Kodi Baibulo Limadzitsutsa Lokha?
“MULUNGU SAKHOZA kunama,” likulengeza tero Baibulo. (Ahebri 6:18) Chotero ndimotani mmene bukhu lake lingadzazidwire ndi kusagwirizana kowala ndi kutsutsana kowonekera ndipo kumatchedwabe Mawu a Mulungu? Ilo silingatero. ‘Nchifukwa ninji, ngakhale kuli tero, pali kusiyana koteroko?’ mukufunsa tero.
Monga mmene chingayembekezedwere, m’bukhu limene kwa zaka mazana angapo linalembedwanso motopetsa ndi manja ndipo linafunikira kutembenuzidwa mu zinenero zotchuka za dzikolo, kusiyana kwa kalembedwe kwina kunaloŵamo. Koma palibe kulikonse kumene kuli ndi kawonedwe koteroko ndi mphamvu kotero kuti kungapangitse chikaikiro pa kuuziridwa ndi ulamuliro wa Baibulo monga lathunthu. Mwa kusanthula mosamalitsa, komwe kumawoneka kukhala kutsutsana kungasonyezedwe kukhala ndi yankho lowona mtima. Kaŵirikaŵiri, anthu amene amanena kuti Baibulo limadzitsutsa lokha sanapange kufufuza kosamalitsa iwo eni, koma amangolandira chabe lingaliroli lomwe limaikidwa pa iwo ndi awo amene safuna kukhulupirira Baibulo kapena kutsogozedwa ndi ilo. “Wobwezera mawu asanamvetse apusa, nadzichititsa manyazi,” likuchenjeza tero Baibulo pa Miyambo 18:13.
Nthaŵi zina, ena amatsutsa chenicheni chakuti olemba Baibulo nthaŵi zonse samawoneka kukhala ogwirizana pa nkhani zogwirizana ndi ziŵerengero, dongosolo la zochitika, katchulidwe ka mawu, ndi zina zotero. Koma talingalirani: Ngati munayenera kufunsa mboni zowona ndi maso zochulukira za chochitika kulemba zimene anawona, kodi mbiri zonsezo zidzagwirizana kotheratu m’katchulidwe ka mawu ndi tsatanetsatane? Ngati izo zinatero, kodi simudzakaikira za kuwombana pakati pa olembawo? Chotero, kachiŵirinso, olemba Baibulo anavomerezedwa ndi Mulungu kusunga mtundu wawowawo wa kalembedwe ndi chinenero, pamene iye anawona ku icho kuti malingaliro ake ndi nsonga zofunikira zinaperekedwa molondola.
Kugwira mawu kuchokera ku zolembedwa zakale kungasinthidwe pang’ono kuchokera ku ziganizo zoyambirira kukumana ndi zosowa ndi chifuno cha mlembi watsopanoyo, pamene kuli kwakuti akusungirirabe tanthauzo lenileni ndi lingaliro. Chofananacho chinganenedwe ponena za kusonkhanitsa zochitika. Kulibe mmodzi angatsatire dongosolo la zochitika mosamalitsa, pamene wina angandandalitse zochitikazo mogwirizana ndi kuyanjana kwawo ndi malingaliro. Kusiya mawu mofananamonso kungakhale mogwirizana ndi kawonedwe ka wolembayo ndi kusonkhanitsa kwake nkhaniyo. Chotero, Mateyu analankhula za amuna aŵiri akhungu kukhala anachiritsidwa ndi Yesu, pamene kuli kwakuti Marko ndi Luka anatchula mmodzi yekha. (Mateyu 20:29-34; Marko 10:46; Luka 18:35) Mbiri ya Mateyu siiri yotsutsa. Iye akungokhala chabe wachindunji ponena za chiŵerengero, pamene Marko ndi Luka akulunjikitsa chidwi pa munthu mmodzi kwa amene Yesu analunjikitsa kukambitsirana kwake.
Panalinso njira zosiyana zolembera nthaŵi. Mtundu wa Chiyuda unagwiritsira ntchito makalenda aŵiri—kalenda yopatulika ndi kalenda ya kudziko, kapena ya malimidwe,—iriyonse ikuyambira ndi nthaŵi yosiyana ya chaka. Olemba omwe amasiyana mu miyezi ndi tsiku pamene akulozera ku chochitika chimodzimodzicho angakhale anali kugwiritsira ntchito makalenda osiyana. Popeza olemba a ku m’Mawa sikaŵirikaŵiri kuti amagwiritsira ntchito ziŵerengero zosakwanira, mbali za chaka zinali kuŵerengedwa monga zaka zathunthu. Zinali kulinganizidwa ku nambala yathunthu yoyandikana nayo. Dziwani ichi, mwachitsanzo, m’mbiri ya mbadwa yopezeka mu Genesis mutu 5.
Kugwirizanitsa “Zotsutsana”
Koma kodi palibe malemba m’Baibulo omwe amanena zinthu zotsutsana ndi malemba ena? Tiyeni tilingalire ochepa omwe agwidwa mawu ndi osuliza a Baibulo ena.
Pa Yohane 3:22 timaŵerenga kuti Yesu “anabatiza,” pamene kokha titangopita patsogolo pang’ono, pa Yohane 4:2, mbiriyo ikunena kuti “Yesu sanabatize.” Koma monga mmene lemba lonselo likusonyezera, anali ophunzira a Yesu omwe anabatiza m’dzina lake ndi pansi pa chitsogozo chake. Ichi chiri chofanana ndi nkhani mu imene munthu wa bizinesi ndi mlembi wake onse aŵiri angadzinenere kukhala atalemba kalata yachindunji.
Kenaka palinso lemba la pa Genesis 2:2 lomwe limanena kuti Mulungu anapuma “ku ntchito yake yonse.” Kusiyanitsa ndi ichi iri ndemanga ya Yesu pa Yohane 5:17 pamene iye ananena kuti Mulungu “amagwira ntchito kufikira tsopano.” Koma monga mmene mawu ozungulira lembalo akusonyezera, mbiri ya mu Genesis ikulankhula mwachindunji za ntchito ya Mulungu ya chilengedwe chakuthupi, pamene Yesu akulozera ku ntchito ya Mulungu yogwirizana ndi chitsogozo chake cha umulungu ndi chisamaliro kaamba ka mtundu wa anthu.
Kusiyana kwina kowonekera kumapezeka mwa kuyerekeza Eksodo 34:7 ndi Ezekieli 18:20. Lemba loyambalo limanena kuti Mulungu adzabweretsera “chilango ana ndi zidzukulu chifukwa cha mphulupulu ya atate awo,” pamene lomalizira limanena kuti “mwana sadzasenza mphulupulu za atate wake.” Nchifukwa ninji malemba amenewa akuwoneka kukhala otsutsana? Chifukwa iwo saali mkati mwa mawu owazungulira. Santhulani nkhani yowazungulira ndi kakhazikitsidwe. Icho chotero chimakhala chodziŵikiratu kuti pamene Mulungu anatchula chilango kukhala chikubwera osati kokha pa atate komanso pa ana ndi zidzukulu, iye anali kulankhula za chimene chidzatulukapo kwa Aisrayeli monga mtundu ngati iwo anachimwa molimbana ndi iye ndipo anatengedwa mu ukapolo. Kumbali ina, pamene anali kutchula kuti mwana sadzaŵerengera kaamba ka mphulupulu ya atate wake, iye anali kulankhula za kuŵerengera kwaumwini.
Kusiyananso kungapezeke, monga ngati m’mbiri za kubadwa kwa Yesu monga kwalembedwera pa Mateyu 1:18-25 ndi Luka 1:26-38. Koma kodi izo zinasonyeza kutsutsana?
Kodi munayamba mwaŵerengapo mbiri zolembedwa za moyo wa munthu ziŵiri zonena za munthu wotchuka mmodzimodziyo? Ngati ndi tero, kodi munawona kuti mbiri zolembedwa za moyo wa munthu zimenezi zimasiyana popanda kutsutsana kwenikweni? Kaŵirikaŵiri, chimakhala chifukwa cha zitsimikizo zaumwini za wolembayo kapena magwero amene anagwiritsira ntchito. Chimadaliranso pa zimene mkonziyo amaganiza kukhala zofunika kuzilongosola m’nkhani yake, mkhalidwe umene iye akuikulitsira iyo, ndi kukhala ndi khamu limene akulembera m’maganizo. Chotero, mbiri zolembedwa atakhala ndi aŵerengi Achikunja m’maganizo zidzasiyana ndi izo zolembedwa kaamba ka aŵerengi Achiyuda, omwe anamvetsetsa kale ndi kulandira nsonga zina.
Izi ziri kokha zitsanzo zochepa za ndime m’Baibulo zimene, popanda kulinganiza kosamalitsa, zimawoneka kukhala zotsutsana ina ndi inzake. Koma pamene zisanthulidwa mosamalitsa, kumasunga m’maganizo kawonedwe ka wolembayo ndi mawu ozungulira lembalo, iwo saali otsutsana nkomwe koma kokha ndime zomwe zimafunikira kufufuza kowonjezereka. Anthu ambiri amalephera kuika kuyesetsa kofunikira kumeneku, ngakhale kuli tero, akumapeza icho kukhala chopepuka kunena kuti: “Baibulo limadzitsutsa lokha.”
Limafunikira Chidaliro Chathu
Mzimu woyera wa Mulungu unalola olemba Baibulo ufulu wochuluka m’kalembedwe kawo ka zochitika. (Machitidwe 3:21) Chotero, iwo ali okhoza kutulutsa chithunzi chowoneka bwino ndi chowala cha zimene anawona. Kusiyana kwawo, ngakhale kuli tero, m’chenicheni kunakhazikitsa kukhulupirika kwawo ndi kukamba kwawo zowona, kusapereka malo a chinyengo ndi kuwombana. (2 Petro 1:16-21) Pamene kuli kwakuti olemba anasiyana mu mtundu wawo wa kaperekedwe, onse analoza ku njira imodzimodziyo ndipo anali ndi chifuno chimodzi: kusonyeza anthu chimene Yehova Mulungu adzachita kupangitsa mtundu wa anthu kukhala wachimwemwe ndi chimene anthu afunikira kupanga ku mbali yawo kuti alandire chivomerezo cha Mulungu.—Miyambo 2:3-6, 9.
Baibulo liri bukhu limene limasangalatsa mphamvu yathu ya kulingalira. Liri logwirizana ilo lonse. Silimadzitsutsa lokha. Mabukhu onse 66 (mitu 1,189 kapena maversi 31,173 mogwirizana ndi King James Version) amafunikira chikhulupiriro chathu chotheratu. Inde, inu mungakhulupirire Baibulo!
[Bokosi patsamba 6]
Ngati Mupeza Baibulo Kukhala “Lodzitsutsa,” Kodi Chingakhale Chifukwa Chakuti:
◆ Simudziŵa nsonga zina za mbiri yakale kapena miyambo yamakedzana?
◆ Mwalephera kutenga m’malingaliro mawu ozungulira lembalo?
◆ Mwanyalanyaza kawonedwe ka wolembayo?
◆ Mukuyesera kugwirizanitsa malingaliro olakwika achipembedzo ndi chimene Baibulo kwenikweni limanena?
◆ Mukugwiritsira ntchito matembenuzidwe a Baibulo osakhala achindunji kapena akale?
[Zithunzi patsamba 7]
Mateyu ananena kuti amuna aŵiri anachiritsidwa ndi Yesu. Marko ndi Luka anatchula mmodzi yekha. Kodi uku ndi kutsutsana?