Yehova Amafunikira Chitamando Chosatha
“Masiku onse ndidzakudalitsani, ndipo ndidzatamanda dzina lanu ku nthaŵi za nthaŵi, ngakhale kosatha.”—SALMO 145:2, “NW.”
1. Kodi nchifukwa ninji Davide anali ndi zifukwa zambiri zotamandira Yehova?
DAVIDE mtumiki wokhulupirika wa Yehova adali ndi zifukwa zambiri zotamandira Mulungu. Mfumu yotchukayi ya Israyeli wakalekale inadziŵa ukulu ndi ubwino wa Yehova ndipo inazindikira kuti ufumu Wake unali wosatha. Wam’mwambamwambayo anayenerera kutamandidwa kaamba ka kukwaniritsa zokhumba chamoyo chonse ndi kutambasulira chifundo kwa atumiki ake okhulupirika.
2. (a) Kodi Salmo 145 yakonzekeredwa motani? (b) Kodi tidzalingalira mafunso otani?
2 Davide anapereka chitamando choterocho kwa Mulungu m’Salmo la 145. Vesi lirilonse la salmo la ndakatuloli limayamba ndi chilembo chatsatanetsatane cha alifabeti Yachihebri, chinkana kuti chilembo chimodzi (nun) chinasiidwa. Makonzedwe a ndakatulowa angakhale anatumikira monga zothandizira kukumbukira. Salmo 145 limakweza Yehova, monga m’mawu awa: “Masiku onse ndidzakudalitsani, ndipo ndidzatamanda dzina lanu ku nthaŵi za nthaŵi, ngakhale kosatha.” (Salmo 145:2, NW) Koma kodi salmoli lingatiyambukire motani ife? Kodi ingachitenji kaamba ka unansi wathu ndi Mulungu? Kuti tipeze mayankho, choyamba tiyeni tilingalire vesi 1 mpaka 10.
Ukulu wa Yehova Ngwosasanthulika
3. Mofanana ndi Davide, kodi timafunikira kuchitanji kwa ‘Mulungu wathu, Mfumu,’ ndipo nchifukwa ninji?
3 Davide anali mfumu, koma anavomereza kulamulira kwa Yehova pa iye, naati: ‘Ndidzakukwezani Mulungu wanga, Mfumu; ndipo [ndidzadalitsa, “NW”] dzina lanu ku nthaŵi za nthaŵi.’ (Salmo 145:1) Ndi ulemu wofananana ndi uwu, Mboni za Yehova zimakweza dzina la Mulungu ndikumlemekeza padziko lonse lapansi. Moyo wathu umalemeretsedwa pamene tikhalamo ndi phande m’ntchito yoteroyo. Mofanana ndi Davide, timayenera kusonyeza chimvero ndi chigonjero kwa Yehova monga ‘Mulungu wathu, Mfumu.’ Ndipo tingalekerenji kutero? Pakuti iye ndiye ‘Mfumu ya nthaŵi zosatha.’ (Chibvumbulutso 15:3) Ndiponso, Davide Wamkulu, Yesu Kristu, yemwe wakhala akulamulira pa Phiri la Ziyoni lakumwamba chiyambire 1914, amatisonyeza chitsanzo chabwino koposa cha kugonjera kwa Yehova, Mfumu Yosatha.
4. Kodi ‘tingalidalitse motani dzina la Mulungu’?
4 Davide anati akatha ‘kudalitsa dzina la Mulungu.’ Kodi uku kungatheke bwanji kwa munthu wamba? Eya, kuphatikiza pa zinthu zina, kudalitsa munthu wina kumatanthauza kumthokoza. Kudalitsa dzina la Mulungu kumasonyeza kuti ife tiri ndi chikondi champhamvu kwa iye ndi dzina lake loyera lakuti, Yehova. Sitimadandaula naye Mulungu, sitimafunafuna zophophonya kwa iye, sitimakaikira ubwino wake. Pokhapo titakhala ndi mkhalidwe umenewo, titapanga kudzipereka kwa Yehova, ndi kusunga umphumphu monga Mboni zake zobatizidwa mpamene tinganene monga mmene ananenera Davide kuti ife ‘tidzadalitsa dzina la Mulungu ku nthaŵi za nthaŵi.’ Titakhalabe m’chikondi cha Mulungu, tidzalandira mphatso ya moyo wosatha ndipo motero tidzakhala okhoza kudalitsa Yehova ku nthaŵi zosatha.—Yuda 20, 21.
5. Kodi kukhumba kudalitsa Yehova “masiku onse” kuyenera kukhala ndi chiyambukiro chotani pa ife?
5 Ngati timamkondadi Mpatsi wathu wa Moyo, tidzanena momwe ananenera Davide kuti: “Masiku onse ndidzakudalitsani, ndipo ndidzatamanda dzina lanu ku nthaŵi za nthaŵi, ngakhale kosatha.” (Salmo 145:2, NW) Ha tsiku likakhala logwetsa ulesi chotani nanga litapita popanda kudalitsa Mulungu! Tisakhaletu otanganitsidwa kwenikweni kapena akuda nkhaŵa kwambiri ndi zinthu zakuthupi kwakuti tilephere kuthokoza Atate wathu wakumwamba kapena kupemphera kwa iye tsiku lirilonse. Yesu anatanthauza kuti tiyenera kupemphera tsiku lirilonse pamene anati m’pemphero lake lachitsanzo: ‘Tipatseni ife tsiku ndi tsiku chakudya cha patsiku.’ (Luka 11:3) Ambiri muutumiki wa nthaŵi zonse akutamanda Mulungu tsiku lirilonse pamene akulowa muuminisitala Wachikristu. Koma uliwonse umene ungakhale mkhalidwe wathu, mtima wathu uyenera kutifulumiza kutamanda Mulungu m’njira inayake tsiku lirilonse. Ndipo tangolingalirani anthuni! Monga Mboni zodzipereka za Yehova zokhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha, ife tiri ndi chiyembekezo choposapo cha kutamanda dzina lake kosatha.—Yohane 17:3.
6. Kodi nchifukwa ninji Yehova ‘amayenerera kutamandidwa kwakukulu’?
6 Indetu ife tiri ndi chifukwa cha kutamandira Mulungu tsiku lonse, pakuti Davide anawonjezera kuti: ‘Yehova ndi wamkulu, nayenera [kutamandidwa, “NW”] kwakukulu; ndi ukulu wake ngwosasanthulika.’ (Salmo 145:3) Yehova ngwamkuludi kwakuti ngwosalingana ndi chinthu kapena munthu aliyense, ndipo ulamuliro wake ngwa iye yekha. Nebukadinezara, mfumu ya ku Babulo anathadi kuvomereza motere: ‘Palibe woletsa dzanja lake [la Mulungu], kapena wakunena naye, Muchitanji?’ (Danieli 4:34, 35) Yehova “ayenera amuope koposa milungu yonse.” (Salmo 96:4) Nkosadabwitsa kuti iye ‘ayenera kutamandidwa kwakukulu.’ Eya, palibetu mawu achitamando omwe angakhale opatulika kwenikweni kwakuti nkusamthokozera nawo Yehova! Iye ngwoyenerera chitamando chopanda polekezera, cha kunthaŵi zosatha.
7. Kodi nchiyani chimene chimatsimikizira kuti ‘ukulu wa [Mulungu] ngwosasanthulika’?
7 “Ukulu [wa Yehova] ngwosasanthulika.” Mosasamala kanthu za ukulu wa thupi lake, ukulu wake umatsimikiziridwa ndi mtundu umene Mulungu ameneyu aliri. Inde, zinthu zimene wazilenga nzodabwitsa zedi kwa ife kuzizindikira, ndipotu anthufe ‘tinapangidwanso modabwitsa.’ (Salmo 139:14; Yobu 9:10; 37:5) Ndiponso, Yehova Mulungu mwiniyekhayo amachita zinthu zake mozizwitsa chotani nanga! Iye amasunga malonjezo ake mokhulupirika ndikuvumbula zifuno zake mwachikondi. Komabe, sitidzadziŵapo zinthu zonse za Mulungu. Kupyola kunthaŵi zosatha, tidzakhala okhoza kukulitsa kumdziŵa kwathu, kudziŵa chilengedwe chake, ndi zifuno zake.—Aroma 11:33-36.
Thokozani Ntchito za Yehova
8. (a) Kodi ndimotani mmene ‘mbadwo ndi mbadwo’ wathokozera ntchito za Yehova? (b) Ngati tiphunzitsa ana athu ponena za ntchito ndi zochita za Yehova, kodi iwo mwachidziŵikire adzakulingalira motani kumlambira iye? (c) Monga “mbadwo” wachisangalalo, kodi otsalira odzozedwa achitanji?
8 Zambiri zinganenedwe kutamanda Mulungu wathu wamkulu wosasanthulika kwakuti Davide anafulumizidwa kunena kuti: “Mbadwo wina udzathokozera ntchito zanu mbadwo unzake, ndipo udzalalikira zamphamvu zanu.” (Salmo 145:4, NW) Mibadwo yotsatizana ya anthu yathokoza ntchito za Yehova ndi kusimba za ntchito zake zamphamvu. Ha ndi mwaŵi wotani nanga kusimba zinthu izi kwa anthu amene timatsogozako maphunziro Abaibulo apanyumba! Mwachitsanzo, tingawafotokozere kuti Mulungu ndiye analenga zinthu zonse. (Genesis 1:1–2:25; Chibvumbulutso 4:11) Tingalankhule za ntchito zake zamphamvu panthaŵi imene anapulumutsa Aisrayeli kutuluka muukapolo wa ku Igupto, mmene anawathandizira kugonjetsa adani Achikanani, mmene anapulumutsira mtunduwo kusafa m’Perisiya wakale, ndi zina zambiri. (Eksodo 13:8-10; Oweruza 4:15; Estere 9:15-17) Ndipo kodi sitikufulumizidwa kufotokozera ana athu ponena za ntchito ndi zochita za Yehova? Ngati tapatsa mbadwa zathu malangizo oterewa ndipo ngati iwo atiwona ife tikutumikira Mulungu mwachisangalalo, mwachidziŵikire iwo adzazindikira kuti kumlambira nkosangalatsa ndipo adzakula ndi ‘chimwemwe cha Yehova monga mphamvu yawo.’ (Nehemiya 8:10; Salmo 78:1-4) Otsalira odzozedwa amapanga “mbadwo” umodzi wa Mboni za Yehova wosangalala umene umathokoza ntchito za Mulungu kwa ‘khamu lalikulu,’ mbali ina ya mbadwo umene udzalowa m’Paradaiso wa padziko lapansi.—Chibvumbulutso 7:9.
9. Pamene tiwona ntchito ndi zochita zazikulu za Mulungu, kodi tingakhale otsimikizira chiyani?
9 Pamene tiwona ntchito ndi zochita zamphamvu za Mulungu, timakhutiritsidwa kwenikweni kuti ‘Yehova sadzasiya anthu ake chifukwa cha dzina lake lalikulu.’ (1 Samueli 12:22; Salmo 94:14) Pamene tiyang’anizana ndi ziyeso, nsautso, ndi chizunzo, ife tingathe kukhala abata ndikudalira kuti “mtendere wa Mulungu” udzasunga mitima ndi maganizo athu. (Afilipi 4:6, 7) Chotero nkoyenera chotani nanga kuti tifotokozere ena ponena za Atate wathu wakumwamba wachikondi, wotetezera!
10. Kodi ‘ntchito zodabwitsa’ za Yehova zimaphatikizapo chiyani, ndipo kodi timapindula motani ndi kusinkhasinkha pa izo?
10 Tiyenera kupeza nthaŵi ya kusinkhasinkha pa ukulu ndi ntchito za Yehova, pakuti Davide anawonjezera kuti: ‘Ndidzalingalira ulemerero waukulu wa ulemu wanu, ndi ntchito zanu zodabwitsa.’ (Salmo 145:5) Ulemu wa Mulungu ngwowopsya ndipo ngwosalingana ndi uliwonse. (Yobu 37:22; Salmo 148:13) Chotero, Davide anapanga ulemerero waukulu wa ulemu wa Yehova kukhala chinthu chochilingalira iye. Wamasalmoyu analingaliranso nkhani zokhudza ‘ntchito zodabwitsa’ za Mulungu. Izi zimaphatikiza kusonyezedwa kwa chilungamo chaumulungu mwa kuwononga ochimwa ndi kupulumutsa opembedza, monga zomwe zinachitika pa Chigumula. (Genesis 7:20-24; 2 Petro 2:9) Kusinkhasinkha pa nkhanizi kumalimbitsa unansi wathu ndi Yehova ndikutitheketsa kufotokozera ena ponena za ulemu wake ndi ntchito zake zodabwitsa. M’masiku 40 okhala m’chipululu, Yesu analimbitsidwa kutsutsa chiyeso mwa kusinkhasinkha pa zinthu zimene m’mwamba motseguka munavumbula kuti azilingalire. (Mateyu 3:13–4:11) Pambuyo pake iye anafotokozera ena ponena za ulemu ndi ntchito zodabwitsa za Yehova.
11. (a) Kodi nchifukwa ninji mantha anagwera nzika za Yeriko? (b) Kodi Mboni za Yehova zimafotokoza za ‘zowopsya za Mulungu’ ndi ‘ukulu’ wake ndi mzimu wotani?
11 Pamene tilankhula za ulemu ndi ntchito za Mulungu, timafulumiza ena kuzifotokoza. Davide anati: ‘Ndipo adzanenera mphamvu za ntchito zanu zowopsya; ndi ukulu wanu ndidzaufotokozera.’ (Salmo 145:6) Rahabi anafotokoza za mantha amene anagwera nzika za Yeriko pamene zinamva mmene Yehova anapulumutsira Aisrayeli pa Nyanja Yofiira ndikuwachititsa kulaka mafumu aŵiri a Amori. Muyenera kukhala munali kulankhula kwankhaninkhani ponena za ‘zowopsya’ zoterozo mu Yeriko. (Yoswa 2:9-11) Ndipo kuyandikira kwa ‘chisautso chachikulu’ motsimikizirika kudzakhala kowopsya. (Mateyu 24:21) Komatu zinthu zowopsya kwenikweni kwa anthu otalikirana ndi Mulungu zimauzira m’mitima yolungama “kuopa Yehova,” kumuwopadi iye. (Miyambo 1:7) Pokhala ndi mzimu wa kuwopa woterowo, Mboni za Yehova zimafotokoza ponena za mphamvu za Mulungu zowonekera. Eya, Mpangi wa Zodabwitsa wamkuluyu ndiye mutu waukulu wokambirana pakati pa odzozedwa ndi mabwenzi anzawo apadziko lapansi! Ndipo ngakhale chizunzo sichimawaletsa kufotokozera ena ponena za zinthu izi ndi “ukulu” wa Yehova.—Machitidwe 4:18-31; 5:29.
Tamandani Yehova Kaamba ka Ubwino Wake
12. Kodi ubwino wa Yehova umatipangitsa bwanji ‘kubukitsa’?
12 Mulungu ngwoyenerera kutamandidwa osati chifukwa cha ukulu wake wokha komanso chifukwa cha ubwino wake ndi chilungamo. Davide ananena motere: “Iwo adzabukitsa mwa kutchula kuchuluka kwa ubwino wanu, nadzafuulira chilungamo chanu.” (Salmo 145:7, NW) Ubwino wa Yehova ngwaukuludi kwakuti ‘timaubukitsa’ ndi mawu achisangalalo onena za uko. M’Chihebri, lingaliro lomwe liri pano nlakuthithima kwa madzi otuluka pa kasupe. Chotero lolani kuti tibukitse chitamando chachikulu cha Mulungu, mofananadi ndi mtsinje wodzala. (Miyambo 18:4) Israyeli anaiŵala ubwino wa Yehova, ndi kudzivulaza okha mwauzimu. (Salmo 106:13-43) Koma lolani kuti mitima yathu isefukire ndi chiyamikiro choterocho kwakuti ena alape ataphunzira mmene Yehova aliri wabwino kwa Mboni zake zodzipereka.—Aroma 2:4.
13. Kodi kuwonetseredwa kwa chilungamo ndi chilunjiko chaumulungu kuyenera kukhala ndi chiyambukiro chotani pa ife?
13 Lolani kuti kuwonetsedwa kwa chilungamo chaumulungu ndi chilunjiko zitisonkhezerenso kufuula mwachisangalalo. Ngati tikhala ndi malingaliro otere, tidzafunafuna choyamba osati Ufumu wa Mulungu wokha komanso ndi chilungamo chake. Nthaŵi zonse tidzafuna kuti mayendedwe athu abweretse chitamando kwa Yehova. Inde, tidzakhala alengezi okhazikika a Ufumu okhala ndi zambiri zochita muutumiki wa Mulungu. Sitidzakhalapo chete osatamanda Yehova.—Mateyu 6:33; 1 Akorinto 15:58; Ahebri 10:23.
Yehova Ngwachifundo
14. Kodi pali umboni wotani wakuti ‘Yehova ngwachisomo ndi wachifundo’?
14 Potchula mikhalidwe yowonjezereka yotheketsa Mulungu kutamandidwa, Davide anati: ‘Yehova ndiye wachisomo, ndi wachifundo; osakwiya msanga, ndi wa [kukoma mtima kwachikondi kwakukulu, “NW”].’ (Salmo 145:8) Mulungu ngwachisomo m’njira yakuti ngwabwino ndi wowolowa manja ponseponse. (Mateyu 19:17; Yakobo 1:5) Iye amachita zinthu zabwino ngakhale kwa anthu osamtumikira. (Machitidwe 14:14-17) Yehova alinso wachifundo, wakumva chisoni, ‘pokumbukira kuti ndife fumbi.’ Iye samapeputsa munthu wa mtima wosweka kapena kuchita nafe mogwirizana ndi machimo athu komatu ngwachifundo zedi kuposa bambo waumunthu wachikondi koposa. (Salmo 51:17; 103:10-14) Eya, kusonyeza kwake chifundo chachikulu, anatumiza Mwana wake wokondedwa kudzatifera kotero kuti tiyanjanitsidwe kwa Mulungu ndi kulaŵadi chisomo chake!—Aroma 5:6-11.
15. Kodi nchifukwa ninji kunganenedwe kuti Yehova Mulungu ‘samakwiya msanga’ ndipo ali ndi ‘kukoma mtima kwachikondi kwakukulu’?
15 Atate wathu wakumwambayu samakwiya msanga. Iye samazaza nawo ukali. Yehova alinso ndi “kukoma mtima kwachikondi kwakukulu.” Panonso Chihebri chikutanthauza kukoma mtima kumene kumatuluka m’chikondi ndikukaphatikana ndi chinthu chinachake. Iko kumakhalapobe pachinthucho mpaka chifuno chonkira komweko chitapezedwa. Kumasulira kwina ndiko “chikondi chokhulupirika.” Pakati pa zinthu zina, kukoma mtima kwachikondi kwa Mulungu, kapena chikondi chokhulupirika, kwasonyezedwa m’machitidwe a kupulumutsa, kusunga, kutetezera, kupatsa mpumulo kumavuto, ndi kuchira kuuchimo kupyolera m’dipo. (Salmo 6:4; 25:7; 31:16, 21; 40:11; 61:7; 119:88, 159; 143:12; Yohane 3:16) Nsonga yokha yakuti Yehova sanabweretse Armagedo pambuyo penipeni pa ‘nkhondo m’mwamba’ imatheketsa khamu la anthu kupeza chipulumutso, chisonyezero chachikulu cha kukoma mtima kwachikondi kwaumulungu.—Chibvumbulutso 12:7-12; 2 Petro 3:15.
16. Kodi ndimotani mmene Yehova watsimikizira kukhala ‘wabwino kwa onse’?
16 Chifukwa cha chifundo cha Mulunguchi, kunganenedwe kuti iye ali ndi mtima waukulu. Davide analengeza kuti: “Yehova ngwabwino kwa onse, ndipo chifundo chake chigwera ntchito zake zonse.” (Salmo 145:9, NW) Inde, Mulungu anali wabwino kwa Aisrayeli. Chifukwa cha ichi, ‘iye amakwezera dzuwa lake pa oipa ndi pa abwino, namavumbitsira mvula pa olungama ndi pa osalungama.’ (Mateyu 5:43-45) Mu Edeni, Yehova analonjeza ‘mbewu’ yomwe ikakhala dalitso. Pambuyo pake iye anauza Abrahamu kuti: ‘M’mbewu yako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa.’ (Genesis 3:15; 22:18) Ndipo ubwino wa Mulungu ngwaukulu kwambiri ‘m’nthaŵi za chimaliziro’ zino kwakuti munthu aliyense ‘angabwere kudzamwa madzi amoyo kwaulere.’ (Danieli 12:4; Chibvumbulutso 22:17) Yehova ngwofunitsitsa kuchita zabwino ku zolengedwa zaluntha zonse, ndipo ubwino wake uyenera kutikokerabe chifupi ndi iye.
17. Kodi ndim’lingaliro lotani mmene ‘chifundo [cha Yehova] chiriri pantchito zake zonse’?
17 ‘Chifundo [cha Yehova] chigwera ntchito zake zonse’ m’njira yakuti iye amapanga makonzedwe okwanira kaamba ka anthu ndi nyama. Iye ndiye ‘wakupatsa nyama zonse chakudya.’ (Salmo 136:25; 147:9) Mulungu samalemekeza olemera ndi kunyoza osauka, samakweza odzikuza ndi kunyalanyaza ofatsa, samatukula opusa ndi kupondereza anzeru. Ichi chimachitidwa ndi anthu ochimwa osati Atate wathu wachifundo wakumwamba. (Salmo 102:17; Zefaniya 3:11, 12; Mlaliki 10:5-7) Ndipo chifundo cha Mulungu, ubwino, ndi kukoma mtima kwachikondi nzazikulu chotani nanga popangitsa chipulumutso kukhala chothekera kupyolera m’nsembe yadipo ya Mwana wake wokondedwa!—1 Yohane 4:9, 10.
Okhulupirika Adalitsa Yehova
18. (a) Kodi ntchito za Mulungu ‘zimamuyamika’ motani iye? (b) Kodi ndiliti pamene tiyenera kusonkhezeredwa kulemekeza Yehova?
18 Mulungu amayenerera kutamandidwa ponseponse. Davide ananena motere: ‘Ntchito zanu zonse zidzakuyamikani, Yehova; ndi okhulupirika anu [adzakudalitsani, “NW”].’ (Salmo 145:10) Ntchito za Mulungu za chilengedwe ‘zimamuyamika,’ mongadi mmene nyumba yomangidwa bwino imathokozetsa woimanga ndipo choumba chokongola chimatukula m’misili wake waluso. (Yerekezerani ndi Ahebri 3:4; Yesaya 29:16; 64:8.) Ntchito zachilengedwe cha Yehova nzodabwitsa zedi kwakuti zasonkhezera angelo ndi anthu omwe kumtamanda iye. Ana aungelo a Mulungu anafuula ndi chithokozo mwachisangalalo pamene anakhazikitsa dziko lapansi. (Yobu 38:4-7) Davide anati ‘zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo liwonetsa ntchito ya manja ake.’ (Salmo 19:1-6) Nafenso tingamuyamike Yehova pamene tiwona kabawi auluka mumlengalenga kapena pamene tiwona mphoyo ikudzinyolola pamapiri a mipata. (Yobu 39:26; Nyimbo ya Solomo 2:17) Chitamando chimayenerera titatuta dzinthu kapena kusangalala ndi chakudya ndi mabwenzi. (Salmo 72:16; Miyambo 15:17) Matupi athu olinganizidwa modabwitsa angafulumizenso mawu a chitamando choyamikira Mulungu.—Salmo 139:14-16.
19. Kodi ndani omwe ali ‘okhulupirika,’ ndipo kodi amachitanji?
19 Lerolino, ‘okhulupirika’ odzozedwa ndi mzimu a Yehova padziko lapansi amam’dalitsa. Iwo amamuthokoza ndipo amakhumba kuwona chifuniro chake chikuchitika padziko lapansi monga momwe ziriri kumwamba. (Mateyu 6:9, 10) Pamene odzozedwa afotokozera ena ponena za ntchito zodabwitsa za Mulungu, khamu lalikulu limavomereza m’chiŵerengero chomawonjezerekawonjezereka nthaŵi zonse. Limodzi ndi odzozedwa okhulupirika, iwo amatumikira mokangalika monga alengezi Aufumu. Kodi chiyamikiro chikukufulumizani kukhalamo ndi phande mokhazikika m’ntchito imeneyi yotamanda Mulungu?
20. (a) Kodi dzina la Yehova lidzapatulikitsidwa motani? (b) Ponena za Salmo 145, kodi ndi mafunso ati omwe atsalira kulingaliridwa?
20 Monga Mboni za Yehova, tiri ofanana ndi Davide m’kupereka chitamando kwa Mulungu. Kwa ife kupatulikitsidwa kwa dzina loyera la Yehova ndi kulitamanda kuli nkhani yolingalirapo kwenikweni. Popeza kuti dzina laumulungu lidzapatulikitsidwa ndi Ufumu wa Mulungu, chiphunzitso ichi cha Baibulo chonena za Ufumu chiri mbali yaikulu ya mbiri yabwino imene timalengeza. Kodi Salmo 145 likupereka kuwala kwauzimu m’nkhaniyi? Kodi kukambirana kwathu kwa salmo lonseli kudzavumbulanji? Kodi ndim’njira zina ziti mmene imatsimikizira kuti Yehova ngoyenerera chitamando chosatha?
Kodi Ndemanga Zanu Nzotani?
◻ Kodi tingalidalitse motani dzina la Yehova?
◻ Kodi ndiziti zimene ziri ntchito zina zoyenera kuthokozedwa za Mulungu?
◻ Kodi tidzachita motani ngati tiyamikira ubwino wa Yehova?
◻ Kodi chifundo cha Mulungu chasonyezedwa m’njira zotani?
[Chithunzi patsamba 12]
Kodi mumafotokozera ana anu ponena za ntchito zazikulu za Yehova, monga mmene anachitira makolo opembedza mu Israyeli wakale?
[Chithunzi patsamba 15]
Monga mmene nyumba yomangidwa bwino imathokozetsa woimanga, choteronso ntchito za chilengedwe cha Yehova zimabweretsa chitamando kwa Iye