‘M’Dzina la Mzimu Woyera’
‘Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la . . . mzimu woyera.’—MATEYU 28:19.
1. Kodi ndimawu atsopano ati amene Yohane Mbatizi anagwiritsira ntchito ponena za mzimu woyera?
M’CHAKA cha 29 cha Nyengo Yathu ino, Yohane Mbatizi anali wokangalika m’Israyeli kukonzera Mesiya njira, ndipo mkati mwa uminisitala wake, analengeza kanthu kena katsopano ponena za mzimu woyera. Ndithudi, Ayuda anali odziŵadziŵa zimene Malemba Achihebri ananena za mzimuwo. Komabe, iwo angakhale anadabwa pamene Yohane anati: ‘Inetu ndikubatizani inu ndi madzi kuloza kukutembenuka mtima; koma iye wakudza pambuyo panga, . . . adzakubatizani inu ndi mzimu woyera.’ (Mateyu 3:11) ‘Ubatizo ndi mzimu woyera’ anali mawu atsopano.
2. Kodi ndimawu atsopano ati oloŵetsamo mzimu woyera amene Yesu ananena?
2 Wakudzayo anali Yesu. M’moyo wake wapadziko lapansi, Yesu sanabatizedi aliyense ndi mzimu woyera, ngakhale kuti nthaŵi zambiri analankhuladi za mzimuwo. Ndiponso, pambuyo pa kuukitsidwa kwake, anautchula mzimu woyera m’njira inanso yatsopano. Iye anauza ophunzira ake kuti: ‘Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera.’ (Mateyu 28:19) Mawuwo “m’dzina la” amatanthauza “kuzindikira.” Ubatizo wa m’madzi wozindikira Atate, Mwana, ndi mzimu woyera unayenera kukhala wosiyana ndi ubatizo wa mzimu woyera. Unalinso lingaliro latsopano lokhudza mzimu woyera.
Kubatiza ndi Mzimu Woyera
3, 4. (a) Kodi ndiliti pamene maubatizo oyambirira ndi mzimu woyera anachitika? (b) Kuwonjezera pa kuwabatiza, kodi mzimu woyera unachitanji kwa ophunzira a Yesu pa Pentekoste wa 33 C.E.?
3 Ponena za kubatiza ndi mzimu woyera, Yesu analonjeza ophunzira ake kutatsala pang’ono kuti akwere kumwamba kuti: ‘Inu mudzabatizidwa ndi mzimu woyera asanapite masiku ambiri.’ (Machitidwe 1:5, 8) Mwamsanga pambuyo pake, lonjezolo linakwaniritsidwa. Mzimu woyera unatsikira pa ophunzira pafupifupi 120 omwe anasonkhana m’chipinda chosanja m’Yerusalemu pamene Yesu, ali kumwamba, anachita maubatizo ake oyamba ndi mzimu woyera. (Machitidwe 2:1-4, 33) Kodi panali chotulukapo chotani? Ophunzirawo anakhala mbali ya thupi lauzimu la Kristu. Monga momwe mtumwi Paulo alongosolera, ‘mwa mzimu umodzi [iwo] anabatizidwa kuloŵa m’thupi limodzi.’ (1 Akorinto 12:13) Panthaŵi imodzimodziyo, anadzozedwa kukhala mafumu ndi ansembe amtsogolo mu Ufumu wakumwamba wa Mulungu. (Aefeso 1:13, 14; 2 Timoteo 2:12; Chivumbulutso 20:6) Mzimu woyera unagwiranso ntchito monga chizindikiro ndi chikole cha choloŵacho chamtsogolo chaulemerero, koma sizinali zokhazo ayi.—2 Akorinto 1:21, 22.
4 Zaka zingapo poyambirira, Yesu anati kwa Nikodemo: ‘Ngati munthu sabadwa mwatsopano, sakhoza kuwona ufumu wa Mulungu. . . . Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi mzimu, sakhoza kuloŵa ufumu wa Mulungu.’ (Yohane 3:3, 5) Tsopano anthu okwanira 120 anabadwa mwatsopano. Kupyolera mwa mzimu woyera, analandiridwa monga ana auzimu a Mulungu, abale a Kristu. (Yohane 1:11-13; Aroma 8:14, 15) Zochita za mzimu woyera zonsezi nzapadera kuposa pakukhala zozizwitsa wamba. Ndiponso, mosiyana ndi zozizwitsa zimene zinalipo panthaŵi ina, mzimu woyera sunalekeke pambuyo pa imfa ya atumwi koma wapitirizabe kukhala wogwira ntchito mwanjirayi kufikira leroli. Uli mwaŵi wa Mboni za Yehova kukhala ndi omalizira a ziŵalo zobatizidwa ndi mzimu za thupi la Yesu pakati pawo, ndipo zimenezi zimatumikira monga “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kupereka chakudya chauzimu panthaŵi yake.—Mateyu 24:45-47.
Kubatiza “m’Dzina la . . . Mzimu Woyera”
5, 6. Kodi ndimotani mmene maubatizo oyambirira ndi mzimu woyera anatsogolerera kumaubatizo am’madzi?
5 Koma bwanji ponena za ubatizo wolonjezedwa wam’madzi m’dzina la Atate, la Mwana, ndi la mzimu woyera? Ophunzira oyambirirawo amene anabatizidwa ndi mzimu sanalandira ubatizo wam’madzi wotero. Anali atalandira kale ubatizo wam’madzi wa Yohane, ndipo popeza kuti umenewo unali wolandirika kwa Yehova panthaŵiyo, sanafunikira kubatizidwanso. Koma pa Pentekoste wa 33 C.E., khamu lalikulu la anthu linalandiradi ubatizo wam’madzi watsopanowo. Kodi zimenezi zinachitika motani?
6 Pamene okwanira 120 anabatizidwa ndi mzimu woyera panakhala phokoso lalikulu limene linakopa makamu. Anthuŵa anadabwa kumva atumwi akulankhula m’malirime, ndiko kuti, m’zinenero zachilendo zomveka kwa amene analipo. Mtumwi Petro analongosola kuti chozizwitsachi chinali umboni wakuti mzimu wa Mulungu udatsanuliridwa ndi Yesu, amene anaukitsidwa kwa akufa ndi amene tsopano alikhale kudzanja lamanja la Mulungu kumwamba. Petro analimbikitsa omvetsera ake kuti: ‘Lizindikiritse ndithu banja lirilonse la Israyeli, kuti Mulungu anamuyesa Ambuye ndi Kristu, Yesu amene inu munampachika.’ Ndiyeno anamaliza mwakunena kuti: ‘Lapani, batizidwani yense wa inu m’dzina la Yesu Kristu kuloza ku chikhululukiro cha machimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya mzimu woyera.’ Pafupifupi miyoyo 3,000 inalabadira.—Machitidwe 2:36, 38, 41.
7. Kodi obatizidwa pa Pentekoste wa 33 C.E. okwanira 3,000 anabatizidwa motani m’dzina la Atate, la Mwana, ndi la mzimu woyera?
7 Kodi tinganene kuti ameneŵa anabatizidwa m’dzina la (mwakuzindikira) Atate, Mwanayo, ndi mzimu woyera? Inde. Ngakhale kuti Petro sanawauze kubatizidwa m’dzina la Atate, iwo anali omzindikira kale Yehova monga Mfumu Ambuye, popeza kuti anali Ayuda akuthupi, ziŵalo za mtundu wodzipatulira kwa Iye. Petro ananenadi kuti: ‘Batizidwani m’dzina la Mwanayo.’ Chotero ubatizo wawo unaimira kuzindikira kwawo Yesu monga Ambuye ndi Kristu. Iwo tsopano anali ophunzira ake ndipo chifukwa cha chimenecho anavomereza kuti chikhululukiro cha machimo chinali kupyolera mwa iye. Pomalizira pake, ubatizowo unali mwakuzindikira mzimu woyera, ndipo unachitika monga kukwaniritsidwa kwa lonjezo lakuti akalandira mzimuwo monga mphatso yaulere.
8. (a) Kuwonjezera pa ubatizo wam’madzi, kodi ndiubatizo wina uti umene Akristu odzozedwa alandira? (b) Kodi ndani ena kusiyapo a 144,000 amene amalandira ubatizo wam’madzi m’dzina la mzimu woyera?
8 Awo amene anabatizidwa m’madzi patsiku la Pentekoste wa 33 C.E. anabatizidwanso ndi mzimu, kukhala odzozedwa monga mafumu ndi ansembe amtsogolo mu Ufumu wakumwamba. Malinga ndi bukhu la Chivumbulutso, ameneŵa ali okwanira chabe 144,000. Choncho obatizidwa ndi mzimu woyera ndiyeno ‘kuikidwa chizindikiro’ monga oloŵa Ufumu amapanga chiŵerengero cha 144,000 basi. (Chivumbulutso 7:4; 14:1) Komabe, ophunzira onse atsopano—mosasamala kanthu za chiyembekezo chawo—amabatizidwa m’madzi m’dzina la Atate, la Mwana, ndi la mzimu woyera. (Mateyu 28:19, 20) Pamenepa, kodi nchiyani chimene ubatizo m’dzina la mzimu woyera umatanthauza kwa Akristu onse, kaya akhale a “kagulu ka nkhosa” kapena “nkhosa zina”? (Luka 12:32; Yohane 10:16) Tisanayankhe funsolo, tiyeni tiwone zina za ntchito za mzimuwo m’nyengo ya Chikristu.
Chipatso cha Mzimuwo
9. Kodi ndintchito iti ya mzimu woyera imene iri yofunika kwa Akristu?
9 Ntchito yofunika ya mzimu woyera ndiyo kutithandiza kukulitsa maumunthu Achikristu. Zowona, chifukwa cha kupanda ungwiro sitingapeŵe kuchimwa. (Aroma 7:21-23) Koma pamene tilapa mowona mtima, Yehova amatikhululukira pamaziko a nsembe ya Kristu. (Mateyu 12:31, 32; Aroma 7:24, 25; 1 Yohane 2:1, 2) Ndiponso, Yehova amatiyembekezera kulimbana ndi chikhoterero chakuchita tchimo, ndipo mzimu woyera umatithandiza kutero. ‘Muyendeyende ndi mzimu,’ anatero Paulo, ‘ndipo musafitse chilakolako cha thupi.’ (Agalatiya 5:16) Paulo anapitiriza kusonyeza kuti mzimuwo ungabale mikhalidwe yabwino koposa mwa ife. Iye analemba kuti: ‘Chipatso cha mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso.’—Agalatiya 5:22, 23.
10. Kodi zipatso za mzimu zimakulitsidwa motani mwa Mkristu?
10 Kodi ndimotani mmene mzimuwo umabalira zipatso zotero mwa Mkristu? Sikumangochitika kokha chifukwa chakuti ndife Akristu odzipatulira ndi obatizidwa. Tiyenera kugwirirapo ntchito. Koma ngati tiyanjana ndi Akristu ena amene amasonyeza mikhalidwe imeneyi, ngati tipemphera kwa Mulungu kuti atipatse mzimu wake kutithandiza kukulitsa mikhalidwe yakutiyakuti, ngati tipeŵa mayanjano oipa ndipo tiphunzira Baibulo kuti tipeze uphungu ndi zitsanzo zabwino, pamenepo zipatso za mzimu zidzabadwa mwa ife.—Miyambo 13:20; 1 Akorinto 15:33; Agalatiya 5:24-26; Ahebri 10:24, 25.
Oikidwa ndi Mzimu Woyera
11. Kodi ndimotani mmene akulu amaikidwira ndi mzimu woyera?
11 Pamene anali kulankhula kwa akulu a ku Efeso, Paulo anatchula ntchito ina ya mzimu woyera pamene anati: ‘Tadzichenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo mzimu woyera unakuikani oyang’anira, kuti muŵete [mpingo, NW] wa Mulungu, umene anaugula ndi mwazi wa [Mwana wake, NW].’ (Machitidwe 20:28) Inde, oyang’anira mpingo, kapena akulu, amaikidwa ndi mzimu woyera. Mwanjira yotani? M’chakuti akulu oikidwa ayenera kufitsa ziyeneretso zondandalikidwa m’Baibulo lowuziridwa. (1 Timoteo 3:1-13; Tito 1:5-9) Iwo angakulitse ziyeneretso zimenezo kokha mothandizidwa ndi mzimu woyera. Ndiponso, bungwe la akulu limene lavomereza mkulu watsopano limapempherera chitsogozo cha mzimu woyera kuti lizindikire ngati iyeyo afitsa ziyeneretsozo kapena ayi. Ndipo kuikidwa kwenikweniko kumachitidwa pansi pa chitsogozo cha kapolo wokhulupirika ndi wanzeru wodzozedwa ndi mzimu.
Khalani Otsogozedwa ndi Mzimuwo
12. Kodi ndimotani mmene mzimu ungatisonkhezerere kupyolera m’Baibulo?
12 Akristu amazindikira kuti Malemba Oyera analembedwa mosonkhezeredwa ndi mzimu woyera. Chifukwa chake, iwo amawasanthula mwakuya kufunafuna nzeru yowuziridwa ndi mzimu, monga zinachitira mboni za Yehova zokhalako Chikristu chisanadze. (Miyambo 2:1-9) Iwo amawaŵerenga, kuwasinkhasinkha, ndi kuwalola kutsogoza miyoyo yawo. (Salmo 1:1-3; 2 Timoteo 3:16) Motero amathandizidwa ndi mzimuwo ‘kusanthula zakuya za Mulungu.’ (1 Akorinto 2:10, 13; 3:19) Kutsogoza atumiki a Mulungu mwanjirayi ndintchito yofunika ya m’nthaŵi yathu ya mzimu wa Mulungu.
13, 14. Kodi Yesu anagwiritsira ntchito chiyani posamalira mavuto mumpingo, ndipo kodi ndimotani mmene amachitira zofananazo lerolino?
13 Ndiponso, m’bukhu la Chivumbulutso, Yesu woukitsidwayo anatumiza mauthenga kumipingo isanu ndi iŵiri m’Asia Minor. (Chivumbulutso, mitu 2 ndi 3) M’mauthengawo iye anavumbula kuti anaifufuza mipingoyo nazindikira mkhalidwe wawo wauzimu. Anapeza kuti ina inali kupereka chitsanzo chabwino cha chikhulupiriro. M’mipingo inayo, akulu analola magaŵano, chisembwere, ndi kufunda kuipitsa gulu lankhosa. Mpingo wa ku Sarde, kusiyapo miyoyo yochepa yokhulupirika, unali wakufa mwauzimu. (Chivumbulutso 3:1, 4) Kodi Yesu anawasamalira motani mavuto ameneŵa? Ndi mzimu woyera. Popereka uphungu kumipingo isanu ndi iŵiriyo, uthenga wa Yesu uliwonse unatha ndi mawu akuti: ‘Iye wokhala nalo khutu amve chimene mzimu unena kwa mipingo.’—Chivumbulutso 2:7, 11, 17, 29; 3:6, 13, 22.
14 Lerolinonso, Yesu akuifufuza mipingo. Ndipo pamene awona mavuto, amawasamalirabe ndi mzimu woyera. Mzimuwo ungatithandize kuzindikira ndi kulaka mavuto mwachindunji kupyolera m’kuŵerenga kwathu Baibulo. Chithandizo chingadzenso kupyolera m’mabuku ofotokoza Baibulo ofalitsidwa ndi kapolo wokhulupirika ndi wanzeru wodzozedwa ndi mzimu. Kapena chingadze kuchokera kwa akulu oikidwa ndi mzimu mumpingo. Mulimonse mmene zingakhalire, kaya uphungu uli wa munthu mmodzi kapena mpingo wonse, kodi timalabadira mawu a Yesu akuti: ‘Iye wokhala nalo khutu amve chimene mzimu unena’?
Mzimuwo ndi Ntchito Yolalikira
15. Kodi mzimu unatani kwa Yesu ponena za ntchito yolalikira?
15 Pachochitika china pamene Yesu analalikira m’sunagoge ku Nazareti, anasonyezanso ntchito ina ya mzimu. Cholembedwacho chimatiuza kuti: ‘Adafunyulula bukhulo, napeza pomwe panalembedwa, Mzimu wa [Yehova, NW] uli pa ine, chifukwa chake iye anandidzoza ine ndiuze anthu osauka uthenga wabwino: Anandituma ine kulalikira am’nsinga mamasulidwe, ndi akhungu kuti apenyenso, kutulutsa ndi ufulu ophwanyika. Ndipo anayamba kunena kwa iwo, kuti, Lero lembo ili lakwanitsidwa m’makutu anu.’ (Luka 4:17, 18, 21; Yesaya 61:1, 2) Inde, Yesu anadzozedwa ndi mzimu woyera kuti alalikire mbiri yabwino.
16. M’zaka za zana loyamba, kodi ndimotani mmene mzimu woyera unaliri woloŵetsedwa kwambiri m’kulalikidwa kwa mbiri yabwino?
16 Imfa yake iri pafupi, Yesu ananeneratu za ndawala yaikulu yakulalikira yoyenera kuchitidwa ndi otsatira ake. Iye anati: ‘Uthenga wabwino uyenera uyambe kulalikidwa kwa anthu a mitundu yonse.’ (Marko 13:10) Mawu ameneŵa anali ndi kukwaniritsidwa koyamba m’zaka za zana loyamba, ndipo mbali yochitidwa ndi mzimu woyera inali yowonekera. Unali mzimu woyera umene unatsogolera Filipo kukalalikira kwa mdindo wa ku Aitiopiya. Mzimu woyera unatsogoza Petro kwa Korneliyo, ndipo mzimu woyera unalamula kuti Paulo ndi Barnaba atumizidwe monga atumwi kuchokera ku Antiokeya. Pambuyo pake, pamene Paulo anafuna kulalikira mu Asiya ndi Bituniya, mzimu woyera unamletsa mwanjira inayake. Mulungu anafuna kuti ntchito yochitira umboni ipite ku Yuropu.—Machitidwe 8:29; 10:19; 13:2; 16:6, 7.
17. Lerolino, kodi ndimotani mmene mzimu woyera uliri woloŵetsedwa m’ntchito yolalikira?
17 Lerolino, mzimu woyera ulinso woloŵetsedwa kwambiri m’ntchito yolalikira. M’kukwaniritsidwa kowonjezereka kwa Yesaya 61:1, 2, mzimu wa Yehova wadzoza abale a Yesu kuti alalikire. M’kukwaniritsidwa komalizira kwa Marko 13:10, odzozedwa ameneŵa, mothandizidwa ndi khamu lalikulu, alalikira mbiri yabwino m’lingaliro lenileni ku “mitundu yonse.” (Chivumbulutso 7:9) Ndipo mzimu umawachirikiza onsewo m’ntchitoyi. Mofanana ndi m’zaka za zana loyamba, umatsegula magawo ndi kutsogoza kupita patsogolo konse kwa ntchitoyo. Umalimbikitsa anthu aliyense payekha, kuwathandiza kugonjetsa mantha ndi kukulitsa maluso awo akuphunzitsa. Ndiponso, Yesu anauza ophunzira ake kuti: ‘Adzamuka nanu kwa akazembe ndi mafumu chifukwa cha ine, kukhala mboni ya kwa iwo, ndi kwa anthu akunja. Koma pamene paliponse angakuperekeni inu, musamadera nkhaŵa mudzalankhule bwanji kapena mudzanene chiyani; . . . pakuti wolankhula sindinu, koma mzimu wa Atate wanu ukulankhula mwa inu.’—Mateyu 10:18-20.
18, 19. Kodi mzimu umagwirizana motani ndi mkwatibwi m’kuitanira ofatsa ‘kutenga madzi a moyo kwaulere’?
18 M’bukhu la Chivumbulutso, Baibulo limagogomezeranso kuloŵetsedwamo kwa mzimu woyera m’ntchito yolalikira. M’menemo mtumwi Yohane akudziŵitsa kuti: “Mzimu ndi mkwatibwi anena, Idzani. Ndipo wakumva anene, Idzani. Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere.” (Chivumbulutso 22:17) Mkwatibwiyo, woimiriridwa ndi otsalira a 144,000 omwe adakali padziko lapansi, akuitanira onse kudzatenga madzi a moyo kwaulere. Koma tawonani, mzimu woyera nawonso ukuti “Idzani.” Mwanjira yotani?
19 Mwakuti uthenga umene ukulalikidwa ndi kagulu kamkwatibwi—kochirikizidwa lerolino ndi khamu lalikulu la nkhosa zina—ngwochokera m’Baibulo, lolembedwa pansi pa chisonkhezero chachindunji cha mzimu woyera. Ndipo mzimu umodzimodziwo watsegula mitima ndi maganizo a kagulu kamkwatibwi kuti kamvetsetse Mawu owuziridwawo ndi kuwalongosola kwa ena. Awo amene abatizidwa monga ophunzira atsopano a Yesu Kristu amasangalala kutenga madzi a moyo kwaulere. Ndipo amakondwera kugwirizana ndi mzimu ndi mkwatibwi kumati “Idzani” kwa enanso. Lerolino, oposa mamiliyoni anayi amagwira ntchito imeneyi pamodzi ndi mzimuwo.
Kukhala ndi Moyo Mogwirizana ndi Ubatizo Wathu
20, 21. Kodi ndimotani mmene tingakhalire ndi moyo mogwirizana ndi ubatizo wathu m’dzina la mzimu woyera, ndipo ndimotani mmene tiyenera kuuwonera ubatizo umenewu?
20 Kubatizidwa m’dzina la mzimu woyera ndiko chilengezo chapoyera chakuti ife timauzindikira mzimu woyera ndi kuvomereza ntchito imene umaichita m’zifuno za Yehova. Kumatanthauza kuti tidzagwirizana ndi mzimuwo, kusachita kalikonse kotsekereza kugwira ntchito kwake pa anthu a Yehova. Motero, timazindikira ndi kugwirizana ndi kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. Timagwirizana ndi kakonzedwe kakukhala ndi akulu mumpingo. (Ahebri 13:7, 17; 1 Petro 5:1-4) Timakhala ndi moyo mogwirizana ndi nzeru yauzimu, osati yakuthupi, ndipo timalola mzimuwo kuumba umunthu wathu, kuupanga kukhala wonga wa Kristu mowonjezereka. (Aroma 13:14) Ndipo timagwirizana mwamtima wonse ndi mzimu ndi mkwatibwi m’kunena kuti “Idzani” kwa mamiliyoni amene angalabadirebe.
21 Ha, ndichinthu chowopsa chotani nanga kubatizidwa ‘m’dzina la mzimu woyera’! Komabe, iko kungadzetse madalitso aakulu chotani nanga! Motero, chiŵerengero cha obatizidwa chipitirizetu kuwonjezereka. Ndipo tonsefe tipitirizetu kukhala ndi moyo mogwirizana ndi tanthauzo la ubatizo umenewo, pamene tikutumikira Yehova ndi kupitiriza kukhala ‘achangu mumzimu.’—Aroma 12:11.
Kodi Mukukumbukiranji Ponena za Mzimu Woyera?
◻ Kodi mzimu woyera unagwira ntchito motani pa Pentekoste wa 33 C.E.?
◻ Kodi ndimotani mmene tingabalire zipatso za mzimu?
◻ Kodi akulu amaikidwa ndi mzimu woyera m’njira zotani?
◻ Kodi ndimotani mmene Yesu amasamalirira mavuto mumpingo ndi mzimu woyera?
◻ Kodi ndimotani mmene mzimu uliri woloŵetsedwa kwambiri m’ntchito yolalikira?
[Chithunzi patsamba 15]
Ubatizo umene Petro analalikira unalinso m’dzina la Atate ndi la mzimu woyera
[Chithunzi patsamba 17]
Mzimu uli woloŵetsedwa kwambiri m’kulalikidwa kwa mbiri yabwino