Kukhulupirira Yehova Kumatsogolera ku Kudzipereka ndi Ubatizo
“Khulupirira Yehova, ndipo chita chokoma; khala m’dziko, ndipo tsata chowonadi.”—MASALMO 37:3.
1. Ndi umboni wotani wa anthu anzeru za ku dziko umene umasonyeza kuti chiri chopusa kukhulupirira mwa atsogoleri a anthu?
NDI MWANDANI mmene tingakhulupirire? Mwa atsogoleri a anthu? Zolembera zawo zimasonyeza kuti chiri chopusa kukhulupirira mwa anthu opanda ungwiro. Nkulekelanji, popeza ngakhale anthu anzeru za kudziko amazindikira nsonga imeneyo! Chotero, magazini ya zamalonda ya ku Europe Vision pa nthaŵi imodzi inanena kuti chimene chiri “choipitsitsa ponena za mkhalidwe wamakono chiri chakuti palibe wina aliyense yemwe akuwona njira yotulukira ku icho.” Ndipo wodziŵa mbiri ya zachuma Robert Heilbroner anadziŵa kuti: “Pali chinachake chomwe chikutichecheta ife. Chiri chikaikiro chakuti palibe wina aliyense amene ali mtsogoleri, kuti palibe aliyense yemwe ali wokonzekera kuchita ndi mavuto amene akuthamangira kwa ife.”
2. Nchiyani chimene chinganenedwe ponena za mapindu a sayansi yamakono?
2 Zowona, anthu apanga kupita patsogolo kokulira m’mbali zosiyanasiyana za sayansi. Koma kodi zonsezi zakhala zaphindu? Ayi, izo sizinatero. Monga mmene chinasonyezedwera ndi mkonzi Lewis Mumford: “Lingaliro lakuti zopangapanga ndi kupita patsogolo kwa sayansi kunapereka mapindu olinganizika kwa anthu . . . tsopano lakhala kotheratu losafikirika.” Nkhani mu nsongayi iri mvula ya acid, yomwe ikuwononga nyanja ndi mitsinje ndipo ikuthandizira kuwononga mitengo mu unyinji wa mamiliyoni. M’kuwonjezerapo, mkhalidwe womvetsa chisoni wa dziko—kuwonjezeka kwa upandu, chiŵaŵa, ndi uchigaŵenga, m’kumwa anamgoneka ndi kumwerekera koledzeretsa, ndi m’matenda opatsirana mwa kugonana, ndi mkhalidwe wopanda chitetezero wa zachuma—zonse zimachitira umboni kuti chiri chopanda phindu kuika chikhulupiriro chathu mwa atsogoleri a umunthu.
3. Mawu a Mulungu amapereka uphungu wotani ponena za kumene tiyenera kuika chikhulupiriro chathu?
3 Mawu a Mulungu moyenerera amatichenjeza ife kuti: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye. Mpweya wake uchoka, abwerera kumka ku nthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitaika.” (Masalmo 146:3, 4) Ngati si mwa anthu, chotero ndi mwandani mmene tingaike chikhulupiriro chathu? Tingaike chikhulupiriro chathu mwa Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi, monga mmene timaŵerengera: “Wodala munthu amene akhulupirira Yehova, amene chikhulupiriro chake ndi Yehova.”—Yeremiya 17:7.
Nchifukwa Ninji Kukhulupirira mwa Yehova?
4. Ndi iti imene iri mikhalidwe yodziŵika ya Yehova, ndipo ndimotani mmene iyo imaperekera zifukwa zoyenerera kaamba ka kuika chikhulupiriro chathu mwa iye?
4 Tingakhulupirire mwa Yehova kaamba ka zifukwa zomvekera. Choyamba cha zonse, tingaike chikhulupiriro chathu mwa iye chifukwa cha mikhalidwe yake yodziŵika—chikondi, nzeru, chiweruzo cholungama, ndi mphamvu—ndi mikhalidwe ina yosangalatsa. Mawu ake amatitsimikizira ife kuti iye ali wamphamvuyonse, limodzi la maina ake aulemu likumakhala “Mulungu Wamphamvuyonse.” (Genesis 28:3) Ndi maziko otani nanga kaamba ka kukhulupirira! Palibe ndi mmodzi yemwe amene mwachipambano angalimbane ndi Yehova, ndipo palibe wina amene angaletse zifuno zake. Iye ali wanzeru zonse. Iye samadziŵa kokha mapeto kuchokera ku chiyambi, mtsogolo mukumakhala bukhu lotsegulidwa kwa iye, koma mwa iye mulinso chidziŵitso chonse ndi nzeru, monga mmene zimawonedwera m’ntchito yake yozizwitsa ya chilengedwe. Palibe ndi kalelonse m’zochita zake zonse pamene iye anapanga chophophonya nchimodzi chomwe. (Yesaya 46:10; Aroma 11:33-35) Kuposa chimenecho, Yehova ali wodalirika mwangwiro, Mulungu wa chilungamo ndi chowonadi. Chiri chosatheka kwa iye kunama. (Deuteronomo 32:4; Tito 1:2; Ahebri 6:18) Pamwamba pa zonse, popeza chikondi chopanda dyera chiri mkhalidwe wake wodziŵika kwambiri, icho chanenedwa moyenerera kuti: “Mulungu ndiye chikondi.”—1 Yohane 4:8, 16.
5. Ndi cholembera chotani chimene Mawu a Mulungu ali nacho, kutsimikizira ku kukhulupiririka kwake?
5 Zochita za Yehova ndi mtundu wa anthu zimachitira umboni wowonjezereka kukukhala kwake Mulungu wamphamvuyonse wodalirika, nzeru, chiweruzo cholungama, ndi chikondi. Mose anatsimikizira Aisrayeli kuti Yehova amasunga pangano ndi chikondi cha chifundo ndi awo omwe amamkonda iye ndi kusunga malamulo ake. (Deuteronomo 7:9) Kumayambiriro, Yehova anasunga Nowa wowopa Mulungu ndi banja lake kupyola Chigumula chachikulu. Mulungu anapulumutsa Loti wolungama ndi ana ake a akazi aŵiri kuchokera ku chiwonongeko cha moto cha Sodomu ndi Gomora. Pambuyo pake, Mulungu anatulutsa Aisrayeli kuchokera mu Igupto ndi kuwapatsa iwo dziko la Kanani m’chigwirizano ndi lonjezo lake kwa Abrahamu. (Genesis 7:23; 17:8; 19:15-26) Ndipo kodi Yehova sanapulumutse Ahebri atatu omwe anaponyedwa m’ng’anjo ya moto, limodzinso ndi Danieli kuchokera ku dzenje la mikango?—Danieli 3:27; 6:23.
6. Ndi chitsimikiziro chamakono chotani chimene tiri nacho chakuti kukhulupirira mwa Yehova sikuli kolakwika?
6 Kuti Yehova ali mmodzi mwa amene tingaike chikhulupiriro chathu chikuchitiridwanso umboni ndi zokumana nazo za Mboni zake zamakono. Mwachitsanzo, Adolf Hitler anadzikuza kuti iye akakhoza kuthetsa “mbadwo” wa Mboni za Yehova mu Germany. Koma m’malomwake Hitler ndi gulu lake la chiNazi anathetsedwa, ndipo lerolino gulu limenelo la Mboni lachuluka nthaŵi zambiri m’chiŵerengero chapamwamba cha 119,000. Kuwonjezerapo, m’chenicheni mazana a nkhani za moyo weniweni za Mboni za Yehova zofalitsidwa mu Nsanja ya Olonda ndi magazini inzake ya Galamukani! zimachitira umboni wowonekeratu ku chenicheni chakuti Yehova ndithudi ali Mulungu mwa amene tingakhulupirire.
Chifukwa Chimene Ena Sakhulupirira mwa Yehova
7. Nchifukwa ninji munthu mmodzi ananena kuti iye anali “Woimira Pambali wa Yehova”?
7 Komabe, ndi ochepa chotani nanga lerolino amene amaika chikhulupiriro chawo mwa Yehova! Ngakhale ambiri amene aphunzira za mikhalidwe yake ndi zipambano amalephera kuika chikhulupiriro chawo mwa iye. Nkhani yowonekera mu magazini ya U.S. Catholic (January 1979) inanena za munthu mmodzi woteroyo: “Pamene wosonkhanitsa chidziŵitso anafunsa munthuyo ponena za chipembedzo chimene amakonda, iye anayankha, ‘Ndikhulupirira kuti Ndiri Woimira Pambali wa Yehova.’ Ataitanidwa kulongosola iye analongosola kuti, ‘Ndimakhulupirira zambiridi zimene Mboni za Yehova zimakhulupirira—koma sindikufuna kulowetsedwamo.’” Magaziniyo inachitira ndemanga kuti: “Mboni ya Yehova yodzipereka iribe chosankha koma kulowetsedwamo mozama.”
8. Ndi zinthu zenizeni ziti zimene zimapanga munthu kufuna kuloŵetsedwa m’kutumikira Yehova?
8 Nchifukwa ninji chiri chakuti ena samafuna kudzilowetsamo? Chifukwa chakuti iwo alibe mkhalidwe wabwino wa mtima. Munthu ayenera kukhala “woikidwiratu kaamba ka moyo wosatha.” (Machitidwe 13:48) Monga mmene Yesu anadziŵitsira mu fanizo lake la wofesa, awo obala zipatso amalandira mawu a chowonadi ‘m’mitima yabwino.’ (Luka 8:15) Inde, chowonadi sichisangalatsa kwa osafunitsitsa. Chofunikira chenicheni chiri mtima wowona. Chowonadi cha Mawu a Mulungu sichisangalatsanso kwa awo amene ali onyada. Mkhalidwe wodzichepetsa uli wofunikira. (Yakobo 4:6) M’kuwonjezerapo, chowonadi sichisangalatsa kwa odzikhutiritsa, odzilungamitsa. Koma chimasangalatsa kwa awo amene ali odera nkhaŵa za zosowa zawo zauzimu, omwe ali anjala ndi ludzu kaamba ka chilungamo, ndi omwe amausa moyo ndi kulira pa zonyansa zonse zikuchitika m’dziko lerolino.—Mateyu 5:3, 6; Ezekieli 9:4.
Kukhulupirira Yehova Kumatsogolera ku Kudzipereka
9, 10. (a) Nchiyani chimene chiri choyenerera munthu asanaike chikhulupiriro mwa Yehova, ndipo ndimotani mmene awo amene ali ndi mkhalidwe wabwino wa mtima amavomerezera? (b) Ndi mwandani mmene anthu oterewo amaika chikhulupiriro?
9 Munthu asanaike chikhulupiriro chake mwa Yehova, ayenera kumva ponena za Iye. Koma “adzaitana bwanji pa iye amene sanamkhulupirira? Ndipo adzakhulupirira bwanji iye amene sanamva za iye? Ndipo adzamva bwanji wopanda wowalalikira?” (Aroma 10:14) Pamene atumiki a Yehova alalikira, awo amene ali ndi mkhalidwe wabwino wa mtima amavomereza, monga mmene anachitira ambiri mu Tesalonika wakale. Ponena za awa, Paulo analemba kuti: “Pakulandira mawu a uthenga wa Mulungu simunawalandira monga mawu a anthu, komatu monga momwe ali ndithu, mawu a Mulungu, amenenso achita mwa inu okhulupirira.”—1 Atesalonika 2:13.
10 Kuphunzira ponena za Yehova, a mitima yabwino oterowo amasonyeza chikhulupiriro mwa iye. Ichi chiri chofunika, popeza kuti “wopanda chikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna iye.” (Ahebri 11:6) Chofunikanso chiri kusonyeza chikhulupiriro mwa Mwana wa Mulungu. “Palibe chipulumutso mwa wina aliyense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo”—inde, palibe dzina lina lirilonse loposa lija la Yesu Kristu.—Machitidwe 4:12.
11. Kukhulupirira mwa Yehova kudzapangitsa munthu kutsatira uphungu uti woperekedwa ndi mtumwi Petro?
11 Kukhulupirira mu Mawu a Mulungu, mwa Yehova, ndi mwa Mwana wake Yesu Kristu kudzasonkhezera munthu kulabadira uphungu wa mtumwi Petro kwa Ayuda a m’tsiku lake: “Lapani, bwererani kuti afafanizidwe machimo anu, kotero kuti zidze nyengo zakutsitsimutsa zochokera ku nkhope ya [Yehova, NW].” (Machitidwe 3:19) Mwakutenga chidziŵitso cha Yehova ndi zifuno Zake, munthu amaphunzira kuti chifuno cha Mulungu chiri kukhala mtsatiri wa Yesu Kristu. Monga mmene Petro anachilongosolera icho kuti: “Pakuti kudzachita ichi mwaitanidwa; pakutinso Yesu anamva zoŵaŵa m’malo mwanu, nakusiirani chitsanzo kuti mukalondole mapazi ake.” (1 Petro 2:21) Yesu anachimveketsa bwino chimene chinalowetsedwamo pamene iye ananena kuti: “Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge mtengo wake wozunzirapo nanditsate ine.” (Mateyu 16:24, NW) Chimenecho chimatanthauza kudzipereka iyemwini kwa Yehova Mulungu kuchita chifuniro chake ndi kutsatira mapazi a Yesu Kristu.
Kudzipereka Sikuli Kokha Ntchito Ina
12. Ndimotani mmene liwu lakuti “ntchito” kaŵirikaŵiri limagwiritsiridwa ntchito m’Chikristu cha Dziko?
12 Mu Chikristu cha Dziko liwu lakuti “ntchito” limagwiritsiridwa ntchito mobwerezabwereza m’chigwirizano ndi kukhala Mkristu. Chotero timauzidwa kuti Alaliki a mu United States “amagogomezera ntchito yaumwini kwa Yesu.” Nduna za chipembedzo cha Roma Katolika zimalankhula za “Ntchito ya chipembedzo ya Chikatolika.” M’kuchinjiriza kudziloŵetsamo kwake m’ndale zadziko, wansembe wa Chikatolika pa nthaŵi imodzi ananena kuti: “Kupita m’ndale zadziko kunali kufutukuka kwa ntchito yanga (ya unsembe).” Ndipo makampani a zamalonda amafalitsa kuti “Ntchito Yathu kwa Ogula Athu.” Chotero, m’chenicheni, munthu angakhale ndi ntchito zambiri panthaŵi imodzimodziyo: ntchito ya malonda, ntchito za mayanjano, ntchito za ndale zadziko, ndi ntchito za chipembedzo.
13. Nchiyani chimene chikuphatikizidwa m’kudzipereka kwa Yehova?
13 Komabe, kudzipereka kwa Yehova Mulungu sikuli kokha ntchito ina. Ntchito iri chabe “kumvana kapena pangano la kuchita chinachake mtsogolo.” Koma kupanga kudzipereka kumatanthauza ‘kudzipatulira mwini kotheratu ku utumiki kapena kulambira kwa wokhalako waumulungu kapena kukugwiritsiridwa ntchito kopatulika.’ Anthu ambiri ali okhutiritsidwa kupanga ntchito m’malo mwa kudzipereka. Ichi mosakaikira chimaŵerengera kaamba ka chenicheni chakuti chipembedzo chawo chiri kokha mofanana ndi nyimbo yomvekera kumbuyo. Iyo imakhala yosangalatsa kumvetserako koma simasokoneza ndi chirichonse chimene munthu kwenikweni akufuna kuchita.
14. Nchifukwa ninji ntchito yokha siiri yolandirika kwa Yehova Mulungu?
14 Kudzipereka kwa Mulungu kumapanga kuchita chifuniro chake kukhala chinthu chofunika koposa m’moyo. Chimafuna kuti munthuyo asamalire lamulo loyamba ndipo lalikulu koposa, lotchulidwa ndi Yesu pamene iye ananena kuti: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse ndi moyo wako wonse ndi nzeru zako zonse ndi mphamvu yako yonse.” Yesu anagogomezera mtundu wotheratu wa kutumikira Yehova pamene iye ananena kuti: “Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye aŵiri; pakuti pena adzamuda mmodziyo, ndi kukonda winayo; pena adzakangamira kwa mmodzi, nadzanyoza wina. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa chuma.” (Marko 12:30; Mateyu 6:24) Chotero, mwachimvekere, ntchito yokha siiri yolandirika kwa Yehova.
Nchifukwa Ninji Kumizidwa M’madzi?
15. Ndi chitsanzo chotani chimene Yesu anakhazikitsa ponena za kupanga chisonyezero chapoyera cha chikhulupiriro mwa Mulungu?
15 Nchifukwa ninji kuchitira chithunzi cha kudzipereka kwa Mulungu mwa kubatizidwa? Ngati munthu afuna kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova, iye alibe chosankha china. Chofananacho chiri chowona ngati iye akhumba kudziŵika monga Mkristu, wotsatira wa Yesu Kristu. “Mboni Yokhulupirika,” ya Yehova, Yesu, anakhazikitsa chitsanzo kaamba ka ichi, popeza kuti iye anabatizidwa mu Mtsinje wa Yordano. Popeza Yohane anali kubatiza ochimwa olapa, iye sanamvetsetse chifukwa chimene Yesu anafuna kubatizidwira, koma Yesu anamuuza iye kuti: “Balola tsopano, pakuti kuyenera ife kukwaniritsa chilungamo chonse motero.” (Chivumbulutso 1:5; Mateyu 3:13-17) Chotero Mwana wa Mulungu anapanga chisonyezero chapoyera cha chikhulupiriro chake mwa kudzipereka iyemwini kwa Yehova, kukhazikitsa chitsanzo kaamba ka onse amene akakhumba kuchita chifuniro chaumulungu.
16. Ndi lamulo lotani limene Yesu anapereka kwa otsatira ake ponena za ubatizo, ndipo nchiyani chimene chikusonyeza kuti ophunzira ake anamvera lamulo limenelo?
16 Kuposa chimenecho, mwamsanga asanabwerere kwa Atate wake kumwamba, Yesu analamulira otsatira ake kuti: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate ndi la Mwana ndi la mzimu woyera, ndi kuwaphunzitsa asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” (Mateyu 28:19, 20) Cholembera cha bukhu la Machitidwe chimasonyeza kuti ophunzira a Yesu anamvera mwachangu lamulo limenelo.—Machitidwe 2:40, 41; 8:12; 9:17, 18; 19:5.
17. Nchifukwa ninji kungowaza madzi kokha sikungakhale ubatizo wokwanira?
17 Ndimotani mmene awa anabatizidwira? Kokha mwa kungowaza madzi pa iwo, monga mmene uliri mwambo m’matchalitchi ambiri a Chikristu cha Dziko? Kutalitali! Yesu ‘anakwera kutuluka m’madzi’ pambuyo pa kubatizidwa. Ichi mwachiwonekere chimasonyeza kuti iye anamizidwa m’madzi. (Marko 1:9, 10) M’chenicheni, palibe china chirichonse chimene chikakhala ubatizo, popeza liwu la Chigriki lolembedwa “kubatiza” limatanthauza “kumiza, kuviika.”—Machitidwe 8:36-39.
18. Nchifukwa ninji kumizidwa kuli chizindikiro choyenerera cha kudzipereka kwa munthu kwa Mulungu?
18 Kubatiza koteroko kuli chisonyezero choyenerera cha kudzipereka. Kupita pansi pa madzi kumachitira chitsanzo bwino lomwe kufa kwa munthuyo ku njira yake yakale ya mkhalidwe. Kunyamulidwa kwake kuchoka m’madzi kumachitira chithunzi kuukitsidwa kwake ku njira yatsopano ya moyo. Monga mmene phwando laukwati limathandizira kusindikiza pa mkhalidwe wawo wokwatirana pa mkwatibwi ndi mkwati, choteronso kumizidwa m’madzi pamaso pa mboni kuli mwachiwonekere koyenera kupanga chitsimikiziro chosatha pa wophunzira wopita ku ubatizo. Palibe chikaikiro chirichonse ponena za icho: Mwa chochitika cha kubatizidwa, kudzipereka kwa wina kwa Yehova kuyenera kusindikizidwa kotheratu m’maganizo a wina ndi m’chikumbukiro monga chochitika chofunika kwambiri m’moyo wa wina. Chimaika chizindikiro posinthira pa kudzitumikira kupita ku kutumikira Yehova Mulungu.
19. Nchiti chimene chiri chifukwa chowonjezereka cha kubatizidwira?
19 Lolani kuti tisanyalanyaze chenicheni chakuti ubatizo wa m’madzi uli wofunikira kaamba ka kupeza chikumbumtima chabwino ndi Yehova. Ichi chimamveketsedwa bwino pa 1 Petro 3:21, pamene pamaŵerenga kuti: “Chimenenso chifaniziro chake chikupulumutsani tsopano, ndicho ubatizo, (osati kutaya kwa litsiro lake la thupi, komatu funso lake la chikumbumtima chokoma kwa Mulungu), mwa kuuka kwa Yesu Kristu.”
Kubatizidwa pa Msinkhu Wanji?
20. Nchifukwa ninji makanda sangakhale oyenerera kaamba ka ubatizo?
20 Mawu a Yesu pa Mateyu 28:19, 20 amasonyeza kuti ali awo amene apangidwa kukhala ophunzira ake amene ayenera kubatizidwa. Chotero, chimatsatiranso kuti palibe khanda kapena mwana wamng’ono amene angafikire zifuno za m’Malemba kaamba ka ubatizo. Khanda silingasonyeze chikhulupiriro m’Mawu a Mulungu, mwa Mulungu Mlengi, ndi mwa Mwana wake Yesu Kristu. Khanda silingamvetsetse kuti mzimu woyera uli mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu; ndiponso silingalape za machimo apapitapo ndi kupanga lumbiro lotsimikizirika la kuchita chifuniro cha Mulungu.
21. Kodi chiri choyenera kaamba ka achichepere kubatizidwa?
21 Koma chikuwoneka kuti ena pakati pa anthu a Yehova apita kumbali ina yoipirapo. Makolo ambiri Achikristu amalola ana awo kufikira atafika m’zaka zawo za kumapeto kwa zaka za pakati pa 13 ndi 19 asanabweretse nkhani ya ubatizo. Nthaŵi ndi nthaŵi, timamva za achichepere amene amapanga kudzipereka kogwira ntchito kokha mwakufuna kwa iwo eni. Mwachitsanzo, mwana wamwamuna wosafika zaka 13 wamkulu mofunitsitsa anafuna kubatizidwa. Chotero atate ake ndi akulu ena atatu anakambitsirana ndi wachichepereyo mafunso okonzekeretsedwa kaamba ka awo ofuna kubatizidwa.a Mapeto awo anali akuti, ngakhale kuti anali wachichepere, iye anayenera kubatizidwa monga mtumiki woikidwa wa Yehova Mulungu. Nkulekelanji, popeza kuti opezeka pa Sukulu Yautumiki wa Upainiya mu Bahamas posachedwapa anali atumiki aŵiri anthaŵi zonse omwe anali ndi mwana wamkazi wa zaka khumi wobatizidwa!
22. Pamene makolo amangirira mikhalidwe ya Chikristu mwa ana awo, nchiyani chimene angayembekezere kuchokera kwa ana awo?
22 M’chigwirizano ndi ichi, chikuwoneka kuti makolo ena akulephera. Ndi kuutali wotani kumene iwo akugwiritsira ntchito ‘zomangira zosanyeka ndi moto’ kumangira mikhalidwe ya Chikristu mwa ana awo? (1 Akorinto 3:10-15) Choyamba cha zonse, kuchita tero kumafunikira kuti kulambira koyera kwa Yehova kukhale chinthu chofunika kwambiri m’miyoyo ya makolo. M’kuwonjezerapo, makolowo ayenera kumalabadira uphungu wofunika kwambiri woperekedwa pa Deuteronomo 6:6, 7 ndi Aefeso 6:4. Chotulukapo cha ichi chingakhale chakuti makolo adzafunikira kuletsa ana awo kubatizidwa akali a ang’ono kwambiri, m’malo mofunikira kuwathandiza iwo pambuyo pake.
23. Pamene munthu afika pa nsonga ya kudzipereka ndi ubatizo, nchiyani chimene chimafunikiranso?
23 Pamene munthu wasonyeza kukhulupirira Yehova mwa njira ya kudzipereka ndi ubatizo wa m’madzi, iye ayenera kupitiriza kusonyeza chikhulupiriro chimenecho. Nkhani yotsatira, “Kumatumikira monga Ogwira Ntchito Anzake Okhulupirira a Yehova,” idzatithandiza ife kuyamikira chimene ichi chimaphatikizapo.
[Mawu a M’munsi]
a Ndandanda ya mafunso oyenera kuyankhidwa ndi awo omwe akukhumba kubatizidwa monga Mboni za Yehova amapezeka mu bukhu la Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu. Limakhalapo kwa awo omwe akukonzekera kaamba ka ubatizo.
Kodi Mukayankha Motani?
◻ Ndi nsonga zotani zimene zimawunikira kupusa kwa kuika chikhulupiriro chathu mwa anthu?
◻ Nchifukwa ninji mikhalidwe ya Yehova ndi zochita zake zimatipatsa ife zifukwa zomvekera bwino za kukhulupirira mwa iye?
◻ Nchifukwa ninji kuika chikhulupiriro mwa Yehova kumafunikira kudzipereka ndipo osati kokha ntchito?
◻ Ndimotani mmene makolo angaikire mwa ana awo chikhumbo cha kudzipereka iwo eni kwa Yehova pa msinkhu wachichepere?
[Chithunzi patsamba 10]
Tingaike chikhulupiriro chathu mwa Yehova monga Mpulumutsi Wamkulu