Khalani Akuchita Mawu, Osati Akumva Okha
‘Si yense wakunena kwa ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu ufumu wakumwamba; koma wakuchitayo chifuniro cha Atate wanga wakumwamba.’—MATEYU 7:21.
1. Kodi atsatiri a Yesu ayenera kupitirizabe kuchitanji?
DZIPEMPHANIBE. Dzifunafunanibe. Dzigogodanibe. Limbikirani m’pemphero, kuphunzira, ndikulabadira mawu a Yesu olembedwa mu Ulaliki wa pa Phiri. Yesu akuwauza atsatiri ake kuti ali mchere wa dziko lapansi, okhala ndi uthenga wosungitsa wokometseredwa ndi mchere umene sunafunikire kuloledwa kusukuluka, kutaikiridwa ukoma wake kapena mphamvu zake zosungitsa. Iwo ndiwo nyali yadziko, owunikira kuwunika kuchokera kwa Kristu Yesu ndi Yehova Mulungu osati kupyolera m’zimene amanena zokha komanso ndi m’zimene amachita. Ntchito zawo zabwino zimawalikira kwambiri mofanana ndi mawu awo owunikirawo—ndipo angalankhule mofuula kwambiri m’dziko logwiritsiridwa ntchito ndi chinyengo cha Afarisi ponse paŵiri ndi atsogoleri achipembedzo ndi andale zadziko, amene amanena zambiri ndikuchita zochepa.—Mateyu 5:13-16.
2. Kodi Yakobo akupereka malangizo otani, koma kodi ndi kaimidwe kachitonthozo kotani kamene ena amakatenga molakwika?
2 Yakobo akulangiza kuti: ‘Khalani akuchita mawu, osati akumva okha, ndi kudzinyenga nokha.’ (Yakobo 1:22) Ambiri amadzinyenga okha ndi chiphunzitso chakuti ‘utapulumutsidwa kamodzi umakhala wopulumutsidwa nthaŵi zonse,’ monga ngati tsono angangokhala phee ndikuyembekezera mphotho yolingaliridwa kukhala kumwamba. Ichi nchiphunzitso chonama ndi chiyembekezo chabodza. “Iye amene adzapirira mpaka potsirizira,” anatero Yesu, “ndiye adzapulumuka.” (Mateyu 24:13, NW) Kuti mupeze moyo wosatha, inu muyenera ‘kukhala wokhulupirika kufikira imfa.’—Chibvumbulutso 2:10; Ahebri 6:4-6; 10:26, 27.
3. Kodi ndi malangizo otani onena za kuweruza amene Yesu akupereka chotsatira mu Ulaliki wa pa Phiri?
3 Pamene Yesu anapitiriza ndi Ulaliki wake wa pa Phiri, mawu ambiri anafotokozedwa amene Akristu ayenera kukalamira kuwatsanzira. Panopa pali ena amene amawonekera kukhala opepuka, koma amatsutsa chimodzi cha zikhoterero zovuta kwenikweni kuzichotsa: ‘Musaweruze, kuti mungaweruzidwe. Pakuti ndi kuweruza kumene muweruza nako, inunso mudzaweruzidwa; ndipo ndi muyeso umene muyesa nao, kudzayesedwa kwa inunso. Ndipo upenya bwanji kachitsotso kali m’diso la mbale wako, koma mtanda uli m’diso la iwemwini suuganizira? Kapena udzati bwanji kwa mbale wako, Tandilola ndichotse kachitsotso m’diso lako; ndipo ona, mtandawo ulimo m’diso lakoli. Wonyenga iwe! tayamba kuchotsa m’diso lako mtandawo, ndipo pomwepo udzapenyetsa kuchotsa kachitsotso m’diso la mbale wako.’—Mateyu 7:1-5.
4. Kodi ndi malangizo owonjezereka otani amene cholembedwa cha Luka chikupereka, ndipo kodi kuŵagwiritsira ntchito kumatulukapo chiyani?
4 M’cholembedwa cha Luka cha Ulaliki wa pa Phiri, Yesu anauza amvetseri ake kusafunafuna zolakwa mwa ena. Mmalo mwake, apitirize ‘kumasulana,’ ndiko kuti, kukhululukirana zophophonya. Ichi chingapangitse enawo kuvomereza mokoma mtima, monga mmene Yesu ananenera kuti: ‘Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu; muyeso wabwino, wotsendereka, wokhuchumuka, wosefukira, anthu adzakupatsani m’manja mwanu. Pakuti kudzayesedwa kwa inu ndi muyeso womwewo muyesa nawo inu.’—Luka 6:37, 38.
5. Kodi nchifukwa ninji kuli kopepuka kwambiri kuwona zophophonya mwa ena kuposa zomwe tiri nazo?
5 M’zaka za zana loyamba C.E., chifukwa cha miyambo yapakamwa, Afarisi ochuluka anakhoterera kuweruza ena mwansontho. Aliyense wa amvetseri a Yesu amene anali ndi chizoloŵezi cha kuchita ichi anafunikira kuleka. Nkopepuka kuwona zitsotso m’diso la ena kuposa mitanda yokhala mwathu—ndipo kumasangalatsa malingaliro athu! Monga mmene mwamuna wina ananenera kuti, “Ndimakonda kusuliza ena chifukwa kumandipangitsa kudzimva bwino kwambiri!” Chizoloŵezi cha kuloza chala ena chingatipatse malingaliro akudziganiza kukhala abwino kumene kungaphimbe zophophonya zathu zimene tikufuna kubisa. Koma ngati kuwongolera kuli koyenerera, kuyenera kuperekedwa mumzimu wofatsa. Wopereka chiwongoleroyo ayenera nthaŵi zonse kulingalira zophophonya zake.—Agalatiya 6:1.
Yesani Kumvetsetsa Musanaweruze
6. Kodi ziweruzo zathu zitafunikira, ziyenera kuzikidwa pamaziko otani, ndipo kodi ndi thandizo lotani limene tiyenera kufunafuna kuti tisakhale osuliza mopambanitsa?
6 Yesu sanabwere kudzaweruza dziko koma kudzalipulumutsa. Ziweruzo zonse zimene iye anapereka sizinali zake koma zinazikidwa pamawu amene Mulungu anampatsa kuti awalankhule. (Yohane 12:47-50) Ziweruzo zirizonse zimene tingapange ziyeneranso kukhala zogwirizana ndi Mawu a Yehova. Tiyenera kupeŵa chikhoterero chaumunthu cha kukhala oweruza. Pochita tero, tiyenera kupitirizabe kupempherera thandizo la Yehova: “Dzipemphanibe, ndipo kudzapatsidwa kwa inu; dzifunafunanibe, ndipo mudzapeza; dzigogodanibe, ndipo kudzatsegulidwa kwa inu. Pakuti yense wopempha amalandira, ndipo yense wofunafuna amapeza, ndipo aliyense wogogoda kudzatsegulidwa kwa iye.” (Mateyu 7:7, 8, NW) Ngakhale Yesu anati: ‘Sindikhoza kuchita kanthu kwa ine ndekha; monga momwe ndimva ndiweruza; ndipo maweruzidwe anga ali olungama; chifukwa kuti sinditsata chifuniro changa, koma chifuniro cha iye wondituma ine.’—Yohane 5:30.
7. Kodi ndi chizoloŵezi chotani chimene tiyenera kupititsa patsogolo chimene chidzatithandiza pogwiritsira ntchito Lamulo la Makhalidwe Abwino?
7 Tiyenera kupititsa patsogolo chizoloŵezi, osati cha kuweruza anthu, koma cha kuyesera kuwamvetsetsa mwa kudziika tokha mmalo mwawo—ichi sichinthu chopepuka kuchichita koma nchinthu chofunika ngati tikufuna kugwirizana ndi Lamulo la Makhalidwe Abwino, limene Yesu chotsatira analengeza kuti: ‘Chifukwa chake zinthu ziri zonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero; pakuti icho ndicho chilamulo ndi aneneri.’ (Mateyu 7:12) Chotero atsatiri a Yesu ayenera kukhala atcheru ndi kuzindikira mkhalidwe wa maganizo, malingaliro, ndi wauzimu wa ena. Iwo ayenera kuzindikira ndi kumvetsetsa zosoŵa za ena ndikutenga chikondwerero chaumwini m’kuwathandiza. (Afilipi 2:2-4) Zaka zingapo pambuyo pake Paulo analemba kuti: ‘Pakuti mawu amodzi akwaniritsa chilamulo chonse ndiwo; Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.’—Agalatiya 5:14.
8. Kodi Yesu anafotokoza njira ziŵiri ziti, ndipo kodi nchifukwa ninji imodzi ya izi imasankhidwa ndi anthu ambiri?
8 ‘Lowani pa chipata chopapatiza,’ anatero chotsatira Yesu, ‘chifukwa chipata chiri chachikulu, ndi njira yakumuka nayo kukuonongeka iri yotakata; ndipo ali ambiri amene alowa pa icho. Pakuti chipata chiri chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenechi ali owerengeka.’ (Mateyu 7:13, 14) Ambiri m’masiku amenewo anasankha njira yonka ku chiwonongeko ndipo ambiri adakachitabe tero. Njira yotakata imalola anthu kuganizira m’njira imene amakonda ndi kuchita zinthu zodzifunira: mulibe malamulo, mulibe mabande omamatirako, muli njira ya moyo yochita zinthu mosavutitsidwa ndi chikumbumtima basi, chirichonse nchopepuka. Palibe ndi mmodzi yense wa awa amene ‘amayesetsa kulowa pa khomo lopapatiza’!—Luka 13:24.
9. Kodi chimafunikira nchiyani kuti tiyende m’njira yopapatiza, ndipo kodi ndi chenjezo lotani limene Yesu akupereka kwa oyendamowo?
9 Koma ndinjira yopapatizayi imene imakalowa mumsewu wonka ku moyo wosatha. Ndinjira imene imaitanira kudziletsa. Kungafunikire chilango chimene chidzasanthula zakuya za zolinga zanu ndikusanthula mtundu wa kudzipereka kwanu. Chizunzo chitabwera, njirayi imakhala ya majidumajidu ndipo imafunikira chipiriro. Yesu akuchenjeza oyenda m’njira imeneyi kuti: ‘Yang’anirani mupewe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zovala zankhosa, koma m’kati mwawo ali afisi olusa.’ (Mateyu 7:15) Kufotokozaku kunawayenerera bwino Afarisi. (Mateyu 23:27, 28) Iwo ‘anadzikhazika okha pampando wa Mose,’ akumati akumlankhulira Mulungu pamene anali kutsatira miyambo ya anthu.—Mateyu 23:2.
Mmene Afarisi ‘Anatsekera Ufumu’
10. Kodi ndi panjira yapadera iti pamene alembi ndi Afarisi anafunafuna ‘kutsekera anthu ufumu’?
10 Kuwonjezerapo, atsogoleri achipembedzo Achiyuda anafunafuna kutsekereza ofunafuna kulowa pa chipata chopapatizachi. ‘Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! chifukwa mutsekera anthu ufumu wakumwamba pamaso pawo; pakuti inu nokha simulowamo, ndipo muwaletsa amene alikulowamo, kuti asalowemo.’ (Mateyu 23:13) Njira ya Afarisi inafananadi ndendende ndi chimene Yesu anachenjeza. Iwo ‘adzalitaya dzina lanu [la ophunzira ake] monga loipa, chifukwa cha Mwana wa munthu.’ (Luka 6:22) Chifukwa chakuti mwamuna wina wobadwa wakhungu ndikuchiritsidwa ndi Kristu anakhulupirira Yesu kukhala Mesiya, iwo anamupitikitsa m’sunagoge. Makolo ake sananene kanthu kuwopera kuti nawonso angathamangitsidwe m’sunagoge. Ena, amene anakhulupirira Yesu kukhala Mesiya anazengereza kumuvomereza poyera kaamba ka chifukwa chimodzimodzi.—Yohane 9:22, 34; 12:42; 16:2.
11. Kodi atsogoleri achipembedzo a Chikristu Chadziko amabala zipatso zotani zowazindikiritsa?
11 Yesu anati, ‘Mudzawazindikira ndi zipatso zawo. Mtengo wabwino uliwonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphuchi upatsa zipatso zoipa.’ (Mateyu 7:16-20) Lamulo limodzimodzili limagwira ntchito lerolino. Atsogoleri achipembedzo ambiri a Chikristu Chadziko amanena chinthu china ndikuchita chinanso. Ngakhale kuti amati amaphunzitsa Baibulo, iwo amamamatira ku zochita zamwano zonga ngati Utatu ndi moto wa helo. Ena amakana dipo, amaphunzitsa chisinthiko mmalo mwa chilengedwe, ndipo amalalikira nthabwala kuti agonthetse makutu. Mofanana ndi Afarisi, atsogoleri achipembedzo ambiri alerolino ngokonda ndalama, akumadyerera nkhosa zawo madola mamiliyoni ambiri. (Luka 16:14) Onsewo amafuula kuti, “Ambuye, Ambuye,” koma yankho la Yesu kwa iwo ndi ili: ‘Sindinakudziwani inu nthaŵi zonse; chokani kwa ine, inu akuchita kusayeruzika.’—Mateyu 7:21-23.
12. Kodi nchifukwa ninji ena amene nthaŵi ina anayenda m’njira yopapatiza atulukamo, ndipo ndi chotulukapo chotani?
12 Lerolino, anthu ena amene panthaŵi ina anayendapo m’njira yopapatiza angakhale anatulukamo. Iwo amati amakonda Yehova, koma samamvera malamulo ake a kulalikira. Iwo amati amakonda Yesu, koma sakudyetsa nkhosa zake. (Mateyu 24:14; 28:19, 20; Yohane 21:15-17; 1 Yohane 5:3) Iwo samafuna kumangidwa mgoli ndi oyenda m’mapazi a Yesu. Iwo anaiwona njira yopapatizayi kukhala yopapatizadi thithithi. Iwo anatopa ndi kuchita zabwino, chotero ‘anatuluka mwa ife, komatu sanali a ife; pakuti akadakakhala a ife akadakhalabe ndi ife.’ (1 Yohane 2:19) Iwo anabwereranso mumdima, ndipo ‘mdimawo ngwaukulu ndithu!’ (Mateyu 6:23) Iwo ananyalanyaza kuchonderera uku kwa Yohane: ‘Tiana, tisakonde ndi mawu, kapena ndi lilime, komatu ndi kuchita ndi m’chowonadi.’—1 Yohane 3:18.
13, 14. Kodi ndi fanizo lotani lonena za kugwiritsira ntchito mawu ake m’miyoyo yathu limene Yesu anapereka, ndipo kodi linawayenerera motani okhala m’Palestina?
13 Yesu anamaliza Ulaliki wake wa pa Phiri ndi fanizo lalikulu ili: ‘Yense amene akamva mawu anga amenewa, ndi kuwachita, ndidzamfanizira iye ndi munthu wochenjera, amene anamanga nyumba yake pathanthwe; ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; koma siinagwa; chifukwa inakhazikika pathanthwepo.’—Mateyu 7:24, 25.
14 Mu Palestina mvula yamphamvu ingapangitse madzi kuyenda motsikira ku chigwa chouma m’mathithi owopsya. Kuti nyumba zisagwe, maziko ake anafunikira kuikidwa pathanthwe. Cholembedwa cha Luka chimasonyeza kuti munthu “anakumba pansi ndithu, namanga maziko a nyumbayo pathanthwe.” (Luka 6:48) Iyi inali ntchito yolimba, koma inabweretsa mphotho pamene mvula yamkuntho inabwera. Chotero kumanga mikhalidwe Yachikristu pa mawu a Yesu kudzakhala kodzetsa mphotho pamene mathithi a chivuto akantha.
15. Kodi chidzatulukapo nchiyani kwa awo amene amatsatira miyambo ya anthu mmalo mwa kumvera zonena Yesu?
15 Nyumba ina inamangidwa pamchenga: ‘Aliyense akamva mawu anga amenewa, ndi kusawachita, adzafanizidwa ndi munthu wopusa, yemwe anamanga nyumba yake pamchenga; ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; ndipo inagwa; ndi kugwa kwake kunali kwakukulukulu.’ Ndi mmene zidzakhalira kwa omwe amati “Ambuye, Ambuye” koma amalephera kuchita zonena Yesu.—Mateyu 7:26, 27.
‘Wosanga Alembi Awo’
16. Kodi panali chiyambukiro chotani kwa omwe anamva Ulaliki wa pa Phiri?
16 Kodi nchiyani chimene chinali chiyambukiro cha Ulaliki wa pa Phiri? ‘Ndipo panakhala pamene Yesu anatha mawu amenewa, makamu a anthu anazizwa ndi chiphunzitso chake: pakuti anawaphunzitsa monga mwini mphamvu, wosanga alembi awo.’ (Mateyu 7:28, 29) Iwo anachititsidwa chidwi zedi ndi munthu amene analankhula ndi mphamvu imene sanaimvepo ndi kale lonse.
17. Kodi alembi anafunikira kuchitanji kuti ayeneretse chiphunzitso chawo, ndipo kodi ananenanji ponena za ngwazi zimene zinafa kale zimene zinagwidwa mawu?
17 Palibe mlembi amene analankhula ndi mphamvu yake, monga mmene cholembera cha m’mbiri ichi chikusonyezera motere: “Alembi analowetsa ukoma m’ziphunzitso zawo kuchokera ku miyambo, ndi atate awo: ndipo palibe ulaliki wa mlembi aliyense umene unali ndi mphamvu kapena phindu, popanda [kuitchula] . . . Arabi ali ndi mwambo, kapena . . . Amuna anzeru amati; kapena miyambo ina yapakamwa ya mtundu woterowo. Hillel Wamkulu anaphunzitsa mowonadi, ndipo popeza kuti mwambo unakhudza chinthu chakutichakuti; ‘Koma, ngakhale kuti anapereka nkhani yoteroyo tsiku lonse, . . . iwo sanalandire chiphunzitso chake, kufikira pomalizira pake anati, Ndinamva tero kwa Shemaia ndi Abtalion [akuluakulu omwe analiko Hillel asanakhale].’” (A Commentary on the New Testament From the Talmud and Hebraica, yolembedwa ndi John Lightfoot) Afarisi anatchuladi ngakhale ngwazi zimene zinafa kale kuti: “Pakamwa pa olungama, pamene munthu wina atchula chiphunzitso cha lamulo lopangidwa ndi iwo—pakamwa pawo pamagwirizana nawo m’manda.”—Torah—From Scroll to Symbol in Formative Judaism.
18. (a) Kodi panali kusiyana kotani pakati pa chiphunzitso cha alembi ndi cha Yesu? (b) Kodi ndim’njira iti mmene chiphunzitso cha Yesu chinali chapadera kwenikweni?
18 Alembi anagwira mawu anthu akufa kale kukhala mphamvu; Yesu analankhula ndi mphamvu yochokera kwa Mulungu wamoyo. (Yohane 12:49, 50; 14:10) Arabi anatunga madzi osayenda kuchokera pa chitsime cholekedwa; Yesu anabweretsa akasupe a madzi abwino amene anathetsa ludzu lamkati. Iye anapemphera ndi kuganizirapo usiku wonse, ndipo pamene analankhula, iye anafotokoza zakuya kwa anthu zimene sanazidziŵepo ndi kale lonse. Iye analankhula ndi mphamvu imene iwo anathadi kuimva, mphamvu imene ngakhale alembi, Afarisi, ndi Asaduki anawopa kuitokosa. (Mateyu 22:46; Marko 12:34; Luka 20:40) Palibe munthu ndi kalelonse amene analankhulapo motere! Pamapeto a ulalikiwo, makamu a anthu anasiidwa ali ozizwa!
19. Kodi njira zina zophunzitsira za Mboni za Yehova lerolino zimafanana motani ndi za Yesu mu Ulaliki wa pa Phiri?
19 Bwanji ponena za lerolino? Monga aminisitala a ku nyumba ndi nyumba, Mboni za Yehova zimagwiritsira ntchito njira yofananayo. Mwininyumba akati: “Tchalitchi changa chimati dziko lapansi lidzatenthedwa lonse ndi moto.” Inu mumayankha kuti: “Baibulo lanu la Revised Nyanja Union Version pa Mlaliki 1:4 limaŵerengedwa motere: ‘Dziko lingokhalabe masiku onse.’” Munthuyo amadabwitsidwa nazo. “Bwanawe, sindinadziŵe kuti zimenezo zinalimo m’Baibulo langa!” Winanso akuti: “Nthaŵi zonse ndimamva kuti ochimwa adzaotchedwa m’moto wa helo.” “Koma Baibulo lanu pa Aroma 6:23 limati: ‘Mphotho yake ya uchimo ndi imfa.’” Kapena pa Utatu kuti: “Mlaliki wanga amati Yesu ndi Atate wake ngofanana.” “Koma pa Yohane 14:28 (New Testament in Modern Chicheŵa) Baibulo lanu limagwira mawu Yesu kukhala akunena kuti: ‘Atate amandiposa.’” Munthu wina akuti kwa inu: “Ndamva kukunenedwa kuti Ufumu wa Mulungu uli mwa munthuwe.” Inu muyankha kuti: “Pa Danieli 2:44 Baibulo lanu limati: ‘M’masiku a mafumu aja Mulungu wakumwamba adzaika ufumu woti sudzaonongeka ku nthawi zonse, . . . koma udzaphwanya ndi kutha maufumu ao onse, nudzakhala chikhalire.’ Kodi ufumuwo ungakhale bwanji mwa inu?”
20. (a) Kodi pali kusiyana kotani pakati pa kuphunzitsa kwa Mboni ndi kwa atsogoleri achipembedzo a Chikristu Chadziko? (b) Kodi ino tsopano ndi nthaŵi ya kuchita chiyani?
20 Yesu analankhula ndi mphamvu yochokera kwa Mulungu. Mboni za Yehova zimalankhula ndi mphamvu ya Mawu a Mulungu. Atsogoleri achipembedzo a Chikristu Chadziko amafotokoza miyambo yachipembedzo yoipitsidwa ndi ziphunzitso zochokera ku Babulo ndi Igupto. Pamene anthu owona mtima akumva zikhulupiriro zawo zikutsutsidwa ndi Baibulo, iwo amazizwitsidwa ndikudzuma kuti: ‘Sindinadziŵe kuti zimenezo zinalimo m’Baibulo langa!’ Koma zirimo. Ino tsopano ndiyo nthaŵi ya odera nkhaŵa zosoŵa zawo zauzimu onse kulabadira zonena Yesu pa Ulaliki wa pa Phiri ndipo mwakutero kumanga pamaziko a thanthwe lolimba.
Mafunso Akubwereramo
◻ Mmalo mwa kupereka chiweruzo, kodi tiyenera kuchitanji, ndipo nchifukwa ninji?
◻ Kodi nchifukwa ninji anthu ambiri lerolino amasankha njira yotakata?
◻ Kodi nchifukwa ninji njira ya Yesu ya kuphunzitsira imamvekera kukhala yosiyana kwambiri ndi ya alembi?
◻ Kodi nchiyani chimene chinali chiyambukiro cha Ulaliki wa pa Phiri kwa amvetseri ake?