Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Kuthetsa Namondwe Wochititsa Mantha
TSIKU LA YESU linadzazidwa ndi ntchito kuphatikizapo kuphunzitsa makamu a anthu pagombe ndipo pambuyo pake kulongosola zifaniziro mwapadera kwa ophunzira ake. Pamene madzulo afika, iye akuti: “Tiyeni tiwoloke ku gombe lina.”
Ku tsidya la gombe la kum’mawa la Nyanja ya Galileya kuli gawo lotchedwa Dekapoli, kuchokera ku liwu la Chigriki lakuti de’ka, kutanthauza “khumi,” ndi po’lis, “mzinda.” Mizinda ya Dekapoli iri malo apakati a mwambo Wachigriki, ngakhale kuti mosakaikira iyo irinso kwawo kwa Ayuda ambiri. Ntchito ya Yesu mu gawolo, ngakhale kuli tero, iri ndi malire. Ngakhale pa ulendo umenewo, monga mmene tidzawonera, posachedwapa iye akuletsedwa kukhala nthawi yaitali.
Pamene Yesu akufunsa kuti achoke kupita ku gombe lina, ophunzira ake apita limodzi naye mu ngalawa. Komabe kunyamuka kwawo, sikunakhale kosadziwidwa. Mwamsanga ena akukwera ngalawa zawo ndi kupita limodzi nawo. Siliri tsidya lakutali kwambiri. Mchenicheni, Nyanja ya Galileya iri kokha nyanja ya ukulu wa chifupifupi makilomita 21 mulitali ndi ukulu wa makilomita 12 mulifupi.
Yesu momvekera ali wotopa. Chotero mwamsanga pambuyo pakunyamuka ulendo wa pamadzi iye agona pansi kumbuyo kwa ngalawa, ndipo naika mutu wake pa mtsamiro, iye agona tulo tofa nato. Ambiri a atumwiwo ali amalinyero odziwa bwino, popeza anasodza nsomba mokulira pa Nyanja ya Galileya. Chotero akutsogolera kuyendetsa ngalawa.
Komabe umenewo sudzakhala ulendo wosavuta. Chifukwa cha kutentha koposerapo kwa pamwamba panyanja komwe kuli chifupifupi mamita 210 pansi pa malekezero a nyanja, ndi mpweya wozizira kwambiri wa m’mapiri apafupi, nthawi zina mphepo yolimba imatenga malo ndi kupangitsa namondwe wamkulu wa mphepo wamwadzidzidzi pa nyanja. Ichi ndi chimene chikuchitika tsopano. Mwamsanga mafundewo amenya pa ngalawa ndi kugavira mu iyo, kotero kuti iri pafupi kumizidwa. Koma, Yesu akupitirizabe kugona!
Amalinyero odziwa bwino akugwira ntchito molimbika kuti ayendetse bwino ngalawa. Mosakaikira anali atayendetsapo kale mu anamondwe. Koma pa nthawi ino ali pamapeto pa zoyesayesa zawo zonse. Kuwopera miyoyo yawo, iwo akumudzutsa Yesu. ‘Mphunzitsi, kodi simusamala? Tiri kumira!’ anaitana. ‘Tipulumutseni, tiri kumira!’
Pakuuka iye, Yesu analamula mphepo ndi nyanja: ‘Tonthola! khala bata!’ Ndipo mphepo inaleka ndipo nyanja inakhala bata. Kutembenukira kwa ophunzira ake, iye akufunsa: ‘Muchitiranji mantha? Kufikira tsopano mulibe chikhulupiriro kodi?’
Pa icho, ophunzira agwidwa ndi mantha achilendo. ’Mwamunayu ndani kodi?’ anafunsana wina ndi mnzake. ‘Popeza alamula ngakhale mphepo ndi madzi, ndipo zimumvera iye.’
Ndi mphamvu yotani nanga imene Yesu akusonyeza! Chiri chopereka chiyembekezo chotani nanga kudziwa kuti Mfumu yathu iri ndi mphamvu pa zinthu zachilengedwe ndipo kuti pamene chisamaliro chake chonse chilunjikitsidwa ku dziko lathu lapansi mkati mwa ulamuliro wa Ufumu wake, onse adzakhala m’chisungiko kuchokera ku chiwopsyezo cha ngozi zachilengedwe!
Nthawi ina pambuyo pa kuleka kwa namondwe, Yesu ndi ophunzira ake anafika ku gombe la kum’mawa bwino lomwe. Mwina mwake ngalawa zinazo zinachita mantha ndi kukula kwa namondwe ndipo zinabwerera kwawo. Marko 4:35-5:2; Mateyu 8:18, 23-28; Luka 8:22-27.
◆ Kodi Dekapoli nchiyani, ndipo kodi iri kuti?
◆ Kodi ndi zinthu ziti zomwe ziri ndi thayo kaamba ka mphepo yolimba pa Nyanja ya Galileya?
◆ Pamene maluso awo a kuyendetsa ngalawa alephera kuwapulumutsa iwo, nchiyani chimene ophunzira
[Chithunzi chachikulu patsamba 8]