Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Kukonzekera Kuyang’anizana ndi Chizunzo
PAMBUYO pakulangiza atumwi ake njira zochitira ntchito yolalikira, Yesu akuwachenjeza iwo ponena za otsutsa. lye akuti: “Tawonani! ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu . . . Koma chenjerani ndi anthu; pakuti adzakuperekani inu kwa akulu a mlandu, nadzakukwapulani inu m’masunagoge mwawo, ndiponso adzamuka nanu kwa akazembe ndi mafumu chifukwa cha ine.”
Mosasamala kanthu za chizunzo chowopsya chimene otsatira ake adzayang’anizana nacho, Yesu motsimikizira akulonjeza: “Pamene pali ponse angakuperekeni inu, musamadera nkhawa mudzalankhule bwanji kapena mudzanene chiyani; pakuti chimene mudzachilankhula, chidzapatsidwa kwa inu nthawi yomweyo; pakuti wolankhula si ndinu, koma mzimu wa Atate wanu [ukulankhula, NW] mwa inu.”
“Ndipo,“ Yesu akupitiriza, “mbale adzapereka mbale wake ku imfa, ndi atate mwana wake, ndipo ana adzatsutsa akuwabala, nadzawafetsa iwo.” lye akuwonjezera: “Ndipo adzada inu anthu onse chifukwa cha dzina langa; koma iye wakupirira kufikira chimariziro, iyeyu adzapulumutsidwa.”
Kulalikira kuli kofunika koposa, chotero Yesu akugogomezera kufunika kwa kuchenjera kotero kuti akhalebe afulu kuchita ntchitoyo. “Koma pamene angakuzunzeni inu m’mudzi uwu, thawirani mwina,” iye Akutero, indetu ndinena kwa inu simudzaitha mizinda ya Israyeli, kufikira Mwana wa munthu atadza.”
Chiri chowona kuti Yesu anapereka malangizo awa, chenjezo, ndi chilimbikitso kwa atumwi ake 12, koma chinatanthauzidwanso kaamba ka awo omwe adzagawanamo mu kulalikira kwa dziko lonse pambuyo pa imfa yake ndi chiukiriro. Ichi chikusonyezedwa ndi chenicheni chakuti iye ananena kuti ophunzira ake ‘adzadedwa ndi anthu onse, ’osati kokha ndi Aisrayeli kwa amene atumwiwo anatumizidwa kukalalikira. Kuwonjezerapo, atumwiwo mwachiwonekere sanaperekedwe pamaso pa olamulira ndi mafumu pamene Yesu anawatumiza iwo ku ndawala zawo zazifupi zolalikira. Ndiponso, okhulupirirawo sanaperekedwe ku imfa ndi ziwalo zabanja.
Chotero pamene ananena kuti ophunzira ake sadzamaliza gawo lawo la kulalikira “kufikira Mwana wa munthu atadza,” Yesu anali kutiuza ife mwaulosi kuti ophunzira ake sadzamaliza gawo lonse ladziko lapansi lokhalidwa ndi anthu ndi kulalikira ponena za Ufumu wokhazikitsidwa wa Mulungu Mfumu Yesu Kristu wolemekezedwa asanafike monga nduna yopereka chilango pa Armagedo.
Kupitiriza ndi malangizo ake akulalikira, Yesu akuti: “Wophunzira saposa mphunzitsi wake, kapena kapolo kuposa mbuye wake.” Chotero otsatira a Yesu ayenera kuyembekezera kulandira kachitidwe koipa kofananako ndi chizunzo monga mmene iye anachitira chifukwa cha kulalikira Ufumu wa Mulungu. Komabe iye akuchenjeza: “Ndipo musawope amene akupha thupi, koma moyo sangathe kuupha; koma makamaka muwope iye, wokhoza kuwononga moyo ndi thupi lomwe m’gehena.”
Yesu anakhazikitsa chitsanzo mu nkhani imeneyi. lye mopanda mantha anapirira imfa m’malo mwakupotoza kukhulupirira kwake kwa uyo Amene ali ndi mphamvu zonse, Yehova Mulungu. Inde, ali Yehova amene sangawononge kokha “moyo“ wa munthu (mu nkhaniyi kutanthauza ziyembekezo za mtsogolo za munthuyo monga wamoyo) koma angathe ngakhale kuukitsa munthu kusangalalandi moyo wosatha. Yehova ali Tate wakumwamba wachikondi, ndi womvera chifundo chotani nanga!
Yesu kenaka akulimbikitsa ophunzira ake ndi fanizo lomwe likugogomezera chisamaliro chachikondi cha Yehova kaamba ka iwo. “Kodi mpheta ziwiri sizigulidwa kakobiri?“ lye akufunsa: “Ndipo imodzi ya izo siigwa pansi popanda Atate wanu [kudziwa, NW]. Komatu inu matsitsi onse a m’mutu mwanu awerengedwa. Chifukwa chake musamawopa, inu mupambana mpheta ziwiri.”
Uthenga wa Ufumu umene Yesu wagawira ophunzira ake kuulalikira umagawanitsa zinyumba, pamene ziwalo zina zabanja zimaulandira iwo ndipo zina zimaukana. “Musalingalire kuti ndinadzera kuponya mtendere pa dziko lapansi,“ iye akulongosola. “Sindinadzera kuponya mtendere, koma lupanga.” Chotero, kuti chiwalo chabanja chikupatire chowonadi cha Baibulo kumafunikira kulimba mtima. “lye wakukonda atate wake, kapena amake koposa ine,” Yesu akulongosola, “ndi iye wokonda mwana wake wamwamuna, kapena wamkazi koposa ine, sayenera ine.”
Kumaliza malangizo ake, Yesu akulongosola kuti awo amene amawalandira ophunzira ake amalandiranso iye. “Ndipo amene aliyense adzamwetsa mmodzi wa ang’ono awa chikho chokha cha madzi ozizira, pa dzina la wophunzira, indetu ndinena kwa inu, iye sadzataya mphotho yake.” Mateyu 10:16-42.
◆ Kodi ndi machenjezo otani amene Yesu anapereka kwa ophunzira ake?
◆ Kodi ndi chilimbikitso ndi chitonthozo chotani chimene iye anawapatsa iwo?
◆ Kodi nchifukwa ninji malangizo a Yesu amagwiranso ntchito kwa Akristu amakono?
◆ Ndi m’njira yotani mmene wophunzira wa Yesu saliri woposa mphunzitsi wake?