Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Njira ya ku Moyo
NJIRA ya ku moyo ndiyo kulabadira ziphunzitso za Yesu. Koma zimenezi siziri zosavuta kuzichita. Mwachitsanzo, Afarisi, anali ndi chikhoterero cha kuweruza ena mwankhalwe, ndipo mwachiwonekere ambiri amawatsanzira. Chotero pamene Yesu akupitirizabe Ulaliki wake wa pa Phiri, akupereka malangizo awa: “Musaweruze, kuti mungaweruzidwe. Pakuti ndikuweruza kumene muweruza nako, inunso mudzaweruzidwa.”
Kuli kwaupandu kulondola chitsanzo cha Afarisi osuliza kwambiriwo. Mogwirizana ndi kunena kwa cholembedwa cha Luka, Yesu akufotokoza mwafanizo ngozi imeneyi mwa kunena kuti: “Kodi munthu wakhungu angathe kutsogolera mnzake wakhungu? Kodi sadzagwa onse awiri m’mbuna?“
Kusuliza ena mopambanitsa, kukulitsa zolakwa zawo ndi malovu ndi kuzilondalonda, ndiko liwongo lalikulu. Chotero Yesu akufunsa kuti: “Udzati bwanji kwa mbale wako, Tandilola ndichotse kachitsotso m’diso lako; ndipo wona, mtandawo ulimo m’diso lakoli? Wonyenga iwe!Tayamba kuchotsa m’diso lako mtandawo, ndipo pomwepo udzapenyetsa kuchotsa kachitsotso m’diso la mbale wako.”
Zimenezi sizitanthauza kuti ophunzira a Yesu sakagwiritsira ntchito luntha konse pochita ndi anthu ena, pakuti iye akuti: “Musamapatsa chopatulikacho kwa agalu, ndipo musamaponya ngale zanu patsogolo pa nkhumba.” Chowonadi chochokera m’Mawu a Mulungu nchopatulika. Chiri chofanana ndi ngale zophiphiritsira. Koma ngati anthu ena, amene ali mofanana ndi agalu kapena nkhumba, sasonyeza chiyamikiro kaamba ka chowonadi chamtengo wapatali chimenechi, ophunzira a Yesu ayenera kusiya anthu amenewo ndi kukafunafuna anthu omvetsera amene ali olabadira kwambiri.
Ngakhale kuti Yesu wafotokoza pemphero kuchiyambiyambi kwa ulaliki wake, iye tsopano akugogomezera kufunika kwa kuchitamo khama. ‘Pitirizani kupempha,’ iye akulimbikitsa, ‘ndipo chidzapatsidwa kwa inu (NW).’ Kufotokoza mwafanizo kufunitsitsa kwa Mulungu kuyankha mapemphero, Yesu akufunsa kuti: “Munthu ndani wa inu, amene pompempha mwana wake mkate, adzampatsa mwala?. . . chomwecho, ngati inu muli oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kopambana kotani nanga Atate wanu wakumwamba adzapatsa zinthu zabwino kwa iwo akumpempha iye?“
Kenako Yesu akupereka limene lafikira kukhala lamulo lotchuka la makhalidwe abwino, lodziwika kwambiri monga Lamulo la Makhalidwe Amtima Abwino. lye akuti: Chifukwa chake zinthu zirizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero.”Kukhala ndi moyo mogwirizana ndi lamulo limeneli kumaphatikizapo kuchita motsimikizira pochitira ena zabwino, kuwachitira iwo monga momwe inu mumafuna kuchitiridwa.
Kuti Njira ya ku moyo siiri yosavuta kwavumbulutsidwa ndi chilangizo cha Yesu chakuti: “Lowani pa chipata chopapatiza; chifukwa chipata chiri chachikulu, ndi njira ya kumuka nayo kukuwonongeka iri yotakata; ndipo ali ambiri amene alowa pa icho. Pakuti chipata chiri chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo ya kumuka nayo ku moyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali owerengeka.”
Upandu wa kusochezedwa ngwaukulu, chotero Yesu akuchenjeza kuti: “Yang’a nirani mupewe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zovala zankhosa, koma mkati mwawo ali afisi olusa.” Monga momwedi mitengo yabwino ndi mitengo yoipa ingadziwike ndi zipatso zake, Yesu akulongosola kuti, aneneri onyenga angadziwike mwakhalidwe lawo ndi ziphunzitso.
Kupitirizabe, Yesu akulongosola kuti siziri kokha zimene munthuyo amanena zimene zimampangitsa kukhala wophunzira Wake koma zimene achita. Anthu amanena kuti Yesu ndiye Ambuye wawo, koma ngati iwo sakuchita chifuniro cha Atate wake, iye akuti: “Ndidzafukulira iwo, Sindinakudziwani inu nthawi zonse; chokani kwa ine, inu akuchita kusayeruzika.”
Potsirizira pake, Yesu akupereka mapeto osaiwalika ku ulaliki wake, lye akuti: “Yense amene akamva mawu anga amenewa, ndi kuwachita, ndidzamfanizira iye ndi munthu wochenjera, amene anamanga nyumba yake pathanthwe; ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinawomba mphepo, zinagunda panyumbayo; koma sinagwa; chifukwa inakhazikika pathanthwepo.”
Kumbali ina, Yesu akulengeza kuti: ‘‘Yense akamva mawu anga amenewa, ndi kusawachita, adzafanizidwa ndi munthu wopusa, yemwe anamanga nyumba yake pamchenga; ndipo inagwa mvula nidzala mitsinje, ndipo zinawomba mphepo, zinagunda panyumbayo; ndipo inagwa; ndi kugwa kwake kunali kwakukulu.”
Pamene Yesu amaliza ulaliki wake, khamulo likuchita chidwi ndi kaphunzitsidwe kake, pakuti akuwaphunzitsa monga munthu waulamuliro ndipo osati monga atsogoleri awo achipembedzo. Mateyu 7:1-29; Luka 6:27-49.
◆ Kodi Yesu akunenanji ponena za kuweruza ena; komabe iye anasonyeza motani kuti ophunzira ake anafunikira kugwiritsira ntchito luntha ponena za anthu?
◆ Kodi Yesu akunenanso chiyani ponena za pemphero, ndipo ndilamulo lotani la khalidwe limene akupereka?
◆ Kodi Yesu akusonyeza motani kuti njira ya kumoyo siikakhala yosavuta ndi kuti pali ngozi ya kusochezedwa?
◆ Kodi Yesu akumaliza motani ulaliki wake, ndipo nchiyambukiro chotani chimene ukukhala nacho?