Kodi Chikristu Chowona Chimatulutsa Akristu a Chikhulupiriro Chopanda Maziko?
DZIKO LA CHIPEMBEDZO lokhala ndi akhulupiriri ake opanda maziko—kuchokera ku anthu omwe anazikhazikitsa pa moto wa kuukira kwa ndale zadziko kufika ku anthu omachita mosalolalena kulinga kwa awo okhala ndi kawonedwe ka chipembedzo kosiyana. Mwachitsanzo, Nkhondo yoyamba ya Chipembedzo inauziridwa ndi Tchalitchi cha Chikatolika kumasula Yerusalemu kuchokera m’manja mwa anthu omwe amawalingalira kukhala osakhulupirira. Chinayambika ndi magulu a anthu atatu osalangidwa amene chiwawa chawo chopitirira chinaphatikizapo kuphedwa kwa chiwembu kwa Ayuda mu Rhineland. Pamene gulu lankhondo la Nkhondo ya Chipembedzo imeneyi linapambana m’kutenga Yerusalemu, asilikari a nkhondo amenewo otchedwa Akristu anatembenuza makwalala mu mitsinje ya mwazi.
Mu bukhu lake The Outline of History, H. G. Wells ananena za Nkhondo ya Chipembedzo yoyamba: “Kuphanako kunali kochititsa mantha; mwazi wa ongonjetsedwa unatsikira mu makwalala, kufikira anthu analowa mu mwazi pamene anali kuyenda. Pamene mdima unagwa, ‘akusisima chifukwa cha kuchuluka kwa chimwemwe,’ omenya nkhondo ya chipembedzowo anafika ku Sepulchre kuchokera ku kuponda kwawo mpesa, ndipo anaika manja awo oipitsidwa ndi mwazi pamodzi m’pemphero.”
Mu Nkhondo ya Chipembedzo yotsatira yotchedwa ndi Papa Innocent III, Albigenses ndi Waldenses amtendere, omwe anakana ziphunzitso za Roma ndi kumwerekera kwa atsogoleri a chipembedzo, anaphedwa mwachiwembu. Ponena za kukhulupirira kopanda maziko kosonyezedwa motsutsana ndi iwo, Wells analemba kuti: “Ichi chinali chokwanira kwa Lateran, ndipo chotero ifenso tinali ndi kawonedwe ka Innocent m kakulalikira Nkhondo ya Chipembedzo yotsutsa magulu ampatuko opanda mwawi amenewo, ndi kuvomereza kundandalitsa kwa munthu wopanda pake aliyense woyendayenda . . . ndi kuukira kokhutiritsa kulikonse pakati pa nzika za mtendere koposa za Mfumu ya ku France. Mbiri za nkhalwe ndi kunyansa kwa Nkhondo ya Chipembedzo imeneyi ziri zochititsa mantha kwambiri kuziwerenga kuposa mbiri iriyonse ya kufera Chikristu kochitidwa ndi achikunja.”
Mbiri ya Dziko la Chipembedzo iri yodzaza ndi mbiri ya akhulupiriri opanda maziko, ndipo iwo kawirikawiri atulutsa zipatso za chiwawa. Chotero tingamalize kuti kukhulupirira kopanda maziko sikutulutsa zipatso zabwino. Funk ndi Wagnalls New Standard Dictionary of the English Language (kusindikizidwa kwa mu 1929) imalongosola kukhulupirira kopanda maziko m’njira iyi: “Changu chopitirira muyezo kapena cha kanthawi.” Ndipo imapitiriza kuchitira chitsanzo icho ndi mawu awa: “Palibe nyengo ya mbiri yakale imene imasonyeza unyinji waukulu wa nkhalwe, kusoweka kwamalamulo a makhalidwe abwino, ndi kukhulupirira kopanda maziko kuposa Nkhondo ya Chipembedzo.
Chirinso chosangalatsa kudziwa kulongosoledwa kopatsidwa ku liwu lakuti “kukhulupirira kopanda maziko” ndi Webster’s Third New International Dictionary, 1961 edition. Iyo imati: ’Kukhulupirira kopanda maziko—Latin, kuuziridwa ndi mulungu. 1. kugwidwa ndi kapena monga ngati ndi chiwanda; mokulira: kuchititsidwa misala, kusokonezeka kwa maganizo, kufuntha. 2. kutsogoleredwa, kutulutsidwa, kapena kusonyezedwa ndi changu chachikulu koposa: kupitirira muyezo, kusalingalira; kute nthedwa maganizo kopitirira muyezo, makamaka pa nkhani za chipembedzo.’ Ndi malingaliro awa m’maganizo, kodi chinganenedwe kuti Akristu owona ali akhulupiriri opanda maziko?
Kuzindikiridwa ndi Zipatso
Monga mmene chipatso chamtengo chimazindikiritsa uwo, choteronso zotulukapo za zochita za anthu zimazindikiritsa iwo ndi mtundu wa anthu umene iwo akutulutsidwako. Yesu Kristu, Muyambitsi wa Chikristu, analoza ku ichi. Iye anati: “Sungathe mtengo wabwino kupatsa zipatso zoipa, kapena mtengo wamphuchi kupatsa zipatso zokoma. Indie chomwecho pa zipatso zawo mudzawazindikira iwo.”—Mateyu 7:18, 20.
Yesu anakazikitsa Chikristu chowona monga mtengo wabwino. Iwo chotero, siwukakhoza kutulutsa zipatso zoipa za kukhulupirira kopanda maziko. Palibe nthawi ndi imodzi yomwe pamene Yesu anafulumiza otsatira ake kuchita kusakaza kwa kuthupi kwa iwo eni kapena kwa ena. M’malo mwake, m’kugwira mawu a limodzi la malamulo akulu kwambiri, iye anati: “Uzikonda mnzako monga udzikondera iwe mwini.” (Mateyu 22:39) Atsatiri ake anayenera kukhala achifundo ngakhale kwa adani awo. Yesu anati: “Kondanani nawo adani anu; chitirani zabwino iwo akuda inu, dalitsani otemberera inu, pemphererani iwo akuchitira inu chipongwe.”—Luka 6:27, 28.
Atsatiri owona a Yesu anapita pakati pa anthu amitundu yosiyanasiyana, osati ndi moto ndi lupanga, koma ndi Mawu olembedwa a Mulungu ndi chikakamizo cha mtendere. Palibe magulu ankhondo amene anatsatana nawo ku maiko ena ndi cholinga cha kukapha, kuzunza, ndi kugwirira chigololo awo amene anakana ubatizo Wachikristu. M’malo mwake, ophunzira a Yesu anatsatira chitsanzo chake cha mtendere cha kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu kwa onse, kuwalimbikitsa iwo kulingalira pa chidziwitso choperekedwa kuchokera m’Malemba. Zipatso za ntchito yawo zinaphatikizapo chipatso cha mzimu wa Mulungu—“chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso.”—Agalatiya 5:22, 23.
Sichiri chosiyana lerolino. Chikristu chowona chikupitirizabe kutulutsa chipatso chabwino. Mtengo, gulu Lachikristu, limene Yesu anabzyala zaka 1, 900 zapitazo unali wabwino, ndipo udakali wabwinobe. Chotero suli wokhoza kutulutsa choipa, kusalolena, zipatso za chiwawa za kukhulupirira kopanda maziko. Chotero, nchifukwa ninji, kukhulupirira kopanda maziko kwakhala kofala m’dziko la Chipembedzo?
Mtumwi Paulo anasonyeza kuti nthawi idzabwera pamene Akristu onyengezera adzawonekera. Iwo adzakhala ndi dzina Lachikristu koma sadzakhala mogwirizana nalo kapena kutulutsa zipatso zake zabwino. Iye anauza akulu a ku Aefeso: “Ndidziwa ine kuti, nditachoka ine adzalowa mimbulu yosautsa, yosalekerera gululo; ndipo mwa inu nokha adzauka anthu, olankhula zokhotakhota, kupatula ophunzira awatsate.” (Machitidwe 20:29, 30) Kuchokera kwa ampatuko amenewa kunauka Dziko la Chipembedzo ndi mazana ake a magulu a zipembedzo owombana ophunzitsa zinthu zomwe zinangoimiridwa kokha monga Akristu. M’chenicheni, izo ziri “zinthu zokhotakhota,” malingaliro a anthu ndipo osati chowonadi cha Mawu a Mulungu. Pakhala pakati pa Akristu onyenga amenewa pamene zipatso zoipa za kukhulupirira kopanda maziko kwadzisonyezera iko kokha.
Kodi Changu cha Chikristu Chiri Chopanda Maziko?
Chiri chowona kuti kukhulupirira kopanda maziko kuli mtundu wa changu. Koma kukhulupirira kopanda maziko kuli “changu chopitirira muyezo kapena chamisala,” changu “chopanda tanthauzo”. Ichi sichinganenedwe ponena za Chikristu chowona. Mobwerezabwereza, Baibulo limachenjeza Akristu kukhala olingalira. Mwachitsanzo, Afilipi 4:5 amanena kuti: [“Lekani kulingalira kwanu kudziwike kwa anthu onse”, NW.] Ndipo Akristu akupatsidwa uphungu wa “kusachitira mwano munthu aliyense, kusakhala andewu, [kukhala wolingalira, NW], kuwonetsera chifatso chonse pa anthu onse.”—Tito 3:2.
Chifukwa chakuti Mboni za Yehova zimachezera anthu m’nyumba zawo kulankhula ponena za mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu, izo ziri zosiyana kuchokera ku unyinji wa awo omadzinenera kukhala Akristu. Changu chimenechi cha utumiki Wachikristu sichiri maziko akuwonera iwo monga akhulupiriri opanda maziko. Chiri changu cholingalira chantchito imene Yesu anachita ndi kulamulira otsatira ake kuchita. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Munthu amene amaika pambali nthawi ya zochitachita zaumwini zochuluka za kutha nthawi ndi cholinga chofuna kupereka nthawi yochuluka monga mmene kungathekere ku ntchito yolalikira Ufumu sali mkhulupiriri wopanda maziko.
M’malo mwake, iye akusonyeza chiyamikiro chake kaamba ka kufulumiza kwakuthandiza ena kuphunzira ponena za chowonadi chopatsa moyo cha Mawu a Mulungu m’nthaŵi yochepa yotsalira kaamba ka ntchitoyi kuti ichitike. Ichi chiri cholingalirika ndi chopindulitsa. M’malo mokhala ntchito yopahda chikhulupiriro yomwe imavulaza ena, ntchito imeneyi imamangirira chikhulupiriro mwa Mulungu ndi Mawu ake. Imapereka chiyembekezo kwa awo opanda chiyembekezo, imabweretsa ufulu kuchokera ku kukhulupirira mizimu kwa zipembedzo ndi kusadziwa, ndipo kumasintha anthu osaˆerengeka amakhalidwe oipa ndi achiwawa kukhala oyera mwa makhalidwe ndi Akristu a mtendere. Zipatso zabwino zimenezo zimasonyeza kugwirizana kwabwino.
M’maiko oposa 200, Mboni za Yehova zikusunga kukhulupirika kwawo kwa Ufumu wa Mulungu, ngakhale ngati izo ziri pansi pa kuletsa kwa boma m’malo ambiri. Kukhulupirika kwawo kwa Mulungu, Wolamulira Wamkulukulu, sikungaikidwe pamodzi ndi kukhulupirira kopanda maziko. Iye ali Wolamulira wapamwamba koposa, ndipo pamene pali kusagwirizana pakati pa malamulo ake ndi awo a boma la munthu, Mkristu wowona amakakamizidwa kumvera iye. Pansi pa maboma a anthu, malamulo a kumaloko nthawi zina amanyalanyazidwa chifukwa amawombana ndi malamulo a chigwirizano cha ndale. Mofananamo, kwa Mkristu wowona malamulo a munthu amanyalanyazidwa pamene awombana ndi awo a Wolamulira wa Chilengedwe Chonse, Yehova Mulungu. Popeza Mkristu wowona sangavomereze malamulo awiri owombana, iye angachite chimene atumwi anachita. Iwo anati: “Tiyenerakumvera Mulungu koposa munthu.” (Machitidwe 5:29) Ichi chiri chanzeru.
Kulingalira kofananako kukusonyezedwa ndi Mboni za Yehova ponena za ulemu ku zikondwerero za utundu ndi za zipembedzo zomwe ziri zowombana ndi Mawu a Mulungu. Sikuli kukhulupirira kopanda maziko kukana kutenga mbali mu zimene ambiri m’dziko amasangalala nazo. Kukhala osiyana chifukwa cha chikumbumtima chawo cha chipembedzo kumaika Mbonizo m’malo ofanana ndi Akristu oyambirira, omwe sanatenge mbali mu zikondwerero zofala za m’tsiku lawo. Ndipo Mboni za Yehova ziri zachimwemwe kupereka chifukwa cha m’Malemba kaamba ka kusatengamo mbali kwawo.—1 Petro 3:15.
Anthu ena angaike Mbonizo monga akhulupiriri opanda maziko chifukwa chakukana kwawo kulandira mwazi, njira ya kachitidwe ka zinthu yomwe iri yofala ndi madokotala ambiri. Pano kachiwirinso iri nkhani ya kumvera ku lamulo la Mulungu. Atsatiri owona a Yesu Kristu analamuliridwa kuti “asale . . . mwazi.” —Machitidwe 15:28, 29.
Kodi munthu angakhale wokhulupirira wopanda maziko chifukwa chakuti, kaamba ka chikumbumtima, iye akukana njira ya mankhwala yomwe yakhala yofala posachedwapa? Anthu ena omwe sali Mboni za Yehova amakana kuthiridwa mwazi kokha chifukwa chamantha akuyambukiridwa ndi AIDS kapena matenda ena. Chotero kodi iko kuli kusalingalira kwa Mboni kufunsa njira ya mankhwala yomwe simavulaza chikumbumtima chawo?
Nchiyani, tsopano, chimene tiyenera kumaliza kuchokera ku ichi? Kuti Mboni za Yehova siziri akhulupiriri opanda maziko chifukwa chakuti izo ziri zosiyana ndi ambiri ndipo zamamatira ku kukhala zomvera kwa Mulungu. Ngakhale kuti izo ziri ndi changu kaamba ka Mulungu, izo siziri ndi “changu chopitirira muyezo kapena chamisala” ngati kuti zagwidwa ndi ziwanda: ndiponso izo siziwoneka kukhala “zamisala, zosokonezeka maganizo,” kapena “zofuntha.” Palibe nthawi ndi imodzi yomwe imene chifukwa cha changu cha chipembedzo izo zinavulaza ena kapena izo zeni. M’malo mwake, m’chigwirizano ndi chimene Baibulo limanena ponena za Akristu owona, izo ziri “za mtendere ndi anthu onse.”—Aroma 12:18.
Chotero gulu Lachikristu limene Yesu Kristu analiyamba mu zaka za zana loyamba monga mtengo wabwino likupitirizabe lerolino kutulutsa kokha chipatso chabwino. Chotero, icho chiri, chosatheka kwa Chikristu chowona kutulutsa akhulupiriri opanda maziko.
[Mawu Otsindika pa tsamba 30]
Palibe chifukwa cha kuwonera Mboni za Yehova monga akhulupiriri opanda maziko chifukwa cha changu chawo mu utumiki Wachikristu