Pamene ‘Mphepo Idza Nikomana Nafe’
Pofotokoza zimene zinachitikiradi ophunzira a Yesu pamene ankavutika kudutsa Nyanja ya Galileya pa bwato, wolemba Uthenga Wabwino Marko anati, anali “kuvutika ndi kupalasa, pakuti mphepo inadza nikomana nawo.” Adakali pagombe, Yesu anaona kusoŵa thandizo kwawo ndipo mozizwitsa anayenda panyanja kuti akawapeze. Pamene iye anakwera, naloŵa kwa iwo m’ngalawa, ndipo mphepo inaleka.—Marko 6:48-51.
Wolemba Baibulo wofananayu anati panthaŵi ina izi zisanachitike “panauka namondwe . . . wa mphepo.” Pamenepo, Yesu ‘anadzudzula mphepo, ndipo mphepoyo inaleka, ndipo kunagwa bata lalikulu.’—Marko 4:37-39.
Ngakhale kuti ife lerolino tilibe mwayi woona zozizwitsa ngati zimenezi, zingatiphunzitse zochuluka. Monga anthu opanda ungwiro amene tikukhala mu nthaŵi zovuta, sitili otetezeka ku mphepo ya nsautso. (2 Timoteo 3:1-5) Ndithudi, nthaŵi zina tingamve kuti kuvutika kwathu pamene tiyesedwa kumakhala kwakukulu ngati namondwe. Koma thandizo lilipo! Yesu akuitana kuti: “Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo ine ndidzakupumulitsani inu.”—Mateyu 11:28.
Pamene kukuonekera kuti ‘mphepo ikudza kukomana nafe,’ tingathe kupeza “bata lalikulu” la mu mtima. Motani? Mwa kudalira malonjezo osalephera a Yehova Mulungu.—Yerekezani ndi Yesaya 55:9-11; Afilipi 4:5-7.