Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Ophunzira Akutsutsana pamene Imfa ya Yesu Iyandika
YESU ndi ophunzira ake ali pafupi ndi Mtsinje wa Yordano, pamene akudutsa kuchokera ku boma la Pereya kuloŵa m’Yudeya. Ena ambiri akuyenda limodzi nawo kupita ku Paskha wa 33 C.E., imene iri kokha mlungu umodzi kapena ingapo kutsogolo.
Yesu akuyenda patsogolo pa ophunzira, ndipo iwo akudabwa ndi kugamulapo kwake kolimba mtima. Kumbukirani kuti milungu yoŵerengeka poyambirira pamene Lazaro anamwalira ndipo Yesu anali pafupi kupita kuchokera ku Pereya kuloŵa m’Yudeya, Tomasi analimbikitsa ena kuti: “Tipite ifenso kuti tikafere naye pamodzi.” Kumbukiraninso kuti pamene Yesu anawukitsa Lazaro, Bwalo Lamilandu Lalikulu Lachiyuda linapanga makonzedwe a kumupha iye. Nchosadabwitsa kuti mantha akugwira ophunzira pamene iwo tsopano akuloŵanso m’Yudeya.
Kuti awakonzekeretse iwo kaamba ka chimene chiri kutsogolo, Yesu akutenga 12 amenewo kupita nawo mseri ndi kuwawuza iwo kuti: “Tawonani, tikwera ku Yerusalemu; ndipo Mwana wa munthu adzaperekedwa kwa ansembe akulu ndi alembi; ndipo iwo adzamweruza kuti ayenera imfa, nadzampereka iye kwa anthu a mitundu; ndipo adzamnyoza iye, nadzamthira malovu, nadzamkwapula iye, nadzamupha; ndipo pofika masiku atatu adzauka.”
Iyi iri nthaŵi yachitatu m’miyezi ya posachedwapa kuti Yesu wawuza ophunzira ake ponena za imfa yake ndi chiwukiriro. Ndipo ngakhale kuti iwo akumvetsera kwa iye, iwo akulephera kumvetsetsa. Mwinamwake chiri chifukwa chakuti iwo amakhulupirira m’kubwezeretsedwa kwa ufumu wa Israyeli pa dziko lapansi, ndipo akuyang’ana kutsogolo kusangalala ndi ulemerero ndi ulemu mu ufumu wa Kristu wa pa dziko lapansi.
Pakati pa apaulendo opita ku Paskha pali Salome, mayi wa atumwi Yakobo ndi Yohane. Yesu watcha amuna amenewa kukhala “Ana a bingu,” mosakaikira chifukwa cha mikhalidwe yawo yotentha ya maganizo. Kwa kanthaŵi aŵiri amenewa asungirira chikhumbo cha kukhala otchuka mu Ufumu wa Kristu, ndipo apanga zikhumbo zawo kudziŵika kwa mayi wawo. Iye tsopano akufikira Yesu chifukwa cha iwo, kugwada pamaso pake, ndi kupempha kaamba ka chiyanjo.
“Ufuna chiyani?” Yesu akufunsa.
“Lamulirani kuti ana anga aŵiri amenewa adzakhale, wina ku dzanja lanu lamanja, ndi wina kulamanzere, mu ufumu wanu.”
Atazindikira magwero a pempholo, Yesu akunena kwa Yakobo ndi Yohane kuti: “Inu simudziŵa chimene mupempha. Kodi mukhoza kumwera chikho nditi ndidzamwere ine?”
“Ife tikhoza,” iwo akuyankha tero. Ngakhale kuti Yesu wangowauza iwo kuti akuyang’anizana ndi chizunzo chowopsya ndipo pomalizira kuphedwa, iwo mwachiwonekere sakumvetsetsa kuti ichi ndicho chimene akutanthauza ndi “chikho” chimene ali pafupi kumwera.
Ngakhale kuli tero, Yesu akuwawuza iwo kuti: “Chikho changa mudzamweradi; koma kukhala ku dzanja lamanja kwanga ndi kulamanzere, sikuli kwanga kupatsa, koma kuli kwa iwo omwe kwakonzedweratu ndi Atate wanga.”
M’kupita kwa nthaŵi atumwi khumi ena akudziŵa chimene Yakobo ndi Yohane achipempha, ndipo akwiya. Mwinamwake Yakobo ndi Yohane anali otchuka m’kutsutsana koyambirira pakati pa atumwi ponena za amene ali wokulirapo. Pempho lawo latsopano likuvumbula kuti iwo sanagwiritsire ntchito uphungu umene Yesu wapereka pa nkhani imeneyi. Mwachisoni, chikhumbo chawo kaamba ka kutchuka chidakali cholimbabe.
Chotero kuti achite ndi mkangano waposachedwa umenewu ndi maganizo oipa omwe iwo wapanga, Yesu akuitana 12 amenewo pamodzi. Powapatsa uphungu mwachikondi, iye akunena kuti: “Mudziŵa kuti mafumu a anthu amadziyesa okha ambuye awo, ndipo akulu awo amachita ufumu pa iwo. Sikudzakhala chomwecho kwa inu ayi; koma amene aliyense akafuna kukhala wamkulu mwa inu, adzakhala mtumiki wanu.”
Yesu wakhazikitsa chitsanzo chimene iwo ayenera kutsanzira, pamene akulongosola kuti: “Monga Mwana wa munthu sanadza kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.” Yesu sanangotumikira kokha chifukwa cha ena koma adzachita tero ku ukulu wa kufera mtundu wa anthu! Ophunzirawo afunikira mkhalidwe wa maganizo umenewo wonga wa Kristu wa kukhumba kutumikira m’malo mwa kutumikiridwa ndi kukhala wochepa m’malo mwa kukhala m’malo otchuka. Mateyu 20:17-28; Marko 3:17; 9:33-37; 10:32-45; Luka 18:31-34; Yohane 11:16.
◆ Kodi nchifukwa ninji mantha tsopano akugwira ophunzira?
◆ Kodi ndimotani mmene Yesu akukonzekeretsera ophunzira ake kaamba ka chomwe chiri mtsogolo?
◆ Kodi ndi pempho lotani limene lapangidwa kwa Yesu, ndipo kodi ndimotani mmene atumwi ena ayambukiridwira?
◆ Kodi ndimotani mmene Yesu akuchitira ndi vutolo pakati pa atumwi ake?