PHUNZIRO 19
Kodi a Mboni za Yehova Ndi Akhristu Enieni?
A Mboni za Yehovafe timakhulupirira kuti ndife Akhristu enieni. N’chifukwa chiyani tikutero? Tikutero chifukwa cha kumene timatenga zimene timakhulupirira, dzina limene timadziwika nalo ndiponso chikondi chimene timasonyezana.
1. Kodi zimene a Mboni za Yehova amakhulupirira zimachokera kuti?
Yesu anati: “Mawu [a Mulungu] ndiwo choonadi.” (Yohane 17:17) Mofanana ndi Yesu, zimene a Mboni za Yehova amakhulupirira zimachokera m’Mawu a Mulungu. Mwachitsanzo, taganizirani zimene anachita a Mboni za Yehova omwe poyamba ankatchedwa kuti Ophunzira Baibulo. Mu 1870, gulu la Ophunzira Baibulowa linayamba kuphunzira Baibulo mosamala kwambiri kuti limvetse zimene limaphunzitsa. Iwo anayamba kukhulupirira zimene Baibulo limaphunzitsa ngakhale pamene zikhulupiriro zawozo zinkasiyana ndi zimene matchalitchi ena ankaphunzitsa. Kenako anayamba kuuzako ena mfundo za choonadi zimene ankazipeza m’Baibulozo.a
2. N’chifukwa chiyani timadziwika ndi dzina lakuti Mboni za Yehova?
Yehova amatchula anthu amene amamulambira kuti Mboni zake chifukwa amanena zoona zokhudza iye. (Aheberi 11:4–12:1) Mwachitsanzo, kale kwambiri Mulungu anauza atumiki ake kuti: “Inu ndinu mboni zanga.” (Werengani Yesaya 43:10.) Yesu nayenso amatchedwa kuti “Mboni Yokhulupirika.” (Chivumbulutso 1:5) Choncho mu 1931 tinayamba kudziwika ndi dzina lakuti Mboni za Yehova. Kudziwika ndi dzina limeneli ndi mwayi waukulu.
3. Kodi a Mboni za Yehova amatsanzira bwanji Yesu pa nkhani yosonyeza chikondi?
Yesu ankakonda kwambiri ophunzira ake moti ankawaona ngati abale ake enieni. (Werengani Maliko 3:35.) Choncho a Mboni za Yehova nawonso ndi banja limodzi logwirizana la padziko lonse. N’chifukwa chake timati ndife abale ndi alongo. (Filimoni 1, 2) Timamveranso lamulo lakuti: “Kondani gulu lonse la abale.” (1 Petulo 2:17) A Mboni za Yehova amasonyeza kuti amakonda abale awo m’njira zambiri. Mwachitsanzo, Akhristu anzawo padziko lonse lapansi akakumana ndi mavuto amawathandiza.
FUFUZANI MOZAMA
Fufuzani kuti mudziwe zambiri zokhudza mbiri ya Mboni za Yehova ndipo muone umboni wina wosonyeza kuti ndifedi Akhristu enieni.
4. Zimene timakhulupirira zimachokera m’Baibulo
Yehova ananeneratu kuti atumiki ake azidzamvetsa choonadi cha m’Baibulo mwapang’onopang’ono. Werengani Danieli 12:4, kenako mukambirane funso ili:
Malinga ndi lembali, kodi atumiki a Mulungu adzadziwa chiyani akamapitiriza kufufuza mfundo za m’Baibulo?
Onani zimene Ophunzira Baibulo, kuphatikizapo Charles Russell, ankachita pophunzira Mawu a Mulungu. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso ili:
Muvidiyoyi, kodi Charles Russell ndi Ophunzira Baibulo anzake ankatsatira njira iti pophunzira Baibulo?
Kodi mukudziwa?
Nthawi zina timatha kusintha zinthu zimene takhala tikukhulupirira. N’chifukwa chiyani timatero? Dzuwa likamatuluka limawala pang’onopang’ono. Mofanana ndi zimenezi, Mulungu amatithandiza kumvetsa Mawu ake mwapang’onopang’ononso. (Werengani Miyambo 4:18.) Baibulo silimasintha, koma tikamalimvetsa bwino timasintha zomwe takhala tikukhulupirira.
5. Timachita zinthu zogwirizana ndi dzina lathu
N’chifukwa chiyani tinayamba kudziwika ndi dzina lakuti Mboni za Yehova? Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso lotsatira.
Kodi dzina lakuti Mboni za Yehova ndi loyenerera chifukwa chiyani?
N’chifukwa chiyani Yehova amasankha anthu kuti akhale Mboni zake? Chifukwa amafuna kuti azithandiza anthu kudziwa kuti iye ndi Mulungu woona. Zili choncho chifukwa anthu akhala akuphunzitsa zinthu zabodza zokhudza iyeyo. Tiyeni tione mabodza awiri.
Zipembedzo zina zimaphunzitsa kuti Mulungu amafuna tizigwiritsa ntchito mafano polambira. Koma kodi zimenezi ndi zoona? Werengani Levitiko 26:1, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi zoona zake ndi ziti? Kodi Yehova amamva bwanji anthu akamalambira mafano?
Atsogoleri azipembedzo ena amaphunzitsa kuti Yesu ndi Mulungu. Koma kodi zimenezi ndi zoona? Werengani Yohane 20:17, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi zoona zake ndi ziti? Kodi Yesu nayenso ndi Mulungu?
Kodi mukumva bwanji mukaganizira kuti Yehova amatumiza Mboni zake kuti zilalikire choonadi chokhudza iyeyo ndi Mwana wake?
6. Timakondana
Baibulo limanena kuti Akhristu ayenera kukhala ogwirizana ngati ziwalo za thupi la munthu. Werengani 1 Akorinto 12:25, 26, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi Akhristu enieni amachita chiyani akaona kuti Akhristu anzawo akuvutika?
Kodi inuyo mwaona zotani pa nkhani ya mmene a Mboni za Yehova amasonyezerana chikondi?
A Mboni za Yehova akamavutika m’dziko linalake, a Mboni anzawo padziko lonse lapansi amayesetsa kuwathandiza mwamsanga. Kuti muone chitsanzo cha zimenezi, onerani VIDIYO. Kenako mukambirane funso lotsatirali:
Kodi zimene a Mboni za Yehova amachita pothandizana zimasonyeza bwanji kuti amakondana?
ZIMENE ENA AMANENA: “N’chifukwa chiyani mumatchedwa kuti Mboni za Yehova osati Mboni za Yesu?”
Kodi Yehova anayamba liti kutchula anthu amene amamulambira kuti Mboni zake?
ZOMWE TAPHUNZIRA
A Mboni za Yehova ndi Akhristu enieni. Ndife banja limodzi la padziko lonse lapansi ndipo zimene timakhulupirira zimachokera m’Baibulo komanso timauza ena choonadi chonena za Yehova.
Kubwereza
N’chifukwa chiyani tinayamba kudziwika ndi dzina lakuti Mboni za Yehova?
Kodi timachita bwanji zinthu ndi Akhristu anzathu?
Kodi inuyo mukuganiza kuti a Mboni za Yehova ndi Akhristu enieni?
ONANI ZINANSO
Dziwani zambiri zokhudza mbiri yathu.
Mboni za Yehova Zinasonyeza Chikhulupiriro, Gawo 1: Kutuluka mu Mdima 1:00:53
Onani zitsanzo zosonyeza zimene Mboni za Yehova zachita pothana ndi ziphunzitso zabodza.
Pezani mayankho a mafunso amene muli nawo okhudza a Mboni za Yehova.
A Stephen ankakonda kuchita zachiwawa. Werengani nkhaniyi kuti mupeze zomwe anaona a Mboni za Yehova akuchita zomwe zinawathandiza kuti asinthe.
“Moyo Wanga Unkangoipiraipirabe” (Nsanja ya Olonda, July 1, 2015)
a Magazini yathu ya Nsanja ya Olonda yomwe ndi yodziwika bwino yakhala ikufotokoza mfundo za choonadi cha m’Baibulo kuyambira mu 1879.