Lingaliro la Baibulo
Ziwonetsero za Kusakondwa ndi Zisonyezero za Kuipidwa Kodi Zingasinthe Dziko?
“TIYENERA Kulankhula Poyera, Tiyenera Kusonyezera Kuipidwa m’Makwalala.” Unatero mutu wa nkhani ya mkonzi mu National Catholic Reporter, nyuzipepala ya Roma Katolika, mwamsanga nkhondo ya ku Persian Gulf isanaulike mu 1991. Ikumasonkhezera oŵerenga kukhala ndi phande m’maligubo ndi zisonyezero za kuipidwa zabata kuzungulira United States yense, nkhani ya mkonziyo inapitirizabe kuti: “Kudzafunikira anthu mamiliyoni ambiri ndi zoyesayesa zosalekeza zaphamphu kuti mtendere ukhomerezedwe muumbuli ndi kudzitukumula kwa boma limeneli. . . . Anthu ayenera kusonyezera kuipidwa m’makwalala.”
Zifunsiro za kuchitapo kanthu zoterozo zimamvedwa mwakaŵirikaŵiri lerolino. Pokhala pali mavuto ambiri andale, achuma, amalo okhala owopseza zokomera anthu chotero, anthu amalingalira kukhala okakamizidwa “kusonyezera kuipidwa m’makwalala” m’ziwonetsero za kusakondwa, michezo, ndi zisonyezero za kuipidwa. Zifukwa zimayambira pa kuletsa upandu wa m’chitaganya kufikira kukukhazikitsa mtendere wa dziko lonse. Mokondweretsa, zambiri za zisonyezero za kuipidwa zimenezi zimakhala ndi chivomerezo cha magulu atchalitchi ndi atsogoleri achipembedzo.
Komabe, kodi kuli koyenera kwa Akristu kuphatikizidwa m’zisonyezero za kuipidwa zoterozo? Ndipo kodi ziwonetsero za kusakondwazo—kaya zikhale mumpangidwe wa maligubo aphokoso kapena wa michezo makendulo atayatsidwa—zimasinthadi dziko kukhala labwinopo?
Zisonyezero za Kuipidwa—Lingaliro Lachikristu
Zisonyezero za kuipidwa zafotokozedwa ndi katswiri wa zamakhalidwe wina kukhala “mtundu wogwira mtima mwapadera wa chisonyezero chandale zadziko . . . chosonkhezera maulamuliro amene angodzikhalira popanda kuchitapo kanthu kuti achitepo kanthu moyenerera.” Inde, awo amene amaguba mowonetsera kusakondwa kapena amene amachita zisonyezero za kuipidwa kaŵirikaŵiri amatero akumayembekezera kuti zoyesayesa zawo zakhama zingawongolere zisalungamo ndi chivundi zowonedwa m’madongosolo amakhalidwe ndi andale zadziko amakono.
Komabe, kodi nchitsanzo chotani, chimene Yesu Kristu anasiira otsatira ake? Yesu anakhalako panthaŵi pamene anthu Achiyuda anadzipeza kukhala anali pansi pa nkhalwe za Ulamuliro Wachiroma. Mwachiwonekere, mpumulo kugoli lotsendereza Lachiroma unalakalakidwa kwambiri ndi anthuwo. Komabe, Yesu sanalimbikitse konse otsatira ake kupanga chiwonetsero, kuguba mowonetsera kusakondwa, kapena kuphatikizidwa mwandale m’njira iriyonse. Mosiyana, iye mobwerezabwereza ananena kuti ophunzira ake “siali a dziko lapansi.”—Yohane 15:19; 17:16; wonaninso Yohane 6:15.
Mofananamo, pamene mosayenerera Yesu anali kugwidwa ndi akuluakulu aboma, iye sanayese kuyambitsa chiwonetsero cha kusakondwa, ngakhale kuti iye mosakaikira akanatero akanasankha kutero. Mmalo mwake, iye anauza wolamulira Wachiroma kuti: “Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi; ufumu wanga ukadakhala wa dziko lino lapansi, anyamata anga akadalimbika nkhondo, kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda; koma tsopano ufumu wanga suli wochokera konkuno.” (Yohane 18:33-36) Atayang’anizana ndi mkangano, Yesu anapewa mchitidwe uliwonse wa kuwonetsera kusakondwa, akumadziŵa kufunika kwa kusakhala ndi mbali iriyonse ya zochita zandale. Ndipo analimbikitsa otsatira ake kuchita chimodzimodzi.
Chifukwa chake, kuphatikizidwa m’zisonyezero za kuipidwa, kukakhala kuswa lamulo lamakhalidwe abwino lalikulu la uchete Wachikristu wophunzitsidwa ndi Yesu. Zoposa zimenezo, kuphatikizidwa koteroko kungatsogolere ngakhale kumkhalidwe wina wosakhala Wachikristu. Motani? Zisonyezero za kuipidwa zolinganizidwira zifuno zabwino kaŵirikaŵiri zimakhala ndi mzimu wopandukira modzifunira, ophatikizidwawo akumachita chipolowe, kutukwana, kapena chiwawa. Kuphatikizidwa m’machitidwe ododometsa kuyenda kwazinthu kosalolekako kungapeze chisamaliro, koma nkosagwirizana kwambiri ndi chichizo la Baibulo la ‘kumvera maulamuliro akulu’ ndi ‘kukhala ndi mtendere ndi anthu onse.’ (Aroma 12:18; 13:1) Mmalo mwa kulimbikitsa kusamvera kwa nzika, Baibulo limalimbikitsa Akristu kusunga mayendedwe awo kukhala abwino pakati pa amitundu ndi kukhalabe ogonjera maboma aumunthu, ngakhale ngati olamulirawo ali ovuta kukondweretsa kapena ali osalingalira.—1 Petro 2:12, 13, 18.
‘Komatu sizisonyezero za kuipidwa zonse zimene ziri zaupandu kapena zachiwawa,’ ena angatero. Nzowona, ndipo zisonyezero za kuipidwa zina zimawonekeradi kukhala ndi zotulukapo zabwino. Koma kodi ziwonetsero za kusakondwazo—ngakhale ngati ziri zamtendere ndi zochitidwira chifukwa chabwino—zingasinthedi dziko kukhala labwinopo?
Kodi Zingasinthe Dziko?
Akristu amadera nkhaŵa kwambiri anansi awo ndipo amafuna kuŵathandiza. Koma kodi kuphatikizidwa m’zisonyezero za kuipidwa ndikodi njira yabwino kopambana yoperekera chithandizo? Bukhulo Demonstration Democracy likufotokoza kuti: “Nzochepa kwambiri zimene zingachitidwe ndi chiŵiya chirichonse cha chisonyezero chandale zadziko.” Mosakanika, kuthetsa masoka oyang’anizana ndi anthu kumafunikira masinthidwe amene sangakwaniritsidwe ndi kuwonetsera kusakondwa kulikonse kapena kuguba.
Yesu analankhula mfundo yofananayo pofotokoza dongosolo lachipembedzo lazaka mazana ambiri la m’tsiku lake. Ponena za dongosolo lonyenga la kulambira kochitidwa ndi Afarisi limenelo, iye anati: ‘Ndipo kulibe munthu aphathika chigamba cha nsalu yaiwisi pa chofunda chakale; pakuti chigamba chake chizomoka ku chofundacho, ndipo chichita chibowo chachikulu.’ (Mateyu 9:16) Kodi Yesu anali kutanthauzanji? Kuti Chikristu chowona sichingathe kugwirizana ndi madongosolo oipa othaitha amene anali pafupi kutaidwa. Iye anazindikira kuti kuika chigamba pa dongosolo lopanda ntchito kukanakhala kopanda pake.
Zirinso chimodzimodzi ndi dongosolo ladziko limene lagonjetsera anthu ku chisalungamo, nkhalwe, ndi chitsenderezo kwazaka mazana ambiri. Mlaliki 1:15 amalongosola mwachindunji kuti: ‘Chokhotakhota sichingawongokenso.’ Inde, dongosolo ladziko lamakono silingawongokenso, mosasamala kanthu za zoyesayesa zabwino kopambana. Kulekeranji? Chifukwa chakuti, monga momwe 1 Yohane 5:19 amanenera, “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo,” Satana Mdyerekezi. Yesu anasonya kwa ameneyo kukhala “mkulu wa dziko ili lapansi.” (Yohane 12:31) Malinga ngati dongosolo iri ligwirabe ntchito pansi pa chisonkhezero cha Satana, palibe mlingo wa kuika chigamba umene udzabweretsa mpumulo wokhalitsa.
Zimenezi sizikutanthauza kuti Akristu amanyalanyaza mavuto adziko kapena ali osafunitsitsa kuchitapo kanthu motsimikiza. Kwenikweni, Akristu akuuzidwa kukhala okangalika kwambiri, osati m’ziwonetsero za kusakondwa, koma m’ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu—boma la Ufumu lenilenilo limene Yesu anaphunzitsa otsatira ake kupempherera. (Mateyu 6:10; 24:14) Baibulo limasonyeza kuti Ufumuwo sudzayesa kuwongolera dziko losasinthikali; udzathetseratu maboma oipa ndi madongosolo a anthu amene tsopano amatsendereza anthu ndi kuwalowetsa m’malo ndi dongosolo limene lingayambitse chiweruziro chenicheni ndi chilungamo padziko lonse lapansi. (Danieli 2:44) Pansi pa dongosolo loterolo, palibe aliyense amene adzafunikira kuguba mowonetsera kusakondwa pakuti Yehova Mulungu, amene ‘akukwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chawo,’ adzatsimikiziranso kuti zosoŵa zathu zonse zapezedwa kotheratu.—Salmo 145:16.
[Mawu a Chithunzi patsamba 30]
Sitalaka ya antchito, Leslie’s