Kuyesedwa ndi Kusefedwa mu Nthawi Zamakono
“Koma ndani adzapirira tsiku la kudza kwake? Ndipo adzaima ndani powoneka iye?—MALAKI 3:2.
1. Pamene Yehova anabwera ku kachisi wauzimu mu nthawi zamakono, kodi nchiyani chimene iye anapeza, kudzutsa funso lotani?
PAMENE “Ambuye Wowona” anafika ku kachisi wauzimu limodzi ndi “mthenga wa chipangano,” wake, mwamsanga pambuyo pa kukhazikitsidwa kwa Ufumu kumwamba mu 1914, kodi nchiyani chimene Yehova anapeza? Anthu ake anafunikira kuyengedwa ndi kuyeretsedwa. Kodi iwo akadzigonjetsera iwo eni ku ichi ndi kupirira kuyeretsedwa kofunikira kulikonse kwa gulu lawo, ntchito yawo, ziphunzitso zawo, ndi khalidwe? Monga mmene Malaki analembera icho: “Koma ndani adzapirira tsiku la kudza kwake? Ndipo adzaima ndani powoneka iye?”—Malaki 3:1, 2.
2. Mu nthawi zamakono, kodi ndani amene ali “ana a Levi” a Malaki 3:3?
2 Yehova amalandira thayo la kuyeretsa ndi kuyenga “ana a Levi.” (Malaki 3:3) Mu Israyeli wakale, pfuko la Levi linapereka zosowa za ansembe ndi othandiza pa kachisi. “Ana a Levi” amenewo amagwirizana ndi gulu lonse la odzozedwa lerolino lotumikira monga ansembe pansi pa Yesu, Wansembe Wamkulu. (1 Petro 2:7-9; Ahebri 3:1) Iwo ali amene poyamba anapita mkuyesedwa pamene Yehova anabwera ku kachisi wake wauzimu ndi “mthenga wake wa chipangano.” Tsopano, kodi ndi umboni wotani umene ulipo wakuti kuyenga kumeneku kunachitika kuyambira m’masiku omalizira a Nkhondo ya Dziko I kunka mtsogolo?
Nthawi ya Mayeso owopsya
3. Pofika mu ngululu ya 1918, kodi ndi uti womwe unali mkhalidwe wa mboni za Mulungu?
3 Pamene Yehova anapita ndi “mthenga wake wa chipangano” ku kachisi wauzimu, iye anapeza otsalira ali osowa kuyengedwa ndi kuyeretsedwa. Mwachitsanzo, Nsanja ya Olonda inalimbikitsa awerengi ake kuika pambali May 30, 1918, monga tsiku la mapemphero kaamba ka chipambano champhamvu za demokratiki, monga mmene chinafunsidwira ndi U. S. congress ndi Prezidenti Wilson. Ichi chinafikira kukuphwanya kwa uchete wa Chikristu.—Yohane 17:14, 16.
4. Kodi nchiyani chomwe chinabukapo ponena za chizunzo cha atumiki a Yehova?
4 Atsogoleri achipembedzo ndi maboma anabweretsa chitsenderezo chachikulu pa atumiki odzozedwa a Yehova. Oimbidwa mwabodza mlandu wa kupanduka, otsalira odzozedwa anayesera kupanga kukhala kwawo opanda liwongo kumvekera bwino mwapoyera. Komabe, pa May 7, 1918, zilolezo zinaperekedwa za kumanga ziwalo zisanu ndi zitatu zotsogolera ndi bungwe la mkonzi la Watch Tower Bible and Tract Society, kuphatikizapo prezidenti, J. F. Rutherford. Mlandu wawo unayamba Lolemba, June 3. Pa June 20 bwalo la milandulo linapereka chigamulo chakupezeka olakwa pa zifukwa zinayi. Kenaka pa July 4, 1918, amuna odzipereka Achikristu amenewa anatengedwa pa sitima kundende mu Atlanta, Georgia, U. S. A.
5. Kodi chinali chodziwika motani kuti panali kufunika kwa kusefa pakati pa awo amene anali kutumikira Mulungu, ndipo kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti ichi chinachitika?
5 Pofika mu chilimwe cha 1918, liwu lomwe linali poyamba lamphamvu, lolinganizidwa kulalikira poyera kaamba ka Ufumu wa Yehova la odzozedwa linachepetsedwa mokulira mu unyinji. Chinali monga ngati kuti ‘anaphedwa’ ponena za ntchito yawo yapoyera. (Chivumbulutso 11:3, 7) Panthawi ya misonkhano ya Sosaite chilimwe chimenecho, ampatuko ena anatembenuka ndi kuyambitsa timagulu tawo tawo tachipembedzo totsutsa. Kusonyeza zikhoterero za “kapolo woipa,” iwo ‘anauluzidwa’ monga “mankhusu” kuti alekanitsidwe kuchokera kwa otsalira okhulupirika a Yehova. (Mateyu 3:12; 24:48-51) Chikumbutso cha imfa ya Kristu chinakumbukiridwa pa Sande, April 13, 1919, ndi opezekapo 17, 961 mu maiko ambiri. Kuyerekezedwa ndi ripoti lochepera la 1917, chiŵerengero cha opezeka pa Chikumbutso chinatsika ndi oposa 3, 000, kusonyeza zotulukapo za kusefa.
6. Kodi ndimotani mmene kuvomereza kwa Yehova mayeso oterowo kunakhala ndi dalitso la mwamsanga la anthu ake m’chiyang’aniro?
6 Komabe, kuvomereza kwa Yehova kwa mavuto owopsya oterowo kugwera pa anthu ake linali dalitso lawo loyembekezereka mchiyang’aniro. Iye sanawasiye iwo kotheratu. Lachiŵiri, March 25, 1919, J. F. Rutherford ndi oyanjana nawo anzake asanu ndi aŵiri anamasulidwa kuchokera m’ndende kwakanthawi ndipo kenaka anapezedwa kukhala opanda liwongo kotheratu. Mwadzidzidzi, kwa opulumuka anyengo ya kuyesa imeneyi, unali utabwera ufulu kuchokera ku ukapolo! Inde, “mzimu wamoyo wochokera kwa Mulungu unawalowerera, ndipo anakhala chiliri,” okonzekera kaamba ka ntchito.—Chivumbulutso 11:11.
7. (a) Kodi nchiyani chimene mboni zobwezeretsedwa zimenezi zinachita tsopano? (b) Kodi nchiyani chimene chinatulukapo kuchokera ku kuyenga ndi kuyeretsa kumeneku?
7 Kodi nchiyani chimene iwo adzachita tsopano? Monga mudzi wobwezeretsedwanso Wachikristu, otsalira anadziyang’anitsitsa iwo eni. Iwo anapemphera kwa Yehova kaamba ka chikhululukiro kaamba ka machimo aliwonse omwe anagonjerako. (Yerekezani ndi Masalmo 106:6; Yesaya 42:24. ) Iwo anapita patsogolo monga anthu oyeretsedwa. Monga chotulukapo cha kuyengedwa, otsalira okhulupirika ‘anakhala kwa Yehova anthu opereka zopereka m’chilungamo.’ (Malaki 3:3) Nsembe zauzimu za kuyamika zimene zinaperekedwa zinakhala zokondweretsa kwa Mulungu. (Ahebri 13:15) Iwo anasangalala kuti kanthawi kochepera ka kudukiza ka kusakondwera kwa Yehova kanali katatha. Iwo anali ndi chidaliro kuti utumiki wawo wa mtsogolo udzakhala wolandiridwa kwa iye. (Yesaya 12:1) Kuyambira September 1 mpaka 8, 1919, msonkhano wachimwemwe unachitidwa pa Cedar Point, Ohio, ndi opezekapo 7, 000 ndipo 200 anabatizidwa. Izi zonse zinasonyeza kubwezeretsedwa ndi kufunitsitsa kwakukwaniritsa ntchito yolalikira ya Yehova.
8. (a) Kodi ndimotani mmene njira ya kuyenga ndi kuyeretsa imatikhudzira ife lerolino? (b) Kuwonjezera ku “ana a Levi,” amakono, kodi ndani ena amene ayenera kuyesedwa ndi kusefedwa?
8 Kodi ndimotani mmene zonsezi zimakhudzira anthu a Mulungu okhala mnthaŵi ino? Malinga ndi ulosi, Yehova, motsagana ndi mthenga wake, akabwera ndi “kukhala pansi monga woyenga ndi woyeretsa.” (Malaki 3:3) Inde, ntchito ya kuyenga ndi kuyeretsa ikapitiriza ndipo iye “akakhala pansi” ndi kuyang’anira mosamalitsa. Chenicheni chakuti otsalira okhulupirika anabwera kupyola mu nthawi ya mayeso owopsya kumayambiriro kwa zana lino sichinatanthauze kuti Woyenga Wamkulu anamaliza kuwayeretsa kwake. Kuyesa ndi kusefa kwapitirizabe mu tsiku lathu. Yehova adakali pa kachisi wake, kukhala pansi mu chiweruzo. Iye sanakhale akuyeretsa kokha “ana a Levi,” otsalira odzozedwa. Ulosi wa Malaki ukusonyeza kudera nkhawa Kwake kaamba ka “alendo,” kuchitira chithunzi “khamu lalikulu,” limene chiyembekezo chake chiri moyo padziko lapansi. (Malaki 3:5; Chivumbulutso 7:9, 10) Inde, mkati mwa zaka 69 zapita, pakhala pali kuyeretsa kopitirira kwa anthu a Yehova mu njira zinayi zodziwika.
Kuyenga kwa Gulu
9. Kodi ndi ziti zomwe ziri zotulukapo zina zopita mtsogolo mu kakonzedwe ka gulu kuyambira1919?
9 Choyamba, kuyeretsa kunachitika mwa kugwirizanitsa kopita patsogolo kwa mpingo wa dziko lonse ndi maprinsipulo Amalemba omveketsedwa chatsopano. Panayenera kukhala kuika pambali mwapang’onopang’ono kwanjira za demokratiki za kutsogozera kachitidwe kazinthu ka mpingo. Talingalirani zina za zotulukapo zopita mtsogolo mu mzera uwu.
1919: Kusankhidwa ndi Bungwe Lolamulira kunayamba mwa kuloza kuchokera ku malikulu a Watch Tower Society wotsogoza wa ntchito yautumiki wokhazikika kaambaka mpingo uliwonse woyang’anira ntchitoya utumiki wa m’munda.
11932: Kusankha kwa pachaka kwa akulu ndi madikoni kunasiyidwa; kusankha kwa mpingo kwa amuna kaamba ka mathayo amenewo kunalowedwa mmalo ndi kusankhidwa kwa komiti ya ntchito kuthandiza (ndi kuphatikizapo) wotsogoza wa ntchito wosankhidwa ndi Sosaite.
1937: Chinazindikiridwa kuti “aYonadabu” [awo amene ali ndi chiyembekezo cha padziko lapansi] angakhale ndi malo a mathayomu mpingo.
1938: Oyang’anira onse ndi owathandiza awo anayenera kusankhidwa ndi Sosaite mu njira ya teokratiki.
1972: Chinamveketsedwa bwino kuti njira ya Malemba yoyang’anira mpingo uliwonse sinayenera kokha kuchitidwa ndi Mkristu mmodzi wachikulire koma ndi bungwe la akulu, monga losankhidwa ndi Sosaite.
1975: Kukhazikitsidwa kwa makomiti a Bungwe Lolamulira kusamalira kaamba ka mathayo osiyanasiyana; palibe munthu mmodzi amene adzatsogolera zinthu, ngakhale mkati mwa komiti, koma onse adzakhala ndi liwu lofanana, ndipo onse mogwirizana adzayang’ana ku utsogoleri wa Kristu Yesu.
10. (a) Kodi nchiyani chimene chatulukapo kuchokera ku kuyenga koteroko? (b) Kodi mumamva motani ponena za makonzedwe oterowo?
10 Kodi nchiyani chimene chakhala chotulukapo cha kuwongolera kumeneku? Dalitso la Yehova mosakaikira lakhala lochuluka, monga latsimikiziridwa ndi kukula kwauzimu ndi kochuluka kwa olambira ake. (Yerekezani ndi Machitidwe 6:7; 16:5. ) Zowonadi, oyang’anira ena ndi anthu ena asefedwa chifukwa iwo mokhulupirika sanagonjere kunjira yotsogozedwa ndi Mulungu. Mokulira unyinji wa anthu a Yehova, ngakhale kuli tero, atsimikizira kukhala omvera ndi ogonjera ku kuwongoleredwa kwa gulu. (Ahebri 13:17) Iwo amayamikira kuti mwanjira ya kukonzanso koteroko Woyenga Wamkulu wabweretsa iwo m’chigwirizano chathithithi ndi njira za Malemba kaamba ka mipingo.
Utumiki wa M’munda
11. Kodi ndi njira zopita patsogolo zotani zimene ntchito yolalikira yatenga mu zaka makumiaposachedwa?
11 Chachiwiri, kuyeretsa kwatenga malo kupyolera mu kuyesa m’chigwirizano ndi kutenga mbali mu utumiki wa m’munda.
1922: Ziwalo zonse za mipingo zinafulumizidwa kugawana mu ntchito ya utumiki wa m’munda ya kunyumba ndi nyumba. Bulletin ya Mwezi ndi mwezi tsopano (Utumiki Wathu wa Ufumu) yokhala ndi zitsogozo za utumiki inakhalako.
1927: Kulalikira kwa kunyumba ndi nyumba kokhazikika pa Sande kunayamba, mabukhu ndi timabukhu anagawiridwa pa chopereka.
1937: Kabukhu koyambirira Kaphunziro Lachitsanzo kaamba ka maphunziro a Baibulo a panyumba kanalandiridwa
1939: Ndawala ya kulembetsa koyambirira kwa pachaka kwa Nsanja ya Olonda inachitika; kulembetsa kwatsopano koposa 93, 000 kunapezedwa.
1940: Ntchitoya magaziniya m, mdkhwalala inayamba.
Kulalikira kwapoyera kumeneku kunatenga mtundu wina wa kupita patsogolo, kuphatikizapo kupanga maulendo obwereza ndi kutsogoza maphunziro a Baibulo a panyumba.
12. (a) Kodi nziti zomwe zakhala zotulukapo za kuyenga kwa utumiki wa m’munda kumeneko? (b) Kodi ndimotani mmene tingachitire chitsanzo kukhulupirika kwathu mnjira imene Yehova wayengera anthu ake?
12 Kodi nchiyani chimene chakhala chotulukapo chake? Mkati mwa zaka ena akhala akusefedwa chifukwa sanali ofunitsitsa kukhala Akristu obala zipatso. (Yohane 15:5) Koma mwachidziŵikire unyinji wa anthu a Yehova avomereza ku kuitana kaamba ka alaliki a Ufumu. Nkulekelanji, popeza gulu laling’ono limenelo losakwanira 8, 000 kumbuyoku mu 1919 linakula kufika ku chiwerengero chapamwamba cha ofalitaa a Ufumu 3, 229, 022 mu 1986! Bwanji ponena za utumiki wanthawi zonse? Kuyerekezedwa ndi makopyutala (apainiya) achangu 150 mu ngululu ya 1919, chaka chatha chinawona avereji ya ofalitsa a chipainiya achangu oposa 391, 000 mwezi uliwonse—chiwerengero chapamwamba kwambiri mu mibiri ya Mboni za Yehova za makono! Mwa kukhala ndi kugawana kokangalika mu ntchito yolalikira mbiri yabwino, timachitira chitsanzo chilikizo lathu lokhulupirika lanjira mu imene Yehova wapitirizira kuyeretsera anthu ake.—1 Akorinto 9:16.
Kuwala Kowonjezereka
13. Kodi ndi ziti zomwe ziri zitsanzo za mmene Yehova waunikira anthu ake?
13 Chachitatu, kuyeretsa kunawoneka pamene anthu a Mulungu anayesedwa ponena za kulandira kuunikira kwauzimu kopita patsogolo kuchokera mu Baibulo. (Miyambo 4: 18) Kuyambira 1919 kufikira tsopano chowonadi chomveketsedwa kumene chakhala chikusefukira.
1925: Chinazindikiridwa momvekera bwino kuti pali magulu awiri odziwika bwino ndi otsutsana—la Yehova ndi la Satana.
1931: Dzina latsopano lakuti Mboni za Yehova linatengedwa.
1935: “Khamu lalikulu” la pa Chivumbulutso 7:9-15 linazindikiridwa monga gulu lokhala ndi chiyembekezo cha padzikolapansi.
1941: Kuyenera kwa ulamuliro wa dziko lonse kwa Yehova kunasonyezedwa kukhala nkhani yoyambirira yodzutsidwa ndi chitokoso cha Satana.
1962: “Maulamuliro a akulu” a Aroma 13:1 moyenerera anadziwikitsidwa kukhala maulamuliro a boma a dziko, kwa amene Akristu ayenera kugonjera.
1986: Chinayamikiridwa kuti ponse paŵiri otsalira ndi “khamu lalikulu” ayenera mophiphiritsira kudya thupi ndi mwazi wa Yesu mwakulandira nsembe yake ndi cholinga chofuna kukhala m’chigwirizano ndi iye.—Yohane 6:53-56.
Mkati mwa zaka makumi angapo, pamene Yehova akuunikira anthu ake, chinakhala chomvekera bwino kuti panali kufunika kaamba ka chisamaliro cha mpingo ku kusunga gulu loyera, lachete lomwe limalemekeza kupatulika kwa mwazi.—1 Akorinto 5:11-13; Yohane 17:14, 16; Machitidwe 15:28,29.
14. (a) Kodi ndimotani mmene anthu a Yehova avomerezera kuunikira kopita patsogolo kumeneko? (b) Kodi nchiyani chomwe chiri chigamulo chanu chaumwini ponena za njira ya kulankhulira ya Yehova?
14 Kodi ndimotani mmene anthu a Mulungu avomerezera ku kuunikiridwa kopita patsogolo koteroko? Ku nthawi zonse, pakhala ochepa omwe sakanalandira makonzedwe ena ake. Amenewa ‘anaulutsidwa.’ (Mateyu 3:12) Kumbali ina, ali achimwemwe chotani nanga atumiki okhulupirika a Yehova kaamba ka kuunikira kwauzimu kumeneko! Panthawi imene Dziko la chipembedzo likudzandira mumdimba wauzimu, njira ya anthu a Yehova imankabe niiwala. Kodi sitiyenera kukhala olimba mtima kumamatira kufupi ndi njira ya kulankhulana imene Yehova akuigwiritsira ntchito, kulandira kuunikira kopita mtsogolo koteroko monga “chakudya pa nthawi yake”?—Mateyu 24:45.
Kuchotsa Machitachita Oipa
15. Kodi ndimotani mmene Yehova mopita patsogolo wayengera anthu ake ponena za makhalidwe oipa kapena machitachita a Chibabulo?
15 Chachinayi, kuyeretsa kunachitika pamene chinakhala chalamulo kuchotsa zonya nsa kapena machitachita a Chibabulo. Mu ma-1920 anthu a Mulungu analeka kukondwerera Krisimasi ndi masiku atchuthi ena amene anasonyezedwa kukhala achiyambi cha chikunja. Mu 1945 kaimidwe ka Chikristu ka kupereka mwazi kanalongosoledwa. Mkat mwa ma-1960 ndi ma-1970, pamene mkhalidwe wa makhalidwe a mdziko unapitirira kuipabe, Nsanja ya Olonda inapitiriza kupereka uphungu wa chindunji kaamba ka anthu a Mulungu pankhani zonga ngati khalidwe labwino pakati pa anthu osiyana ziwalo ndi kufunika kwa kukhala omasuka ku fodya ndi mankhwala ena.
16. Kodi ndimotani mmene makonzedwe oterowo ponena za machitachita oipa ayenera kuwonedwera?
16 Komabe, makonzedwe oterowo okhudza machitachita oipa nthawi zonse anatumikira monga chiyeso cha kukhulupirika kwa anthu a Mulungu. Komabe, awo amene anapanga masinthidwe oyenerera ayang’ana pa kusintha koteroko monga thandizo mkuchotsa chovala choipa. (Akolose 3:9, 10) Iwo anazindikira kuti ngakhale kuti miyambo yogwirizana ndi masiku a matchuthi ena inawoneka kukhala yosaphula ngozi, kanali kayang’anidwe ka Yehova kamene kayenera kutidetsa nkhawa; iye anawona poyamba machitachita a chipembedzo akunja kuchokera ku amene izi zinachokera. Kunena za chifuno cha makhalidwe abwino a Mulungu, iwo anawona izo monga chilikizo osati chiletso, chotero iwo anadalitsidwa ndi Yehova kaamba kakukhala oyera. Ngati kakonzedwe kanawoneka kukhala kovuta kukamvetsetsa, iwo anadalira kuti Yehova anali ‘kutiphunzitsa ife kupindula.’—Yesaya 48:17.
17, 18. (a) Kodi ndimotani mmene ife aliyense payekha tikuyesedwera ndi Woyenga Wamkulu? (b) Kodi nchiyani chimene chiyenera kukhala chigamulo chathu pamene tikudikira tsiku la Yehova?
17 Chaka ndi chaka Yehova akupitirizabe kuyenga ndi kuyeretsa anthu ake. Onse pamodzi, iwo adzigonjetsera iwo eni ku njira ya kuyenga kulinga ku gulu lawo, ntchito zawo, ziphunzitso zawo, ndi khalidwe loyera. Koma bwanji ponena za ife monga aliyense payekha? Kupyolera mu gulu lake Yehova akupitiriza kugawira “chakudya chotafuna” kaamba ka chitsogozo chomwe chimayenga mtima. Malingaliro athu amayesedwa ndi kusanthulidwa. (Ahebri 4:12; 5:14) Mwakuvomereza kunjira ya kuyenga, kuyeretsa kwa Woyenga Wamkulu, timakhala oyera pamene tikudikira “kubwera kwa tsiku lalikulu ndi lowopsya la Yehova.”—Malaki 4:5.
18 Chiyamikiro chikhale kwa Yehova, “Mbuye wowona,” ndi “mthenga wa chipangano” wake, Yesu Kristu, amene amatiyenga ife ndikutipulumutsa kuchokera ku zonyansa mu nthawi ino ya kuyesa ndi kusefa. Tiyeni tonse tikhale olimba mtima kupitiriza kuyenda mu njira zoyera za Yehova za mtendere pansi pa “Kalonga wa Mtendere,” Kristu Yesu, ndipo chotero kusunga unansi wanthu wachimwemwe ndi Yehova.—Yesaya 9:6; Masalmo 72:7.
Kodi Ndimotani Mmene Yehova Wayengera Anthu Ake Ponena Za—
◻ Kuwongolera kwa gulu?
◻ Kutenga mbali mu utumiki wa m’munda?
◻ Kulandira kuunikiridwa kopita mtsogolo?
◻ Kuchotsa machitachita oipa?
[Mawu Otsindika patsamba 16]
Monga chotulukapo cha kuyeretsedwa ndi kuyengedwa, otsalira okhulupirika ‘anakhala kwa Yehova anthu opereka zopereka m’chilungamo
[[Mawu Otsindika patsamba 19]
Chaka ndi chaka Yehova amapitiriza kuyenga ndi kuyeretsa anthu ake
[Chithunzi patsamba 17]
Woyenga wamakedzana anachotsa zoipa, kapena mphala. Mofananamo, Yehova amalola kuyesedwa ndi kusefedwa kuyenga anthu ake
[Chithunzi patsamba 18]
Ochepera ‘auluzidwa’ monga “mankhusu,” koma atumiki okhulupirika a Yehova m wachimwemwe amalandira kuunikira kopita mtsogolo kwauzimu
[Mawu a Chithunzi]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est