-
N’chifukwa Chiyani Muyenera Kudzipereka Ndiponso Kubatizidwa?Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
2. Kodi Yehova amawadalitsa bwanji atumiki ake omwe abatizidwa?
Mukabatizidwa mudzalowa m’banja labwino kwambiri la Yehova. Kenako mudzaona kuti Yehova amakukondani kwambiri m’njira zosiyanasiyana ndipo mudzakhala naye pa ubwenzi wolimba kuposa panopa. (Werengani Malaki 3:16-18.) Mudzayamba kuona Yehova monga Atate wanu ndipo mudzakhala ndi abale ndi alongo padziko lonse lapansi omwe amakonda Yehova komanso omwe amakukondani kwambiri. (Werengani Maliko 10:29, 30.) Komabe, pali zinthu zina zomwe muyenera kuchita musanabatizidwe. Mukufunika kuphunzira zokhudza Yehova, kumukonda komanso kukhulupirira Mwana wake. Kenako mudzipereke kwa Yehova, kutanthauza kuti mumuuze m’pemphero kuti mudzamutumikira moyo wanu wonse. Mukachita zinthu zimenezi n’kubatizidwa mudzakhala ndi mwayi wodzakhala ndi moyo mpaka kalekale. N’chifukwa chake Mawu a Mulungu amanena kuti ubatizo umapulumutsa munthu.—1 Petulo 3:21.
-
-
N’zotheka Kupirira Ena AkamakuzunzaniMungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
Yesu ankadziwa bwino kuti anthu ena am’banja lathu sangagwirizane ndi zimene tasankha zoti tizilambira Yehova. Werengani Mateyu 10:34-36, kenako mukambirane funso ili:
Mogwirizana ndi lembali, kodi achibale athu angachite chiyani tikasankha kutumikira Yehova?
Kuti muone chitsanzo cha zimenezi, onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso lotsatirali.
Kodi mungatani ngati wachibale kapena mnzanu akufuna kuti musiye kutumikira Yehova?
Werengani Salimo 27:10 ndi Maliko 10:29, 30. Pambuyo powerenga lemba lililonse, mukambirane funso ili:
Kodi lonjezoli lingakuthandizeni bwanji achibale kapena anzanu akamakutsutsani?
-