Kodi Mudzakhala Mboni ya Mulungu Wowona?
“‘Inu ndinu Mboni zanga,’ ati Yehova, ‘ndipo Ine ndine Mulungu.’”—YESAYA 43:12.
1. Nchifukwa ninji tiyenera kulemekeza Mulungu wowona?
MWAMSANGA Yesu asanafe, iye ‘anakweza maso ake kumwamba’ napemphera. Iye anatchula Mmodzi kwa amene anali kupemphera monga “Mulungu yekha wowona.” (Yohane 17:1, 3) Moyenerera, pangakhale kokha Mulungu mmodzi wa moyo ndi wowona, Wolamulira wa chilengedwe chonse, Mlengi. Popeza tiri ndi mangawa a kukhalapo kwathu kwa Mulungu wowona, tiyenera kupereka kwa iye ulemu umene amauyenerera. Monga mmene Chivumbulutso 4:11 chimalongosolera icho kuti: “Muyenera inu, [Yehova NW] ndi Mulungu wathu, kulandira ulemelero ndi ulemu ndi mphamvu, chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwachifuniro chanu zinakhala, nizinalengedwa.”
2. (a) Nchiyani chimene chiri chanzeru kukhulupirira ponena za Mulungu wowona? (b) Ndimotani mmene iye amalankhulira ndi awo omwe amafuna kumulambira iye?
2 Chingakhale chanzeru kuyembekezera kuti Mulungu wowona sangalekerere kosatha mikhalidwe yoipa imene yaipitsa zolengedwa zake za pa dziko lapansi. Ndipo chingakhalenso chanzeru kukhulupirira kuti iye adzasunga alambiri ake odziŵitsidwa ponena za chimene iye adzachita ndi chimene iye akufuna iwo kuchita asanapereke ziweruzo zake. (Amosi 3:7) Ndimotani mmene iye amalankhulizana ndi ofunafuna chowonadi? Iye amagwiritsira ntchito anthu ofunitsitsa monga olankhula ake. “‘Inu ndinu Mboni zanga,’ ati Yehova . . . ‘Panalibe Mulungu wolengedwa, ngakhale pambuyo panga sipadzakhala wina. Ine—Ndine Yehova, ndipo palibe mpulumutsi, koma ine ndekha.’” (Yesaya 43:10, 11) Koma ndimotani mmene munthu angazindikirire awo amene Mulungu wowona akuwagwiritsira ntchito monga mboni zake? Ndimotani mmene iwo, ndi uthenga wawo, amasiyanirana ndi alambiri a milungu ina?
Chitokoso kwa Milungu Ina
3. Ndi chitokoso chotani chimene Yehova akupereka kwa milungu ina yonse?
3 Yehova anauzira Yesaya kulemba chitokoso ichi kwa milungu ina: “Ndani mwa iwo [milungu ya mitundu ya anthu] anganene ichi [ulosi wolongosoka]? Kapena kuwonetsa ife zinthu zakale [zomwe zidzachitika mtsogolo]? Aloleni iwo [monga milungu] atenge mboni zawo, kuti iwo [monga milungu] avomerezeke [kukhala NW] olungama, kapena aloleni iwo [anthu amitundu] amve ndi kunena, [‘Nchowonadi!’ NW]” (Yesaya 43:9) Chotero Yehova akutokosa milungu yonse imene anthu amailambira kutsimikizira kuti iyo iri milungu. Mboni zawo ziyenera kutulutsa chitsimikiziro chakuti milungu yawo iri yodalirika ndi yoyenera kulambiridwa.
4. Ndimotani mmene timadziŵira kuti milungu ya mitundu yakale inali yopanda phindu?
4 Koma nchiyani chimene milungu imeneyi ndi alambiri awo atulutsa? Kodi iwo atitsogoza ku mtendere weniweni, kutukuka, umoyo wabwino, ndi moyo? Mbiri imatsimikizira kuti milungu yambiri ya mitundu yakale inatsimikizira kukhala yopanda pake ndi yopanda mphamvu. Iyo sikanatha ngakhale kupulumuka monga zinthu zolambiridwa, popeza kuti iyo kulibe pa nthaŵi ino. Milungu yambiri ya Igupto, Asuri, Babulo, Medi-Peresiya, Grisi, Roma, ndi mitundu ina inatsimikizira kukhala yonyenga. Iyo imakhalapo kokha m’mabukhu a mbiri yakale kapena m’malo osungira zinthu zakale kumene zithunzi zawo ziri kokha zinthu zochititsa chidwi.
5. Nchiyani chimene tingafunse ponena za milungu ya nthaŵi yamakono?
5 Komabe, kodi milungu yamakono ndi alambiri awo iri yabwinopo kuposa milungu yakale? Chipembedzo cha Chihindu chokha chiri ndi mamiliyoni a milungu. Abudda, Akatolika, Aconfucianist, Ayuda, Asilamu, Aprotestanti, Ashinto, Ataoist, ndi ambiri ena ali ndi milungu yawoyawo. Mu Africa, Asia, ndi kwina kulikonse, mphamvu za chilengedwe, zinyama ndi zinthu zimalambiridwa monga milungu. Utundu ndi kukondetsa zinthu za kuthupi, ndipo ngakhale kudzikonda, kwakhala milungu, m’chakuti anthu ambiri amapereka kwa izo kudzipereka kwenikweni. Ndi njira iti ya kulambira m’chenicheni imene imaimira amene amadzilengeza kuti: “Ine ndiri Yehova, ndipo palibe winanso. Popanda ine palibe Mulungu”?—Yesaya 45:5.
“Mudzawazindikira Ndi Zipatso Zawo”
6. Ndimotani mmene tingasiyanitsire kulambira kowona kuchokera ku kulambira konyenga?
6 Yesu anakhazikitsa lamulo lodalirika la kuzindikirira chimene chiri chipembedzo chowona kapena chonyenga m’chigwirizano ndi chipembedzo. Iye ananena kuti: “Mudzawazindikira ndi zipatso zawo. . . . Mtengo wabwino uli wonse upatsa zipatso zokoma, koma mtengo wamphuchi upatsa zipatso zoipa. . . . Mtengo uli wonse wosapatsa chipatso chokoma, audula, nautaya kumoto.” (Mateyu 7:16-19) Chotero, kuti mudziŵe Mulungu wowona kuchokera ku yonyenga, ndi alambiri owona kuchokera kwa onyenga, timafunikira kusanthula zimene iwo amatulutsa. Kodi zipatso zawo ziri “zabwino,” kapena ziri “zoipa”?
7. Nchiyani chimene mbiri ya zana lino imatiuza ife ponena za zipembedzo za dziko iri?
7 Mwachitsanzo, nchiti cha zipembedzo za dziko chimene chakhazikitsa mtendere weniweni pakati pa atsatiri ake kuzungulira pa dziko lonse lapansi? Ndithudi, ziŵalo za chipembedzo chowona, abale auzimu, sayenera kuphana wina ndi mnzake. Koma anthu mamiliyoni zana limodzi anaphedwa mu nkhondo za m’zana lino la 20, ndipo nkhondo zonsezo zinachirikizidwa ndi zipembedzo za dziko lino. Monga chotulukapo chake, anthu achipembedzo apha anthu achipembedzo ena. M’nthaŵi zambiri, iwo anapha anthu achipembedzo chawo chenicheni. Akatolika anapha Akatolika, Aprotestanti anapha Aprotestanti, Asilamu anapha Asilamu, ndi awo azipembedzo zina atsatira njira yofananayo.
8. Ndimotani mmene openyerera amachitira ndemanga pa kulephera kwa chipembedzo m’nthaŵi yathu?
8 M’ndemanga ya akonzi a nyuzipepala yokhala ndi mutu wakuti “Chiwawa Chochitidwa M’dzina la Mulungu,” Mike Royko, akumachita ngati akuuza Mulungu, ananena za zipembedzo za dziko lino kuti: “Iwo akusonyeza kudzipereka kwawo kwa inu mwa kuphana wina ndi mnzake mu unyinji wa mazana. Ndikhulupirira kuti iwo amaganiza kuti ngati mbali imodzi ingathe psyiti mbali ina, idzatsimikizira kuti njira yawo ya kukulambirani iri yolondola.” Iye ananena kuti pamene kuli kwakuti papa anadziwonetsera iyemwini monga munthu wamtendere, “atsatiri ake adziŵika kukhala akukhetsa mamiliyoni a magaloni angapo a mwazi pamene mkwiyo wawo ubuka.” Kachiŵirinso, pamene Prezidenti wakale wa United States Carter anawona kuti “dziko lachita misala,” iye ananena kuti: “Chitsimikizo chozama cha chipembedzo, chomwe chiyenera kumangirira anthu m’chikondi, chikuwoneka kaŵirikaŵiri kukhala mbali ya msala ndi kuphana.”
9. Nchifukwa ninji sitifunikira kutsatira “milungu yopanda phindu”?
9 Chipatso choipa choterocho chiri chosiyana ndi zimene ziyenera kutulutsidwa ndi awo amene amalambira Mulungu wowona. (Agalatiya 5:19-23) Chotero, awo amene amachirikiza zipembedzo zochita nkhondo ndi nthanthi ali mbali ya kulambira konyenga monga mmene motsimikizirika analiri Igupto wakale, Asuri, Babulo, ndi ena amene anayang’ana kwa “milungu yopanda phindu yomwe siilankhula.” (Habakuku 2:18, NW) Ndipo monga mmene mawu a ulosi a Mulungu wowona anakwaniritsidwira pa kulambira konyenga kwakale, chotero chidzatero m’nthaŵi yathu: “Milungu yopanda phindu yeniyeni idzatha psyiti.” (Yesaya 2:18, NW) Lodalirika liri chenjezo lake lakuti: “Musamatembenukira kwa [milungu yopanda phindu NW.]”—Levitiko 19:4.
Kodi Ndani Akuchitira Umboni Kaamba ka Yehova?
10. Kodi atsatiri a zipembedzo za dziko iri ali mboni kaamba ka Mulungu wowona?
10 Mboni kaamba ka Mulungu wowona iyenera kukhala imodzi imene imachitira umboni ponena za iye. Kodi atsatiri a zipembedzo za dziko iri amasonyeza umboni woterowo? Ndi mwakwaŵirikaŵiri chotani kuti anthu a zipembedzo zimenezi amalankhula kwa inu ponena za kulambira kwawo? Ndi liti pamene iwo anaitanira panyumba yanu kuchitira umboni ponena za mulungu wawo? Chitokoso chimene Mulungu wowona wachipereka kwa yonyenga cha kutulutsa mboni sichimapita chosalabadiridwa. Anthu a zipembedzo zadziko lino samachitira umboni woterowo. Iwo sangakuuzeni amene ali Mulungu wowona kapena chimene zifuno zake ziri. Atsogoleri awo achipembedzo alephera kuwaphunzitsa iwo chowonadi. “Ali atsogoleri akhungu. Ndipo ngati wakhungu amtsogolera wakhungu, onse aŵiri adzagwa m’mbuna.”—Mateyu 15:14.
11. Ndi ndani okha amene akuchitira umboni ku dzina la Mulungu wowona?
11 Ndani amene ali ofunitsitsa kupereka nthaŵi, magwero a zinthu zakuthupi, ngakhale miyoyo yawo, kuchitira umboni kaamba ka Mulungu wowona? Ndani amene amauza anthu chimene Mulungu wowona akulengeza: “Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi lomwelo?” (Yesaya 42:8) Ndani amene amaphunzitsa kuti “dzina lanu ndinu Yehova, ndinu wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi”? (Masalmo 83:18) M’nthaŵi yake, Yesu anakhoza kunena kwa Mulungu wowona kuti: “Ndaliwonetsera dzina lanu.” (Yohane 17:6) M’nthaŵi yathu, kokha Mboni za Yehova zinganene chimenecho. Dzina lawo liri loyenerera chotani nanga—Mboni za Yehova!
Kuchitira Umboni Ponena za Ufumu
12. Ndi chiphunzitso chofunika chotani chimene mboni zowona ziyenera kumauza ena?
12 M’kuwonjezera ku kudziŵikitsa dzina la Mulungu wowona, nchiyani, makamaka, chimene mboni zake zidzinena ponena za zifuno zake? Yesu anakhazikitsa chitsanzo mwa kuphunzitsa otsatira ake kupemphera kwa Mulungu wowona kuti: “Ufumu wanu udze.” (Mateyu 6:10) Ufumu wa kumwamba wa Mulungu uli boma limene lidzalamulira kotheratu dziko lonse lapansi. (Danieli 2:44) Unali mutu wa kuphunzitsa kwa Yesu. (Mateyu 4:23) Chifukwa chakuti Ufumuwo uli yankho lokha ku mavuto a mtundu wa anthu, iye anafulumiza kuti: “Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake.”—Mateyu 6:33.
13. (a) Nchiyani chimene nsonga imasonyeza ponena za kulalikira kwa Mboni za Yehova ponena za Ufumu wa Mulungu? (b) Ndimotani mmene kulalikira Ufumu kuliri chitsimikiziro chakuti Yehova ali Mulungu yekha wa ulosi wowona?
13 Ndi ndani lerolino amene amachitira umboni kaamba ka Ufumu wa Mulungu? Profesa C. S. Braden, wophunzira wosamalitsa wa zipembedzo za dziko, ananena kuti: “Mboni za Yehova m’chenicheni zakuta dziko lapansi ndi umboni wawo. . . . Chinganenedwe mowonadi kuti palibe gulu limodzi lirilonse la chipembedzo pa dziko lapansi linasonyeza changu chopitirira ndi kuumirira ku kuyesera kubukitsa mbiri yabwino ya Ufumu kuposa Mboni za Yehova.” Koma iye analemba chimenecho chifupifupi zaka 40 zapita! Lerolino umboni wokulira wa Ufumu ukukwaniritsidwa, popeza pali Mboni zoposa kuwirikiza nthaŵi khumi tsopano! Chifupifupi mamiliyoni atatu ndi theka a iwo, m’mipingo yoposa 54,900 pa dziko lonse lapansi, akuchitira umboni kaamba ka Ufumu, ndipo ziŵerengero zawo zikukula mofulumira. Chipatso chabwino chimenechi chiri chitsimikiziro chakuti Yehova ali Mulungu wa ulosi wowona. Iye ali amene anauzira Mwana wake, Yesu, kuneneratu ponena za nthaŵi yathu kuti: “Ndipo mbiri yabwino imeneyi ya Ufumu idzalalikidwa pa dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kwa mitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.”—Mateyu 24:14, NW; Yohane 8:28.
Kutsanzira Chikondi cha Mulungu
14. Ndi mkhalidwe wotani umene mboni zowona za Mulungu ziyenera kutsanzira, ndipo nchiyani chimene icho chimatanthauza ngati iwo satero?
14 Mboni zowona za Mulungu ziyenera kutsanzira mkhalidwe wake wapamwamba—chikondi. “Iye wosakonda sazindikira Mulungu, chifukwa Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) Ndithudi, “mmenemo awoneka ana a Mulungu ndi ana a Mdyerekezi: Yense wosachita chilungamo saali wochokera kwa Mulungu, ndi iye wosakonda mbale wake. . . . Tikondane wina ndi mnzake; osati monga Kaini, anali wochokera kwa woipayo, namupha mbale wake.”—1 Yohane 3:10-12.
15. Nchifukwa ninji tinganene kuti Mboni za Yehova zimasonyeza chikondi chenicheni?
15 Mboni za Yehova zokha ziri ndi mtundu umenewu wa chikondi. Izo sizimagonjera kwa milungu ya nkhondo, utundu, ndi ufuko. Izo sizimachirikiza nkhondo iriyonse ya dziko iri ndipo chotero sizinakhalepo mu mkhalidwe umene izo zingachirikize kupha abale awo auzimu m’mbali zina za dziko. Iwo, monga mmene Yesu ananenera, “saali mbali ya dziko” ndipo ‘aika pansi lupanga lawo.’—Yohane 17:14; Mateyu 26:52.
16. Ndimotani mmene ena amathandizira kuzindikiritsa mboni zowona za Mulungu?
16 Phunziro lokhala ndi mutu wakuti “Zambiri Zonena za Kulungamitsa Chiwawa” linanena kuti: “Mboni za Yehova zasungirira mokhazikika kaimidwe kawo kopanda chiwawa ‘uchete Wachikristu’ . . . kaimidwe kawo kopitiriza motsutsana ndi utumiki wa utundu wa mtundu uliwonse, wa nkhondo kapena ntchito, ndi kukana kwawo kulemekeza zizindikiro zautundu zatulukapo m’nyengo zachizunzo, kuikidwa m’ndende, ndi kachitidwe ka kuukira kwa gulu m’maiko ambiri . . . Mboni, ngakhale kuli tero, sizinavomerezeko mwachiwawa.” Nyuzipepala ya ku Brazil O Tempo inanena ponena za iwo kuti: “Ngakhale kuti pali zipembedzo zambiri zodzinenera ndi kusatsa kwawo malonda m’mbali zambiri za chiwunda cha dziko, palibe ndi chimodzi chomwe pa nkhope ya pa dziko lapansi lerolino chimene chimasonyeza chikondi chofananacho.” Chikondi chowona chimenechi, Yesu ananena kuti, chimazindikiritsa mboni zowona za Mulungu. “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.”—Yohane 13:35.
Chizunzo Chimawonjezera Umboni
17, 18. Ndi chitsanzo chaposachedwapa chotani chimene chimasonyeza mmene chizunzo chingawonjezere ku umboni wa Ufumu?
17 Chizunzo chingatulukepo ngakhale mu umboni wofutukuka wa Ufumu. Mwachitsanzo, mu India muli kokha Mboni za Yehova 8,000. Komabe, posachedwapa dzina la Yehova ndi zifuno zake zinapatsidwa kufalitsidwa kokulira m’dziko limenelo mwa chimene ana a Mboni 11 anachita m’kutsanzira Akristu a m’zana loyamba omwe ananena ku bwalo la milandu kuti: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.” (Machitidwe 5:29) Ana a ku India anali atachotsedwa ku sukulu chifukwa cha kukana kuimba nyimbo ya utundu. Koma Bwalo Lalikulu Koposa la Milandu la India linalamulira, monga mmene chasimbidwira mu Deccan Herald ya ku Bangalore, kuti “palibe thayo m’dziko lino la kuimba Nyimbo ya Utundu.” Bwalo la milandulo linadziŵa kuti anawo “anasonyeza ulemu woyenera” ndipo kuti kusaimba kwawo “sikunasonyeze kusagonjera m’njira ina iriyonse.” Bwalo la milandulo linalamula kuti anawo abwezeretsedwe ku sukulu.
18 Nyuzipepala imodzimodziyo inawonanso kuti: “Ana amenewa anakana kuimba Nyimbo ya Utundu chifukwa Mboni za Yehova zimadzilingalira izo zokha kukhala Akristu ndipo zodzipereka kotheratu ku Ufumu wa Mulungu. . . . Iwo chotero samatenga mbali mu mtundu uliwonse wa machitachita a ndale za dziko a boma.” Ndiponso, The Telegraph ya ku Calcutta inasimba kuti: “Kachitidwe ka ana a sukuluko kabweretsa powonekera . . . Mboni za Yehova, zomwe mokulira zinali zosadziŵika m’dziko lathu kufikira posachedwapa.” Inde, ‘mbiri yabwino imeneyi ya Ufumu idzalalikidwa kaamba ka umboni kwa mitundu yonse’ mapeto asanafike.—Mateyu 24:14, NW.
Kusonkhanitsa Mboni Kaamba ka Mulungu Wowona
19. Nchiyani chimene anthu owona mtima amafunikira kuchita ngati iwo akufuna kulambira Mulungu wowona?
19 Lerolino, Mulungu wowona, Yehova, akupangitsa anthu kuchitira umboni ku ulamuliro ndi zifuno zake. Pamene iwo akulengeza uthenga wake ndi mphamvu yowonjezerekawonjezereka, iye akusonkhanitsa chiŵerengero chomakulakula cha anthu owona mtima kuchokera ku mitundu yonse kudzayanjana ndi alambiri ake. (Yesaya 2:2-4) Iwo amasiya milungu yawo yonyenga ndi kutembenukira ku kulambira kwa Mulungu wowona, monga mmene awo amene anafuna kulambira Yehova anamasulidwira kuchokera ku ukapolo ku Babulo wakale, kumene kulambira kwa milungu yonyenga kunali kofala.—Yesaya 43:14.
20, 21. Nchifukwa ninji chiri chofunika koposa kusiya milungu yonyenga tsopano ndiponso kusangokhala oimirira pambali?
20 Kodi mudzakhala mboni ya Mulungu wowona? Kodi mudzatenga kaimidwe kanu kaamba ka kulambira kowona ndi kupewa kugawana m’thayo la mwazi ndi liwongo la mkhalidwe woipa wachisembwere wa dziko iri ndi milungu yake yonyenga? Mawu a Mulungu amafulumiza kuti: “Tulukani mmenemo [kulambira konyenga kwa Chibabulo], anthu anga, kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake.” (Chivumbulutso 18:4) Inde, “Tulukani,” chitanipo kanthu kusanakhale kuchedwa! Musakhale ngati munthu amene, pamene anafunsidwa ponena za chipembedzo chimene amakonda ndi magazini a Chikatolika, ananena kuti: “Ndikhulupirira kuti ndiri Woimirira Pambali wa Yehova. Ndimakhulupirira zambiri zimene Mboni za Yehova zimakhulupirira—koma sindikufuna kudziloŵetsamo.”
21 Komabe, munthu aliyense pa dziko lapansi posachedwapa adzaloŵetsedwamo pamene Yehova adzawononga milungu yonyenga ya dziko iri ndi alambiri ake: “Milungu imene siinalenge miyamba ndi dziko lapansi, iyo idzatha ku dziko lapansi ndi pansi pa miyambayi.” (Yeremiya 10:11) Sipadzakhala woimirira pambali pa nthaŵi imeneyo. Padzakhala kokha awo amene ali mboni kaamba ka Mulungu wowona ndi awo amene saali. (Mateyu 24:37-39; 2 Petro 2:5; Chivumbulutso 7:9-15) Kodi mudzakhala mboni kaamba ka Mulungu wowona? Muyenera kutero, popeza “Mulungu [wowona NW] akhala kwa ife Mulungu wa chipulumutso; ndipo Yehova Ambuye [Mfumu NW] ali nazo zopulumutsira ku imfa.”—Masalmo 68:20.
Mafunso Akubwereramo
◻ Ndi chitokoso chotani chimene Mulungu wowona wapereka kwa milungu yonyenga?
◻ Ndi mwalamulo lodalirika liti limene tingadziŵire kulambira kowona kuchokera ku kulambira konyenga?
◻ Ndi chipatso chotani chimene chimasonyeza milungu ya dziko iri kukhala yopanda phindu monga mmene inaliri yakale?
◻ Ndi chipatso chabwino chotani chimene Mboni za Mulungu wowona ziyenera kutulutsa, ndipo ndi ndani amene akusonyeza icho?
◻ Nchifukwa ninji chiri chofunika koposa kuchitapo kanthu tsopano kusiya kulambira konyenga?
[Zithunzi patsamba 16]
Milungu yopanda phindu ya mitundu yakale inasiya kukhala monga zinthu zolambiridwa
[Chithunzi patsamba 17]
M’zana lathu chifupifupi anthu mamiliyoni zana limodzi anaphedwa mu nkhondo zochirikizidwa ndi zipembedzo za dziko lino
[Mawu a Chithunzi]
U.S. Army photo
[Chithunzi patsamba 18]
Yesu ananena kuti Mboni zowona zidzadziŵika ndi chikondi chimene zidzakhala nacho pakati pawo