Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Ulendo Wina Wolalikira wa ku Galileya
PAMBUYO pa chifupifupi zaka ziwiri za kulalikira kwamphamvu, kodi Yesu tsopano akayamba kukhwethemuka ndi kukutenga iko mosasamala? Mosiyana, iye akufutuluka ntchito yake yolalikira mwa kukhazikitsa ulendo wina, ulendo wachitatu wa ku Galileya. lye akuchezera mizinda ndi midzi yonse m’gawolo, kuphunzitsa m’masunagoge ndi kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu. Chomwe akuwona pa ulendowu chikumukhutiritsa iye kuposa ndi kale lonse za kufunika kwa kufutukula ntchito yolalikira.
Kuli konse kumene Yesu akupita, iye akuwona makamu ofuna kuchiritsidwa kwauzimu ndi chitonthozo. Iwo ali monga nkhosa zopanda mbusa, zokambululidwa ndi kumwazidwa, ndipo iye akuwamvera chisoni iwo. lye auza ophunzira ake:“Inde, zotuta zichulukadi, koma antchito ali owerengeka.”
Yesu ali ndi makonzedwe akugwirirapo ntchito. lye akuuza atumwi 12, amene iye wawasankha chifupifupi chaka chimodzi chapita. lye akuwagawa iwo mu magulu awiri awiri, kupanga magulu asanu ndi limodzi a olalikira, ndi kuwapatsa iwo malangizo, akumati: “Musapite ku njira ya kwa anthu a kunja, ndi m’mudzi wa Asamariya musalowemo; koma m’malo mwake makamaka mupite ku nkhosa zosokera za banja la Israyeli. Ndipo pamene mulikupita lalikirani kuti, ‘Ufumu wa kumwamba wayandikira.’”
Ufumu umenewo umene iwo ayenera kulalikira ponena za iwo uli umodzi umene Yesu anawaphunzitsa iwo kupempherera mu pemphero lachitsanzo. Ufumuwo unayandikira mlingaliro lakuti Mfumu yokhazikitsidwa ya Mulungu, Yesu Kristu, analipo. Kukhazikitsa chitsimikiziro cha ulamuliro wa ophunzira ake monga oimira a boma losakhala la munthu limenelo, Yesu akuwapatsa iwo mphamvu ya kuchiritsa odwala ndipo ngakhale kuukitsa akufa. lye akuwalangiza iwo kuchita mautumiki amenewa kwaulere.
Kenaka iye akuuza ophunzira ake kusapanga zokonzekera zakuthupi kaamba ka ulendo wolalikira. “Musadzitengere ndalama zagolidi, kapena zasiliva, kapena zakobiri m’malamba mwanu; kapena thumba la kamba la kunjira, kapena malaya awiri, kapena nsapato, kapena ndodo; pakuti wantchito ayenera kulandira zakudya zake.” Awo amene amauyamikira uthengawo adzavomereza ndi kugawira chakudya ndi malo ogona. Monga mmene Yesu ananenera: “Ndipo m’mzinda uliwonse, kapena m’mudzi mukalowamo, mufunsitse amene ali woyenera momwemo; ndipo bakhalani komweko kufikira mutulukamo.”
Yesu kenaka akupereka malangizo a mmene ayenera kufikira eninyumba ndi uthenga wa Ufumu. “Ndipo polowa m’nyumba,“ iye akulangiza, “muwalankhule; ndipo ngati nyumbayo iri yoyenera, mtendere wanu udze pa iyo, koma ngati siiri yoyenera, mtendere wanu ubwerere kwa inu. Ndipo yemwe sadzakulandirani inu, kapena kusamva mawu anu, pamene mutuluka m’nyumbayo, kapena m’mudzimo, sansani fumbi m’mapazi anu.”
Ponena za mudzi womwe ukakana uthenga wawo, Yesu akuti: “Tsiku la kuweruza, mlandu wawo wa Sodomu ndi Gomora udzachepa koposa wa mudzi umenewo.” Ichi chikusonyeza kuti chifupifupi osalungama ena kwa amene ophu nzira ake akawalalikira adzakhalapo mkati mwa Tsiku la Chiweruzo. Pamene nzika zakale zimenezi zidzaukitsidwa mkati mwa Tsiku la Chiweruzo, ngakhale kuli tero, chidzakhalabe chovuta kwa izo kudzichepetsa izo zeni ndi kulandira Kristu monga Mfumu koposa ndi awo omwe adzaukitsidwa kuchokera ku mizinda ya makhalidwe oipa ya Sodomu ndi Gomora. Mateyu 9:35-10:15; Marko 6:6-12; Luka 9:1-5.
◆ Kodi ndi liti pamene Yesu akayamba ulendo wake wachitatu wolalikira wa ku Galileya, ndipo kodi nchiyani chimene chikumukhutiritsa iye?
◆ Pamene akutumiza atumwi ake 12 kukalalikira, kodi ndi malangizo otani amene iye akuwapatsa iwo?
◆ Kodi nchifukwa ninji chinali cholondola kwa ophunzirawo kuphunzitsa kuti Ufumu wayandikira?
◆ Kodi ndimotani mmene chikakhalira chopiririka kwa Sodomu ndi Gomora kuposa ndi awo omwe anakana ophunzira a Yesu?