Muzichitira Anthu Zimene Mungafune Kuti Akuchitireni
“Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zomwezo.”—MAT. 7:12.
1. (a) Fotokozani zinthu zosangalatsa zimene zinachitika ku Fiji. (b) Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? (Onani chithunzi pamwambapa.)
ZAKA zingapo zapitazo banja lina ku Fiji limaitanira anthu ku Chikumbutso cha imfa ya Khristu. Ndiyeno akulankhula ndi mayi wina, mvula inayamba kugwa. M’baleyo anapereka ambulera imodzi kwa mayiyo, iye ndi mkazi wake n’kufunda ina. Banjali linasangalala kuona mayiyo atafika pa Chikumbutso. Iye ananena kuti sankakumbukira bwinobwino zimene banjali linamufotokozera pomuitana. Koma analolera kupita ku Chikumbutsocho chifukwa choti anasangalala ndi zimene banjalo linamuchitira pokambirana naye. Kodi zonsezi zinatheka bwanji? Zinatheka chifukwa chakuti banjalo linatsatira mfundo ina yofunika kwambiri imene Yesu anatchula.
2. (a) Tchulani mfundo yofunika kwambiri imene Yesu ananena. (b) Kodi tingatsatire bwanji mfundoyi?
2 Kodi mfundo yofunika imene Yesu anatchulayo ndi iti? Ndi yakuti: “Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zomwezo.” (Mat. 7:12) Kodi tingatsatire bwanji mfundo imeneyi? Pali zinthu ziwiri zimene tiyenera kuchita. Choyamba, tiyenera kudzifunsa kuti: “Kodi ineyo ndikanakhala munthuyo, ndikanafuna kuti anthu andichitire zotani?” Chachiwiri, tiyenera kuyesetsa kuchitira munthuyo zimene ifeyo tikanafuna kuchitiridwazo.—1 Akor. 10:24.
3, 4. (a) Kodi tiyenera kutsatira mfundo imene Yesu ananena tikamachita zinthu ndi Akhristu okha? Fotokozani. (b) Kodi tikambirana chiyani m’nkhani ino?
3 Nthawi zambiri, timatsatira mfundo imene Yesu anatchulayi pochita zinthu ndi Akhristu anzathu. Koma Yesu sananene kuti tizingoitsatira pochita zinthu ndi okhulupirira anzathu okha. Iye anatchula mfundoyi ponena mmene tiyenera kuchitira zinthu ndi munthu aliyense ngakhale amene amadana nafe. (Werengani Luka 6:27, 28, 31, 35.) Ndiye funso n’kumati, ‘Ngati tiyenera kutsatira mfundoyi pochita zinthu ndi anthu amene amadana nafe, kuli bwanji anthu amene timawalalikira? Pajatu ambiri amene timawalalikira akhoza kukhala ndi ‘maganizo abwino amene angawathandize kukapeza moyo wosatha.’—Mac. 13:48.
4 M’nkhani ino, tikambirana mafunso anayi amene tiyenera kudzifunsa tikamalalikira. Mafunso ake ndi awa: Kodi munthu amene ndilankhule naye ndi wotani? Kodi ndizichita chiyani ndikafika panyumba ya munthu? Kodi ndizilalikira pa nthawi iti? Nanga ndiziyamba bwanji kulankhula ndi anthu? Kudzifunsa mafunso amenewa kungathandize kuti tizitha kusintha n’cholinga choti tizichita zinthu moganizira munthu aliyense amene tikumulalikira.—1 Akor. 9:19-23.
KODI MUNTHU AMENE NDILANKHULE NAYE NDI WOTANI?
5. Kodi tingachite bwino kudzifunsa mafunso ati tisanayambe kukambirana ndi munthu?
5 Anthu amene timawalalikira amakhala osiyanasiyana ndipo mavuto awo amakhalanso osiyana. (2 Mbiri 6:29) Choncho tisanayambe kukambirana ndi munthu, tiyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndikanakhala munthuyu ndikanafuna kuti ndizionedwa bwanji? Kodi ndikanasangalala atamangonditenga ngati munthu winawake wokhala m’deralo kapena atasonyeza kuti akufuna kundidziwa bwinobwino?’ Kudzifunsa mafunso ngati amenewa kungatithandize kuti tizichita zinthu moganizira munthu aliyense payekha.
6, 7. Kodi tiyenera kutani ngati munthu wina watikwiyira mu utumiki?
6 Palibe munthu amene amafuna kunenedwa kuti ndi wovuta. Mwachitsanzo: Akhristufe timayesetsa kutsatira malangizo a m’Baibulo akuti ‘mawu athu azikhala achisomo.’ (Akol. 4:6) Koma poti ndife opanda ungwiro, nthawi zina timalankhula zolakwika ndipo timamva nazo chisoni. (Yak. 3:2) Ndiyeno tikalakwitsa choncho, mwina chifukwa choti sitinadzuke bwino pa tsikulo, timafunabe kuti anthu azitimvetsa. Sitifuna kunenedwa kuti ndife amwano kapena osaganizira anzathu. Kodi nafenso sitiyenera kuwamvetsa anthu amene sanatilankhule bwino?
7 Munthu wina akatikwiyira mu utumiki, sitiyenera kuweruziratu kuti ndi wokanika. Mwinatu pa nthawiyo wangopanikizika ndi zinthu zina zakuntchito kapena zakusukulu. N’kuthekanso kuti akuvutika ndi matenda enaake. Nthawi zambiri anthu amene amaoneka ovuta pa ulendo woyamba, amasintha ngati Akhristu amene akulalikirawo atawayankha mofatsa komanso mwaulemu.—Miy. 15:1; 1 Pet. 3:15.
8. N’chifukwa chiyani tiyenera kulalikira uthenga wa Ufumu mopanda tsankho kwa “anthu osiyanasiyana”?
8 Polalikira timakumana ndi anthu osiyanasiyana. Mwachitsanzo, m’zaka za posachedwapa, m’magazini a Nsanja ya Olonda mwatuluka nkhani za anthu oposa 60 za mutu wakuti “Baibulo Limasintha Anthu.” Ena mwa anthu ofotokozedwa m’nkhani zimenezi anali akuba, achiwerewere, zidakwa, zigawenga kapena ogwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Ena anali andale kapena atsogoleri achipembedzo ndipo ena ankakonda kwambiri ntchito zawo zapamwamba. Koma onsewa atamva uthenga wabwino, anavomera kuphunzira Baibulo ndipo anasintha moyo wawo n’kukhala Mboni za Yehova. Choncho si bwino kuganiza kuti anthu ena sangasinthe n’kuyamba kumvetsera uthenga wa Ufumu. (Werengani 1 Akorinto 6:9-11.) M’malomwake, tizidziwa kuti “anthu osiyanasiyana” akhoza kusintha pambuyo pomva uthenga wabwino.—1 Akor. 9:22.
KODI NDIZICHITA CHIYANI NDIKAFIKA PANYUMBA YA MUNTHU?
9. N’chifukwa chiyani tiyenera kufika mwaulemu kunyumba za anthu?
9 Anthu ambiri timawalalikira kunyumba kwawo. (Mat. 10:11-13) Ndiyeno kodi ifeyo timafuna kuti anthu azichita chiyani akafika kunyumba kwathu? Timafuna kuti azifika mwaulemu komanso asamachite zinthu zokayikitsa. Ndiyetu tikakhala mu utumiki, ndi bwino kuganizira zimene timachita tikafika panyumba ya munthu wina. Nafenso tiyenera kufika mwaulemu komanso kupewa kuchita zinthu zokayikitsa.—Mac. 5:42.
10. Kodi tingapewe bwanji kukhumudwitsa anthu mu utumiki?
10 Masiku ano, dzikoli laipa kwambiri ndipo anthu ambiri amakayikira aliyense amene wangotulukira kunyumba kwawo. (2 Tim. 3:1-5) N’chifukwa chake tiyenera kupewa kuchita zinthu zokayikitsa tikafika pakhomo la munthu. Tiyerekeze kuti tafika pakhomo n’kuodira kapena kugogoda koma palibe amene akuyankha. Kodi timayamba kusuzumira m’mawindo kapena kuzungulirazungulira panyumbayo kuti tipeze mwiniwake? Kodi zimenezi sizingasokoneze mwininyumbayo? Nanga anthu apafupi atationa tikuchita zimenezi, kodi angaganize zotani? N’zoona kuti tiyenera kuyesetsa kupeza anthu kuti tiwalalikire. (Mac. 10:42) Komanso cholinga chathu n’chakuti anthu amve uthenga wabwino kwambiri. (Aroma 1:14, 15) Ngakhale zili choncho, tiyenera kupewa kuchita zinthu zimene zingasokoneze kapena kukhumudwitsa anthu m’dera lathu. Paja mtumwi Paulo analemba kuti: “Sitikuchita chilichonse chokhumudwitsa, kuti utumiki wathu usapezedwe chifukwa.” (2 Akor. 6:3) Kufika mwaulemu panyumba za anthu kungathandize kuti anthuwo ayambe kuphunzira Baibulo.—Werengani 1 Petulo 2:12.
KODI NDIZILALIKIRA PA NTHAWI ITI?
11. N’chifukwa chiyani timafuna kuti anthu ena azitiganizira n’kumapewa kutitayitsa nthawi?
11 Akhristu ambirife timakhala otanganidwa kwambiri. Choncho kuti tikwanitse kuchita zinthu bwinobwino timafunika kuona kuti zofunika kwambiri ndi ziti ndiponso kukonza ndandanda yabwino. (Aef. 5:16; Afil. 1:10) Ndiyeno chinachake chikasokoneza mapulani athu, sitimva bwino. Choncho timasangalala ngati anthu ena amasonyeza kutiganizira popewa kutisokonezera mapulani kapena kutitayitsa nthawi. Ndiyeno kodi tingatsatire bwanji malangizo a Yesu a pa Mateyu 7:12 tikakhala mu utumiki?
12. Kodi tingadziwe bwanji nthawi yabwino yolalikira?
12 Malinga ndi zimene takambiranazi, ndi bwino kuganizira nthawi imene timalalikira. Kodi anthu amakonda kupezeka kunyumba kwawo pa nthawi iti? Nanga ndi nthawi iti imene angatilandire bwino? Tikapeza mayankho a mafunsowa, tingachite bwino kusintha ndandanda yathu kuti igwirizane ndi zimenezozo. M’madera ena, ntchito yathu yolalikira imayenda bwino madzulo chifukwa chakuti ndi nthawi imene anthu ambiri amapezeka panyumba. Ngati umu ndi mmene zilili kwanuko, kodi mungasinthe ndandanda yanu kuti nthawi zina muzilalikira madzulo? (Werengani 1 Akorinto 10:24.) Yehova adzatidalitsa kwambiri ngati tisintha zinthu kuti tizilalikira pa nthawi imene anthu ambiri m’dera lathu angamvetsere uthenga wa Ufumu.
13. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza anthu amene tikuwalalikira?
13 Kodi pali zinanso zimene tingachite posonyeza kuti timalemekeza anthu? Ee zilipo. Mwachitsanzo, ngati munthu watilandira bwino panyumba yake, tiyenera kumulalikira mogwira mtima koma si bwino kuchedwapo kwambiri. N’kutheka kuti pali zinthu zina zimene munthuyo akufuna kuchita, zomwenso ndi zofunika kwa iyeyo. Ngati munthu watiuza kuti alibe mpata, ndiyeno tamupempha kuti tingolankhula naye mwachidule, tizilankhuladi mwachidule. (Mat. 5:37) Posiyana ndi munthuyo, tingamufunse nthawi yabwino imene tingabwerereko. Abale ndi alongo ena amakonda kuuza anthu kuti: “Ndidzabweranso tsiku lina kuti tidzakambirane. Kodi mungakonde kundipatsa nambala yanu kuti ndidzakuimbireni foni kapena kukutumizirani meseji ndisanafike?” Tikamasintha ndandanda yathu kuti igwirizane ndi nthawi imene anthu ambiri angatilandire ndiye kuti tikutengera chitsanzo cha Paulo. Iye anati: “Sikuti ndikungofuna zopindulitsa ine ndekha ayi, koma zopindulitsa anthu ambiri, kuti apulumutsidwe.”—1 Akor. 10:33.
KODI NDIZIYAMBA BWANJI KULANKHULA NDI ANTHU?
14-16. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kufotokoza cholinga chathu tikafika panyumba ya munthu? Perekani chitsanzo. (b) Kodi woyang’anira woyendayenda wina amayamba bwanji kukambirana ndi anthu?
14 Tayerekezani kuti tsiku lina mwalandira foni koma munthu amene waimbayo simukumudziwa. Ndiyeno munthuyo wayamba kukufunsani kuti, “Kodi mumakonda chakudya cha mtundu wanji?” Mukhoza kudabwatu eti? Komabe mwina chifukwa cha ulemu, mungakambirane naye mwachidule kenako n’kumusonyeza kuti simukufuna kucheza naye. Koma mungamve bwanji ngati munthuyo atayamba watchula dzina lake, kenako n’kunena kuti amagwira ntchito yothandiza anthu kudya zamagulu ndipo ali ndi malangizo othandiza? Apatu simungamukayikire ndipo mukhoza kucheza naye. Kunena zoona timafuna kuti anthu anene kaye zolinga zawo komanso azilankhula nafe mwaulemu. Kodi tingachite bwanji zimenezi mu utumiki?
15 M’madera ambiri, zimakhala bwino ngati tayamba ndi kutchula dzina lathu komanso kufotokoza cholinga chathu momveka bwino. N’zoona kuti timakhala ndi uthenga wofunika kwambiri kwa munthuyo. Koma kodi munthu angamve bwanji ngati titangofikira kumufunsa funso? Mwina kungoti: “Mukanakhala ndi mphamvu yothetsa vuto lililonse m’dzikoli, kodi ndi vuto liti limene mukanalithetsa?” Tingafunse funsoli pofuna kumva maganizo ake kuti tikambirane zimene Baibulo limanena. Komatu mwininyumbayo angakhale akudzifunsa kuti: ‘Kodi munthu ameneyu ndi ndani? N’chifukwa chiyani akundifunsa zimenezi? Kwenikweni akufuna chiyani?’ Choncho ndi bwino kuyamba ndi mawu amene angamukhazike mtima pansi. (Afil. 2:3, 4) Kodi tingachite bwanji zimenezi?
16 Woyang’anira woyendayenda wina anatulukira njira imene imamuthandiza kuchita zimenezi. Iye amayamba wapereka moni, kenako amapereka kapepala kakuti Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi? Ndiyeno amanena kuti: “Lero tikugawira anthu onse m’derali kapepala aka. Kali ndi mafunso 6 amene anthu amadzifunsa. Inu kanu ndi aka.” M’baleyu ananena kuti anthu ambiri amamasuka akadziwa chifukwa chimene tafikira panyumba pawo. Zikatero, nthawi zambiri sizivuta kukambirana mfundo zina. Kenako m’baleyu amafunsa kuti: “Kodi papepalalo pali funso limene munadzifunsapo?” Ndiyeno akasankha funso limodzi, m’baleyo amatsegula kapepalako n’kukambirana naye zimene Baibulo limanena pa nkhaniyo. Koma munthuyo akavutika kusankha, amangosankha yekha funso limodzi n’kuyamba kukambirana naye. Kunena zoona, tikhoza kuyamba kukambirana ndi anthu m’njira zambiri. M’madera ena anthu amafuna kuti timasukirane n’kucheza nkhani zingapo tisanatchule cholinga cha ulendo wathu. Choncho mfundo ndi yakuti tiziyesetsa kukambirana ndi anthu mogwirizana ndi zimene iwowo angafune.
PITIRIZANI KUCHITIRA ANTHU ZIMENE MUNGAFUNE KUTI AKUCHITIRENI
17. Malinga ndi zimene takambirana m’nkhaniyi, kodi tingatsatire bwanji mfundo ya Yesu ija?
17 M’nkhaniyi, taona zimene tiyenera kuchita mu utumiki potsatira mfundo imene Yesu anatchula ija. Choyamba, tizimudziwa bwino munthu amene tikukambirana naye. Chachiwiri, tizifika panyumba za anthu mwaulemu. Chachitatu, tizipita kunyumba za anthu pa nthawi imene angapezeke komanso kutilandira bwino. Ndipo chomaliza, tiziyamba kukambirana ndi anthu m’njira imene iwowo angafune.
18. Kodi chimachitika n’chiyani ngati tichitira anthu zimene ifeyo tingafune kuti atichitire?
18 Zinthu zimayenda bwino kwambiri tikamachitira anthu zimene ifeyo tingafune kuti atichitire. Tikamachita zinthu moganizira ena, timasonyeza kuti mfundo za m’Malemba zimene timatsatira ndi zothandiza kwambiri komanso timalemekeza Atate wathu wakumwamba. (Mat. 5:16) Zimene timachita pofikira anthu mu utumiki zingathandize kuti anthuwo ayambe kuphunzira Baibulo. (1 Tim. 4:16) Kaya anthuwo amvetsera kapena ayi, timasangalala podziwa kuti tachita zonse zimene tingathe pokwaniritsa utumiki wathu. (2 Tim. 4:5) Tiyeni tonse tizitsanzira mtumwi Paulo amene analemba kuti: “Ndikuchita zinthu zonse chifukwa cha uthenga wabwino, kuti ndiugawirenso kwa ena.” (1 Akor. 9:23) Choncho tikamalalikira, tiyeni tipitirize kuchitira anthu zimene tingafune kuti atichitire.