Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Ulendo Wachinsinsi ku Yerusalemu
IRI ngululu ya 32 C.E., ndipo Phwando la Misasa liyandikira. Yesu watsekereza ntchito yake makamaka ku Galileya kuyambira pa Paskha wa 31 C.E. pamene Ayuda anayesa kumupha iye. Mwachiwonekere, nthaŵi yokha imene Yesu wachezera ku Yerusalemu kuyambira pamenepo inali kukapezekapo pa mapwando apachaka atatu a Ayuda.
Abale a Yesu tsopano akumufulumiza: “Chokani pano mumuke ku Yudeya.” Yerusalemu uli mzinda waukulu wa Yudeya ndi malo apakati a chipembedzo a dziko lonselo. Abale ake akupereka chifukwa: “Palibe munthu achita kanthu mobisika nafuna yekha kukhala poyera.”
Ngakhale kuti Yakobo, Simoni, Yosefe, ndi Yudase sakukhulupirira kuti mbale wawo wachikulire, Yesu, alidi Mesiya, iwo akumfuna iye kusonyeza mphamvu zake zozizwitsa kwa awo onse osonkhana pa phwandolo. Yesu, ngakhale kuli tero, akudziŵa za ngozi. “Dziko lapansi silingathe kudana ndi inu,” iye akutero, “koma ine lindida popeza ine ndilichitira umboni kuti ntchito zake ziri zoipa.” Chotero Yesu akuuza abale ake: “Kwerani inu kunka ku phwando; sindikwera ku phwando iri tsopano apa.”
Phwando la Misasa liri chikondwerero cha masiku asanu ndi aŵiri, chomwe chimafika ku mapeto ake ndi machitachita osiyanasiyana pa tsiku la chisanu ndi chitatu. Phwandolo limaika chizindikiro cha kutha kwa chaka cha malimidwe ndipo iri nthaŵi ya kusangalala kwakukulu ndi kuyamikira. Masiku angapo pambuyo pa kuchoka kwa abale a Yesu kukapezeka limodzi ndi bungwe lalikulu la oyenda, iye ndi ophunzira ake apita mwachinsinsi, akumakhala mobisika. Iwo atenga msewu wopita kupyola m’Samariya, m’malo mwa umene anthu ambiri amaugwiritsira ntchito pafupi ndi Mtsinje wa Yordano.
Popeza Yesu ndi gulu lake akafunikira malo ogona m’mudzi wa Samariya, iye akutumiza athenga patsogolo pake kukapanga makonzedwe. Anthuwo, ngakhale kuli tero, akukana kuchita chirichonse kaamba ka Yesu pambuyo pa kudziŵa kuti iye akupita ku Yerusalemu. Mopsya mtima, Yakobo ndi Yohane afunsa: “Ambuye, kodi mufuna kuti tiuze moto utsike kumwamba ndi kuwanyeketsa iwo?” Yesu awadzudzula iwo kaamba ka kulingalira chinthu choterocho, ndipo iwo apita ku mudzi wina.
Pamene akuyenda m’mphepete mwa msewu, mlembi anena kwa Yesu: “Mphunzitsi, ine ndidzakutsatani kumene kulikonse mukapitako.”
“Nkhandwe ziri nazo nkhwima, ndi mbalame za kumwamba zisa,” Yesu akuyankha tero, “koma Mwana wa munthu alibe potsamira mutu.” Yesu akusonyeza kuti mlembiyo adzakumana ndi zovuta ngati akhala wotsatira wake. Ndipo chisonyezero chikuwoneka kukhala kuti mlembiyo ali wonyada kwambiri kulandira mkhalidwewu wamoyo.
Kwa munthu wina, Yesu ananena kuti: “Unditsate ine.”
“Mundilole ine, Ambuye, ndithange ndamuka kuika maliro a atate wanga,” munthuyo akuyankha.
“Leka akufa aike akufa a eni okha,” Yesu akuyankha tero, “koma muka iwe nubukitse mbiri yake ya Ufumu wa Mulungu.” Mwachiwonekere atate a mwamunayo sanafe, popeza ngati iwo anafa, chingakhale chosayenera kuti mwana wake angakhale pano kumvetsera kwa Yesu. Mwanayo akufunsa kaamba ka nthaŵi ina kuyembekezera kaamba ka imfa ya atate wake. Iye sali wokonzekera kuika Ufumu wa Mulungu choyamba m’moyo wake.
Pamene anapita pa msewu kulinga ku Yerusalemu, munthu wina anauza Yesu: “Ambuye, ndidzakutsatani inu; koma muthange mwandilola kulawirana nawo a kunyumba kwanga.”
M’kuyankha Yesu akuti: “Palibe munthu wakugwira chikhasu, nayang’ana za kumbuyo, ayenera ufumu wa Mulungu.” Awo amene akakhala ophunzira a Yesu ayenera kuika maso awo pa utumiki wa Ufumu. Monga mmene mzere mowonekera ungakhale wokhota ngati wogwira chikhasu sapitiriza kuyang’ana kutsogolo, choteronso aliyense amene ayang’ana kumbuyo ku dongosolo iri la kachitidwe ka zinthu lakale angakhumudwe pa msewu wotsogolera ku moyo. Yohane 7:2-10; Luka 9:51-62; Mateyu 8:19-22.
◆ Ndani amene ali abale a Yesu, ndipo ndimotani mmene akudzimverera ponena za iye?
◆ Nchifukwa ninji Asamariya ali amwano, ndipo nchiyani chimene Yakobo ndi Yohane anafuna kuchita?
◆ Ndi kukambitsirana kutatu kotani kumene Yesu ali nako pa msewu, ndipo ndimotani mmene iye akugogomezera kufunika kwa utumiki wodzipereka?