Kodi Muli ku Mbali ya Ulamuliro wa Yehova?
“Nenani mwa amitundu, Yehova achita ufumu.”—SALMO 96:10.
1, 2. (a) Kodi n’chinthu chofunika kwambiri chiti chomwe chinachitika cha mu October, m’chaka cha 29 C.E.? (b) Kodi chochitika chimenechi chinali ndi tanthauzo lotani kwa Yesu?
CHA mu October, m’chaka cha 29 C.E. panachitika chinthu chofunika kwambiri chomwe chinali chisanachitikepo ndi kale lonse. Mateyo, amene analemba Uthenga Wabwino, anati: “Atabatizidwa, nthawi yomweyo Yesu anavuuka m’madzimo; pamenepo kumwamba kunatseguka, ndipo Yohane [Mbatizi] anaona mzimu wa Mulungu ukutsika ngati nkhunda kudzatera pa [Yesu]. Ndipo panamvekanso mawu ochokera kumwamba onena kuti: ‘Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwera naye.’” Iyi ndi nkhani imodzi mwa nkhani zochepa zimene anthu onse anayi amene analemba Mauthenga Abwino anafotokoza.—Mateyo 3:16, 17; Maliko 1:9-11; Luka 3:21, 22; Yohane 1:32-34.
2 Kutsanuliridwa kwa mzimu woyera pa Yesu kunam’dziwikitsa kukhala Wodzozedwa, mawu otanthauza Mesiya kapena kuti Khristu. (Yohane 1:33) Apa tsopano, “mbewu” yomwe inakhala ikuyembekezeredwa kwanthawi yaitali inaoneka. Yesu anali munthu amene adzalaliridwa chitende ndi Satana, ndiyeno iye adzalalira mutu wa Satana, yemwe ndi mdani wamkulu wa Yehova ndiponso wa ulamuliro Wake. (Genesis 3:15) Kuyambira nthawi imeneyo, Yesu ankadziwa bwino kuti anafunika kuyesetsa kukwaniritsa cholinga cha Yehova chokhudza ulamuliro ndiponso Ufumu Wake.
3. Kodi Yesu anachita chiyani pokonzekera ntchito yake yolimbikitsa ulamuliro wa Yehova?
3 Pokonzekera ntchito yomwe anali nayo, “Yesu anachoka ku Yorodano atadzazidwa ndi mzimu woyera. Ndipo mzimuwo unamutenga ndi kumuyendetsa uku ndi uku m’chipululu.” (Luka 4:1; Maliko 1:12) Yesu anakhala m’chipululumo masiku 40, ndipo nthawi imeneyi iye anali kuganizira mozama za nkhani ya ulamuliro yomwe Satana anayambitsa ndiponso za zimene Iye anafunika kuchita polimbikitsa ulamuliro wa Yehova. Nkhani imeneyi ikukhudza zolengedwa zonse zanzeru zimene zili kumwamba ndi padziko lapansi. Choncho ndi bwino kuganizira za kukhulupirika kwa Yesu ndi kuona zomwe tiyenera kuchita posonyeza kuti nafenso tikufuna kukhala ku mbali ya ulamuliro wa Yehova.—Yobu 1:6-12; 2:2-6.
Satana Anatsutsa Poyera Ulamuliro wa Yehova
4. Kodi Satana anachita chiyani chomwe chinakhudza kwambiri nkhani ya ulamuliro?
4 N’zodziwikiratu kuti Satana ankaona zinthu zonse zimene tatchulazi. Mosataya nthawi, iye anayamba kulimbana ndi Yesu yemwe ali mbali yofunika kwambiri ya “mbewu” ya ‘mkazi’ wa Mulungu. (Genesis 3:15) Satana anayesa Yesu katatu, ndipo anali kumupempha kuti achite zinthu zimene zinali kuoneka kuti zithandiza Yesuyo m’malo mochita zimene Atate wake ankafuna. Chiyeso chachitatu chinakhudza kwambiri nkhani ya ulamuliro. Atasonyeza Yesu “maufumu onse a padziko ndi ulemerero wawo,” Satana anauza Yesu kuti: “Zinthu zonsezi ndikupatsani ngati mugwada pansi ndi kundilambirako ine.” Popeza kuti Yesu ankadziwa kuti Mdyerekezi ndi amene akulamulira “maufumu onse a padziko,” iye anasonyeza mbali yomwe anali pa nkhani ya ulamuliroyi pamene anayankha kuti: “Choka Satana! Pakuti Malemba amati, ‘Yehova Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira, ndipo utumiki wako wopatulika uyenera kupita kwa iye yekha basi.’”—Mateyo 4:8-10.
5. Kodi ndi ntchito yovuta kwambiri iti imene Yesu anafunika kuchita?
5 Pamoyo wake, Yesu anasonyezeratu kuti cholinga chake chachikulu chinali kulimbikitsa ulamuliro wa Yehova. Iye ankadziwiratu kuti afunika kukhala wokhulupirika mpaka nthawi imene anaphedwa ndi Satana n’cholinga choti asonyeze kuti Mulungu ndiye woyenera kulamulira. Ulosi unanena kuti kuphedwa kumeneku kudzakhala kulalira chitende cha “mbewu” ya mkazi. (Mateyo 16:21; 17:12) Komanso Yesu anafunika kuchitira umboni kuti Ufumu wa Mulungu ndi njira yomwe Yehova adzagwiritse ntchito pogonjetsa Satana ndiponso kubwezeretsa bata ndi mtendere m’chilengedwe chonse. (Mateyo 6:9, 10) Kodi Yesu anachita chiyani kuti akwaniritse ntchito yovuta imeneyi?
“Ufumu wa Mulungu Wayandikira”
6. Kodi Yesu anachita chiyani podziwitsa anthu kuti Ufumu ndi njira imene Mulungu adzagwiritse ntchito ‘powononga ntchito za Mdyerekezi’?
6 Poyamba ntchito yake, “Yesu anapita ku Galileya kukalalikira uthenga wabwino wa Mulungu.” Iye analalikira kuti: “Nthawi yoikika yakwaniritsidwa, ndipo ufumu wa Mulungu wayandikira. Lapani anthu inu, ndipo khulupirirani uthenga wabwino.” (Maliko 1:14, 15) Ndipotu iye anati: ‘Ndiyenera kulengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu . . . chifukwa ndizo anandituma kudzachita.’ (Luka 4:18-21, 43) Yesu anayendayenda m’dziko lonse, “akulalikira ndi kulengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu.” (Luka 8:1) Yesu anachitanso zamphamvu zambiri, monga kudyetsa makamu a anthu, kuthetsa mkuntho, kuchiritsa odwala, ndiponso kuukitsa akufa. Mwa kugwiritsa ntchito zozizwitsa zimenezi, Yesu anatsimikizira kuti Mulungu adzathetsa mavuto onse amene anayamba chifukwa cha kupanduka kwa mu Edene ndi ‘kuwononga ntchito za Mdyerekezi.’—1 Yohane 3:8.
7. Kodi Yesu analangiza otsatira ake kuti achite chiyani, ndipo zotsatira zake zinali zotani?
7 Pofuna kuti uthenga wabwino wa Ufumu ulalikidwe mokwanira, Yesu anasonkhanitsa otsatira ake okhulupirika ndi kuwaphunzitsa ntchitoyi. Choyamba, iye anakonzekeretsa atumwi ake 12 ndi ‘kuwatumiza kukalalikira ufumu wa Mulungu.’ (Luka 9:1, 2) Kenako, anatumiza anthu ena 70 kukalengeza uthenga wakuti: “Ufumu wa Mulungu wayandikira pafupi ndi inu.” (Luka 10:1, 8, 9) Ophunzira amenewa atabwerako ndi kufotokozera Yesu mmene ntchito yolalikira za Ufumu yayendera bwino, iye anati: “Ndinayamba kuona Satana atagwa kale ngati mphezi kuchokera kumwamba.”—Luka 10:17, 18.
8. Kodi Yesu anasonyeza zotani pamoyo wake wonse?
8 Yesu anadzipereka kwambiri pantchito yolalikira za Ufumu ndipo anagwiritsa ntchito mpata uliwonse umene anapeza. Iye anagwira ntchitoyi mwakhama kwambiri, moti analibe nthawi yopeza zinthu zina zofunika pamoyo wake. Iye anati: “Nkhandwe zili nawo mapanga ndipo mbalame za m’mlengalenga zili ndi zisa, koma Mwana wa munthu alibiretu poti n’kutsamiritsa mutu wake.” (Luka 9:58; Maliko 6:31; Yohane 4:31-34) Atatsala pang’ono kuphedwa, iye anafotokoza molimba mtima pamaso pa Pontiyo Pilato kuti: “Chimene ndinabwerera m’dziko, ndicho kudzachitira umboni choonadi.” (Yohane 18:37) Pamoyo wake wonse, Yesu anasonyeza kuti sanangobwera pa dziko lapansi kudzakhala mphunzitsi waluso kapena wochita zinthu zozizwitsa kapenanso kudzakhala Mpulumutsi wodzimana, koma anasonyezanso kuti anabwera kudzalimbikitsa chifuniro cha Yehova chokhudza ulamuliro Wake, ndiponso kudzachitira umboni kuti Mulungu adzakwaniritsa chifuniro chake chimenechi pogwiritsa ntchito Ufumu wake.—Yohane 14:6.
“Zonse Zakwaniritsidwa!”
9. Kodi Satana anatha bwanji kulalira chitende cha “mbewu” ya mkazi wa Mulungu?
9 Satana Mdyerekezi, yemwe ndi Mdani wa Mulungu, sanasangalale ndi zonse zimene Yesu anachita zokhudza Ufumu. Iye mobwerezabwereza anayesa kupha “mbewu” ya mkazi wa Mulungu, pogwiritsa ntchito anthu andale ndiponso achipembedzo, omwe ndi mbali yapadziko lapansi ya “mbewu” yake. Kuchokera pamene Yesu anabadwa mpaka mapeto a moyo wake padziko lapansi, Satana ndiponso anzake analimbana naye kwambiri. Kenako, m’nyengo ya masika m’chaka cha 33 C.E., nthawi inafika yoti Mwana wa munthu aperekedwe kwa Mdani wa Mulungu n’cholinga choti amulalire chitende. (Mateyo 20:18, 19; Luka 18:31-33) Mauthenga Abwino amasonyeza mmene Satana anagwiritsira ntchito anthu, monga Yudasi Isikarioti, ansembe aakulu, alembi, Afarisi ndiponso Aroma, kuti atsutse Yesu ndi kuchititsa kuti afe imfa yowawa pamtengo wozunzikirapo.—Machitidwe 2:22, 23.
10. Paimfa yake pamtengo wozunzikirapo, kodi Yesu anakwaniritsa chinthu chofunika kwambiri chiti?
10 Kodi n’chiyani chimabwera m’maganizo mwanu mukaganizira za Yesu akufa mozunzika kwambiri pamtengo wozunzikirapo? Mwina mumakumbukira za nsembe ya dipo imene Yesu anapereka mwachikondi m’malo mwa anthu ochimwa. (Mateyo 20:28; Yohane 15:13) Mwinanso mumachita chidwi ndi kukula kwa chikondi chimene Yehova anasonyeza popereka nsembe imeneyi. (Yohane 3:16) N’kutheka kuti mumamva ngati mmene mkulu wa asilikali achiroma anamvera pamene ananena kuti: “Ndithudi uyu analidi Mwana wa Mulungu.” (Mateyo 27:54) M’poyenera kumva choncho. Komabe, kumbukirani mawu omalizira a Yesu ali pa mtengo wozunzikirapo. Iye anati: “Zonse zakwaniritsidwa!” (Yohane 19:30) Kodi n’chiyani chimene chinakwaniritsidwa? Yesu anakwaniritsa zinthu zambiri pamoyo wake ndiponso paimfa yake, koma chinthu chachikulu chimene iye anabwerera pa dziko lapansi ndicho kusonyeza kuti Yehova ndiye ali woyenera kulamulira. Ndiponso ulosi unali utanena kale kuti Yesu monga “mbewu,” adzazunzidwa kwambiri ndi Satana n’cholinga choti achotse chitonzo padzina la Yehova. (Yesaya 53:3-7) Udindo umenewu unali waukulu kwambiri, komatu Yesu anaukwaniritsa bwinobwino. Zimenezi n’zochititsa chidwi kwambiri.
11. Kodi Yesu adzachita chiyani pokwaniritsa ulosi wa m’munda wa Edene?
11 Chifukwa choti anali wokhulupirika, Yesu anaukitsidwa monga “mzimu wopatsa moyo,” osatinso monga munthu. (1 Akorinto 15:45; 1 Petulo 3:18) Yehova analonjeza Mwana wake wolemekezekayu kuti: “Khalani pa dzanja lamanja langa, kufikira nditaika adani anu chopondapo mapazi anu.” (Salmo 110:1) ‘Adaniwa’ akuphatikizapo Satana yemwe ndi wotsutsa wamkulu, ndiponso ena onse amene ali mbali ya “mbewu” yake. Monga Mfumu ya Ufumu wa Mesiya wa Yehova, Yesu Khristu adzatsogolera ntchito yowononga adani onse a Mulungu, kumwamba ndi padziko lapansi. (Chivumbulutso 12:7-9; 19:11-16; 20:1-3, 10) Akadzatero, ulosi wa pa Genesis 3:15 ndiponso pemphero limene Yesu anaphunzitsa otsatira ake zidzakwaniritsidwa. Iye anawaphunzitsa kupemphera kuti: “Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chomwechonso pansi pano.”—Mateyo 6:10; Afilipi 2:8-11.
Yesu Anatisiyira Chitsanzo
12, 13. (a) Kodi masiku ano anthu akulabadira motani uthenga wabwino wa Ufumu? (b) Pankhani yotsatira mapazi a Khristu, kodi tiyenera kuganizira za chiyani?
12 Masiku ano, uthenga wabwino wa Ufumu ukulalikidwa m’mayiko ambiri, mogwirizana ndi mmene Yesu analoserera. (Mateyo 24:14) Izi zachititsa kuti anthu ambiri adzipereke kwa Mulungu. Iwo akusangalala chifukwa cha madalitso amene Ufumu wa Mulungu udzabweretsa. Akuyembekezera kudzakhala kwamuyaya mumtendere ndiponso motetezeka m’dziko lapansi laparadaiso, ndipo amasangalala kufotokozera ena za chiyembekezo chawo. (Salmo 37:11; 2 Petulo 3:13) Kodi inuyo mukulengeza nawo za Ufumuwu? Ngati mukutero mukuchita bwino kwambiri. Komatu, pali mfundo ina imene tonsefe tikufunika kuiganizira.
13 Mtumwi Petulo analemba kuti: “Khristu anavutika chifukwa cha inu, kukusiyirani chitsanzo kuti mutsatire mapazi ake mosamalitsa.” (1 Petulo 2:21) Taonani kuti palembali, Petulo anatchula za kuvutika kwa Yesu, osati changu chake pantchito yolalikira kapena luso lake pophunzitsa. Popeza kuti Petulo anali mboni yoona ndi maso, iye ankadziwa kuti Yesu anali wokonzeka kuvutika n’cholinga cholimbikitsa ulamuliro wa Yehova ndiponso kuonetsa kuti Satana ndi wabodza. Ndiyeno, kodi tingatsatire bwanji mapazi a Yesu? Tiyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndine wokonzeka motani kuvutika n’cholinga cholimbikitsa ndi kukweza ulamuliro wa Yehova? Kodi khalidwe langa ndiponso changu changa muutumiki zimasonyeza kuti chinthu chachikulu m’moyo wanga ndi kulimbikitsa ulamuliro wa Yehova?’—Akolose 3:17.
14, 15. (a) Yesu anatani atapatsidwa malangizo olakwika ndiponso pamene anthu ankafuna kum’chitira zinthu zolakwika, ndipo n’chifukwa chiyani anatero? (b) Kodi ndi nkhani iti imene tiyenera kuikumbukira nthawi zonse? (Phatikizanipo ndemanga za m’bokosi lakuti “Imani ku Mbali ya Yehova.”)
14 Tsiku ndi tsiku timakumana ndi mavuto ndiponso timafunika kusankha zochita kaya pankhani zazikulu kapena zazing’ono. Kodi n’chiyani chimene chiyenera kutithandiza kuona zimene tingachite? Mwachitsanzo, kodi timatani tikamayesedwa kuti tichite zinthu zimene zingawononge moyo wathu wauzimu? Petulo atauza Yesu kuti adzikomere mtima, kodi Yesu anatani? Iye anati: “Ndichokere, Satana!” Ndipo anapitiriza ndi kuti: “Zimene umaganiza si maganizo a Mulungu, koma maganizo a anthu.” (Mateyo 16:21-23) Nanga bwanji tikapatsidwa mwayi wopeza chuma kapena kupititsa patsogolo luso lathu, zimene tikudziwa kuti zingawonongetse moyo wathu wauzimu, kodi timachita ngati mmene Yesu anachitira? Yesu atadziwa kuti anthu amene anaona zozizwitsa zake “akufuna kum’gwira kuti amulonge ufumu,” iye anawathawa mwamsanga.—Yohane 6:15.
15 Kodi n’chifukwa chiyani Yesu anachita zimenezi panthawiyi ndiponso panthawi zina? Anatero chifukwa chakuti ankadziwa kuti nkhani zoterezi zinkakhudzanso nkhani yofunika kwambiri, osati ubwino wake wokha. Iye ankafuna kuchita chifuniro cha Atate wake ndiponso kulimbikitsa ulamuliro wa Yehova, zivute zitani. (Mateyo 26:50-54) Motero, ngati nafenso sitiganizira nkhani ya ulamuliro wa Yehova nthawi zonse, ngati mmene Yesu ankachitira, n’zotheka kugonja kapena kulephera kuchita zinthu zolungama. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chakuti tingagonje mosavuta ku machenjera a Satana, yemwe ndi katswiri popangitsa zinthu zoipa kuoneka ngati zabwino. Izi n’zimene anachita ponyenga Hava.—2 Akorinto 11:14; 1 Timoteyo 2:14.
16. Kodi cholinga chathu chachikulu pothandiza anthu ena chiyenera kukhala chotani?
16 Tikakhala mu utumiki timayesetsa kulankhula ndi anthu za nkhawa zawo ndiponso timawasonyeza zimene Baibulo limanena. Imeneyi ndi njira yabwino kwambiri yothandizira anthu kukhala ndi chidwi chophunzira Baibulo. Komabe, cholinga chathu chachikulu sikuti ndi kungowathandiza kudziwa zimene Baibulo limanena kapena madalitso amene Ufumu wa Mulungu udzabweretsa. Tiyenera kuwathandiza kumvetsa nkhani ya ulamuliro wa Yehova. Kodi iwo n’ngokonzeka kukhala Akhristu oona ndi kunyamula ‘mtengo wawo wozunzikirapo’ ndi kuvutikira Ufumu wa Mulungu? (Maliko 8:34) Kodi n’ngokonzeka kukhala ku mbali ya anthu amene akulimbikitsa ulamuliro wa Yehova ndi kusonyeza kuti Satana ndi wabodza ndiponso wamiseche? (Miyambo 27:11) Ndi mwayi waukulu kwambiri kukhala ku mbali ya Yehova ndiponso kuthandiza anthu ena kuchita chimodzimodzi.—1 Timoteyo 4:16.
Mulungu Akadzakhala “Zinthu Zonse kwa Aliyense”
17, 18. Ngati timasonyeza kuti tili ku mbali ya ulamuliro wa Yehova, kodi tingayembekezere nthawi yosangalatsa iti?
17 Panopa, tikamayesetsa kuti khalidwe lathu ndiponso zimene timachita mu utumiki zizisonyeza kuti tili ku mbali ya ulamuliro wa Yehova, tingayembekezere nthawi yomwe Yesu Khristu “adzapereka ufumu kwa Mulungu wake ndi Atate wake.” Kodi zimenezi zidzachitika liti? Mtumwi Paulo anati: “Atathetsa maboma onse, ulamuliro wonse, ndi mphamvu zonse. Pakuti ayenera kulamulira monga mfumu kufikira Mulungu ataika adani onse pansi pa mapazi ake. . . . Mwanayonso adzadziika pansi pa Uyo amene anaika zinthu zonse pansi pake, kuti Mulungu akhale zinthu zonse kwa aliyense.”—1 Akorinto 15:24, 25, 28.
18 Zinthu zidzakhala zosangalatsa kwambiri Mulungu akadzakhala “zinthu zonse kwa aliyense.” Nthawi imeneyo, Ufumu udzakhala utakwaniritsa cholinga chake, ndipo sipadzakhalanso wina aliyense wotsutsa ulamuliro wa Yehova. M’chilengedwe chonse mudzakhalanso bata ndi mtendere. Mofanana ndi mawu a wamasalmo, chilengedwe chonse chidzaimba kuti: “M’patseni Yehova ulemerero wa dzina lake . . . Nenani mwa amitundu, Yehova achita ufumu.”—Salmo 96:8, 10.
Kodi Mungayankhe?
• Kodi Yesu anasonyeza motani kuti nkhani ya ulamuliro wa Mulungu inali yofunika kwambiri kwa iye?
• Kodi Yesu anakwaniritsa chinthu chofunika kwambiri chiti muutumiki wake ndiponso paimfa yake?
• Kodi tingatsatire motani chitsanzo cha Yesu posonyeza kuti tili ku mbali ya ulamuliro wa Yehova?
[Bokosi/Zithunzi patsamba 29]
IMANI KU MBALI YA YEHOVA
Abale ambiri m’dziko la Korea ndiponso m’mayiko ena akudziwa kuti Akhristu akamakumana ndi mayesero oopsa, zimathandiza kwambiri kuganizira chimene chikuchititsa mayeserowo.
M’bale wina amene anaikidwa m’ndende mu ulamuliro wa boma lakale la Soviet anati: “Kumvetsa nkhani yomwe inayambika m’munda wa Edene yokayikira ulamuliro wa Mulungu ndiko kunatithandiza kuti tipirire. . . . Tinadziwa kuti tili ndi mwayi wokhala ku mbali ya ulamuliro wa Yehova. . . . Izi zinatithandiza kukhala olimba ndiponso kukhalabe okhulupirika.”
M’bale wina anafotokozanso zimene zinawathandiza ali m’ndende. Iye anati: “Yehova anatithandiza. Ngakhale kuti tinkavutika, tinali ogalamuka mwauzimu. Tinkakumbutsana kuti taima ku mbali ya Yehova pankhani yokhudza ulamuliro wachilengedwe chaponseponse, ndipo tinkalimbikitsana pochita zimenezi.”
[Chithunzi patsamba 26]
Kodi Yesu analimbikitsa motani ulamuliro wa Yehova pamene ankayesedwa ndi Satana?
[Chithunzi patsamba 28]
Kodi imfa ya Yesu inakwaniritsa chiyani?