MUTU 103
Yesu Anayeretsanso Kachisi
MATEYU 21:12, 13, 18, 19 MALIKO 11:12-18 LUKA 19:45-48 YOHANE 12:20-27
YESU ANATEMBERERA MTENGO WA MKUYU KOMANSO ANAYERETSA KACHISI
YESU ANAYENERA KUFA KUTI ANTHU AMBIRI ADZAPEZE MOYO WOSATHA
Yesu ndi ophunzira ake anakhala ku Betaniya kwa masiku atatu atachoka ku Yeriko. Kenako Lolemba m’mamawa pa Nisani 10, anayamba ulendo wopita ku Yerusalemu. Ali m’njira, Yesu anamva njala ndipo ataona mtengo wamkuyu anapita kuti akathyole nkhuyu. Kodi anazipezadi nkhuyuzo?
Zimenezi zinachitika chakumapeto kwa mwezi wa March koma nkhuyu zinkayamba kupsa mwezi wa June. Koma poti mtengowo unali utatulutsa kale masamba, Yesu ankaganiza kuti akhoza kupezamo nkhuyu zoyambirira. Atafika pafupi anapeza kuti munalibe chilichonse. Chifukwa cha masambawo, anthu ankaona ngati mumtengowo muli zipatso. Kenako Yesu ananena kuti: “Munthu sadzadyanso zipatso zako kwamuyaya.” (Maliko 11:14) Nthawi yomweyo mtengowo unayamba kufota ndipo ophunzirawo anamvetsa tanthauzo la zimenezi tsiku lotsatira.
Pasanapite nthawi yaitali, Yesu ndi ophunzira ake anafika ku Yerusalemu. Atafika anapita kukachisi kumene anali atayendera zinthu za m’kachisi chadzulo lake masana. Koma pa nthawiyi Yesu sanangoyendera kachisi. Iye anachitanso zimene anachita zaka zitatu m’mbuyomo pa nthawi ya Pasika wa mu 30 C.E. (Yohane 2:14-16) Yesu anathamangitsa “ogula ndi ogulitsa m’kachisimo.” Anagubuduzanso “matebulo a osintha ndalama ndiponso mabenchi a ogulitsa nkhunda.” (Maliko 11:15) Iye sanalolenso kuti munthu aliyense amene wanyamula katundu azidutsa m’bwalo la kachisiyo ngati njira yachidule popita mbali ina ya mzindawo.
N’chifukwa chiyani Yesu anathamangitsa osintha ndalama komanso ogulitsa ziweto m’kachisi? Iye ananena kuti: “Kodi Malemba sanena kuti, ‘Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo mitundu yonse’? Koma inu mwaisandutsa phanga la achifwamba.” (Maliko 11:17) Yesu ananena kuti anthu amenewa anali achifwamba chifukwa chakuti ankagulitsa ziweto, zomwe anthu ankagula kuti apereke nsembe, pamtengo wokwera kwambiri. Choncho Yesu ankaona kuti zimene anthuwa ankachita kunali kuba.
Ansembe aakulu, alembi komanso anthu ena audindo atamva zimene Yesu anachita anayambanso kukonza zoti amuphe. Koma panali vuto limodzi. Sankapeza njira yabwino yoti amuphere chifukwa anthu ambiri ankapita kwa Yesu kuti akamve zimene ankaphunzitsa.
Ayuda komanso anthu otembenukira kuchiyuda anabwera ku mwambo wa Pasika. Ena amene anabwera ku mwambowu anali Agiriki. Agirikiwa ankafuna kukumana ndi Yesu ndipo anapempha Filipo ngati zimenezi zingatheke. Iwo anachita zimenezi mwina chifukwa chakuti dzina lakuti Filipo ndi dzina lachigiriki. N’kutheka kuti Filipo ankakayikira ngati zinali zoyenera kuti anthuwo akumane ndi Yesu choncho anakambirana ndi Andireya. Filipo ndi Andireya anapita kukafunsa Yesu za nkhaniyi ndipo pa nthawiyi Yesu anali adakali m’kachisi.
Yesu ankadziwa kuti kwatsala masiku ochepa kuti aphedwe, choncho sakanagwiritsa ntchito nthawi yotsalayi pongofuna kusangalatsa anthu kapena kuchita zinthu kuti atchuke. Iye anayankha atumwi awiriwo powauza fanizo kuti: “Nthawi yafika yakuti Mwana wa munthu alemekezedwe. Ndithudi ndikukuuzani, Kambewu ka tirigu kakapanda kugwa m’nthaka ndi kufa, kamakhalabe kamodzi komweko. Koma kakafa, kamadzabala zipatso zambiri.”—Yohane 12:23, 24.
N’zoona kuti kambewu kamodzi ka tirigu kangaoneke ngati kopanda ntchito. Koma kakabzalidwa, kambewuko ‘kamafa’ kenako kamamera ndipo kakakula kamadzabala zipatso zambiri. Zimenezi ndi zofanana ndi zimene zinachitikira Yesu yemwe anali wangwiro. Yesu anakhala wokhulupirika mpaka nthawi ya imfa yake. Chifukwa cha zimenezi anthu ambiri omwe ali ndi mtima wodzipereka ali ndi mwayi wodzakhala ndi moyo wosatha. N’chifukwa chake Yesu ananena kuti: “Aliyense wokonda moyo wake akuuwononga, koma wodana ndi moyo wake m’dziko lino akuusungira moyo wosatha.”—Yohane 12:25.
Yesu sankangoganizira za madalitso amene iyeyo adzapeze. Tikutero chifukwa iye ananena kuti: “Ngati munthu wafuna kunditumikira ine, anditsatire, ndipo kumene ine ndidzakhala, mtumiki wanga adzakhalanso komweko. Aliyense wonditumikira ine, Atate adzamulemekeza.” (Yohane 12:26) Umenewutu unali mwayi waukulu kwambiri chifukwa anthu amene amalemekezedwa ndi Atate adzalamulira pamodzi ndi Khristu mu Ufumu.
Chifukwa chakuti Yesu ankadziwa kuti avutika kwambiri komanso afa imfa yopweteka, ananena kuti: “Moyo wanga ukusautsika tsopano, ndinene chiyani kodi? Atate ndipulumutseni ku nthawi yosautsayi.” Sikuti Yesu ankafuna kuti alephere kukwaniritsa zimene Atate wake ankafuna. Tikutero chifukwa anapitiriza kunena kuti: “Komabe nthawi imeneyi iyenera kundifikira pakuti ndiye chifukwa chake ndinabwera.” (Yohane 12:27) Yesu ankafunitsitsa kuchita zonse zimene Mulungu ankafuna kuphatikizapo zoti iyeyo apereke moyo wake monga nsembe.