Kuphunzira Kupembedza Mulungu Kulinga kwa Makolo Okalamba
“Lolani [ana kapena adzukulu] ayambe aphunzire[kupembedza Mulungu, NW] m’banja lawo ndi kubwezera kwa [makolo ndi agogo awo, NW], pakuti ichi ncholandirika pamaso pa Mulungu.”—1 TIMOTEO 5:4.
1, 2. (a) Kodi ndi ndani amene Baibulo limapatsa thayo la kusamalira makolo okalamba? (b) Kodi nchifukwa ninji ingakhale nkhani yovuta kwambiri kwa Mkristu kunyalanyaza thayo lake?
MONGA mwana, munaleledwa ndi kuchinjirizidwa ndi iwo Monga wachikulire, munafuna langizo lawo ndi chirikizo. Koma tsopano akalamba ndipo akufuna wina kuwa chirikiza iwo. Akutero mtumwi Paulo: ‘Koma ngati wamasiye wina ali nawo ana kapena adzukulu, ayambe aphunzire iwo [kupembedza Mulungu, NW] m’banja lawo ndi kubwezera akuwabala awo ndi [agogo awo, NW] pakuti ichi ncholandirika pamaso pa Mulungu. Koma ngati wina sadzisungira mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo am’banja lake, wakana chikhulupiriro iye ndipo aipa koposa wosakhulupirira.”—1 Timoteo 5:4, 8.
2 Zikwi za mboni za Yehova lerolino zimasamalira kaamba ka makolo okalamba. Amachita icho osati kokha kaamba ka “chifundo” (The Living Bible) kapena “ntchito” (The Jerusalem Bible) koma chifukwa cha “kupembedza Mulungu, kunena kuti ulemu kaamba ka Mulungu. Iwo amazindikira kuti kutaya makolo awo panthawi yakusowa kudzakhala kofanana ndi ‘kukana chikhulupiriro (Chachikristu).’—Yerekezani ndi Tito 1:16.
‘Senzani Thayo Lanu’la Chisamaliro
3. Kodi nchifukwa ninji kusamalira makolo kungakhale chitokoso chenicheni?
3 Kuyang’anira makolo okalamba kwakhala chitokoso chenicheni, makamaka kumaiko akumadzulo. Mabanja kaŵirikaŵiri amakhala omwazikana. Ndalama zowonongedwa zakwera osakhoza kuziletsa. Akazi a panyumba kawirikawiri amagwira ntchito zakuthupi. Kusamalira kaamba ka kholo lokalamba kungakhale chotero ntchito yaikulu, makamaka pamene wopereka chisamaliroyo sali wamng’ono iyemwini. “Tsopano tiri mzaka zathu za m’ma 50, ndi ana achikulire ndi zidzukulu omwenso amafuna thandizo,” akutero mlongo yemwe akuyesera kusamalira kaamba ka kholo lake.
4, 5. (a) Kodi Baibulo likusonyeza kuti thayo la chisamaliro kawirikawiri lingagawiridwe ndi ndani? (b) Kodi ndimotani mmene ena analekera thayo lawo kwa makolo awo mu nthawi ya Yesu?
4 Paulo anasonyeza kuti thayolo lingathe kugawiridwa ndi “ana kapena adzukulu.” (1 Timoteo 5:4) Nthawi zina, ngakhale kuli tero, ana amakhala osafunitsitsa ‘kusenza thayo lawo lakusamalira:’ (Yerekezani ndi Agalatiya 6:5. ) “Mlongo wanga wachikulire wangosamba manja ake kuchoka kumkhalidwewo,” akudandaula mkulu mmodzi. Koma kodi njira yoteroyo ingakhale yosangalatsa kwa Yehova? Kumbukirani chimene Yesu kamodzi anauza afalisi: “Mose anati, ‘lemekeza atate ako ndi amako’. . . koma inu munena, “Munthu akati kwa atate wake kapena amake: “Chirichonse chimene ndiri nacho mwachimene inu mungapindule nacho kuchokera kwa ine chiri korban, (kunenakuti, mtulo wa kwa Mulungu, )”’—simulolanso kumchitira kanthu atate wake kapena amayi wake, muyesa achabe mawu a Mulungu mwamwambo wanu.”—Marko 7:10-13.
5 Ngati m’Yuda sanasamalire kuthandiza makolo ake osowa, iye anafunika kokha kutcha zinthu zake “korban”—mphatso yoikidwa pambali kaamba ka kugwiritsira ntchito mu kachisi. (Yerekezani ndi Levitiko 27:1-24. ) Iye mwachiwonekere sanali pansi pachikakamizo chamwamsanga, ngakhale kuli tero, kupereka mphatso yake yoyembekezeredwa. Chotero iye akanasunga (ndipo mosakaikira kugwiritsira ntchito) zinthu zake ku nthawi yosatha. Koma ngati makolo ake anafuna thandizo la ndalama, iye akanathawa kuchoka ku thayo lake modzipereka mwa kulengeza kuti zonse zimene anali nazo zinali “korban.” Yesu anadzudzula kunyengeza koteroko.
6. Kodi nchiyani chimene chingafulumize ena lerolino mofananamo kusiya mathayo awo kwa makolo, ndipo kodi ichi chiri chosangalatsa kwa Mulungu?
6 Mkristu amene amagwiritsira ntchito kudzikhululukira kopanda pake kuchoka kuthayo lake iye mwakutero siali kunamiza Mulungu. (Yeremiya 17:9, 10) zowonadi, mavuto a ndalama, kusoweka kwa umoyo wabwino, kapena mikhalidwe mokulira kungaike malire ndi ku ukulu wotani mmodzi angachite kaamba ka makolo. Koma ena angawone kukhala za mtengo wapatali kuthekera, ndi chinsinsi kuposa umoyo wa makolo awo. Chingakhale chonyengeza chotani nanga ngakhale kuli tero, kulalikira Mawu a Mulungu koma kuwapanga “achabe” ndi kusagwira ntchito kwathu kulinga kwa makolo athu!
Kugwirizana kwa Banja
7. Kodi ndimotani mmene mabanja angagwirizanire mkupereka chisamaliro kwa makolo awo okalamba?
7 Akatswiri ena akuvomereza kuti pamene phokoso libuka lokhudza kholo lokalamba, msonkhano wa banja uyenera kuyitanidwa. Chiwalo chimodzi cha banja chiyenera kunyamula mbali yaikulu ya thayolo. Koma mwakudzilowetsa mu “nkhani ya chinsinsi” modzichepetsa ndi mokhala ndi cholinga, mabanja kawirikawiri apeza njira zakugawanira ntchitoyo. (Miyambo 15:22) Ena okhala kutali kwambiri angakhale okhoza kugawirako ndalama ndi kuwachezera mwa kanthaŵi. Ena angakhale osamalira ntchito kapena okhoza kupereka choyenderamo. Nkulekeranji, popeza kungovomereza kokha kuwachezera makolo mokhazikika kungakhale chogawira chamtengo wapatali. Anatero mlongo mmodzi wamzakazake za m’ma 80 ponena za kuchezera kwa ana ake, “chiri monga chirimbikitso!”
8. (a) Kodi ziwalo zabanja zomwe ziri mu utumiki wa nthawi zonse ziri zopatulidwa mkugawana mu chisamaliro cha makolo awo? (b) Kodi ndi ku utali wotani kumene ena mu utumiki wa nthawi zonse apita m’kukwaniritsa mathayo awo kulinga kwa makolo awo?
8 Mabanja angakumane ndi vuto lowopsya, ngakhale kuli tero, pamene chiwalo chimodzi chiri mu utumiki wa nthawi zonse. Atumiki a nthawi zonse samadzikhululukira iwo eni kuchokera ku mathayo oterowo, ndipo ambiri anali kupanga kuyesayesa kwapadera kupereka chisamaliro chawo kwa makolo awo. Akutero woyang’anira wa dera: “Sitinathe kulingalira nkomwe kuti ndi chovuta chotani mwakuthupi ndi mwamaganizo mmene kusamalira kaamba ka makolo athu kungakhalire, makamaka pamene panthawi imodzimodziyo tikuyesera kukumaniza zifuno za utumiki wa nthawi zonse. Indedi, tabweretsedwa kumalekezero akupirira kwathu ndipo takumva kufunika kwa ‘mphamvu ya ukulu woposa wa munthu.’ ”(2 Akorinto 4:7) Yehova apitirize kuchirikiza oterowo.
9. Kodi ndi chilimbikitso chotani chimene chingaperekedwe kwa awo amene alibe chosankha koma kuleka utumiki wa nthawi zonse kuti asamalire makolo?
9 Panthawi zina, ngakhale kuli tero, pambuyo pofufuzafufuza kuthekera kwina kuli konse, chiwalo chabanja sichikhala ndi chosankha china koma kuleka utumiki wa nthawi zonse. Momvekera, wina angakhale ndi maganizo osakanizika ponena za kuyambanso mwawi wake wa utumiki. ‘Tikudziwa kuti liri thayo lathu Lachikristu kusamalira kaamba ka mayi wanga wokalamba ndi wodwala,’ akutero amene anali kale mishonale. ‘Koma nthawi zina chimawoneka kukhala chachilendo.’ Kumbukirani, ngakhale kuli tero, ‘kuphunzira kupembedza Mulungu kunyumba kuli cholandiridwa mmaso mwa Mulungu.’ (1 Timoteo 5:4) Kumbukirani, kachiwirinso, kuti “Mulungu sali wosalungama kuti aiwale ntchito yanu ndi chikondi munasonyeza ku dzina lake, kuti munatumikira oyera mtima ndikupitiriza kuwatumikira.” (Ahebri 6:10) Banja limodzi lomwe linasiya kumbuyo zaka zambiri za utumiki wa nthawi zonse linati: “Njira imene timachiwonera icho, chiri kokha cha mtengo wapatali kwa ife tsopano kusamalira makolo athu monga mmene chinaliri kwa ife kukhala mu utumiki wa nthawi zonse.”
10. (a) Kodi ndimotani mmene ena angakhale atasiya utumiki wa nthawi zonse popanda chifukwa chenicheni? (b) Kodi ndimotani mmene mabanja ayenera kuwonera utumiki wa nthawi zonse?
10 Mwinamwake, ngakhale kuli tero, ena anasiya utumuki wa nthawi zonse popanda chifukwa chenicheni chifukwa anansi awo anapereka chifukwa chakuti: ‘Suuli womangidwa ndi ntchito ndi mabanja. Chifukwa ninji kuti inu simungasamalire Atate ndi Amayi?’ Komabe, kodi ntchito yolalikira siiri ntchito yofunika kwambiri yomwe ikuchitidwa lerolino? (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Awo amene ali mu utumiki wa nthawi zonae chotero akuchita ntchito yamtengo wapatali koposa. (1 Timoteo 4:16) Kachiwirinso, Yesu anasonyeza kuti, mu mikhalidwe ina, utumiki wa Mulungu uyenera kukhala woyambirira pa nkhani za banja.
11, 12. (a) Kodi nchifukwa ninji Yesu analangiza mwamuna “kulefa akufa ayike akufa a eni okha”? (b) Kodi ndimakonzedwe otani amene mabanja ena apanga pamene pali chiwalo chimene chiri mu utumiki wa nthawi zonse?
11 Mwachitsanzo, pamene mwamuna anakana chiitano cha Yesu kukhala wotsatira wake akumati: “Mundilole ine ndithange ndamuka kuyika maliro a atate wanga, Yesu anayankha: “Leka akufa (mwauzimu) aike akufa a eni okha, koma muka iwe nubukitse mbiri ya ufumu wa Mulungu.” (Luka 9:59, 60) Popeza Ayuda anali kuika akufa awo tsiku lomwe anafalo, chiri chosayenera kuti atate a munthuyo analidi atafa. Mwachiwonekere munthuyo anangofuna kukhala ndi atate ake okalamba kufikira imfa ya tateyo. Komabe, popeza anansi mwachiwonekere anali pafupi kupereka thandizo limeneli, Yesu analimbikitsa munthuyo “kumuka nabukitsa ufumu wa Mulungu.”
12 Mabanja ena mofananamo apeza kuti pamene ziwalo zonse zigwirizana, kawirikawiri zingakonzekeretsedwe kaamba ka mmodzi amene ali mu utumiki wa nthawi zonse kugawana mchisamaliro cha makolo ake popanda kusiya kwake utumiki wa nthatid zonse. Mwachitsanzo, atumiki anthawi zonse ena anathandiza makolo awo kumapeto kwa mlungu kapena pa nthawi ya kupuma. Mokondweretsa, makolo okalamba apitiriza kukakamiza ana awo kukhalabe mu utumiki wa nthawi zonse ngakhale ngati chitaitanira pa kudzipereka kwaumwini kokulira kumbali ya makolo. Yehova molemerera amadalitsa awo amene amaika zikondwerero za Ufumu choyamba—Mateyu 6:33.
“Nzeru” ndi “Kuzindikira” Pamene Makolo Afika Kukhala Nanu
13. Kodi ndi mavuto otani amene angabuke pamene kholo layitanidwa kufika kudzakhala nth ana ake?
13 Yesu anakonzekera kaamba ka mayi wake wamasiye kukhala ndi abale ake okhulupirira. (Yohane 19:25-27) Mboni zambiri mofananamo zaitana makolo awo kusamuka ndi kudzakhala nawo—-ndipo akumana ndi nthawi za chimwemwe zochuluka ndi madalitso monga chotulukapo chake. Komabe, njira za moyo zosagwirizana, kusoweka kwa malo obisa, ndi chipsyinjo chakupereka chisamaliro cha tsiku ndi tsiku kawirikawiri zimapangitsa kutenga makolo kukhala nawo m’nyumba kukhala kokwiyitsa kwa awo amene akukhudzidwa. “Kusamalira amayi kwandipanga ine kukhala wokwinjika mokulira,” akutero Ann, amene apongozi ake amadwala matenda a Alzheimer.”Nthawi zina ndimasowa kuleza mtima kwanga ndi kulankhula mwaukali kwa amayi—ndipo ichi chimandipangitsa ine kudzimva wolakwa”
14, 15. Kodi ndimotani mmene “nzeru” ndi “kulingalira” kungathandizire ‘kumanga’ banja pansi pa mikhalidwe imeneyi?
14 Solomo ananena kuti “nzeru imangitsa nyumba; luntha liikhazikitsa.” (Miyambo 24:3) Ann, mwachitsanzo, anayesera kukhala womvetsetsa vuto la apongozi ake. “Ndimachisunga m’maganizo kuti iwo ali ndi matenda. Ndipo sachita icho ndi cholinga.” Komabe, “pakuti timakhumudwa tonse pa zinthu zambiri. Munthu akapanda kukhumudwa pa mawu iye ndiye munthu wangwiro.” (Yakobo 3:2) Koma pamene mkangano ubuka, sonyezani nzeru mwa kukana kulola kubwezera kumangirira kapena mkwiyo kuyaka. (Aefeso 4:31, 32) Kambitsiranani nkhaniyo monga banja, ndipo funani njira za kupangira kugonjera kapena masinthidwe.
15 Kuzindikira nakonso kumathandiza wina kulankhula mokhutiritsa. (Miyambo 20:5) Mwinamwake kholo lingakhale ndi vuto mkusintha njira yakachitidwe kazinthu ya nyumba yatsopano. Mwinamwake chifukwa cha chiweruzo cholakwika, iye amakhoterera ku kukhala wosagwirizana. Pansi pa mikhalidwe ina, pangakhale popanda chosankha koma kulankhula mwa mphamvu. (Yerekezani ndi Genesis 43: 6-11. ) “Ngati sindinanene ayi kwa mayi wanga,” anatero mlongo wina, “iwo angawononge ndalama zawo zonse.” Mkulu mmodzi, ngakhale kuli tero, amapeza kuti nthawi zina iye angakoke chisamaliro cha mayi wake kaamba ka iye. “Nthawi zambiri pamene kulingalira kulephera, ndimangonena kuti, ‘Mayi, kodi inu mungachite icho kwa ine?’ ndipo amamvetsera.
16. Kodi nchifukwa ninji mwamuna wachikondi ayenera kusonyeza “kulingalira” kulinga kwa mkazi wake? Kodi ndimotani mmene iye angachitire icho?
16 Popeza mkazi kawirikawiri amasenza thayo lokulira la chisamaliro, mwamuna wozindikira adzawona kuti iye sakutopa kwambiri mwa—maganizo, mwakuthupi, kapena mwauzimu. Imatero Miyambo 24:10:“Ukalefuka tsiku la tsoka mphamvu yako ichepa.” Kodi nchiyani chimene mwamuna angachite kuyambitsanso kutenthedwa maganizo kwa mkazi wake? “Mwamuna wanga amabwera kunyumba,” akutero mlongo wina, “ndikuika mmanja ake mondizungulira ine ndikundiuza ndimotani mmene iye amandiyamikirira. Sindikanatha kuchita icho popanda iye!” (Aefeso 5:25, 28, 29) Iye angaphunzirenso Baibulo ndi mzake wa mu ukwati ndipo mokhazikika kupemphera ndi mkazi wake. Inde, ngakhale pansi pa mikhalidwe yovuta kwambiri imeneyi banja “lingamangiriridwe. ”
Nyumba za Chisamaliro cha Okalamba
17, 18. (a) Kodi ndi sitepe lotani limene mabanja ena akakamizidwa kutenga? (b) Mu mikhalidwe yoteroyo, kodi ndimotani mmene ana okula angathandizire makolo awo kusintha?
17 Katswiri mmodzi wodziwa za kuchita ndi okalamba ndi mavuto aukalamba akunena kuti: “Pamafika mfundo pamene banja silikhala ndi kuthekera osatinso ndalama zakusunga [kholo] kunyumba.” Monga mmene mwamuna mmodzi akuchiikira icho: “Tinafika ku utali umene umoyo wa mkazi wanga unalephera kuchokera kukuyesera kupatsa mayi chisamaliro cha maora 24 pa tsiku. Tinalibe chosankha koma kuwaika amayi munyumba za chisamaliro cha okalamba. Koma chinaswa mitima yathu kuchichita ichi.”
18 Nyumba za chisamaliro cha okalamba zingakhale thandizo lopezeka labwino koposa pansi pa mikhalidweyi. Koma, okalamba amene amaikidwa mmalo oterowo kawirikawiri amadabwitsidwa ndi kukhumudwitsidwa, kumadzimva kuti ataidwa. “Mosamalitsa tinalongosola kwa mayi nchifukwa ninji tinayenera kuchita ichi,” akutero mlongo amene tidzamutcha Greta. “Iwo aphunzira kusintha ndipo tsopano amawona malowo monga nyumba.” Maulendo okhazikika nawonso amathandiza makolo kupita mkati mwa kusinthaku ndi kutsimikizira kuwona mtima kwa chikondi chanu kaamba ka iwo. (Yerekezani ndi 2 Akorinto 8:8. ) Kumene utali wa malo liri vuto pitirizani kulankhula nawo mwa lamya, mwa makalata, ndi maulendo apakanthawi. (Yerekezani ndi 2 Yohane 12. ) Mosasamala kanthu za chimenecho, kukhala pakati pa anthu akudziko kuli ndi zobweza m’mbuyo zotsimikizirika. Khalani ‘odera nkhawa ndi zosowa zawo zauzimu.’ (Mateyu 5:3) “Timawapatsa amayi zinthu zowerenga ndipo timayesa kukambitsirana zinthu zauzimu mochulukira monga momwe kungathekere,” akutero Greta.
19. (a) Kodi ndi chisamaliro chotani chimene chiyenera kutengedwa mkusankha ndi kutsogolera nyumba zosamalira makolo okalamba? (b) Kodi ndimotani mmene chimapindulira Mkristu kuchita kuthekera kwake mkusamalira kaamba ka kholo?
19 The Wall Street Journal inasimba pa phunziro la nyumba za chisamaliro 406 za mu U. S. mu zimene “chifupifupi gawo lachisanu linatchedwa kukhala chiwopsyezo chachikulu kwa anthu okhalapo ndipo chifupifupi theka lokha linafikira mikhalidwe yabwinoko yochepera.” Nchachisoni kunena kuti, maripoti oterowo ali mokhumudwitsa ofala. Chotero ngati nyumba za chisamaliro cha okalamba ziri zoyenerera, khalani osamalitsa kusankha imodzi. Pitaniko mwaumwini ndi kuwona ngati iri yoyera, yosu ngidwa bwino, iri ndi ogwira ntchito oyenere tsedwa, mkhalidwe wonga wa kunyumba, ndipo ndi chakudya chokwanira. Tsogolerani monga mmene kungathekere chisamaliro choperekedwa kwa makolo anu. Khalani nkhoswe yawo, kuwathandiza iwo kupewa mikhalidwe yoipa yomwe ingabuke, mwinamwake m’chigwirizano ndi matchuthi a kudziko kapena zosangulutsa. Mwa kuchita kuthekera kwanu kupatsa makolo anu chisamaliro chabwino koposa pansi pa mikhalidweyo, mungathandize kuthetsa malingaliro anu akulakwa omwe mwinamwake angakuvutitseni inu.—Yerekezani ndi-2 Akorinto 1:12.
Opatsa Achimwemwe Olandira Achimwemwe
20. Kodi nchifukwa ninji chiri chofunika kuti ana akhale opatsa achimwemwe?
20 “Chakhala chovuta,” akutero mkazi mmodzi Wachikristu ponena za kusamalira makolo ake. “Ndinayenera kuwaphikira, kuyeretsa, kuchita ndi kulira, kusintha zogonerapo pamene anakodzerapo.” “Koma chirichonse chomwe tinachita kwa iwo,” akutero mwamuna wake, “tinachita mwachimwemwe—mosangalala. Tayesera molimbika kusalola makolo athu kudzimva kuti timadandaula kuti tiyenera kuwasamalira iwo.” (2 Akorinto 9:7) Okalamba kawirikawiri samafuna kulandira thandizo ndipo safuna kukhala cholemetsa pa ena. Chotero khalidwe limene mumasonyeza liri lofunika koposa.
21. (a) Kodi ndimotani mmene makolo angakhalire olandira achimwemwe? (b) Nchifukwa ninji chiri chanzeru kwa kholo kukonzekera pasadakhale kaamba ka ukalamba wake?
21 Pa nthawi imodzimodziyo, khalidwe limene makolo amasonyeza limakhalanso lofunika kwambiri. Akukumbukira mlongo mmodzi: “Chirichonse chimene ndinachita kwa amayi, sichinali chokwanira.” Chotero, makolo, pewani kukhala osalingalira kapena wofunsira mopambanitsa. Ndikonkomwe Baibulo limati “ana sayenera kuwunjikira kaamba ka atate ndi amayi, koma atate ndi amayi kuunjikira ana awo.” (2 Akorinto 12:14) Makolo ena amamaliza ndalama zawo zonse ndi kukhala cholemetsa chosayenerera kwa ana awo. Miyambo 13:22, ngakhale kuli tero, amati: “Wabwino asiira zidzukulu zake cholowa chabwino.” Kumlingo woyenerera, makolo chotero angakonzekere pasadakhale kaamba ka ukalamba wawo, kuika pambali ndalama ndi kupanga makonzedwe ena kaamba ka chisamaliro chawo.—Miyambo 21:5.
22. Kodi ndimotani mmene munthu ayenera kuwonera kuyesayesa koikidwa kusamalira kaamba ka makolo ake okalamba?
22 Paulo anachiika icho bwino pamene iye ananena kuti kusamalira makolo kumafanana ndi “kubwezera.” (1 Timoteo 5:4) Monga mmene mbale mmodzi ananenera: “Amayi anandisamalira ine kwa zaka 20. Kodi nchiyani chimene ndachita m’kuyerekeza ku chimenecho?” Lolani kuti Akristu onse amene ali ndi makolo okalamba mofananamo afulumizidwe ‘kuphunzira kupembedza Mulungu, ku nyumba’ akumadziwa kuti iwo adzafupidwa molemera ndi Mulungu amene amalonjeza awo amene amalemekeza makolo awo: “Kuti ukhale wa nthawi yaikulu pa dziko.”—Aefeso 6:3.
Nsonga Zoyenera Kukumbukira
◻ Kodi ndimotani mmene ena mtsiku la Yesu anafunira kuleka thayo lawo kulinga kwa makolo awo?
◻ Kodi ndani amene ayenera kusamalira kaamba ka makolo okalamba ndipo chifukwa ninji?
◻ Kodi ndi mavuto otani amene mabanja angakumane nawo pamene kholo lifika kukhala nawo, ndipo kodi ndimotani mmene iwo angalakire iwo?
◻ Kodi ndimotani mmene chisamaliro cha nyumba za okalamba chingakhalire chofunika, ndipo kodi ndimotani mmene makolo angathandizidwire kuzolowera?
[Chithunzi patsamba 15]
Msonkhano wa banja ungapangidwe kukambitsirana ndimotani mmene chisamaliro cha makolo chiyenera kugawiridwira
[Chithunzi patsamba 17]
Pamene nyumba za chisamaliro cha okalamba ziri zoyenerera, maulendo okhazikika ali oyenera ku ubwino wa makolo anu mwamaganizo ndi mwauzimu