Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Kupitanso ku Kachisi
YESU ndi ophunzira ake angothera kumene usiku wawo wachitatu mu Betaniya chifikire kuchokera ku Yeriko. Tsopano kuwala kwa m’mawamawa pa Lolemba, Nisani 10, iwo ali kale pa njira akumapita ku Yerusalemu. Yesu ali ndi njala. Chotero pamene awona mtengo wa nkuyu wokhala ndi masamba ake, apita kwa iwo kukawona ngati ungakhale ndi nkuyu.
Masamba a mtengowo aphuka mwamsanga nyengo yake isanafike, popeza kuti nyengo ya nkuyu imafika mu June, ndipo ino iri nthaŵi ya kumapeto kwa March. Komabe, Yesu mwachiwonekere akulingalira kuti popeza kuti masambawo aphuka mwamsanga, nkuyu nazonso ziyenera kubereka mwamsanga. Koma iye akugwiritsidwa mwala. Masambawo apatsa mtengowo mawonekedwe achinyengo. Yesu kenaka atemberera mtengowo, akumati: “Munthu sadzadyanso zipatso zako nthaŵi zonse.” M’kope lotsatira la magazine ano, tidzakondwera kuphunzira zotulukapo za temberero la Yesu la mtengo wa kuyu umenewo ndi chimene chinali phiphiritso la zimenezi.
Akumayendabe, Yesu ndi ophunzira ake mwamsanga afika ku Yerusalemu. Iye apita kukachisi, kumene anafufuza masana apita. Komabe, lero, akuchitapo kanthu, mongadi mmene anachitira zaka zitatu zapita pamene anabwera ku Paskha mu 30 C.E. Yesu akuthamangitsa ogulitsa ndi ogula m’kachisimo ndi kugubuduza matebulo a osintha ndalama ndi zokhalapo za awo ogulitsa nkhunda. Iye sakuloladi aliyense kunyamula chotengera kulowa nacho m’kachisimo.
Potsutsa awo osintha ndalama ndi ogulitsa nyama m’kachisimo, iye akunena kuti: “Sichinalembedwa kodi, nyumba yanga idzatchedwa nyumba ya kupempheramo anthu amitundu yonse? Koma inu mwaiyesa phanga la achifwamba.” Iwo ali achifwamba chifukwa chakuti afuna malipiro apamwamba kwa awo opanda kwina kopitako koma kungogula kwa iwo nyama zoperekera nsembe. Chotero Yesu akuwona machitachita amalonda ameneŵa kukhala mkhalidwe wolanda kapena uchifwamba.
Pamene akulu ansembe, alembi, ndi akuluakulu a anthu akumva zimene Yesu wachita, iwo afunafunanso njira ya kumuphera iye. Mwakutero iwo akudzitsimikizira kuti ali osasinthika. Komabe, iwo sadziŵa njira yowonongeramo Yesu, popeza kuti anthu onse sakumusiya iye kufuna kumvetsera kwa iye.
Pambali pa Ayuda achibadwa, Akunja nawonso abwera ku Paskha. Awa ndi atembenuki, kutanthauza kuti iwo anatembenuzidwira ku chipembedzo cha Ayuda. Agriki ena, mwachiwonekere atembenuki, afika kwa Filipo ndikumpempha kuti awone Yesu. Filipo apita kwa Andreya, mwinamwake kukamfunsa kaya kukumana koteroko kukakhala koyenera. Yesu mwachiwonekere adakali ku kachisi, kumene Agrikiwo ali okhoza kumuwona.
Yesu akudziŵa kuti wangokhala ndi masiku oŵerengeka okhalabe ndi moyo, chotero akuchitira fanizo bwino lomwe mkhalidwe wake akumati: “Yafika nthaŵi, kuti Mwana wa munthu alemekezedwe. Indetu, indetu, ndinena ndi inu, ngati mbewu ya tirigu siigwa m’nthaka, nifa, ikhala pa yokha iyo; koma ngati ifa, ibala chipatso chambiri.”
Mbewu imodzi ya tirigu ndi ya mtengo waung’ono. Komabe, bwanji ngati iyo idzalidwa m’nthaka ndipo “ifa,” nitaya moyo wake monga mbewu? Iyo kenaka imamera ndipo m’kupita kwa nthaŵi imakula nikhala phesi limene limabala mbewu za tirigu, zambirimbiri. Mofananamo, Yesu ali munthu wangwiro yekha. Koma ngati iye amwalira mokhulupirika kwa Mulungu, akakhala njira yoperekera moyo wosatha kwa okhulupirika okhala ndi mzimu umodzimodzi wa kudzipereka nsembe kumene iye anakuchita. Chotero, Yesu akunena kuti: “Iye wokonda moyo wake adzautaya; ndipo wodana ndi moyo wake m’dziko lino lapansi adzausungira ku moyo wosatha.”
Mosakaikira Yesu sakulingalira za iye yekha, popeza kuti iye kenaka akulongosola namati: “Ngati wina anditumikira ine, anditsate; ndipo kumene kuli ine, komwekonso kudzakhala mtumiki wanga. Ngati wina anditumikira ine, Atate adzamchitira ulemu iyeyu.” Ndi mphotho yozizwitsa chotani nanga ya kutsatira Yesu ndi kumtumikira! Iri mphotho ya kulemekezedwa ndi Atateyo kugwirizana ndi Kristu mu Ufumuwo.
Kulingalira ponena za kuvutika kwakukulu ndi imfa yowawitsa yomwe ikumdikirira, Yesu apitirizabe kumati: “Moyo wanga wavutika tsopano; ndipo ndidzanena chiyani? Atate, ndipulumutseni ine ku nthaŵi iyi.” Kokha ngati chimene chikumdikirira chingapeŵedwe! Komabe, sichidzatero, monga mmene iye akunenera kuti: “Chifukwa cha ichi ndinadzera nthaŵi iyi.” Yesu akuvomerezana ndi kakonzedwe konse ka Mulungu, kuphatikizapo imfa yake ya nsembe. Mateyu 21:12, 13, 18, 19; Marko 11:12-18; Luka 19:45-48; Yohane 12:20-27.
◆ Kodi nchifukwa ninji Yesu akuyembekezera kupeza nkuyu ngakhale kuti siiri nyengo yake?
◆ Kodi Yesu atcheranji awo ogulitsa m’kachisi “achifwamba”?
◆ Kodi ndi njira yanji imene Yesu aliri ngati mbewu ya tirigu imene imafa?
◆ Kodi Yesu akulingalira motani ponena za kuvutika ndi imfa yomdikirira?