Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Yesu Apereka Phunziro m’Kudzichepetsa
PAMBUYO pa kuchiritsa m’nyamata wogwidwa ndi chiwanda m’gawo la kufupi ndi Kaisareya wa Filipi, Yesu akukhumba kubwerera kunyumba ku Kapernao. Komabe, iye akufuna kukhala yekha ndi ophunzira ake paulendowo kotero kuti iye angawakonzekeretse iwo mowonjezereka kaamba ka imfa yake ndi mathayo awo pambuyo pake. “Mwana wa munthu aperekedwa m’manja a anthu,” iye akulongosola kwa iwo, “ndipo adzamupha iye, ndipo ataphedwa, adzauka pofika masiku atatu.”
Ngakhale kuti Yesu analankhula kale za ichi, ndipo atumwi atatu m’chenicheni anawona mawalitsidwe mkati mwa kumene “kuchoka” kwake kunalongosoledwa, atsatiri ake anali asanamvetsetsebe ponena za nkhaniyi. Ngakhale kuti palibe m’modzi wa iwo amene akuyesera kukana icho kuti iye adzaphedwa monga mmene Petro anachitira poyambirirapo, iwo akuwopa kumfunsa iye mowonjezereka ponena za icho.
Potsirizira pake iwo afika ku Kapernao, womwe wakhala mtundu wa mudzi wa maziko mkati mwa utumiki wa Yesu. Iwo ulinso mudzi wawo wa Petro ndi unyinji wa atumwi ena. Kumeneko, amuna omwe amasonkhanitsa msonkho wa kachisi amfikira Petro. Mwinamwake akuyesa kumuloŵetsa Yesu m’kuswa mwambo wolandiridwa, iwo akufunsa: “Kodi Mphunzitsi wanu sapereka lupiyalo la msonkho [wa kachisi]?”
“Apereka,” Petro ayankha.
Yesu, yemwe angakhale anafika pa nyumbayo mwamsanga pambuyo pake, akudziŵa za chimene chachitika. Chotero Petro asanabweretse nkhaniyo, Yesu akufunsa kuti: “Simoni, uganiza bwanji? Mafumu a dziko lapansi alandira msonkho kwa yani? Kwa ana awo kodi, kapena kwa akunja?”
“Kwa akunja,” Petro ayankha.
“Chifukwa chake anawo ali aufulu,” Yesu akuwona tero. Popeza atate a Yesu ali Mfumu ya chilengedwe chonse, m’modzi amene akulambiridwa pa kachisi, ndithudi sichiri chifuno cha lamulo kaamba ka Mwana wa Mulungu kupereka msonkho wa kachisi. “Koma kuti tisawakhumudwitse,” Yesu akunena kuti, “pita iwe kunyanja, ukaponye mbedza, nukole nsomba yoyamba kuwedza, ndipo ukaikanula pakamwa pake udzapezamo lupiya [madrakamu anayi]. Tatenga limeneli, nuwapatse ilo pamutu pa iwe ndi ine.”
Pamene ophunzira anafika pamodzi pambuyo pa kubwerera kwawo ku Kapernao, mwinamwake ku nyumba ya Petro, iwo akufunsa: “Ndani kodi ali wopambana mu Ufumu wa Kumwamba?” Yesu akudziŵa chimene chadzutsa funso lawo, pokhala akudziŵa za chimene chinali kuchitika pakati pawo pamene anali kuyenda kumbuyo kwake pobwerera kuchokera ku Kaisareya kwa Filipi. Chotero iye akufunsa kuti: “Munalikutsutsananji panjira?” Atachititsidwa manyazi, ophunzirawo akhala chete, popeza anatsutsana pakati pawo ponena za ndani ali wamkulu pa iwo.
Pambuyo pa chifupifupi zaka zitatu za kuphuzitsa kwa Yesu, kodi chikuwoneka chachilendo kuti ophunzirawo angakhale ndi mtsutsano woterowo? Chabwino, chikuvumbula chisonkhezero champhamvu cha kupanda ungwiro kwa munthu, limodzinso ndi chiyambi chachipembedzo. Chipembedzo cha Chiyuda m’chimene ophunzirawo analeredwa chinagogomezera malo kapena thayo m’zochita zonse. Kuwonjezerapo, mwinamwake Petro, chifukwa cha lonjezo la Yesu la kulandira “mfungulo” zinazake ku Ufumu, anadzimva wapamwamba. Yakobo ndi Yohane angakhale anali ndi malingaliro ofananawo chifukwa cha kuyanjidwa kuchitira umboni mawalitsidwe a Yesu.
Mosasamala kanthu za nkhaniyo, Yesu akukhazikitsa chitsanzo chosonkhezera kuyesa kuwongolera kawonedwe kawo. Iye akuitana kamwana kukaimika iko pakati pawo, kuika manja ake mozungulira iko, ndi kunena kuti: “Ngati simutembenuka nimukhala monga tianato, simudzalowa konse mu ufumu wa kumwamba. Chifukwa chake yense amene adzichepetsa yekha monga kamwana aka, yemweyo ali wopambana mu ufumu wa kumwamba. Ndipo amene adzalandira kamwana kamodzi kotereka chifukwa cha dzina langa, alandira ine.”
Ndi njira yabwino chotani nanga yowongolera ophunzira ake! Yesu sanakwiitsidwe ndi iwo ndi kuwatcha iwo odzikweza, aumbombo, kapena onyada. Ayi, koma iye wachitira chitsanzo kuphunzitsa kwake kowongolera mwa kugwiritsira ntchito ana ang’ono, omwe mwachiwonekere ali odzichepetsa, osadzikweza, ndipo mwachisawawa opanda lingaliro la malo apamwamba pakati pawo. Chotero Yesu akusonyeza kuti ophunzira ake afunikira kukulitsa mikhalidwe imodzimodzi yotereyi imene imasonyeza ana odzichepetsa. Monga mmene Yesu akumalizira: “Pakuti iye wakukhala wamng’onong’ono wa inu nonse, yemweyu ndiye wamkulu.” Mateyu 17:22-27; 18:1-5; Marko 9:30-37; Luka 9:43-48.
◆ Pobwerera ku Kapernao, ndi chiphunzitso chotani chimene Yesu akubwereza, ndipo icho chalandiridwa motani?
◆ Nchifukwa ninji Yesu alibe thayo la kupereka msonkho wa kachisi, koma nchifukwa ninji iye akupereka iwo?
◆ Nchiyani mwinamwake chimene chinathandizira ku kutsutsana kwa ophunzira, ndipo ndimotani mmene Yesu anawawongolera iwo?