anakwaniritsanso Chilamulo; chinachotsedwa m’njira mwa kukhomeredwa pamtengo wake wozunzirapo.—Luka 24:25-27, 44-46; Akolose 2:13, 14; Ahebri 10:1.
17. Mogwirizana ndi mtumwi Paulo, kodi ndimotani mmene Ayuda anaphonyera kudziŵa chilungamo cha Mulungu?
17 Motero, mtumwi Paulo analemba za kulephera kwa Ayuda kufunafuna chilungamo kuti: ‘Pakuti ndiwachitira iwo umboni kuti ali ndi changu cha kwa Mulungu, koma si monga mwa chidziwitso. Pakuti pakusadziwa chilungamo cha Mulungu, ndipo pofuna kukhazikitsa chilungamo cha iwo okha, iwo sanagonja ku chilungamo cha Mulungu. Pakuti Kristu ali chimaliziro cha lamulo kulinga kuchilungamo kwa amene aliyense akhulupira.’ (Aroma 10:2-4) Paulo analembanso motere ponena za Kristu Yesu: ‘Ameneyo sanadziwa uchimo anamyesera uchimo m’malo mwathu; kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye.’—2 Akorinto 5:21.
18. Kodi ‘Kristu wopachikidwa’ anawonedwa motani ndi akatswiri a miyambo Achiyuda, anthanthi Achigiriki, ndi “oitanidwa”?
18 Ayuda anamlingalira Mesiya yemwe anafapoyu kukhala munthu wofooka wopanda pake. Anthanthi Achigiriki anamseka Mesiya ameneyu kuti ngwopusa. Komabe, zidafanana ndi zimene Paulo analengeza kuti: ‘Popeza Ayuda afunsa zizindikiro, ndi Ahelene atsata nzeru: koma ife tilalikira Kristu wopachikidwa, kwa Ayudatu chokhumudwitsa, ndi kwa amitundu chinthu chopusa; koma kwa iwo oitanidwa, ndiwo Ayuda ndi Ahelene, Kristu mphamvu ya Mulungu, ndi nzeru ya Mulungu. Chifukwa kuti chopusa cha Mulungu chiposa anthu ndi nzeru zawo; ndipo chofoka cha Mulungu chiposa anthu ndi mphamvu yawo.’ (1 Akorinto 1:22-25) Kristu Yesu ndiye chiwonetsero cha mphamvu ndi nzeru ya Mulungu ndipo ndiye chobweretsera cha Mulungu cha chilungamo ndi moyo wosatha kwa anthu omvera. ‘Palibe chipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.’—Machitidwe 4:12.
19. Kodi nkhani yotsatira idzasonyezanji?
19 Nkhani yotsatira idzasonyeza kuti ngati titi tipulumuke chiwonongeko ndikupeza moyo wosatha, tiyenera kupitirizabe kufunafuna Ufumu wa Mulungu ndi chilungamo chake. Ichi chiyenera kuchitidwa osati mwa kumvetsera ku mawu a Yesu okha komanso mwa kuwachita.
Mafunso Akubwereramo
◻ Kodi Ayuda achipembedzo anasintha mphatso zawo zachifundo, mapemphero, ndi kusala kudya kukhala chiyani?
◻ Kodi ndikuti kumene kuli malo achisungiko okundikira chuma chanu?
◻ Kodi nchifukwa ninji tiyenera kupeŵa kudera nkhaŵa zosoŵa zathu zakuthupi?
◻ Kodi Ayuda anafotokoza chinyengo chiti ponena za chiyambi cha miyambo yawo yapakamwa?
◻ Kodi Ufumu wa Mulungu ndi chilungamo chake zimadzetsedwa ndi chiyani?
[Chithunzi patsamba 16]
Afarisi anakonda kupemphera ataimirira pa mphambano za makwalala, pomwe akakhoza kuwonedwa ndi anthu