-
‘Mulungu Ndi Amene Amakulitsa’!Nsanja ya Olonda—2008 | July 15
-
-
Wofesa Mbewu Amene Amagona
13, 14. (a) Fotokozani mwachidule fanizo la Yesu la munthu womwaza mbewu. (b) Kodi wofesayu ndiponso mbewu zikuimira chiyani?
13 Pa Maliko 4:26-29, tikupezapo fanizo lina lonena za wofesa mbewu. Fanizoli limati: “Chotero ufumu wa Mulungu uli ngati mmene munthu amamwazira mbewu panthaka, ndipo amagona usiku n’kumadzuka kukacha. Mbewuzo zimamera ndi kukula. Koma kwenikweni mmene zimenezi zimachitikira, mwini wakeyo sadziwa ayi. Payokha nthaka ija imabala zipatso m’kupita kwa nthawi, choyamba mmera umabiriwira, kenako umatulutsa ngala, pamapeto pake maso okhwima a tirigu amaonekera m’ngalamo. Koma zipatso zikacha, iye amamweta ndi chikwakwa, chifukwa nthawi yokolola yakwana.”
14 Kodi wofesa mbewu ameneyu ndani? Anthu ena m’Matchalitchi Achikhristu amakhulupirira kuti wofesayo ndi Yesu mwini wakeyo. Koma kodi n’zomveka kunena kuti Yesu amagona ndipo sadziwa kakulidwe ka mbewu? Kunena zoona, Yesu amadziwa kakulidwe ka mbewu. Choncho wofesayu, mofanana ndi wa m’fanizo loyamba lija, akuimira olengeza Ufumu, amene amafesa mbewu za Ufumu kudzera m’ntchito yolalikira imene amaigwira mwachangu. Mbewu imene amamwaza pa nthaka ndi mawu amene iwo amalalikira.b
15, 16. Kodi ndi mfundo yotani yokhudza kukula kwa mbewu ndi kukula kwauzimu imene Yesu anafotokoza m’fanizo lake la wofesa mbewu?
15 Yesu akufotokoza kuti wofesayo “amagona usiku n’kumadzuka kukacha.” Zimenezi sizikutanthauza kuti wofesayo akunyalanyaza mbewuzo. Zikungosonyeza zimene zimachitika pa moyo wa anthu ambiri. Mawu a m’vesi limeneli akusonyeza zinthu zochitika mobwerezabwereza kwa nthawi yaitali, kugwira ntchito kukacha ndi kugona usiku. Yesu akufotokoza zimene zimachitika pa nthawiyo. Iye akuti: “Mbewuzo zimamera ndi kukula.” Kenako akuwonjezera kuti: “Koma kwenikweni mmene zimenezi zimachitikira, mwini wakeyo sadziwa ayi.” Apa akutsindika mfundo yakuti kukulako kumachitika ‘pakokha.’c
16 Kodi mfundo ya Yesu pamenepa ndi yotani? Onani kuti iye akutsindika za kukula kwa mbewu ndiponso kuti kukulako kumachitika pang’onopang’ono. “Payokha nthaka ija imabala zipatso m’kupita kwa nthawi, choyamba mmera umabiriwira, kenako umatulutsa ngala, pamapeto pake maso okhwima a tirigu amaonekera m’ngalamo.” (Maliko 4:28) Kukulako kumachitika pang’onopang’ono, chinthu chimodzi panthawi yake. Palibe amene angakakamize kapena kufulumizitsa kukulako. Zimateronso ndi kukula kwauzimu. Kukulako kumachitika panthawi yake pamene Yehova akulola choonadi kukula mu mtima wa munthu amene ali ndi maganizo oyenerera.—Mac. 13:48; Aheb. 6:1.
17. Kodi ndani amasangalala nawo mbewu ya choonadi ikabala zipatso?
17 Kodi wofesayo amakolola nawo bwanji “zipatso zikacha”? Yehova akakulitsa choonadi cha Ufumu m’mitima ya ophunzira atsopano, m’kupita kwa nthawi iwo amafika poti chikondi chawo pa Mulungu chimawalimbikitsa kupereka moyo wawo kwa iye. Amasonyeza kudzipereka kwawoko mwa kubatizidwa m’madzi. M’kupita kwa nthawi, abale amene amapitirizabe kukula mpaka kukhwima mwauzimu amatha kukhala ndi maudindo ena mumpingo. Zipatso za Ufumu zimakololedwa ndi wofesa uja ndiponso ndi olengeza Ufumu ena amene mwina sanafese nawo mbewu imene yabala wophunzira ameneyo. (Werengani Yohane 4:36-38.) Inde, ‘wofesa mbewu ndi wokolola amasangalalira pamodzi.’
-
-
‘Mulungu Ndi Amene Amakulitsa’!Nsanja ya Olonda—2008 | July 15
-
-
b M’mbuyomu magazini ino inafotokoza kuti mbewu ikuimira makhalidwe a munthu ofunikira kukula mpaka kukhwima, ndipo kakulidwe ka makhalidwewo kamakhudzidwa ndi zinthu monga malo ndi anthu okhala nawo. Komabe, onani kuti m’fanizo la Yesu mbewu sikusintha kukhala yoipa kapena yovunda. Ikungokula mpaka kukhwima.—Onani Nsanja ya Olonda ya Chingelezi ya June 15, 1980, masamba 17-19.
c Malo enanso pamene pamapezeka mawuwa ndi pa Machitidwe 12:10 basi, pamene pamati chipata chachitsulo chinatseguka “chokha.”
-