Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Nchiyani Chiipitsa Munthu?
CHITSUTSO kwa Yesu chikhala champhamvupo. Osati kokha ambiri a ophunzira ake akuchoka komanso Ayuda mu Yudeya akufunafuna kumupha iye, monga mmene iwo anachitira pamene iye anali mu Yerusalemu mkati mwa Paskha ya 31 C.E.
Tsopano ndi Paskha ya 32 C.E. Mwachiwonekere, m’chigwirizano ndi chifuno cha Mulungu chakupezeka, Yesu akupita ku Paskha mu Yerusalemu. Ngakhale kuli tero, iye akuchita tero mochenjera chifukwa moyo wake uli m’tsoka. Pambuyo pake iye abwerera ku Galileya.
Yesu mwinamwake ali pa Kapernao pamene Afarisi ndi alembi kuchokera ku Yerusalemu akubwera kwa iye. Iwo akufunafuna maziko pamene angamutsutsire iye pa za kuphwanya lamulo la chipembedzo. “Ophunzira anu alumphiranji miyambo ya makolo?” iwo akufunsa. “Pakuti sasamba manja pakudya.” Ichi sichiri chinachake chofunidwa ndi Mulungu, komabe Afarisi akulingalira icho kukhala chimo lalikulu kusachita mwambo wa miyambo umenewu, umene umaphatikizapo kusamba manja kufika ku zigongono.
M’malo mwa kuyankha chidzudzulo chawo, Yesu akuloza ku kuipa kwawo ndi kuswa kwawo mwadala Lamulo la Mulungu. “Mulumphiranji lamulo la Mulungu chifukwa cha miyambo yanu?” iye akufuna kudziŵa. “Pakuti Mulungu anati, ‘Lemekeza atate wako ndi amako’; ndipo, ‘Wakunenera atate wake ndi amake zoipa, afe ndithu.’ Koma inu munena kuti, ‘Amene aliyense anena kwa atate wake kapena kwa amake: “Icho ukanathandizidwa nacho, nchoperekedwa kwa Mulungu,” iyeyo sadzalemekeza atate wake.’”
Ndithudi, Afarisi amaphunzitsa kuti ndalama, chuma, kapena chirichonse choperekedwa monga mphatso kwa Mulungu chiri cha ku kachisi, ndipo icho sichingagwiritsidwe ntchito kaamba ka chifuno china chiri chonse. Komabe, m’chenicheni, mphatso yoperekedwayo imasungidwa ndi munthu amene waiperekayo. M’njira imeneyi mwana, mwakungonena kokha kuti ndalama zake kapena chuma chiri “korbani”—mphatso yoperekedwa kwa Mulungu kapena ku kachisi—amathawa thayo lake la kuthandiza makolo ake okalamba, amene angakhale osowa kopambanitsa.
Moyenerera okwiyitsidwa pa kukhotetsa Lamulo la Mulungu kwa Afarisi, Yesu akunena kuti: “Inu mupeputsa mawu a Mulungu chifukwa cha miyambo yanu. Onyenga inu, Yesaya ananenera bwino za inu, ndi kuti, ‘Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yawo; koma mitima yawo iri kutali ndi Ine. Koma andilambira Ine kwachabe, ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu.’”
Mwinamwake khamulo linali litachoka kulola Afarisiwo kufunsa Yesu. Tsopano, pamene Afarisi alibe yankho ku chidzudzulo champhamvu cha Yesu kwa iwo, iye akuitanira pafupi khamulo. “Imvani [kwa ine,”] Iye anatero, “nimudziŵitse. Si chimene chilowa m’kamwa mwake chiipitsa munthu; koma chimene chituluka m’kamwa mwake, ndicho chiipitsa munthu.”
Pambuyo pake, pamene iwo alowa m’nyumba, ophunzira ake akufunsa: “Mudziŵa kodi kuti Afarisi anakhumudwa pakumva chonenacho?”
“Mmera wonse umene Atate wanga wa kumwamba sanaubzyala, udzazulidwa,” Yesu akuyankha. “Kawalekeni iwo. Ali atsogoleri akhungu. Ndipo ngati, wakhungu amtsogolera wakhungu, onse aŵiri adzagwa m’mbuna.”
Yesu akuwoneka wozizwitsidwa pamene, m’malo mwa ophunzira, Petro akufunsa kaamba ka kumveketsa bwino ponena za chimene chimaiipitsa munthu. “Kodi inunso mukhala chipulukire?” Yesu akuyankha. “Simudziŵa kodi kuti zonse zakulowa m’kamwa zipita m’mimba, ndipo zitaidwa kuthengo? Koma zakutuluka m’kamwa zichokera mu mtima; ndizo ziipitsa munthu. Pakuti mu mtima muchokera maganizo oipa, zakupha, zachigololo, zachiwerewere, zakuba, za umboni wonama, zamwano; izi ndizo ziipitsa munthu, koma kudya osasamba manja sikuipitsa munthu ayi.”
Yesu pano sakutsutsa ukhondo wa nthaŵi zonse. Iye sakutsutsa kuti munthu safunikira kusamba m’manja asanakonzekere kapena kudya chakudya. M’malo mwake, Yesu akutsutsa kunyenga kwa atsogoleri a chipembedzo amene monyenga amayesa kupambutsa malamulo olungama a Mulungu mwa kuumilira pa miyambo yosazikidwa m’malemba. Inde, ziri ntchito zoipa zimene zimaiipitsa munthu, ndipo Yesu akusonyeza kuti izi zimachokera mumtima mwa munthu. Yohane 7:1; Deuteronomo 16:16; Mateyu 15:1-20; Marko 7:1-23; Eksodo 20:12; 21:17; Yesaya 29:13.
◆ Ndi chitsutso chotani chimene Yesu akuyang’anizana nacho tsopano?
◆ Ndi chidzudzulo chotani chimene Afarisi akupanga, koma molingana ndi Yesu, ndimotani mmene Afarisi mwadala akuswera Lamulo la Mulungu?
◆ Ndi chiyani chimene Yesu akuvumbulutsa kuti ziri zinthu zimene zimaiipitsa munthu?