NKHANI YOPHUNZIRA 51
Pitirizani ‘Kumumvera’
“Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndikukondwera naye, muzimumvera.”—MAT. 17:5.
NYIMBO NA. 54 “Njira Ndi Iyi”
ZIMENE TIPHUNZIREa
1-2. (a) Kodi atumwi atatu a Yesu analamulidwa kuchita chiyani, nanga iwo anatani? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?
PAMBUYO pa pasika wa mu 32 C.E., mtumwi Petulo, Yakobo ndi Yohane, anaona masomphenya ochititsa chidwi. Iwo anali paphiri, mwina mbali ina ya phiri la Herimoni pomwe Yesu anasandulika pamaso pawo. “Nkhope yake inawala ngati dzuwa. Malaya ake akunja anawala kwambiri.” (Mat. 17:1-4) Chakumapeto kwa masomphenyawo atumwi anamva Mulungu akunena kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndikukondwera naye, muzimumvera.” (Mat. 17:5) Zimene atumwiwa anachita pa moyo wawo zimasonyeza kuti ankamvera Yesu. Choncho timafunitsitsa kutengera chitsanzo chawo.
2 Munkhani yapita ija tinaphunzira kuti kumvera mawu a Yesu kumatanthauza kusiya kuchita zinthu zina. Munkhaniyi tikambirana zinthu ziwiri zimene Yesu ananena kuti tizichita.
“LOWANI PACHIPATA CHOPAPATIZA”
3. Mogwirizana ndi Mateyu 7:13, 14, kodi tiyenera kuchita chiyani?
3 Werengani Mateyu 7:13, 14. Onani kuti Yesu anatchula zipata iwiri zomwe misewu yake ikulowera kosiyana. Msewu wina ndi “wotakasuka” pomwe winawo ndi “wopanikiza” ndipo palibe msewu wachitatu. Tiyenera kusankha tokha msewu umene tikufuna kuyendamo. Zimene tingasankhe pankhani yofunika kwambiri imeneyi, n’zomwe zingathandize kuti tidzapeze moyo wosatha.
4. Kodi mungaufotokoze bwanji msewu “wotakasuka”?
4 Tiyenera kuganizira kusiyana kwa misewu iwiriyi. Anthu ambiri akuyenda mumsewu “wotakasuka” chifukwa chakuti ndi wosavuta kuyendamo. N’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri asankha kupitiriza kuyenda mumsewu umenewu n’kumangotsatira chikhamu cha anthu omwe akuyendamo. Iwo sazindikira kuti Satana Mdyerekezi ndi amene amalimbikitsa anthu kuti aziyenda mumsewu umenewu, womwe mathero ake ndi kuchiwonongeko.—1 Akor. 6:9, 10; 1 Yoh. 5:19.
5. Kodi anthu ena anachita zotani kuti apeze msewu “wopanikiza” n’kuyamba kuyendamo?
5 Mosiyana ndi msewu ‘wotakasukawu,’ msewu winawu ndi “wopanikiza” ndipo Yesu ananena kuti ndi ochepa amene akuupeza. N’chifukwa chiyani? N’zochititsa chidwi kuti muvesi lotsatira, Yesu anachenjeza otsatira ake za aneneri onyenga. (Mat. 7:15) Anthu ena amanena kuti zipembedzo zilipo masauzande ambiri, ndipo zambiri mwa zipembedzozo zimati zimaphunzitsa choonadi. Chifukwa choti padzikoli pali zipembedzo zambiri, anthu ambiri amasokonezeka ndipo amagwa ulesi moti safufuza n’komwe msewu wopita kumoyo. Komatu n’zotheka kupeza msewu umenewu. Yesu anati: “Mukamasunga mawu anga nthawi zonse, ndiye kuti ndinudi ophunzira anga. Mudzadziwa choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.” (Yoh. 8:31, 32) Tikuyamikira kuti simunangotsatira chikhamu cha anthu, koma munafufuza choonadi. Munayamba kuphunzira mwakhama Mawu a Mulungu kuti mudziwe zimene iye amafuna ndipo munamvera zimene Yesu anaphunzitsa. Mwa zina, munaphunzira kuti Yehova amafuna kuti tizipewa ziphunzitso za zipembedzo zonyenga komanso kuti tisamachite nawo maholide achikunja. Munaphunziranso kuti sizophweka kusiya makhalidwe amene Yehova amadana nawo n’kumachita zimene amafuna. (Mat. 10:34-36) Mwina zinkakuvutani kuti musiye zinthu zina pa moyo wanu. Komabe munayesetsa kuti musinthe chifukwa mumakonda Atate wanu wakumwamba ndipo mumafuna kuti azisangalala nanu. Yehova anasangalalatu kwambiri ndi zimene munachita.—Miy. 27:11.
ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUZIYENDABE PAMSEWU WOPANIKIZA
6. Mogwirizana ndi Salimo 119:9, 10, 45, 133, kodi n’chiyani chingatithandize kuti tiziyendabe pamsewu wopanikiza?
6 Popeza tinayamba kuyenda pamsewu wopanikiza, kodi n’chiyani chingathandize kuti tisachokepo? Taganizirani chitsanzo ichi. Zitsulo zotchingira mphepete mwa msewu zimateteza dalaivala ndi galimoto yake. Zitsulozo zimathandiza madalaivala kuti asagwere kuphedi. Palibe dalaivala amene angadandaule kuti zitsulo zimenezi zimamudodometsa. Mfundo za Yehova zopezeka m’Baibulo zili ngati zitsulo zotchingirazo. Mfundozi zimatithandiza kuti tiziyendabe pamsewu wopanikiza.—Werengani Salimo 119:9, 10, 45, 133.
7. Kodi achinyamata ayenera kuiona bwanji nkhani yoyenda pamsewu wopanikiza?
7 Achinyamata, kodi nthawi zina mumaona kuti mfundo za Yehova ndi zopanikiza kwambiri? Izi ndi zimene Satana amafuna kuti muziganiza. Iye amafuna kuti muziganizira kwambiri zochita za anthu amene akuyenda pamsewu wotakasuka komanso zimene amaoneka ngati akusangalala nazo. Angagwiritse ntchito zomwe anzanu a kusukulu amachita kapena zimene mumaona pa intaneti pokuchititsani kuona ngati mukumanidwa zinthu zabwino. Satana amafuna kuti muziona kuti mfundo za Yehova zikukulepheretsani kusangalala mokwanira.b Koma kumbukirani kuti Satana safuna kuti anthu amene akuyenda pamsewu wake adziwe kuti akumana ndi zotani kutsogolo, pomwe Yehova watidziwitsa kale zimene watisungira ngati tipitirizabe kuyenda pamsewu wopita kumoyo.—Sal. 37:29; Yes. 35:5, 6; 65:21-23.
8. Kodi achinyamata angaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Olaf?
8 Taganizirani zimene tikuphunzira pa zomwe zinachitikira m’bale wina wachinyamata dzina lake Olaf.c Anzake a m’kalasi ankamulimbikitsa kuti azichita zachiwerewere. Iye atawafotokozera kuti a Mboni za Yehova amatsatira mfundo za m’Baibulo za makhalidwe abwino, atsikana ena m’kalasi mwake anayesetsa kwambiri kumunyengerera kuti agone naye. Koma Olaf sanagonje pa mayeserowo. Komatu si mavuto okhawo amene anakumana nawo. Olaf anati: “Aphunzitsi anga ankandilimbikitsa kuti ndidzapite kuyunivesite, chifukwa maphunziro amenewa amachititsa kuti anthu azikulemekeza. Iwo anandiuza kuti popanda maphunzirowa, sindingapeze ntchito yabwino kapena kukhala wosangalala.” Ndiye kodi chinamuthandiza n’chiyani kuti asasokonezedwe ndi zimenezo? Iye anati: “Ndinayamba kugwirizana kwambiri ndi anthu a mumpingo mwathu moti ndinkawaona ngati a m’banja langa. Ndinayambanso kuphunzira Baibulo mwakhama. Pamene ndinkaliphunzira kwambiri, m’pamenenso ndinkatsimikizira kuti chimenechi ndi choonadi. Zimenezi zinandithandiza kuti nditsimikize mtima kutumikira Yehova.”
9. Kodi anthu amene akufuna kuyendabe pamsewu wopanikiza ayenera kuchita chiyani?
9 Satana amafuna kuti muchoke pamsewu wopita kumoyo. Iye amafuna kuti mofanana ndi anthu ambiri, muziyenda pamsewu wotakasuka womwe “ukupita kuchiwonongeko.” (Mat. 7:13) Koma tingamayendebe pamsewu wopanikiza ngati tingapitirize kumvera Yesu komanso kuona msewuwo kuti ndi chitetezo chathu. Tsopano tiyeni tikambirane chinthu chinanso chimene Yesu anati tizichita.
PITA UKAYANJANE NDI M’BALE WAKO
10. Mogwirizana ndi Mateyu 5:23, 24, kodi Yesu anati tiyenera kuchita chiyani?
10 Werengani Mateyu 5:23, 24. Palembali Yesu anafotokoza chinthu chimene chinali chofunika kwambiri kwa Ayuda amene ankamumvetsera. Taganizirani za munthu amene akufuna kupereka nsembe kukachisi ndipo wangotsala pang’ono kupereka nyama yake kwa wansembe. Ngati pa nthawiyo wakumbukira kuti anasemphana maganizo ndi m’bale wake, ankafunika kusiya nyama ya nsembeyo pomwepo ‘n’kupita’ kwa m’bale wakeyo. N’chifukwa chiyani? Chifukwa panali chinthu china chofunika kwambiri chimene ankafunika kuchita asanapereke nsembe yake kwa Yehova. Yesu anafotokoza momveka bwino kuti: “Pita ukayanjane ndi m’bale wako choyamba.”
11. Fotokozani zimene Yakobo anachita kuti akhalenso pamtendere ndi Esau?
11 Tingaphunzire mfundo yofunika kwambiri pankhani yokhazikitsa mtendere, tikaganizira zimene zinachitikira Yakobo. Iye atakhala kudziko lina kwa zaka pafupifupi 20, pogwiritsa ntchito mngelo, Mulungu anamulamula kuti abwerere kwawo. (Gen. 31:11, 13, 38) Koma panali vuto. M’bale wake Esau ankafuna kumupha. (Gen. 27:41) Yakobo “anachita mantha ndi kuda nkhawa kwambiri” poganiza kuti mwina m’bale wakeyo adakamusungirabe chakukhosi. (Gen. 32:7) Ndiye kodi Yakobo anatani kuti akhalenso pamtendere ndi m’bale wake? Choyamba iye anapemphera kwa Yehova za nkhaniyi mochokera pansi pa mtima. Kenako anatumiza mphatso kwa Esau. (Gen. 32:9-15) Pamapeto pake atakumana pamasom’pamaso, anayamba ndi iye kuchitapo kanthu posonyeza kuti amamulemekeza m’bale wakeyo. Iye anagwada pamaso pa Esau osati kamodzi kokha kapena kawiri, koma nthawi 7. Mwaulemu komanso modzichepetsa, Yakobo anakhazikitsa mtendere ndi m’bale wakeyo.—Gen. 33:3, 4
12. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Yakobo?
12 Tikuphunzirapo kanthu pa zimene Yakobo anachita pokonzekera kukumana ndi m’bale wake komanso zimene anachita atakumana naye. Modzichepetsa iye anapempha Yehova kuti amuthandize. Kenako anachita zinthu mogwirizana ndi pemphero lake poyesetsa kuti akhalenso pamtendere ndi Esau. Anthu awiriwa atakumana, Yakobo sanakangane ndi Esau kuti adziwe amene anali wolakwa. Cholinga cha Yakobo chinali kukhazikitsa mtendere ndi m’bale wake. Kodi tingatsanzire bwanji Yakobo?
ZIMENE TINGACHITE KUTI TIZIKHALA MWAMTENDERE NDI ENA
13-14. Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati takhumudwitsa Mkhristu mnzathu?
13 Ife amene tikuyenda pamsewu wopita kumoyo timafuna kukhala mwamtendere ndi abale athu. (Aroma 12:18) Ndiye kodi tiyenera kuchita chiyani tikazindikira kuti takhumudwitsa Mkhristu mnzathu? Mofanana ndi Yakobo tiyenera kupemphera kwa Yehova mochokera pansi pamtima. Tingamupemphe kuti atithandize pamene tikuyesetsa kuti tikhalenso pamtendere ndi m’bale wathuyo.
14 Tingachitenso bwino kudzifufuza. Tingadzifunse mafunso ngati awa: ‘Kodi ndimavomereza ndikalakwitsa zinthu, n’kupepesa modzichepetsa komanso kukhazikitsa mtendere? Kodi Yehova ndi Yesu amamva bwanji ndikamayesetsa kukhazikitsa mtendere ndi m’bale kapena mlongo?’ Mayankho athu pamafunso amenewa angatilimbikitse kumvera Yesu ndipo modzichepetsa tingapite kukakambirana ndi Mkhristu mnzathuyo kuti tikhale nayenso pamtendere. Tikamachita zimenezi tingakhale tikutsanzira Yakobo.
15. Kodi mfundo ya pa Aefeso 4:2, 3, ingatithandize bwanji kuti tikhalenso pamtendere ndi m’bale wathu?
15 Taganizirani zimene zikanachitika ngati Yakobo akanasonyeza mtima wonyada pokakumana ndi m’bale wake. N’zoonekeratu kuti zinthu sizikanayenda bwino. Tikapita kukakhazikitsa mtendere ndi m’bale wathu timafunika kukhala odzichepetsa. (Werengani Aefeso 4:2, 3.) Lemba la Miyambo 18:19 limati: “M’bale amene walakwiridwa amaposa mzinda wolimba, ndipo pali mikangano imene imakhala ngati mtengo wotsekera pachipata cha nsanja yokhalamo.” Kupepesa modzichepetsa kungatithandize kuti tilowe mu “nsanja yokhalamo” imeneyi.
16. Kodi tiyenera kuganizira mosamala za chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?
16 Tiyeneranso kuganizira mosamala zimene tikalankhule kwa m’bale wathu komanso mmene tikazilankhulire. Tikakonzeka, tiyenera kupita kwa munthu amene tamukhumudwitsayo n’cholinga choti tikhalenso naye pa ubwenzi wabwino. N’kutheka kuti mukayamba kukambirana naye angalankhule zinthu zimene simungasangalale nazo. N’zosavuta kuti tikwiye kapena kuyamba kudziikira kumbuyo koma kodi kuchita zimenezi kungathandize kuti tikhazikitse mtendere? Ayi ndithu. Kumbukirani kuti kukhazikitsa mtendere ndi m’bale wanuyo n’kofunika kwambiri kuposa kufufuza yemwe analakwa ndi yemwe sanalakwe.—1 Akor. 6:7.
17. Kodi tingaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Gilbert?
17 Pa nthawi ina m’bale wina dzina lake Gilbert anayesetsa kuti akhazikitse mtendere. Iye anati: “Sindinkagwirizana ndi mwana wanga wamkazi. Kwa zaka zoposa ziwiri ndinayesetsa kumamulankhula moona mtima komanso modekha n’cholinga choti tiyambirenso kugwirizana.” Kodi chinanso n’chiyani chimene Gilbert anachita? Iye anafotokoza kuti: “Ndisanalankhule ndi mwana wangayu, ndinkapemphera komanso kudzikonzekeretsa kuti ndisakhumudwe ndi mawu aliwonse amene angalankhule. Ndinkafunika kukhala wokonzeka kukhululuka. Ndinkadziwa kuti cholinga changa sikumutsimikizira kuti ndine wosalakwa koma kulimbikitsa mtendere.” Kodi zotsatirapo zake zinali zotani? Gilbert anati: “Panopo ndili ndi mtendere wa mumtima chifukwa ndimagwirizana kwambiri ndi anthu onse a m’banja langa.”
18-19. Ngati takhumudwitsa winawake, kodi tiyenera kukhala otsimikiza kuchita chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?
18 Ndiye kodi muyenera kukhala otsimikiza kuchita chiyani mukazindikira kuti mwakhumudwitsa Mkhristu mnzanu? Muzitsatira malangizo a Yesu pa nkhani yokhazikitsa mtendere. Muziuza Yehova nkhaniyo m’pemphero ndipo muzimudalira kuti akupatseni mzimu wake kuti ukuthandizeni kukhala munthu wobweretsa mtendere. Mukamachita zimenezi mudzakhala osangalala ndipo mudzasonyeza kuti mukumvera Yesu.—Mat. 5:9.
19 Ndife osangalala kuti Yehova amatipatsa malangizo achikondi kudzera mwa Yesu Khristu yemwe ndi “mutu wampingo.” (Aef. 5:23) Mofanana ndi mtumwi Petulo, Yakobo ndi Yohane, tiyeni tikhale otsimikiza kuti ‘tizimumvera.’ (Mat. 17:5) Taona mmene tingachitire zimenezi poyesetsa kukhazikitsa mtendere ndi Akhristu anzathu omwe tawakhumudwitsa. Tikamachita zimenezi komanso kupitiriza kuyenda pamsewu wopanikiza womwe ndi wopita kumoyo, tingapeze madalitso ambiri panopa komanso chimwemwe chosatha m’tsogolo.
NYIMBO NA. 130 Muzikhululuka
a Yesu anatilimbikitsa kuti tilowe pachipata chopapatiza chomwe msewu wake ukulowera kumoyo. Anatilangizanso kuti tizikhala pamtendere ndi Akhristu anzathu. Kodi ndi mavuto otani amene tingakumane nawo tikamatsatira malangizo akewa? Nanga tingatani kuti tilimbane nawo?
b Onani funso 6 m’kabuku kakuti, Mayankho a Mafunso 10 Omwe Achinyamata Amadzifunsa, lakuti “Ndingatani Kuti Ndisamangotengera Zochita za Anzanga?” komanso vidiyo yamakatuni yakuti, Musamangotengera Zochita za Anzanu! pa jw.org. (Onani pa ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > ACHINYAMATA.)
c Mayina ena asinthidwa.
d MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Tikamayendabe pamsewu “wopanikiza” womwe uli ndi zotchingira zotiteteza zomwe Yehova Mulungu watipatsa, timapewa zinthu zoopsa monga kuonera zolaula, kuchita zachiwerewere komanso sitingagonje tikamakakamizidwa kuti tiike maphunziro apamwamba pamalo oyamba pa moyo wathu.
e MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Pofuna kukhazikitsa mtendere Yakobo anagwadira m’bale wake Esau mobwerezabwereza.