PHUNZIRO 17
Kodi Yesu Ali Ndi Makhalidwe Otani?
Tikamaphunzira zimene Yesu ananena ndi kuchita ali padziko lapansi, timapeza makhalidwe abwino kwambiri amene amachititsa kuti tizimukonda ndiponso kuti tizikonda Atate wake Yehova. Kodi ena mwa makhalidwe abwino kwambiri amene Yesu ali nawo ndi ati? Nanga tingamutsanzire bwanji?
1. Kodi Yesu amafanana ndi Atate wake m’njira ziti?
Kwa zaka mabiliyoni ambiri, Yesu anakhala kumwamba ndi Atate wake wachikondi. Kwa nthawi yonseyi, iye ankaona ndi kuphunzira kuchokera pa zimene Atate wake ankachita. (Werengani Yohane 5:19.) Choncho iye amaganiza, kukhudzika ndi kuchita zinthu ngati Atate wake. Ndipotu Yesu amatsanzira makhalidwe abwino amene Atate wake ali nawo. Mpake ananena kuti: “Amene waona ine waonanso Atate.” (Yohane 14:9) Mukamaphunzira makhalidwe a Yesu, mudzatha kumudziwa bwino Yehova. Mwachitsanzo, chifundo chomwe Yesu ankasonyeza anthu ndi umboni wakuti Yehova amakuderani nkhawa mukamavutika.
2. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti amakonda Yehova?
Yesu anati: “Kuti dziko lidziwe kuti ndimakonda Atate, ndikuchita izi kutsatira lamulo limene Atatewo anandipatsa.” (Yohane 14:31) Yesu ali padziko lapansi, anasonyeza kuti amakonda kwambiri Atate wake mwa kuwamvera ngakhale pamene zinali zovuta kutero. Iye ankakonda kulankhula zokhudza Atate wake ndipo ankathandiza anthu ena kuti nawonso ayambe kukonda Mulungu.—Yohane 14:23.
3. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti amakonda anthu?
Baibulo limasonyeza kuti Yesu amasangalala kwambiri ndi “ana a anthu.” (Miyambo 8:31) Iye anasonyeza kuti amakonda anthu powalimbikitsa ndi kuwathandiza mosanyinyirika. Zozizwitsa zimene anachita sikuti zinkangosonyeza kuti ali ndi mphamvu, koma zinkasonyezanso kuti ndi wachifundo. (Maliko 1:40-42) Iye ankathandiza anthu mokoma mtima komanso mosakondera. Zomwe ankalankhula zinkatonthoza ndi kupereka chiyembekezo kwa anthu a mtima wabwino omwe ankamumvetsera. Yesu analolera kuvutika komanso kufa chifukwa amakonda anthu onse. Komabe iye amakonda kwambiri anthu amene amakonda zimene ankaphunzitsa.—Werengani Yohane 15:13, 14.
FUFUZANI MOZAMA
Fufuzani kuti mudziwe zambiri zokhudza makhalidwe a Yesu ndipo onani zimene mungachite kuti muzimutsanzira pa nkhani yosonyeza chikondi ndi kukhala opatsa.
4. Yesu amakonda Atate wake
Zimene Yesu ankachita zimatithandiza kudziwa zimene tingachite kuti tizikonda Mulungu. Werengani Luka 6:12 ndi Yohane 15:10 komanso 17:26. Pambuyo powerenga lemba lililonse, kambiranani funso ili:
Potengera chitsanzo cha Yesu, tingasonyeze bwanji kuti timakonda Yehova?
5. Yesu amasamalira anthu ovutika
Yesu ankaganizira kwambiri zofuna za anthu ena kuposa zofuna zake. Iye ankayesetsa kugwiritsa ntchito nthawi ndi mphamvu zake pothandiza anthu ngakhale atatopa. Werengani Maliko 6:30-44, kenako mukambirane mafunso awa:
Munkhaniyi, ndi zinthu ziti zimene Yesu anachita posonyeza kuti amaganizira ena?—Onani vesi 31, 34, 41 ndi 42.
Kodi ndi khalidwe liti limene linachititsa kuti Yesu athandize anthuwo?—Onani vesi 34.
Popeza kuti Yesu amatsanzira makhalidwe a Yehova, kodi zimenezi zikukuphunzitsani chiyani zokhudza Yehova?
Ndi zinthu ziti zimene tingachite potsanzira Yesu pa nkhani yoganizira ena?
6. Yesu ndi wopatsa
Ngakhale kuti Yesu analibe zinthu zambiri zakuthupi, ankakonda kugawira ena zomwe anali nazo. Iye amafuna kuti nafenso tizikhala opatsa. Werengani Machitidwe 20:35, kenako mukambirane funso ili:
Malinga ndi zimene Yesu ananena, tizichita chiyani kuti tizikhala osangalala?
Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso ili:
Kodi tingasonyeze bwanji mtima wopatsa ngakhale titakhala kuti tilibe zinthu zambiri?
Kodi mukudziwa?
Baibulo limatiphunzitsa kuti tizipemphera kwa Yehova m’dzina la Yesu. (Werengani Yohane 16:23, 24.) Tikamapemphera m’dzina la Yesu, timasonyeza kuti timayamikira zimene Yesu anachita potithandiza kuti Mulungu akhale mnzathu.
ZIMENE ENA AMANENA: “Mulungu analemberatu zoti tizikumana ndi mavuto.”
Popeza kuti Yesu amatsanzira makhalidwe a Atate wake, kodi zimene amachita zimasonyeza bwanji kuti si Yehova amene amachititsa mavuto athu?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Yesu amakonda Yehova ndi anthu. Popeza kuti Yesu amatengera makhalidwe a Atate wake, mukadziwa zambiri zokhudza Yesu mudzatha kumudziwa bwino Yehova.
Kubwereza
Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda Yehova ngati mmene Yesu amachitira?
Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda anthu ngati mmene Yesu amachitira?
Ndi khalidwe liti la Yesu lomwe limakuchititsani chidwi kwambiri?
ONANI ZINANSO
Onani ena mwa makhalidwe a Yesu omwe tingatsanzire.
“Kuti Mutsanzire Yesu Muyenera . . .” (Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo, tsamba 317)
Onani chifukwa chake tiyenera kupemphera kudzera m’dzina la Yesu.
“N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kupemphera M’dzina la Yesu?” (Nsanja ya Olonda, February 1, 2008)
Kodi Baibulo limanena chilichonse chokhudza mmene Yesu ankaonekera?
Kodi tikuphunzirapo chiyani pa nkhani ya mmene Yesu ankachitira zinthu ndi akazi?
“Mulungu Amafuna Kuti Akazi Azilemekezedwa” (Nsanja ya Olonda, September 1, 2012)