Yehova—Atate Wathu Wodzala Chifundo
“[Yehova, NW] ali wodzala chikondi, ndi wachifundo.” —YAKOBO 5:11.
1. Kodi nchifukwa ninji osauka amakopeka mtima ndi Yehova Mulungu?
CHILENGEDWE CHONSE nchachikulu kwenikweni kwakuti openda zakuthambo satha konse kuŵerenga milalang’amba yake yonse. Mlalang’amba wathu, wotchedwa Milky Way, ngwaukulu kwambiri kwakuti munthu sangathe kuŵerenga nyenyezi zake zonse. Nyenyezi zina, monga Antares, nzaukulu ndi kuŵala koŵirikiza zikwizikwi kuposa dzuŵa lathu. Ha, ayenera kukhala wamphamvu chotani nanga Mlengi Wamkulu wa nyenyezi zonsezo zokhala m’chilengedwe chonse! Ndithudi, iye ali “Amene atulutsa khamu lawo ndi kuziŵerenga; azitcha zonse maina awo.” (Yesaya 40:26) Komabe, Mulungu wochititsa mantha mmodzimodziyo alinso “wodzala chikondi, ndi wachifundo.” Kudziŵa chimenecho kuli kotonthoza mtima chotani nanga kwa atumiki a Yehova odzichepetsa, makamaka kwa amene akuvutika ndi chizunzo, matenda, tondovi, kapena zovuta zina!
2. Kodi ndimotani mmene anthu a dzikoli kaŵirikaŵiri amaonera mikhalidwe ya chifundo?
2 Anthu ambiri amaona mikhalidwe ya mtima yonga, “chikondi ndi chifundo” cha Kristu kukhala kufooka. (Afilipi 2:1, NW) Posonkhezeredwa ndi nthanthi za chisinthiko, iwo amalimbikitsa anthu kudziika patsogolo ngakhale ngati zimenezo zingapweteke ena. Akatswiri ochuluka otchuka m’zosangulutsa ndi m’zamaseŵera ali anthu osonyeza uchamuna omwe sagwetsa misozi kapena kusonyeza chikondi. Olamulira andale ena amachita mofananamo. Seneca, wafilosofi ya Ustoiki, amene anaphunzitsa mfumu yankhalwe Nero, anagogomezera kuti “chisoni ndi chifooko.” Cyclopædia yolembedwa ndi M’Clintock ndi Strong imanena kuti: “Zisonkhezero za Chistoiki . . . zikupitiriza kugwira ntchito pakati pa anthu ngakhale m’nthaŵi zino.”
3. Kodi Yehova anadzilongosola yekha motani kwa Mose?
3 Mosiyana ndi zimenezo, umunthu wa Mlengi wa mtundu wa anthu uli wotonthoza mtima. Iye anadzilongosola yekha kwa Mose m’mawu aŵa: “Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi; . . . wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kuchimwa; koma wosamasula wopalamula.” (Eksodo 34:6, 7) Zoona, Yehova anamaliza malongosoledwe onena za iye mwini ameneŵa mwa kugogomezera chilungamo chake. Iye sadzamasula ochimwira dala pachilango chowayenera. Chikhalirechobe, choyamba akudzilongosola kukhala Mulungu wachifundo.
4. Kodi ndi tanthauzo lotonthoza mtima lotani la liwu Lachihebri limene kaŵirikaŵiri limatembenuzidwa “chifundo”?
4 Nthaŵi zina liwu lakuti “chifundo” limangolingaliridwa m’ganizo lachiweruzo la kuchotsa chilango. Komabe, kuyerekezera matembenuzidwe a Baibulo kumasonyeza tanthauzo lenileni la mfotokozi Wachihebri wochokera kwa mneni wakuti ra·chamʹ. Malinga ndi kunena kwa akatswiri ena, tanthauzo lake loyambirira ndilo “kukhala wofeŵa.” Buku la Synonyms of the Old Testament limafotokoza kuti “racham, imasonyeza kumva chifundo kwakukulu, konga kuja kodzutsidwa mwa kuona kufooka kapena kuvutika kwa awo amene timawakonda kapena ofunikira thandizo lathu.” Malongosoledwe ena otonthoza mtima a mkhalidwe wabwino umenewu angapezedwe mu Insight on the Scriptures, Voliyumu 2, masamba 375-9.
5. Kodi chifundo chinaonekera motani m’Chilamulo cha Mose?
5 Chifundo cha Mulungu chimaonekera bwino lomwe mu Chilamulo chimene anapatsa mtundu wa Israyeli. Opanda mwaŵi, onga ngati akazi amasiye, ana amasiye, ndi amphaŵi, anayenera kuchitiridwa mwachifundo. (Eksodo 22:22-27; Levitiko 19:9, 10; Deuteronomo 15:7-11) Onse, kuphatikizapo akapolo ndi zinyama, anafunikira kupindula ndi Sabata la mlungu ndi mlungu la kupumula. (Eksodo 20:10) Ndiponso, Mulungu anakumbukira anthu amene anachitira osauka mokoma mtima. Miyambo 19:17 imanena kuti: “Wochitira waumphawi chifundo abwereka Yehova; adzambwezera chokoma chakecho.”
Malire a Chifundo cha Mulungu
6. Kodi nchifukwa ninji Yehova anatumiza aneneri ndi amithenga kwa anthu ake?
6 Aisrayeli anali ndi dzina la Mulungu ndipo analambira pakachisi mu Yerusalemu, amene anali ‘nyumba ya dzina la Yehova Mulungu.’ (2 Mbiri 2:4; 6:33) Komabe, m’kupita kwa nthaŵi iwo analekerera chisembwere, kulambira mafano, ndi mbanda, akumadzetsa chitonzo chachikulu pa dzina la Yehova. Mogwirizana ndi umunthu wake wachifundo, Mulungu moleza mtima anayesayesa kuwongolera mkhalidwe woipa umenewu popanda kudzetsa tsoka pa mtundu wonsewo. Iye “anatumiza kwa iwo ndi dzanja la mithenga yake, nalaŵirira mamawa kuituma, chifukwa anamvera chifundo anthu ake, ndi pokhala pake; koma ananyodola mithenga ya Mulungu, napeputsa mawu ake, naseka aneneri ake, mpaka ukali wa Mulungu unaukira anthu ake, mpaka panalibe cholanditsa.”—2 Mbiri 36:15, 16.
7. Pamene chifundo cha Yehova chinafika pamalire ake, kodi nchiyani chinachitikira ufumu wa Yuda?
7 Ngakhale kuti Yehova ali wachifundo ndi wosakwiya msanga, iye amakwiya mwachilungamo pamene kuli kofunikira. Kalelo, chifundo cha Mulungu chinali chitafika pamalire ake. Timaŵerenga za zotsatirapo zake kuti: “[Yehova] anawakweretsera mfumu ya Akasidi, ndiye anawaphera anyamata awo ndi lupanga, m’nyumba ya malo awo opatulika, osachitira chifundo mnyamata kapena namwali, mkulu kapena nkhalamba; Mulungu anawapereka onse m’dzanja lake.” (2 Mbiri 36:17) Motero Yerusalemu ndi kachisi wake anawonongedwa, ndipo mtunduwo unatengedwa ukapolo ku Babulo.
Chifundo pa Dzina Lake
8, 9. (a) Kodi nchifukwa ninji Yehova analengeza kuti akachitira chifundo dzina lake? (b) Kodi ndimotani mmene adani a Yehova anakhalitsidwira chete?
8 Mitundu yozungulira inasangalala pa tsoka limeneli. Monyodola, iwo anati: “Awa ndi anthu a Yehova, ndipo atuluka m’dziko lake.” Pokhudzidwa ndi chitonzo chimenechi, Yehova analengeza kuti: “Ndidzachitira chifundo dzina langa loyera . . . Ndipo ndidzayeretsadi dzina langa lalikulu, . . . ndipo mitundu idzadziŵa kuti ine ndine Yehova.”—Ezekieli 36:20-23, NW.
9 Mtundu wake utakhala mu ukapolo kwa zaka 70, Mulungu wachifundo, Yehova, anawamasula nawalola kubwerera ndi kukamanganso kachisi mu Yerusalemu. Zimenezi zinathetsa mawu mitundu yozungulira, imene inangopenya mozizwa. (Ezekieli 36:35, 36) Komabe, mwachisoni, mtundu wa Israyeli unagweranso m’machitachita oipa. Myuda wokhulupirika, Nehemiya, anathandiza kuwongolera mkhalidwewo. M’pemphero lapoyera, iye anakumbutsa zinthu zachifundo zimene Mulungu anachitira mtunduwo, akumati:
10. Kodi ndimotani mmene Nehemiya anasonyezera chifundo cha Yehova?
10 “Mu nthaŵi ya kusautsika kwawo anafuula kwa Inu, ndipo munamva m’Mwamba, ndi monga mwa nsoni zanu zambiri munawapatsa apulumutsi akuwapulumutsa m’dzanja la adani awo. Koma atapumula, anabwezera kuchita choipa pamaso panu; chifukwa chake munawasiya m’dzanja la adani awo amene anachita ufumu pa iwo; koma pobwera iwo ndi kufuula kwa Inu, munamva m’Mwamba ndi kuwapulumutsa kaŵirikaŵiri. . . . Koma munawalekerera zaka zambiri.”—Nehemiya 9:26-30; onaninso Yesaya 63:9, 10.
11. Kodi pali kusiyana kotani pakati pa Yehova ndi milungu ya anthu?
11 Pomalizira, atakana mwankhanza Mwana wokondedwa wa Mulungu, mtundu wa Chiyuda unataya chiyanjo chake kotheratu. Mulungu anakhalabe wokhulupirika kwa iwo kwa zaka zoposa 1,500. Iko kuli umboni wosatha wa choonadi chakuti Yehova alidi Mulungu wachifundo. Ha, ngwosiyana kwambiri chotani nanga ndi milungu yankhanza ndi achiuta opanda chifundo opekedwa ndi anthu ochimwa!—Onani tsamba 8.
Chisonyezero Chachikulu Koposa cha Chifundo
12. Kodi nchiyani chimene chinali chisonyezero chachikulu koposa cha chifundo cha Mulungu?
12 Chisonyezero chachikulu koposa cha chifundo cha Mulungu chinali kutumiza kwake Mwana wake padziko lapansi. Zoona, moyo wa Yesu wa umphumphu unakondweretsa Yehova kwambiri, ukumampatsa yankho langwiro pa zinenezo zonama za Mdyerekezi. (Miyambo 27:11) Komabe, panthaŵi imodzimodziyo, kuona Mwana wake wokondedwa alikufa imfa yankhalwe ndi yonyazitsa kunachititsadi mtima wa Yehova kupweteka kwakukulu kumene palibe kholo laumunthu lililonse likanakupirira. Inali nsembe yachikondi kwambiri, yotsegula njira ya chipulumutso kwa mtundu wa anthu. (Yohane 3:16) Monga momwe Zekariya, atate wa Yohane Mbatizi ananeneratu, inasonyeza “mtima wachifundo wa Mulungu wathu.”—Luka 1:77, 78.
13. Kodi ndi mwa njira yaikulu yotani imene Yesu wasonyezera umunthu wa Atate wake?
13 Kutumizidwa kwa Mwana wa Mulungu padziko lapansi kunapatsanso mtundu wa anthu chidziŵitso chabwinopo cha umunthu wa Yehova. Motani? Mwakuti Yesu anasonyeza mwangwiro umunthu wa Atate wake, makamaka mwa njira yachifundo imene anachitira ndi osauka! (Yohane 1:14; 14:9) Pambali imeneyi, olemba Uthenga Wabwino atatu Mateyu, Marko, ndi Luka amagwiritsira ntchito mneni Wachigiriki, splag·khniʹzo·mai, amene amachokera ku liwu Lachigiriki lotanthauza “matumbo.” Katswiri wa Baibulo William Barclay akufotokoza kuti: “Liwulo kumene mneniyo anatengedwako silimatanthauza chisoni kapena chifundo wamba, koma mkhalidwe umene umachititsa munthu kukhudzidwa mtima mozama kwenikweni. Ndilo liwu lamphamvu koposa m’Chigiriki lotchulira kumva chifundo.” Limatembenuzidwa mosiyanasiyana monga “kumva chisoni” kapena “kugwidwa ndi chisoni.”—Marko 6:34, NW; 8:2, NW.
Pamene Yesu Anamva Chisoni
14, 15. Mu mzinda wa m’Galileya, kodi Yesu akugwidwa motani ndi chifundo, ndipo kodi zimenezi zikusonyezanji?
14 Malowo ndi mzinda wa m’Galileya. Munthu “wodzala ndi khate” akufika kwa Yesu popanda kupereka chenjezo lamwambo. (Luka 5:12) Kodi Yesu akumdzudzula mwaukali chifukwa chakuti sanafuule kuti “Wodetsedwa, wodetsedwa,” monga momwe Chilamulo cha Mulungu chinafunira? (Levitiko 13:45) Iyayi. Mmalomwake, Yesu akumvetsera pempho lochonderera la munthuyo lakuti: “Ngati mufuna mukhoza kundikonza.” “Atagwidwa ndi chisoni,” (NW) Yesu atansa dzanja namkhudza wakhateyo, nati: “Ndifuna; khala wokonzedwa.” Pomwepo thanzi la munthuyo libwezeretsedwa. Motero Yesu akusonyeza osati mphamvu zake zozizwitsa zokha zopatsidwa ndi Mulungu, komanso chifundo chake chimene chimamsonkhezera kugwiritsira ntchito mphamvu zoterozo.—Marko 1:40-42.
15 Kodi Yesu ayenera kufikiridwa choyamba kuti asonyeze chifundo? Iyayi. Nthaŵi ina pambuyo pake, akukumana ndi khamu la operekeza maliro likutuluka mumzinda wa Naini. Mosakayikira, Yesu anaonapo kale maliro ochuluka, koma aŵa ali omvetsa chisoni kwambiri. Wakufayo ali mwana wamwamuna mmodzi yekha wa mkazi wamasiye. ‘Atagwidwa ndi chifundo,’ Yesu akufika kwa mkaziyo nati: “Usalire.” Ndiyeno, akuchita chozizwitsa chapadera kwambiri cha kuukitsa mwana wamwamuna wa mkaziyo kumkhalitsanso wamoyo.—Luka 7:11-15.
16. Kodi nchifukwa ninji Yesu akumvera chifundo khamu lalikulu lomtsatiralo?
16 Phunziro lalikulu lotengedwa pa zochitika zotchulidwazo nlakuti pamene Yesu ‘agwidwa ndi chifundo,’ achitapo kanthu kuti athandize. Pachochitika china pambuyo pake, Yesu akuunguza khamu lalikulu limene likupitirizabe kumlondola. Mateyu akusimba kuti iye “anagwidwa m’mtima ndi chisoni chifukwa cha iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.” (Mateyu 9:36) Afarisi sachita zokwanira kuti akhutiritse njala yauzimu ya anthu wamba. Mmalomwake, amatopetsa anthu osauka ndi malamulo ochuluka osafunikira. (Mateyu 12:1, 2; 15:1-9; 23:4, 23) Lingaliro lawo ponena za anthu wamba linavumbuluka pamene iwo ananena za awo amene anamvetsera kwa Yesu kuti: “Khamu ili losadziŵa chilamulo, likhala lotembereredwa.”—Yohane 7:49.
17. Kodi chifundo cha Yesu pa anthu chikumsonkhezera motani, ndipo kodi ndi chitsogozo chothandiza kwambiri chotani chimene akupereka pamenepo?
17 Mosiyana ndi zimenezo, Yesu akukhudzidwa kwambiri ndi mkhalidwe woipa wauzimu wa khamulo. Koma pali anthu okondwerera ochuluka kwambiri kwakuti iye satha kuwasamalira onse mmodzi ndi mmodzi. Motero akuuza ophunzira ake kupempherera antchito owonjezereka. (Mateyu 9:35-38) Mogwirizana ndi mapemphero oterowo, Yesu akutumiza atumwi ake ndi uthenga wakuti: “Ufumu wa Kumwamba wayandikira.” Malangizo operekedwa pa chochitikacho akhala chitsogozo chothandiza kwa Akristu kufikira lerolino. Mosakayikira, chifundo cha Yesu chimamsonkhezera kukhutiritsa njala yauzimu ya mtundu wa anthu.—Mateyu 10:5-7.
18. Kodi Yesu akuchitapo kanthu motani pamene khamu la anthu likudodometsa nthaŵi yake yamseri, ndipo kodi tikutengapo phunziro lanji pazimenezi?
18 Pachochitika china, Yesu akuderanso nkhaŵa zosoŵa zauzimu za khamu la anthu. Panthaŵiyi iye ndi atumwi ake atopa pambuyo pa ulendo waulaliki, ndipo akupeza malo opumulira. Koma posapita nthaŵi anthuwo akuwapeza iwo. Mmalo mwakuti Yesu akwiye ndi kudodometsedwa kwa nthaŵi yawo yamseri, Marko akulemba kuti iye ‘anagwidwa chifundo.’ Ndipo nchifukwa ninji Yesu anakhudzidwa mtima? “Anali ngati nkhosa zopanda mbusa.” Kachiŵirinso, Yesu akuchitapo kanthu pa chifundo chake mwa kuyamba kuphunzitsa khamulo za “Ufumu wa Mulungu.” Inde, iye anakhudzidwa kwambiri ndi njala yawo yauzimu kwakuti analepa mpumulo wake wofunikirawo kuti awaphunzitse.—Marko 6:34; Luka 9:11.
19. Kodi nkhaŵa ya Yesu pa anthu ikupitirira motani pa zosoŵa zawo zauzimu?
19 Ngakhale kuti nkhaŵa yake yaikulu inali pa zosoŵa zauzimu za anthu, Yesu sananyalanyaze konse zosoŵa zawo zazikulu zakuthupi. Pa chochitika chimodzimodzicho, ‘anachiritsa iwo amene anasoŵa kuchiritsidwa.’ (Luka 9:11) Pachochitika china pambuyo pake, khamu la anthu linali litakhala naye kwa nthaŵi yaitali, ndipo linali kutali ndi kwawo. Poona chosoŵa chawo chakuthupi, Yesu anati kwa ophunzira ake: “Mtima wanga uchitira chifundo khamu la anthuwa, pakuti ali chikhalire ndi Ine masiku atatu, ndipo alibe kanthu kakudya, ndipo sindifuna kuwauza iwo amuke osadya, kuti angaziye panjira.” (Mateyu 15:32) Tsopano Yesu akuchitapo kanthu kuti apeŵetse kuvutika kumene kungakhalepo. Mozizwitsa akugaŵira zikwi za amuna, akazi, ndi ana chakudya chopangidwa pa mikate isanu ndi iŵiri ndi tinsomba tingapo.
20. Kodi tikuphunziraponji pa chochitika chomalizira kulembedwa cha kugwidwa ndi chifundo kwa Yesu?
20 Chochitika chomaliza kulembedwa cha kugwidwa ndi chifundo kwa Yesu ndicho cha paulendo wake wotsirizira wopita ku Yerusalemu. Khamu la anthu ambiri likuyenda naye kukachita phwando la Paskha. Iwo adakali m’njira pafupi ndi Yeriko, opemphapempha akhungu aŵiri akufuula mosalekeza kuti: “Ambuye, mutichitire chifundo.” Khamulo likuyesa kuwakhalitsa chete, koma Yesu akuwaitana ndi kuwafunsa zimene afuna kuti iye achite. “Ambuye, kuti maso athu apenye,” iwo akuchonderera motero. ‘Atagwidwa ndi chifundo,’ akukhudza maso awo, ndipo ayamba kuona. (Mateyu 20:29-34) Ha, ndi phunziro lofunika chotani nanga limene tikutengapo pazimenezi! Yesu ali pafupi kuloŵa sabata lotsiriza la utumiki wake wa padziko lapansi. Iye ali ndi ntchito yochuluka yoti achite asanafe imfa yankhalwe pamanja a atumiki a Satana. Komabe, iye sakulola chipsinjo cha nthaŵi yofunika koposa imeneyi kumlepheretsa kusonyeza chifundo chake pa zosoŵa zazing’onopo za anthu.
Mafanizo Amene Amasonyeza Chifundo
21. Kodi kufafaniza ngongole yaikulu ya kapolo wake kwa Mbuyeyo kukuchitira fanizo chiyani?
21 Mneni Wachigiriki wakuti splag·khniʹzo·mai, wogwiritsiridwa ntchito m’zolembedwa zimenezi za moyo wa Yesu, akugwiritsidwanso ntchito m’mafanizo atatu a Yesu. Mu imodzi ya nkhanizo kapolo akupempha nthaŵi yakuti alipire ngongole. Mbuye wake, ‘pogwidwa ndi chifundo,’ afafaniza ngongoleyo. Zimenezi zimachitira fanizo kuti Yehova Mulungu wasonyeza chifundo pofafaniza ngongole yaikulu ya uchimo kwa Mkristu aliyense amene amasonyeza chikhulupiriro mu nsembe ya dipo ya Yesu.—Mateyu 18:27; 20:28.
22. Kodi fanizo la mwana woloŵerera limachitira chitsanzo za chiyani?
22 Ndiyeno pali nkhani ya mwana woloŵerera. Kumbukirani zimene zikuchitika pamene mwana wopandukayo abwerera kunyumba. “Pakudza iye kutali, atate wake anamuona, nagwidwa chifundo, nathamanga, namkupatira pakhosi pake, nampsompsonetsa.” (Luka 15:20) Zimenezi zimasonyeza kuti pamene Mkristu amene wapanduka asonyeza kulapa kwenikweni, Yehova adzagwidwa chifundo ndi kumlandiranso mokoma mtima. Motero, mwa mafanizo aŵiri ameneŵa, Yesu akusonyeza kuti Atate wathu, Yehova, “ali wodzala chikondi, ndi wachifundo.”—Yakobo 5:11.
23. Kodi tikutengapo phunziro lanji pa fanizo la Yesu la Msamariya waunansi?
23 Kugwiritsira ntchito mwafanizo kwachitatu kwa liwu la splag·khniʹzo·mai kumakhudza Msamariya wachifundo yemwe “anagwidwa chifundo” poona mkhalidwe woipa wa Myuda amene anafwambidwa ndi kusiidwa atakomoka. (Luka 10:33) Pochitapo kanthu pa chifundo chimenechi, Msamariyayo anachita zonse zimene anakhoza kuthandiza munthu wosamdziŵayo. Ichi chimachitira fanizo kuti Yehova ndi Yesu amayembekezera Akristu oona kutsatira chitsanzo chawo cha kusonyeza kukoma mtima ndi chifundo. Njira zina zimene tingachitire zimenezi zidzafotokozedwa m’nkhani yotsatira.
Mafunso a Kupenda
◻ Kodi kukhala wachifundo kumatanthauzanji?
◻ Kodi ndimotani mmene Yehova anasonyezera chifundo pa dzina lake?
◻ Kodi chisonyezero chachikulu koposa cha chifundo nchiyani?
◻ Kodi ndi m’njira yapadera yotani imene Yesu amasonyezera umunthu wa Atate wake?
◻ Kodi timaphunziraponji pa machitidwe a Yesu a chifundo ndi pa mafanizo ake?
[Bokosi pamasamba 12, 13]
LIWU LOMVEKETSA BWINO “CHISAMALIRO CHACHIKONDI”
“MATUMBO anga, matumbo anga!” anafuula motero mneneri Yeremiya. Kodi iye anali kudandaula za nthenda ya m’mimba chifukwa cha kudya chinthu china choipa? Iyayi. Yeremiya anali kugwiritsira ntchito liwu lokuluŵika Lachihebri kulongosola nkhaŵa yake yaikulu pa tsoka linalinkudzalo pa ufumu wa Yuda.—Yeremiya 4:19.
Popeza kuti Yehova Mulungu amakhudzidwa mtima, liwu Lachihebri lotanthauza “matumbo,” kapena “m’mimba” (me·ʽimʹ), limagwiritsidwanso ntchito kulongosola nsoni zake zambiri. Mwachitsanzo, zaka makumi ambiri nthaŵi ya Yeremiya isanakhale, ufumu wa mafuko khumi wa Israyeli unatengedwa mu ukapolo ndi mfumu ya Asuri. Yehova analola zimenezi monga chilango cha kusakhulupirika kwawo. Koma kodi Mulungu anawaiŵala pamene iwo anali kundendeko? Iyayi. Iye anali womamatirabe kwa iwo monga mbali ya anthu ake apangano. Mwa kuwatcha ndi dzina la fuko lotchuka la Efraimu, Yehova anafunsa kuti: “Kodi Efraimu ndiye mwana wanga wokondedwa? Kodi ndiye mwana wokondweretsa? nthaŵi zonse zoti ndimnenera zomtsutsa, pakuti ndimkumbukiranso ndithu; chifukwa chake [matumbo anga aŵinduka chifukwa cha iye, NW]; ndidzamchitiradi chifundo.”—Yeremiya 31:20.
Mwa kunena kuti “matumbo anga aŵinduka,” Yehova anagwiritsira ntchito mkuluŵiko kulongosola kukhudzidwa mtima kwake kwakukulu kwa chikondi pa anthu ake okhala m’ndende. M’ndemanga yake yonena za vesi limeneli, katswiri wa Baibulo wa m’zaka za zana la 19, E. Henderson, analemba kuti: “Palibe chimene chingapose chisonyezero chochititsa chidwi cha chifundo cha kholo kulinga kwa mwana wobwerera yemwe anali ataloŵerera, chimene chikusonyezedwa panopa ndi Yehova. . . . Ngakhale kuti iye anali atadzudzula [Aefraimu olambira mafanowo] ndi kuwalanga . . . , sanawaiŵale konse, m’malo mwake, anasangalala ndi kubwerera kwawo koyembekezeredwako.”
Liwu Lachigiriki lotanthauza “m’mimba,” kapena “matumbo,” limagwiritsiridwa ntchito m’njira yofananayo m’Malemba Achigiriki Achikristu. Pamene silinagwiritsiridwe ntchito mwa lingaliro lake lenileni, monga pa Machitidwe 1:18, limatanthauza mtima wachikondi kapena chifundo. (Filemoni 12, NW) Liwulo nthaŵi zina limagwirizanitsidwa ndi liwu Lachigiriki lotanthauza “chokoma” kapena “chabwino.” Atumwiwo Paulo ndi Petro amagwiritsira ntchito liwu logwirizanitsidwalo pamene akulimbikitsa Akristu kukhala “a mtima wachifundo,” m’lingaliro lake lenileni “kukhala ndi maganizo abwino a chifundo.” (Aefeso 4:32; 1 Petro 3:8) Liwu Lachigiriki lotanthauza “m’mimba” lingagwirizanitsidwenso ndi liwu Lachigiriki la pol·yʹ. Liwu logwirizanalo kwenikweni limatanthauza “kukhala ndi m’mimba kwambiri.” Liwu Lachigiriki losapezekapezeka limeneli linagwiritsiridwa ntchito kamodzi kokha m’Baibulo, ndipo limanena za Yehova Mulungu. New World Translation imapereka matembenuzidwe aŵa: “Yehova ali wokoma mtima kwambiri m’chikondi.”—Yakobo 5:11.
Tiyenera kukhala oyamikira chotani nanga kuti wamphamvu koposa m’chilengedwe chonse, Yehova Mulungu, ali wosiyana kwambiri ndi milungu yankhanza yopangidwa ndi anthu opanda chifundo! Potsanzira Mulungu wawo “wa mtima wachifundo,” Akristu oona amasonkhezeredwa kuchita mofananamo m’zochita zawo kwa wina ndi mnzake.—Aefeso 5:1.
[Chithunzi patsamba 10]
Pamene chifundo cha Mulungu chinafika pamalire ake, Yehova analola Ababulo kugonjetsa anthu ake opandukawo
[Chithunzi patsamba 11]
Kupenyerera Mwana wake wokondedwa alikumwalira kuyenera kuti kunachititsa mtima wa Yehova Mulungu kupweteka kwakukulu kumene palibe aliyense amene anakumvapo
[Chithunzi patsamba 15]
Yesu anasonyeza mwangwiro umunthu wachifundo wa Atate wake