Kodi Muyenera Kukhoma Misonkho?
ANTHU ambiri sakonda kukhoma msonkho. Iwo amaona kuti ndalama zawo zamsonkho zimangowonongedwa pa zinthu zosafunika, zimagwiritsidwa ntchito pa zinthu zosayenera, komanso zimabedwa ndi anthu akatangale. Ena amakana kukhoma misonkho chifukwa chakuti ndalama zamsonkho zimagwiritsidwa ntchito pa zinthu zoipa. Pofotokoza chifukwa chimene sakhomera misonkho, anthu a m’tawuni ina ya ku Middle East anati: “Sitingapereke ndalama zoti akagulire zipolopolo zophera ana athu.”
Anthu a m’madera ambiri amakhalanso ndi maganizo amenewa ndipo izi sizinayambe lero. Pofotokoza mmene ankaonera mfundoyi malinga ndi chikumbumtima chake, malemu Mohandas K. Gandhi, yemwe anali mtsogoleri wachihindu wa ku India, anati: “Munthu amene amathandiza dziko lokonda nkhondo mwa njira iliyonse, ndiye kuti akuthandiza nawo kuchita tchimo. Ndipo munthu aliyense amene amakhoma msonkho, wamng’ono kapena wamkulu, amakhala kuti akuthandiza pa tchimo limene boma limachita.”
Nayenso katswiri wina wofufuza nzeru za anthu amene anakhalapo m’zaka za m’ma 1800, dzina lake Henry David Thoreau, anafotokoza kuti sangakhome msonkho chifukwa chakuti ndalama zamsonkho zimagwiritsidwa ntchito pa zinthu zoipa. Iye anafunsa kuti: “Kodi munthu ayenera kulola kuti wopanga malamulo amusankhire pa zinthu zimene angathe kusankha yekha mogwirizana ndi chikumbumtima chake? Ngati ndi choncho, n’chifukwa chiyani munthu aliyense ali ndi chikumbumtima?”
Nkhani imeneyi imakhudzanso Akhristu chifukwa Baibulo limaphunzitsa momveka bwino kuti Akhristu ayenera kukhala ndi chikumbumtima choyera pa zinthu zonse. (2 Timoteyo 1:3) Komabe, Baibulo limanenanso kuti maboma ali ndi udindo wotolera ndalama zamsonkho. Limati: “Munthu aliyense azimvera olamulira akuluakulu [maboma a anthu], chifukwa palibe ulamuliro umene ungakhalepo kupatulapo ngati Mulungu waulola. Olamulira amene alipowa ali m’malo awo osiyanasiyana mololedwa ndi Mulungu. Chotero pali chifukwa chabwino chakuti anthu inu mukhalire ogonjera, osati chabe chifukwa choopa mkwiyo umenewo, komanso chifukwa cha chikumbumtima chanu. N’chifukwa chake mumakhomanso misonkho, pakuti iwo ndi antchito a Mulungu otumikira anthu, ndipo akukwaniritsa cholinga chimenechi nthawi zonse. Perekani kwa onse zimene amafuna. Amene amafuna msonkho, m’patseni msonkho.”—Aroma 13:1, 5-7.
Pa chifukwa chimenechi, Akhristu a m’nthawi ya atumwi ankadziwika kuti ankakhoma misonkho ngakhale kuti mbali yaikulu ya ndalamazo zinkagwiritsidwa ntchito pothandizira nkhondo. N’chimodzimodzinso ndi Mboni za Yehova masiku ano.a Ndiyeno, kodi n’chifukwa chiyani timakhoma misonkho ngakhale kuti ndalama zamisonkhozo amazigwiritsa ntchito pa zinthu zoti Mkhristu sagwirizana nazo? Kodi Mkhristu ayenera kukhomabe msonkho ngakhale pamene chikumbumtima chake chikumuletsa kutero?
Mmene Nkhani Yokhoma Misonkho Imakhudzira Chikumbumtima
N’zochititsa chidwi kudziwa kuti ndalama zina zamsonkho zimene Akhristu a nthawi ya atumwi ankapereka zinkagwiritsidwa ntchito pa zinthu zokhudzana ndi nkhondo. Ngakhale zinali choncho, Akhristuwa ankaperekabe msonkho n’cholinga chakuti akhale ndi chikumbumtima choyera. Koma pa nkhani ya chikumbumtima yomweyi, Gandhi ndi Thoreau ankaona kuti munthu sufunika kupereka msonkho kuti ukhale ndi chikumbumtima choyera.
Onani kuti Akhristu ankamvera lamulo lopezeka mu Aroma chaputala 13, osati chabe chifukwa choopa kulangidwa komanso ‘chifukwa cha chikumbumtima chawo.’ (Aroma 13:5) Kuti Mkhristu akhale ndi chikumbumtima chabwino amayenera kukhoma misonkho ngakhale zitakhala kuti ndalama zamsonkhozo zikagwiritsidwa ntchito pa zinthu zimene Mkhristuyo amaona kuti ndi zoipa. Kuti timvetse bwino nkhani imeneyi, tiyenera kumvetsa mfundo yofunika kwambiri yokhudza chikumbumtima. Chikumbumtima ndi mphamvu yachibadwa imene imatiuza ngati tachita zabwino kapena zoipa.
Monga Thoreau ananenera, munthu aliyense ali ndi chikumbumtima ngakhale kuti si nthawi zonse pamene chimakhala chodalirika. Kuti tikondweretse Mulungu, chikumbumtima chathu chiyenera kugwirizana ndi mfundo zake. Nthawi zambiri timafunika kusintha mmene timaonera zinthu kuti maganizo athu agwirizane ndi maganizo a Mulungu, chifukwa maganizo ake ndi apamwamba kuposa athu. (Salimo 19:7) Choncho, tiyenera kuyesetsa kumvetsa mmene Mulungu amaonera maboma amene alipowa. Kodi iye amawaona bwanji?
Mtumwi Paulo ananena kuti mabomawa ndi “antchito a Mulungu otumikira anthu.” (Aroma 13:6) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Zikutanthauza kuti iwo amathandiza kuti m’dziko mukhale mtendere komanso amagwira ntchito zofunika kwambiri zothandiza anthu. Ngakhale boma limene limachita zinthu zakatangale zambiri, nthawi zambiri limathandizabe anthu pa nkhani monga zotumiza makalata, zamaphunziro, zozimitsa moto komanso kukhazikitsa mtendere. Mulungu amadziwa zinthu zonse zoipa zimene maboma amenewa amachita. Ngakhale zili choncho, walola kuti mabomawo akhalepo kwa kanthawi ndipo amafuna kuti tizikhoma misonkho posonyeza kulemekeza dongosolo limeneli.
Komabe Mulungu walola mabomawa kuti angolamulira kwa kanthawi. Iye wakonza zoti adzachotse maboma amenewa n’kukhazikitsa Ufumu wake wakumwamba. Ufumuwo udzathetsa mavuto onse amene maboma a anthu abweretsa padzikoli pa zaka zonse zimene akhala akulamulira. (Danieli 2:44; Mateyu 6:10) Koma panopa Mulungu sanalamule Akhristu kuti asamamvere boma mwa kukana kukhoma misonkho kapena kuchita zinthu zina.
Koma bwanji ngati mukuonabe kuti kupereka ndalama zamsonkho zimene zimagwiritsidwa ntchito pa nkhondo n’kuchimwa ngati mmene Gandhi ankaonera? Mofanana ndi mmene kuima pamalo okwera kumatithandizira kuona zinthu bwinobwino, kuzindikira kuti maganizo a Mulungu ndi apamwamba kwambiri kuposa athu kungatithandize kusintha maganizo athu kuti agwirizane ndi ake. Kudzera mwa mneneri Yesaya, Mulungu anati: “Monga momwe kumwamba kulili pamwamba kuposa dziko lapansi, momwemonso njira zanga n’zapamwamba kuposa njira zanu, ndiponso maganizo anga ndi apamwamba kuposa maganizo anu.”—Yesaya 55:8, 9.
Kodi Tiyenera Kumvera Boma pa Chilichonse?
Zimene Baibulo limaphunzitsa zoti tiyenera kumakhoma misonkho sizikutanthauza kuti maboma ali ndi mphamvu zolamula nzika zawo kuchita chilichonse chomwe mabomawo angafune. Yesu anaphunzitsa kuti ulamuliro umene Mulungu wapereka kwa maboma amenewa uli ndi malire. Iye atafunsidwa ngati Mulungu ankaona kuti ndi zoyenera kupereka msonkho ku boma la Aroma lomwe linkalamulira pa nthawiyo, anayankha kuti: “Perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma zinthu za Mulungu muzizipereka kwa Mulungu.”—Maliko 12:13-17.
Boma, kapena kuti “Kaisara,” ndi limene limapanga ndalama. Choncho Mulungu amaona kuti boma lili ndi ufulu wouza anthu kuti azibwezera ndalamazo ku boma mwa kukhoma misonkho. Komabe Yesu anasonyeza kuti boma lililonse siliyenera kutiuza kuti tilipatse “zinthu za Mulungu,” zomwe ndi moyo ndiponso kulambira kwathu. Malamulo a boma kapena zimene likufuna kuti tichite zikakhala kuti zikutsutsana ndi malamulo a Mulungu, Akhristu ayenera “kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.”—Machitidwe 5:29.
Akhristu masiku ano akhoza kukhumudwa ndi mmene ndalama zawo zamsonkho zimagwiritsidwira ntchito, komabe sayesa kusintha zinthu kapena kuukira boma mwa kukana kukhoma misonkho kapena kukana kuchita zinthu zina zimene boma lingawauze. Kuchita zimenezi kungasonyeze kuti iwo sakhulupirira kuti Mulungu adzathetsa mavuto onse a anthu. M’malomwake, iwo amadikira moleza mtima nthawi imene Mulungu adzasinthe zinthu kudzera mu Ufumu wa Mwana wake, Yesu, amene ananena kuti: “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino.”—Yohane 18:36.
Ubwino Wotsatira Mfundo za M’Baibulo
Kutsatira zimene Baibulo limanena pa nkhani ya msonkho, kungakuthandizeni kwambiri. Mungapewe kulandira chilango chimene chimaperekedwa kwa anthu ophwanya malamulo komanso simungamakhale ndi mantha oti mugwidwa. (Aroma 13:3-5) Ndipo chofunika kwambiri n’choti mudzakhala ndi chikumbumtima choyera ndiponso mudzalemekeza Mulungu chifukwa cha khalidwe lanu lotsatira malamulo. N’zoona kuti kukhoma misonkho kungapangitse kuti muziwononga ndalama zambiri poyerekeza ndi anthu amene amazemba misonkho kapena kuchita chinyengo. Komabe, kuchita zimenezi kungalimbitse chikhulupiriro chanu pa zimene Mulungu amalonjeza atumiki ake kuti adzawasamalira. Davide, yemwe analemba nawo Baibulo, anafotokoza mfundo imeneyi motere: “Ndinali mwana, ndipo tsopano ndakula, koma sindinaonepo munthu aliyense wolungama atasiyidwa, kapena ana ake akupemphapempha chakudya.”—Salimo 37:25.
Komanso kumvetsa ndiponso kutsatira lamulo la m’Baibulo lakuti muzikhoma misonkho kudzakuthandizani kukhala ndi mtendere wa mumtima. Mulungu sadzakuimbani mlandu chifukwa cha zimene boma limachita ndi ndalama zanu zamsonkho. Izi ndi zofanana ndi zimene zimachitika ngati mwini wake wa nyumba imene mumachita lendi angagwiritse ntchito ndalama zimene mumapereka pa zinthu zoipa. Boma silingakuimbeni inuyo mlandu chifukwa cha zochita zakezo. Asanaphunzire choonadi, Stelvio, yemwe amakhala m’dziko lina la kum’mwera kwa Ulaya ankafunitsitsa kusintha zinthu m’dziko lawo. Pofotokoza chifukwa chimene anasiyira kuchita zimenezo, iye anati: “Ndinazindikira kuti munthu sangathe kukhazikitsa chilungamo, mtendere, ndi ubale weniweni m’dzikoli. Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene ungasinthe zinthu kuti dzikoli likhale labwino.”
Mofanana ndi Stelvio, inunso ngati mokhulupirika ‘mutamapereka zinthu za Mulungu kwa Mulungu,’ mungakhale ndi chikhulupiriro chakuti mudzakhalapo Mulungu akamadzabweretsa ulamuliro wolungama padzikoli. Ulamulirowu udzathetsa zinthu zonse zopanda chilungamo zimene ulamuliro wa anthu wabweretsa.
[Mawu a M’munsi]
a Kuti mudziwe zambiri pa nkhani yakuti a Mboni za Yehova amakhoma misonkho, onani Nsanja ya Olonda ya November 1, 2002, tsamba 13, ndime 15, ndiponso ya May 1, 1996, tsamba 17, ndime 7.
[Mawu Otsindika patsamba 22]
Timafunika kusintha mmene timaonera zinthu kuti maganizo athu agwirizane ndi maganizo a Mulungu, chifukwa maganizo ake ndi apamwamba kuposa athu
[Mawu Otsindika patsamba 23]
Akhristu akamakhoma misonkho mokhulupirika, amakhala ndi chikumbumtima choyera ndipo amasonyeza kuti akudalira Mulungu kuti awathandiza pa zosowa zawo
[Zithunzi patsamba 22]
“Perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma zinthu za Mulungu muzizipereka kwa Mulungu”
[Mawu a Chithunzi]
Copyright British Museum