Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Maphunziro pa Chisudzulo ndi Chikondi Kaamba ka Ana
YESU ndi ophunzira ake ali pa ulendo wawo wopita ku Yerusalemu kukapezeka pa Paskha wa 33 C.E. Iwo akuwoloka Mtsinje wa Yordano ndi kutenga njira yodzera m’boma la Pereya. Yesu anali m’Pereya milungu yoŵerengeka poyambirira, koma kenaka anaitanidwa ku Yudeya chifukwa chakuti bwenzi lake Lazaro anali kudwala. Pamenepo akali m’Pereya, Yesu analankhula kwa Afarisi ponena za chisudzulo, ndipo tsopano iwo akubweretsanso nkhaniyo.
Pakati pa Afarisi pali magulu osiyanasiyana a lingaliro ponena za chisudzulo. Mose ananena kuti mkazi angasudzulidwe chifukwa cha “kanthu kosayenera mwa iye.” Ena amakhulupirira kuti chimenechi chimalozera kokha ku kusakhala woyera. Koma ena amalingalira “kanthu kosayenera” kuphatikizapo milandu ina yaing’ono kwambiri. Chotero, ndi cholinga chofuna kumuyesa Yesu, Afarisi akufunsa kuti: “Kodi nkuloledwa kuti munthu achotse mkazi wake pa chifukwa chirichonse?” Iwo ali achidaliro kuti chirichonse chimene Yesu adzanena chidzamuloŵetsa iye m’vuto ndi Afarisi omwe ali ndi kawonedwe kosiyana.
Yesu akusamalira funsolo mwa ukatswiri, mosakomera kwa lingaliro la munthu lirilonse, koma kulozera kumbuyo ku kalinganizidwe koyambirira ka ukwati. “Kodi simunaŵerenga,” iye akufunsa, “kuti iye amene adalenga anthu pachiyambi, anawalenga iwo mwamuna ndi mkazi, nati, Chifukwa cha ichi mwamuna adzasiya atate wake ndi amake, nadzaphatikizana ndi mkazi wake, ndipo aŵiriwo adzakhala thupi limodzi? Chotero kuti salinso aŵiri koma thupi limodzi. Chifukwa chake ichi chimene Mulungu anachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.”
Chifuno choyambirira cha Mulungu, Yesu akusonyeza tero, chiri chakuti aŵiri okwatirana akhale limodzi, kuti asasudzulane. Ngati chimenechi chiri tero, Afarisi akuyankha kuti, “nanga chifukwa ninji Mose analamulira kupatsa kalata wa chilekaniro, ndi kumchotsa?”
“Chifukwa cha kuwuma mtima kwanu, Mose anakulolezani kuchotsa akazi anu,” Yesu akuyankha tero, “koma pachiyambi sikunakhala chomwecho.” Inde, pamene Mulungu anakhazikitsa muyezo wowona kaamba ka ukwati m’munda wa Edeni, iye sanapange makonzedwe kaamba ka chisudzulo.
Yesu akupitirizabe kuwuza Afarisi kuti: “Amene aliyense akachotsa mkazi wake, kosakhala chifukwa cha chigololo [Chigriki, por·neiʹa], nadzakwatira wina, achita chigololo.” Iye mwakutero akusonyeza kuti por·neiʹa, chimene chiri mkhalidwe woipa wachisembwere, uli maziko okha ovomerezedwa ndi Mulungu kaamba ka chisudzulo.
Atazindikira kuti ukwati uyenera kukhala kugwirizana kosatha kokhala ndi kokha chimenechi monga maziko kaamba ka chisudzulo, ophunzira akusonkhezeredwa kunena kuti: “Ngati mlandu wa munthu ndi mkazi wake uli wotere, sikuli kwabwino kukwatira.” Nchosakaikiritsa kuti munthu yemwe akukonzekera ukwati ayenera mosamalitsa kulingalira kukhalabe kwa chomangira cha ukwati!
Yesu akupitirizabe kulankhula ponena za umbeta. Iye akulongosola kuti anyamata ena anabadwa osabala, osakhoza kukwatira chifukwa cha kusakula m’zakugonana. Ena apangidwa osabala ndi anthu, mwa kulemazidwa mwankhanza m’zakugonana. Pomalizira, ena amadidikiza chikhumbo chawo cha kukwatira ndi kusangalala ndi mayanjano a kugonana kotero kuti adzipereke iwo eni mokwanira kotheratu ku zinthu zogwirizanitsidwa ku Ufumu wakumwamba. “Amene angathe kulandira ichi [umbeta] achilandire,” Yesu akumaliza tero.
Anthu tsopano akuyamba kubweretsa ana awo ang’ono kwa Yesu. Ophunzira, ngakhale kuli tero, akudzudzula anawo ndi kuyesa kuwathamangitsa, mosakaikira akumafuna kutetezera Yesu ku kudidikizidwa kosafunikira. Koma Yesu akunena kuti: “Lolani tiana tidze kwa ine; musatiletse: pakuti ufumu wa Mulungu uli wa totere. Ndithudi ndinena ndi inu, munthu aliyense wosalandira ufumu wa Mulungu ngati kamwana, sadzaloŵamo konse.”
Ndi maphunziro abwino chotani nanga amene Yesu akupereka pano! Kuti tilandire Ufumu wa Mulungu, ife tiyenera kutsanzira kudzichepetsa ndi kuphunzitsika kwa ana aang’ono. Koma chitsanzo cha Yesu chimachitiranso fanizo mmene kuliri kofunika, makamaka kwa makolo, kuthera nthaŵi ndi ana awo. Yesu tsopano akusonyeza chikondi chake kaamba ka aang’ono mwa kuwatengera iwo m’mikono yake ndi kuwadalitsa. Mateyu 19:1-15; Deuteronomo 24:1; Luka 16:18; Marko 10:1-16; Luka 18:15-17.
◆ Kodi ndi mawonedwe osiyana otani omwe Afarisi ali nawo pa chisudzulo, ndipo chotero ndimotani mmene iwo akuyesera kumuyesa Yesu?
◆ Kodi ndimotani mmene Yesu akuchitira ndi kuyesayesa kwa Afarisi kumuyesa iye, ndipo nchiyani chomwe iye akupereka monga maziko okha kaamba ka chisudzulo?
◆ Kodi nchifukwa ninji ophunzira a Yesu akunena kuti sikwabwino kukwatira, ndipo nchivomerezo chotani chomwe Yesu akupereka?
◆ Kodi nchiyani chomwe Yesu akutiphunzitsa mwa zochita zake ndi ana aang’ono?